Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g91 5/8 tsamba 3
  • Mliri wa Lotale—Njuga ya Padziko Lonse

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mliri wa Lotale—Njuga ya Padziko Lonse
  • Galamukani!—1991
  • Nkhani Yofanana
  • Malotale Kodi Nchifukwa Ninji Ali Otchuka?
    Galamukani!—1991
  • Malotale—Kodi Ndani Amapambana? Kodi Ndani Amalephera?
    Galamukani!—1991
  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
    Nsanja ya Olonda—1989
  • Kodi Ndani Afuna Kukhala Mponda Matiki?
    Galamukani!—1992
Onani Zambiri
Galamukani!—1991
g91 5/8 tsamba 3

Mliri wa Lotale—Njuga ya Padziko Lonse

“ZONSE zimene mumafunikira ndi dola imodzi ndi loto.” Lotolo linali lakupambana lotale ya jackpot ya ku New York ya madola mamiliyoni 45. Dola imodziyo inagula mwaŵi wakupambana. Olotawo anabwera mamiliyoni ambirimbiri. Ataimirira pamzera kukagula matikiti awo, iwo anakambitsirana za zombo ndi makoti aubweya wofeŵa ndi nyumba zazikulu—zinthu zomwe akagula ngati apambana mphotho ya ndalamayo. Panthaŵi ina, m’dziko lonselo, iwo anagula matikiti paliŵiro la matikiti 28,000 pamphindi imodzi. M’masiku atatu omalizira asanachite maere pa matikitiwo, iwo anagula matikiti okwanira 37.4 miliyoni.

M’Japan, nthaŵi zonse bizinesi imakhala pachimake m’malo okwanira 10,000 ovomerezedwa mwalamulo ochitira lotale kumene anthu amathamangira kukagula matiki kaamba ka Year-End Jumbo Takarakuji (Lotale). Pamalo ena a ku Tokyo kumene matikiti asanu a mphotho zoyambirira akusimbidwa kuti anagulitsidwako zaka zakumbuyoko, anthu pafupifupi 300 anali kale pamzere pamene malowo anatsegula kuyamba ntchito. Mkazi wina wachichepere, yemwe anakhulupirira kuti mwaŵi umayanja mbalame yoyamba, anakhala akudikirira chiyambire 1:00 a.m. Jackpot yokhumbidwa koposa ya chaka chatha inali ya mtengo wa: 100 miliyoni yen ($714,285, U.S.).

Ku likulu la Kumadzulo kwa Afirika, dera limene anthu akumaloko amalitcha Lotto College nthaŵi zonse limadzazidwa ndi anthu obwera kudzagula matikiti ndi kulingalira za manambala amtsogolo. Mizera yaitali ya manambala opambana akale imagulitsidwa kwa awo oyembekezera kupezamo mfungulo ya zamtsogolo. Kwa awo amene amakhulupirira chidziŵitso chachinsinsi, aneneri a lotale amakhalapo kuti alosere manambala obetchera, kenaka nkuwapatsa malipiro.

Kodi izi nzochitika za apa ndi apo? Kutalitali. Mliri wa lotale ngwachaola. Umakuta kontinenti iriyonse. Ukuchitika m’maiko olemera ndi osauka omwe. Umasangalatsa achichepere ndi okalamba okhala pa mlingo uliwonse m’zachuma, mayanjano, ndi maphunziro m’chitaganya.

Inde, malotale ndi bizinesi yaikulu, ndipo bizinesiyo ikunka patsogolo. Mu United States mokha, malotale Aboma anapeza phindu la madola zikwi 18.5 miliyoni mu 1989. Zaka 27 zokha zapitazo, chiŵerengero chimenecho chinali ziro. Koma tsopano malotale ndiwo mtundu wachiŵiri waukulu koposa wa kutchova njuga mu United States, ndipo indasitaleyo ikukula ndi 17.5 peresenti chaka chirichonse, mofulumira kufanana ndi indasitale ya makompyuta.

Mogwirizana ndi ziŵerengero zaposachedwapa zomwe ziripo kuchokera m’magazini a Gaming and Wagering Business, zinthu zogulitsidwa pa lotale padziko lonse mu 1988 zinafika pa chiwonkhetso chachikulu cha madola zikwi 56.38 miliyoni. Chimenechi chikufika ku oposa madola khumi kwa mwamuna aliyense, mkazi, ndi mwana okhala padziko lapansi! Ndipo chimenecho nchiŵerengero cha chaka chimodzi chokha!

Pamene kuli kwakuti palibe amene angakane kuti malotale akukhupuka, ambiri amatsutsana nawo. Nkhani ziŵiri zotsatirazi zidzasanthula kutchuka komakulakula kwa malotale ndi mkangano womwe ulipo. Pamene mukulingalira mfundozo, mudzakhala wokhoza kusankha kaya ngati mungachite lotale. Kodi ndimaseŵera abwino? Kodi kupambana nkokhweka motani? Kodi mungataye zoposa ndalama zokha?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena