Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w89 7/15 tsamba 30
  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
  • Nsanja ya Olonda—1989
  • Nkhani Yofanana
  • Malotale Kodi Nchifukwa Ninji Ali Otchuka?
    Galamukani!—1991
  • Malotale—Kodi Ndani Amapambana? Kodi Ndani Amalephera?
    Galamukani!—1991
  • Mliri wa Lotale—Njuga ya Padziko Lonse
    Galamukani!—1991
  • Kutchova Njuga Kwatenga Malo Padziko Lonse
    Galamukani!—2002
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1989
w89 7/15 tsamba 30

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

◼ Kodi chiri choyenera kwa Mkristu kugula matikiti a lottery monga chosangulutsa wamba ngati zotulukapozo zikapita ku thandizo?

Baibulo motsimikizirika silimaletsa zosangulutsa zoyenera, popeza kuti Yehova ali “Mulungu wachimwemwe.” (1 Timoteo 1:11) Anthu ake angasangalale ndi nyimbo, kuvina kodekha, kudya ndi kumwa kosapitirira malire, ndi maseŵera ndi zisudzo zolinganizika. (Salmo 150:4; Mlaliki 2:24) Ngakhale kuli tero, kutchova njuga mwachiwonekere kumawombana ndi uphungu wanzeru wa Mulungu, ndipo chiri chowona ponena za kugawanamo mu malottery.

M’chenicheni kodi lottery nchiyani? Iyo imaphatikizapo kugula matikiti kuti mukhale ndi mwaŵi wa kupeza mphoto. Opeza mphotowo amagamulidwa mojambula kapena njira ina yake ya apa ndi apo ya kusankha nambala.a Kaŵirikaŵiri imakhala mphoto imodzi yaikulu, mwinamwake yomafika ku mamiliyoni a madola, mapeso, kapena mapaundi. Chisonkhezero cha mphoto yaikulu koposa yoteroyo chiri chokulira kotero kuti malottery akhala “mtundu wofalikira koposa wa kutchova njuga.” (The World Book Encyclopedia) Mazana a mamiliyoni a anthu amatchova njuga kupyolera mu malottery.

Anthu ena alingalira kuti kukhala oloŵetsedwa mu lottery sikuli kolakwa kapena koipa chifukwa chakuti mtengo wa tikiti (mwaŵi) ungakhale waung’ono, chifukwa chakuti otengamo mbali amachita tero modzifunira, ndipo chifukwa chakuti zina za zopezedwazo zingagwiritsidwe ntchito kaamba ka chifuno cha kuthandiza, monga ngati kuthandiza osauka. Kodi kulingalira koteroko kuli kokhutiritsa motani?

Pamene kuli kwakuti ena amadzinenera kuti kugula tikiti ya lottery kuli kopepuka, chosangulutsa cha mtengo wotsika, palibe kukana nsonga ya umbombo. Anthu amagula matikiti a lottery akumayembekeza kupeza ndalama zambiri. Ichi motsimikizirika chimasemphana ndi uphungu waumulungu wotsutsana ndi umbombo, womwe ungakhale cholakwa chokulira kotero kuti chingaletse munthuyo ‘kuloŵa ufumu wa Mulungu.’ Chotero, ngati Mkristu anasonyeza umbombo wopitiriza mwa kutchova njuga, iye angachotsedwe mu mpingo. (1 Akorinto 5:11; 6:10) Baibulo limanena kuti: “Cholowa chingalandiridwe msangamsanga poyamba pake; koma chitsiriziro chake sichidzadala.” (Miyambo 20:21) Ngati Mkristu amva chisonkhezero china chirichonse cha ‘kutenga mwaŵi’ mu lottery, iye ayenera kulingalira mosamalitsa ponena za umbombo pa umene lottery yazikidwa. Aefeso 5:3 imanena kuti ‘umbombo usatchulidwe ndi kutchulidwa komwe pakati pathu,’ osagonjetseredwako mpang’ono pomwe ndi Mkristu.

Mbali yokulira ya oseŵera lottery kaŵirikaŵiri imapezeka m’midzi yosauka. Chotero ngakhale ngati mtengo wa tikiti uli waung’ono, ndalama zikupatutsidwa zomwe zinafunikira kupita kulinga ku zosoŵa zowona za banja​—chakudya chowonjezereka, zovala zokwanira, chisamaliro cha mankhwala chowongoleredwa. Munthu amene amadzinenera kukhala Mkristu koma amanyalanyaza zosowa za banja zotero “aipa koposa wosakhulupirira.”​—1 Timoteo 5:8.

Ngakhale ngati mtengo wa tikiti ya lottery sungavulaze mowonekera mkhalidwe wa zachuma waumwini wa winawake kapena banja, chimenecho sichimatanthauza kuti palibe chivulazo. Chifukwa ninji tero? Chifukwa chakuti chifupifupi aliyense wogula tikiti ya lottery angakonde kupambana. Kodi mphoto yake ya ndalama ikachokera kuti? Ngati tikiti yake imagulitsidwa pa mapeso khumi ndipo mphotoyo iri mapeso miliyoni imodzi, chimenecho chimatanthauza kuti amatenga ndalama za matikitizo kuchokera kwa anthu ena mazana chikwi chimodzi. Kodi chimenecho chimagwirizana ndi uphungu wa Mulungu wotsutsana ndi kusirira zinthu za ena? (Deuteronomo 5:21) M’chenicheni, mphoto yake idzaphatikizapo ndalama zotengedwa kuchokera kwa anthu ena ambirimbiri, popeza kuti matikiti oposa mazana chikwi chimodzi adzagulitsidwa. Unyinji wabwino wa ndalama za matikiti uyenera kupita kaamba ka zowonongedwa za kuyang’anira, limodzinso ndi zifuno zina zothandiza zomwe zafuulidwa monga cholinga cha lottery. Chotero ngakhale ngati munthuyo angakhoze kupeza mapeso khumi kaamba ka tikiti yake, bwanji ponena za unyinji wokulira wa ena? Ndiko nkomwe, kupambana kwake mwinamwake kudzafalitsidwa, kusonkhezera ambiri kuyamba kuseŵera lottery kapena kugula matikiti owonjezereka, ngakhale ngati iwo sangakhoze kuchita ichi.

Palibenso kukana kuti lomangiliridwa ndi lottery liri loto la kupeza ndalama popanda kuzigwirira ntchito izo. Inde, lottery imalimbikitsa ulesi kapena kusonkhezera ku iwo. Baibulo, ngakhale ndi tero, limafulumiza anthu a Mulungu kukhala okangalika, aluso, ndi ogwira ntchito zolimba. M’malo mwa kuchirikiza mzimu wa ‘peza chinachake popanda thukuta,’ ilo limalangiza kuti: “Ngati munthu safuna kugwira ntchito, asadyenso.”​—2 Atesalonika 3:10; Miyambo 13:4; 20:4; 21:25; 1 Atesalonika 4:9-12.

Kunena kuti ena angagawanemo mu lottery mwa kudzifunira iwo eni ndipo kuti kuli kwa lamulo sikumalungamitsa kudziloŵetsamo kwa Akristu. Maboma ena amapangitsa mitundu ina ya kutchova njuga kukhala ya lamulo, limodzinso ndi dama ndi mitala. Ngakhale kuti zinthu zimenezo zingakhale za lamulo ndipo anthu ambiri angakhale ofunitsitsa kudziloŵetsa mu izo, ichi sichimatanthauza kuti machitachita oterowo ali oyenerera m’maso mwa Mulungu. Akristu, m’malomwake, amakalamira kuwunikira kawonedwe ka Davide: “Mundidziŵitse njira zanu, Yehova; mundiphunzitse mayendedwe anu. Munditsogolere m’chikondi chanu, ndipo mundiphunzitse; pakuti inu ndinu Mulungu wachipulumutso changa.”​—Salmo 25:4, 5.

Ngati Mkristu mowona mtima akufunadi kuthandiza osauka, opunduka, kapena okalamba, iye ndithudi angachite tero mwachindunji kapena m’njira ina yomwe siimaphatikizapo kutchova njuga.

[Mawu a M’munsi]

a Ngakhale kuti mofalikira imadziŵika monga lottery, mtundu umenewo wa kutchova njuga ungatchedwenso pool, sweepstakes, raffle, (maseŵera olimbanirana mphoto) kapena dzina lina la kumaloko.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena