Kodi Muli Otseguka ku Malingaliro Atsopano?
ANTHU ena amatseka maganizo awo ku lingaliro lirilonse latsopano. Iwo angakane ilo chifukwa chakuti limasiyana ndi kawonedwe kawo. Mwachitsanzo, mkazi wina mu Denmark analembera ku magazini ya mlungu ndi mlungu ya Hjemmet ndi kunena kuti: “Ife nthaŵi zonse timavutitsidwa ndi Mboni za Yehova pa khomo pathu. Iwo amandikwiyitsa ine mowopsya, koma sindidziŵa mmene ndingapangire iwo kuchoka. . . . Kodi kuwumirira kwawo sikungaletsedwe ndi lamulo?”
Kwa anthu a ku Japan a mkati mwa zana la 19, kugogoda pa khomo pawo kochitidwa ndi Akumadzulo anawonedwanso monga “kukakamiza kobwerezabwereza.” M’maso mwa ambiri a iwo, chirichonse chochita ndi olowerera chinali chopanda pake kapena ngakhale chovulaza. Monga mmene mwambi wa Kum’mawa umanenera, “Chikaikiro chimayambitsa zowopsya mu mdima.” Mkhalidwe wa maganizo wa anthu ambiri a ku Japan unachitiridwa fanizo bwino mu zojambulidwa zawo zosonyeza Wolamulira Gulu la Sitima ya Pamadzi Perry. Kuchokera pa 50 ena omwe anatsalira, kokha 2 kapena 3 amamuimira iye monga nduna wamba ya gulu lankhondo la pamadzi la ku U.S. Ena amamusonyeza iye monga chithunzi choseketsa cha mphuno yaitali kapena chirombo chowopsya chosatsungula pamaso, monga momwe zachitidwira chithunzi pano.
Ndi kutseguka kwa dziko lawo, ngakhale kuli tero, anthu a ku Japan otseguka maganizo anafika pa kuzindikira kuti alendo sanali mbuli. M’nkhani ya ena opita kukagwira ntchito choyamba a chiJapan ku United States, chinali ngati kuti zikamba zinagwa kuchokera m’maso mwawo pamene iwo anawona mwambo wa Kumadzulo choyambirira. Nduna zapamwamba zinapitirizabe kudandaula ponena za mmene anthu a ku America analiri opanda ulemu kuchokera ku kawonedwe ka anthu a ku Japan. Koma mbadwo wocheperako unapanga kuŵeruza kolinganizika mokulira kwa mwambo watsopanowu.
Kalinde wa nduna yaikulu mmodzi wa zaka 19 zakubadwa pambuyo pake analemba kuti: “Zambiri za nthumwi 70 za ku Japan pa ulendowu zinakana kapena kudana [ndi anthu a ku America]. Ngakhale kuli tero, pa kuchitira umboni mikhalidwe yeniyeni, munthu aliyense payekha pakati pathu anazindikira kuti iwo anali analakwa ndipo anadzimvera chisoni chifukwa chosungirira malingaliro oterowo. Kulingalira alendo kukhala otsika monga agalu kapena akavalo ndi kuwachitira iwo chipongwe kukapeza kokha kuchokera kwa iwo kuwuma khosi kwa kukhala kwathu opanda chifundo ndi osalungama.” Kodi muli otseguka maganizo mokwanira kuyang’ana pa malingaliro atsopano ndi mkhalidwe wopanda kunyada monga uja wa kalinde wachichepere uyu?
Chitsanzo cha Anthu a ku Bereya
M’zana loyamba C.E., Ayuda ambiri anasungirira kunyada kosalingalirika molimbana ndi ziphunzitso za Chikristu. M’njira zina, iko kunafanana ndi kunyada kwa anthu a ku Japan odzipatula motsutsana ndi dziko lakunja. “Kulikonse [Chikristu] achinenera,” anadzinenera tero Ayuda mu Roma wakale. (Machitidwe 28:22) Ponena za Akristu ena mu mzinda wa Tesalonika, Ayuda okhala ndi kulingalira kolakwika anafuula kuti: “Omwe aja asanduliza dziko lokhalamo anthu afika kunonso.”—Machitidwe 17:6.
Mosasamala kanthu za chimenecho, panali anthu ofunitsitsa kuyang’ana kupyola pa kunyada kwawo. Mwachitsanzo, ndimotani mmene nzika za ku Bereya zinavomerezera ku mbiri yabwino yolalikidwa ndi mtumwi Paulo ndi woyanjana naye wake Sila? Ponena za anthu a ku Bereya, wolemba Baibulo Luka ananena kuti: “Amenewa anali mfulu kuposa a mu Tesalonika, popeza analandira mawu ndi kufunitsa kwa mtima wonse, nasanthula m’Malembo masiku onse ngati zinthu zinali tero.” (Machitidwe 17:11) Kodi inu muli “mfulu koposa” monga anthu a ku Bereya?
Chonde lingalirani nkhani ya Masaji. Pa nthaŵi imodzi, iye anali ndi udani wamphamvu kulinga ku Chikristu. Iye anali wofanana ndi odzipatula omwe anatsutsa kutsegulidwa kwa Japan. Pamene mkazi wake, Sachiko, anayamba kuphunzira Baibulo, iye anamutsutsa mwachiwawa. Iye anafikira pa kulingalira za kupha banja lake ndipo kenaka kudzipha. Chifukwa cha chiwawa chake, banja lake linayenera kuthaŵira kunyumba ya mbale wamkulu wa Sachiko kumpoto kwa Japan.
Pomalizira pake, Masaji anaganiza za kutsegula maganizo ake pang’ono ndi kufufuza chipembedzo cha mkazi wake. Pambuyo pa kuŵerenga mabukhu ena a Baibulo, iye anawona chifuno cha kupanga masinthidwe. Pamene anaphunzira Malemba, mkhalidwe wake wachiwawa unasintha kukhala uja wowunikiridwa ndi chipatso cha mzimu wa Mulungu. (Agalatiya 5:22, 23) Masaji anasinkhasinkha kupezeka pa misonkhano ya Mboni za Yehova chifukwa anawopa kuti Mboni zingafune kubwezera kaamba ka chiwawa chake molimbana nawo. Koma pamene iye pomalizira pake anafika pa Nyumba ya Ufumu, iye analandiridwa ndi ukoma woterewo kotero kuti anatulutsa misozi.
Inde, kulaka kunyada ndi kusanthula malingaliro atsopano kungafutukule chizimezime chathu ndipo kungatipindulitse ife m’njira zina. Ngakhale kuli tero, kodi chimenechi chikutanthauza kuti tiyenera kukhala otseguka ku lingaliro lirilonse latsopano limene lingadze?
Khalani Osankha!
Ndi kutha kwa kudzipatula kwa Japan, malingaliro atsopano anasefukira m’dzikolo. Ena a amenewa anapindulitsa anthu a ku Japan, koma iwo akanakhala bwinopo popanda ena. “Motsutsana ndi zikhumbo za Wolamulira Gulu la Sitima ya Pamadzi Perry,” inatero nduna ya ku U.S. Douglas MacArthur pamene analandira kugonjera kwa Japan pambuyo pa Nkhondo ya Dziko ya II, “Japan inasintha chidziŵitso cha Kumadzulo kukhala chida cha kutsendereza ndi ukapolo.” Ikumatsanzira aphunzitsi ake a Kumadzulo, Japan inayamba pa njira yomwe inatsogolera iye m’mipambo ya nkhondo. Izi zinathera mu Nkhondo ya Dziko ya II, pamapeto pa imene mabomba aŵiri a atomu anagwetsedwa pa gawo la chiJapan.
Nchiyani chomwe tingaphunzire kuchokera ku ichi? Kuti tiyenera kukhala osankha ponena za kulandira malingaliro atsopano. Tingachite bwino kutsanzira anthu a ku Bereya mwa “kusanthula Malemba masiku onse ngati zinthu [zophunzitsidwa ndi Paulo] zinali zotero.” (Machitidwe 17:11) Liwu la Chigriki logwiritsiridwa ntchito pano kaamba ka “kusanthula” limatanthauza “kupanga kufufuza kosamalitsa ndipo kwachindunji monga mu nkhani za milandu ya lamulo.” (Word Pictures in the New Testament, lolembedwa ndi A. T. Robertson) M’malo molandira mwakhungu lingaliro lirilonse latsopano loperekedwa kwa ife, tifunikira kuchita kufufuza kosamalitsa ndi kwachindunji, mongadi mmene woŵeruza angachitire m’kumva nkhani ya mlandu.
Ngati tiri osankha, sitidzakokedwa ndi chizolowezi chirichonse chopita kapena ndi malingaliro atsopano omwe ndithudi ali ovulaza. Mwachitsanzo, womwe unatchedwa mkhalidwe watsopano wa mu ma 1960 unawoneka kukhala lingaliro latsopano losangalatsa kwa ena. Koma kufufuza kosamalitsa kukanavumbula iwo kukhala mkhalidwe woipa wakale wovulaza pansi pa dzina latsopano. Ndiponso, mu Germany yovutitsidwa mwa chuma ya mu ma 1920, mosakaikira ambiri anawona Chinazi monga lingaliro latsopano losangalatsa, koma ndi nsautso yotani nanga yomwe chinapangitsa!
Mwachimwemwe, Mulungu wapereka mwala woyesera womwe ungagwiritsiridwe ntchito kuyesa malingaliro atsopano. Iwo uli Mawu ake owuziridwa, Baibulo. Kugwiritsira ntchito zitsogozo zake ku moyo wa banja ndi maunansi a anthu kudzathandiza ife kufufuza ambiri a malingaliro atsopano omvedwa lerolino kuchokera kwa akatswiri a za mayanjano, akatswiri a za malingaliro, ndi ena omwe amadzinenera kukhala akatswiri m’minda imeneyi. (Aefeso 5:21–6:4; Akolose 3:5-14) Uphungu wa Baibulo ponena za unansi wathu ndi Mulungu ndi anansi umatipatsa ife njira yofufuzira malingaliro ambiri olembedwa omwe tsopano akufalitsidwa pa nkhani ya chipembedzo. (Marko 12:28-31) Chidziŵitso cholongosoka cha Baibulo chidzatikonzekeretsa ife kugamulapo ngati lingaliro latsopano liri la phindu lenileni kapena ayi. Ife chotero tidzakhala okhoza ‘kutsimikizira zinthu zonse ndi kugwiritsa ku chimene chiri choyenera.’—1 Atesalonika 5:21.
Mboni za Yehova zimachezera anansi awo kuwalimbikitsa iwo kuphunzira ponena za Baibulo ndipo chotero kukhala okhoza kuŵeruza malingaliro atsopano moyenerera. Mbonizo zimalozanso ku malingaliro a Baibulo omwe ali atsopano kwa ambiri. Pakati pa awa pali chowonadi chonena za nthaŵi zimene tikukhala ndi chimene mtsogolo mwasunga kwenikweni kaamba ka mtundu wa anthu. (Mateyu 24:3-44; 2 Timoteo 3:1-5; Chibvumbulutso 21:3, 4) Chotero musatenge mkhalidwe wa kudzipatula pamene Mboni ziitanira panyumba yanu. M’malomwake, bwanji osatsegula chitseko chanu ndi kumvetsera ku zomwe akufuna kunena? Musatseke maganizo anu ku malingaliro omwe angakhale a phindu losatha kwa inu.
[Mawu a Chithunzi patsamba 5]
Library of Congress photo LC-USC62-7258