Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g91 5/8 tsamba 7-9
  • Malotale—Kodi Ndani Amapambana? Kodi Ndani Amalephera?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Malotale—Kodi Ndani Amapambana? Kodi Ndani Amalephera?
  • Galamukani!—1991
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Chiyambukiro pa Osauka
  • Ndi Nkhani ya Makhalidwe Abwino
  • Malotale Kodi Nchifukwa Ninji Ali Otchuka?
    Galamukani!—1991
  • Mliri wa Lotale—Njuga ya Padziko Lonse
    Galamukani!—1991
  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
    Nsanja ya Olonda—1989
  • Chidziŵitso pa Nyuzi
    Nsanja ya Olonda​—1990
Onani Zambiri
Galamukani!—1991
g91 5/8 tsamba 7-9

Malotale—Kodi Ndani Amapambana? Kodi Ndani Amalephera?

CHIFUKWA chenicheni choyanja malotale aboma nchakuti amabweretsera boma madola mamiliyoni ambiri, ndalama zomwe mwinamwake sakanatha kuzipeza mwakungokweza misonkho. ‘Ndipo nchokhweka chotani nanga!’ amatero ochilikiza. Nkofanana ndi msonkho umene palibe munthu amene afunikira kuulipira; ngodzifunira mwaufulu. Kwenikweni, anthu ngofunitsitsa kuulipira; amadikirira pamzera kuti alipire!

Koma kodi nziti zomwe ziri zinenezo zina zotsutsana ndi malotale?

Chimodzi nchakuti kulengeza lotale kaŵirikaŵiri kumapereka chidziŵitso chosakwanira kapena kumangosokeretsa. Iwo amachilikiza lingaliro lakuti mudzapambana. Kodziŵika koposa ndi kulengeza lotale kwa ku Canada komwe kumati: “Timaikhweketsa kuti . . . MUPAMBANE!!”

Koma kodi kupambana nkokhweka motani? Alie amaseŵera lotale ya Kumadzulo kwa Jeremani. Kulengezako kumati: “Mwaŵi wanu wakuti mungapambane ngwaukulu zedi.” Komabe, Alie akudandaula motere: “Ndakhala ndikuseŵera lotale kwa zaka khumi, ndipo sindinapambanepo kalikonse. Ndipo sindidziŵanso munthu aliyense amene anapambanapo kalikonse.”

Kwa wopambana mphotho yaikulu aliyense, pamakhala mamiliyoni ambiri olephera monga Alie, amene amataya ndalama zawo mlungu ndi mlungu, chaka ndi chaka, koma omwe samapeza kanthu kowabwezera. Mu United States, anthu amene amapambana $1 miliyoni ngokwanira 0.000008 peresenti ya otchova njuga ya lotale okwanira 97 miliyoni a kumeneko.

Mwaŵi wakupambana mphotho yapamwamba suli kokha umodzi mwa miliyoni (pafupifupi kufanana ndi tsoka lakukanthidwa ndi mphenzi); angakhale mmodzi mwa mamiliyoni ambirimbiri. Mwachitsanzo, pamene kunakhala komvekera kuti ngati jackpot njaikulu, pamakhala matikiti ambiri amene amagulitsidwa, mwaŵi wakupambana maseŵera a Lotto a ku New York unakwera kuchokera pa 1 mu 6 miliyoni kufika ku 1 mu 12.9 miliyoni!

Nzosadabwitsa kuti anthu amazenga malotale mlandu wokakamiza ogula opusa osazindikira masoka otsutsana nawo. Dr. Valerie Lorenz, wotsogoza wa U.S. National Center for Pathological Gambling, akufotokoza mokhweka kuti: “Malotale? Ndiwo kubetcha kotha ndalama zedi komwe kulipo. Ziyembekezo za kulephera nzazikulu.”

Ndipo bwanji ngati mungapambanedi madola miliyoni imodzi? Simudzazilandira zonsezo. Pambuyo pakuti amsonkho achotsako ndalama zawo, opambana mu United States amalandira $35,000 chaka chirichonse kwa zaka 20. Zimenezo ndi ndalama zokwanira $700,000, zomwe zimachepetsedwabe ndi kukwera mitengo kwa zinthu m’nyengo ya zaka 20 zimenezo.

Chiyambukiro pa Osauka

Chisulizo china nchakuti anthu amene amawononga ndalama zambiri ngosauka, awo omwe sali okhoza kwenikweni kuzikwanitsa. Ochilikiza lotale amatsutsa kuti zimenezi sizowona, akumanena kuti kufufuza kukusonyeza kuti lotale njotchuka kwambiri pakati pa anthu olandira ndalama zachikatikati. Iwo amati malotale ngodzifunira mwaufulu; palibe amene amakakamizidwa kuwaseŵera. Komabe, kulengeza kumadzutsa dala zikhumbo za oseŵerawo, ndipo ambiri ndi anthu osauka. Wolandira ndalama m’sitolo yogulitsira zakudya wina mu Florida ananena kuti: “Tiri ndi anthu akutiakuti omwe timawawona mlungu uliwonse. Ena amagula matikiti 10 tsiku lirilonse. Ena amagula 100 mlungu uliwonse. Iwo alibe ndalama zogulira chakudya, koma amaseŵerabe ‘Lotto.’”

M’maiko ena osatukuka kwambiri, mkhalidwewo ngoipirako. Posachedwapa boma la Indonesia linasanthulanso lotale yake ya maseŵera a mpira ya Porkas pamene ofalitsa nkhani anasimba kuti midzi yonse “inachita msala ndi Porkas.” Magazini a Asiaweek anasimba kuti: “Manyuzipepala [a ku Indonesia] anali odzaza ndi zochitika zochititsa mantha: amuna akumenya akazi awo kapena ana; ana akumaba ndalama kwa makolo awo; ana akumawononga ndalama zovutikiridwa zoikidwa pambali kaamba ka malipiro a sukulu—zonsezo kaamba ka Porkas.”

Anthu owonjezerekawonjezereka akuphunzitsidwa kutchova njuga chifukwa cha kufalikira kwa malotale padziko lonse. Ena, osati osauka okha, amakhala otchova njuga anthaŵi zonse—omwerekera ndi lotale. Arnie Wexler amayang’anira bungwe la Council on Compulsive Gambling ku New Jersey, U.S.A. Iye akuti: “Opanga malamulo amaganiza kuti apeza njira yosavuta, yokhweka yopezera ndalama, pamene kwenikweni, iwo akusakaza mabanja ambiri, ndi mabizinesi ambiri, ndi anthu ambiri, ndi miyoyo yambiri.”

Ndi Nkhani ya Makhalidwe Abwino

Chodetsa nkhaŵa china chachikulu nchakuti malotale aboma asintha kulingalira kwa anthu ponena za kutchova njuga. Malotale amakono otsogozedwa ndi Boma onga ngati “Play 3” kapena “Lucky Numbers” amapereka mwaŵi wa chikwi chimodzi kufika ku chimodzi koma amangobweza mphotho ya ndalama yokwanira 50 peresenti yokha. Boma lisanaloŵe m’bizinesiyo, maseŵerawo ankawonedwa kukhala “ankhalwe,” malonda oletsedwa, machenjera oipa. Tsopano maseŵera amodzimodziwo akutchedwa osangulutsa, okondweretsa, kachitidwe ka thayo lalamulo!

Ndithudi, kusiyana kofunika pakati pa maseŵera a manambala osakhala alamulo ndi malotale aboma nkwakuti mmalo mwakuti mapindu apite m’matumba a apandu, iwo amachilikiza maprojekiti aboma. Komabe, openyerera ambiri amadera nkhaŵa ndi chisonkhezero chimene malotale ali nacho pa makhalidwe abwino a chitaganya chimene amalingaliridwa kuti amachipindulitsa.

Ichi nchifukwa chakuti malotale amachilikiza chiyembekezo ndi chikhoterero chakukhala wolemera popanda kuchitapo kanthu kwenikweni. Paul Dworin, mkonzi wa Gaming and Wagering Business, anati: “Nthaŵi zakale, boma linanena kuti ngati mutagwira ntchito zolimba, mudzachita bwino. Tsopano limati, ‘Gulani tikiti ndipo mudzakhala mpondamatiki.’ Umenewu ndi uthenga wachilendo umene boma likupereka.” Ndipo George Will analemba mu Newsweek kuti: “Ngati anthu amakhulupirira kwambiri kufunika kwa mwaŵi, za mwadzidzidzi, za apa ndi apo, ndi choikidwiratu, iwo samakhulupirira kwenikweni kufunika kwa mikhalidwe yamphamvu yonga ngati kukangalika, ukhwima, kuika patali chikhutiro, khama, ndi kuphunzira.”

Lingaliro lina, lomwe nlalikulu ku chitaganya cha anthu, ndi ili: Anthu sayenera kuyesera kupeza phindu kuchokera ku masoka a ena. Komabe, ochilikiza malotale amalimbikitsa lingaliro lakuti nkwabwino kwa munthu kupeza phindu ndi chisangalalo kuchokera m’kulephera kwa ena. Kulingalira koteroko nkwadyera; kumaswa chenjezo la Baibulo ili: “Uzikonda mnzako monga udzikonda iwe mwini.”—Mateyu 22:39.

Mosasamala kanthu za zinenezo zambiri zotsutsa, malotale akupitirizabe kuchuluka modabwitsa padziko lonse lapansi. Mlendo wocheza Kumadzulo kwa Afirika anawona kuti anthu mazana ambiri anawunjikana panyumba ya lotale ya Boma. Iye anafunsa nzika ya komweko kuti: “Kodi nchifukwa ninji anthu onsewa akuwonongera ndalama zawo pa lotale, makamaka popeza kuti ngosauka?”

Nzikayo inayankha kuti: “Bwanawe, iwo amaseŵera lotale chifukwa chakuti imawapatsa chiyembekezo. Kwa ambiri a iwo, ndiyo chiyembekezo chokha chomwe ali nacho m’moyo.”

Koma kodi kupambana lotale kulidi chiyembekezo? Iyo kwenikweni ili chinyengo, chizirezire, loto losatheka. Ndithudi Mkristu wachikumbumtima chabwino sakawononga nthaŵi yake ndi chuma m’kulondola chuma chopanda phindu cha kutchova njuga. Kukakhala kwabwino chotani nanga kulabadira uphungu wa mtumwi Paulo, yemwe analemba kuti anthu anzeru ‘sayembekezera chuma chosadziŵika kukhala kwake, koma Mulungu, amene atipatsa ife zonse kuchulukira, kuti tikondwere nazo.’—1 Timoteo 6:17.

[Mawu Otsindika patsamba 8]

“Opanga malamulo amaganiza kuti apeza njira yosavuta, yokhweka yopezera ndalama, pamene kwenikweni, iwo akusakaza mabanja ambiri, ndi mabizinesi ambiri, ndi anthu ambiri, ndi miyoyo yambiri”

[Bokosi patsamba 9]

Mfundo Zabwino Koposa kwa Otchova Njuga

“Palibe chipongwe chachikulu chomwe chingakhalepo kuposa cha wobetchetsa yemwe amapatsa moni wogula wopambana. . . . Pali obetchetsa oŵerengeka okha amene amaletsa wobetcha [wotchova njuga] kuti asabetche chifukwa chakuti akulephera kwambiri. . . . Kumbukiraninso kuti, obetcha opambana sawonekawoneka mofanana ndi obetchetsa osauka.”—Graham Rock, The Times, London.

“Jackpot yotsimikiziridwa ya $45 miliyoni m’kusankha opambana a Lotto ya usiku walero njaikulu koposa m’mbiri ya New York State. Koma mwaŵi wakupambana ndi betchi ya $1 ndi 1 mu 12,913,582.”—The New York Times.

“Chitsiru chimataya ndalama zake mofulumira.” Mwambi womwe udakagwirabe ntchito chiyambire m’zaka za zana la 16.—Familiar Quotations, lolembedwa ndi John Bartlett.

“Wotchova njugawe, usakondwere; amene wapambana lero adzalephera m’mawa.”—Mwambi Wachispanya.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena