Moyo ndi Uminisitala za Yesu
Kufunafuna Kaamba ka Otaika
YESU ali wofunitsitsa kufuna ndi kupeza awo omwe modzichepetsa adzatumikira Mulungu. Chotero iye akufunafuna ndi kulankhula kwa aliyense ponena za Ufumu, kuphatikizapo ochimwa owuma mutu. Anthu oterowo tsopano akusendera pafupi kuti amve iye.
Akumawona ichi, Afarisi ndi alembi asuliza Yesu kaamba ka kukhala ndi anthu omwe iwo akuwalingalira kukhala opanda pake. Iwo akung’ung’udza kuti: “Uyu alandira anthu ochimwa nadya nawo.” Ndi motsikira pa ulemerero wawo chotani nanga mmene icho chiriri! Afarisi ndi alembi amawona anthu wamba monga litsiro pansi pa mapazi awo. M’chenicheni, iwo anagwiritsira ntchito kalongosoledwe ka Chihebri ‛am ha·’aʹrets, “anthu a kudziko lapansi [dziko],” kusonyeza kuipidwa kwawo ndi oterowo.
Ku mbali ina, Yesu akuchita ndi aliyense ndi ulemu, kukoma mtima, ndi chifundo. Monga chotulukapo chake, ambiri a odzichepetsa amenewa, kuphatikizapo anthu odziŵika bwino kaamba ka kuchita zoipa, ali ofunitsitsa kumvetsera kwa iye. Koma bwanji ponena za chisulizo cha Afarisi cha Yesu kaamba ka kupanga zoyesayesa m’malo mwa awo omwe amawalingalira kukhala opanda pake?
Yesu akuyankha chitsutso chawo mwa kugwiritsira ntchito fanizo. Iye akulankhula kuchokera ku kawonedwe kenikeni ka Afarisiwo, kuti iwo ali olungama ndipo achisungiko m’khola la Mulungu, pamene kuli kwakuti ‛am ha·’aʹrets onyozeka asokera ndipo ali mu mkhalidwe wotaika. Mvetserani pamene iye akufunsa:
“Munthu ndani wa inu ali nazo nkhosa makumi khumi, ndipo pa kutaika imodzi ya izo, sasiya nanga m’chipululu zinazo makumi asanu ndi anayi mphambu zisanu ndi zinayi nalondola yotaikayo kufikira aipeza? Ndipo pamene adaipeza aisenza pa mapewa ake wokondwera. Ndipo pofika kunyumba kwake amema mabwenzi ake ndi anansi ake, nanena nawo, ‘Kondwerani ndi ine, chifukwa ndapeza nkhosa yanga yotaikayo.’”
Yesu kenaka akupanga kugwiritsira ntchito kwa nkhani yake, akumalongosola kuti: “Ndinena kwa inu kotero kudzakhala chimwemwe kumwamba chifukwa cha wochimwa mmodzi wotembenuka mtima koposa anthu olungama makumi asanu ndi anayi mphambu asanu ndi anayi amene alibe kusowa kutembenuka mtima.”
Afarisi akudzilingalira iwo eni kukhala olungama ndipo chotero opanda chifuno cha kutembenuka mtima. Pamene ena a iwo anasuliza Yesu zaka zingapo kumayambiriroko kaamba ka kudya ndi osonkhetsa misonkho ndi ochimwa, iye anawauza iwo kuti: “Sindinadza kudzaitana, olungama, koma ochimwa.” Afarisi odzilungamitsa, omwe akulephera kuwona chifuno chawo cha kutembenuka mtima, sabweretsa chimwemwe chirichonse kumwamba. Koma ochimwa otembenuka mtima mowona amatero.
Kuti alimbikitse kuwirikiza kaŵiri nsonga yakuti kubwezeretsedwa kwa wochimwa wotaika kuli chopangitsa cha chimwemwe chachikulu, Yesu akunena fanizo lina. Iye akunena kuti: “Kapena mkazi wanji ali nazo ndalama za siliva khumi, ngati itaika imodzi, sayatsa nyali nasesa m’nyumba yake nafunafuna chisamalire kufikira akaipeza? Ndipo mmene aipeza amema mabwenzi ake ndi anansi ake, nanena, ‘Kondwerani ndi ine, chifukwa ndinapeza ndalama ndidatayayo.’”
Yesu kenaka akupereka kugwiritsira ntchito kofananako, akumanena kuti: “Chomwecho, ndinena kwa inu, kuli chimwemwe pamaso pa angelo a Mulungu chifukwa cha munthu wochimwa mmodzi amene atembenuka mtima.”
Ndi kosangalatsa chotani nanga kudera nkhaŵa kwachikondi kumeneku kwa angelo a Mulungu kaamba ka kubwezeretsedwa kwa ochimwa otaika! Ichi chiri mwapadera tero popeza awa omwe anali odzichepetsa, ‛am ha·’aʹrets onyozedwa kenaka abwera mu mzera kaamba ka kukhala ziwalo mu Ufumu wa kumwamba wa Mulungu. Monga chotulukapo, iwo apeza malo m’mwamba okwezeka kuposa aja a angelo iwo eni! Koma m’malo modzimva ansanje kapena ochepekera, angelowo modzichepetsa amayamikira chenicheni chakuti anthu ochimwawo ayang’anizana ndipo alaka mikhalidwe m’moyo yomwe ikawakonzekeretsa iwo kutumikira monga mafumu ndi ansembe a kumwamba omvera chisoni ndi chifundo. Luka 15:1-10; Mateyu 9:13; 1 Akorinto 6:2, 3; Chibvumbulutso 20:6.
◆ Nchifukwa ninji Yesu akuyanjana ndi ochimwa odziŵika, akumakoka chisulizo chotani kuchokera kwa Afarisi?
◆ Ndimotani mmene Afarisi amawonera anthu wamba?
◆ Ndi mafanizo otani amene Yesu akugwiritsira ntchito, ndipo nchiyani chomwe tingaphunzire kuchokera ku iwo?
◆ Nchifukwa ninji kusangalala kwa angelo kuli kozizwitsa?