Mutu 85
Kufunafuna Otayika
YESU ngwofunitsitsa kufunafuna ndi kupeza awo amene adzatumikira Mulungu modzichepetsa. Chotero iye akufunafuna nalankhula ndi aliyense za Ufumu, kuphatikizapo ochimwa oipitsitsa. Anthu otero tsopano akuyandikira pafupi kudzamumvetsera.
Powona izi, Afarisi ndi alembi akusuliza Yesu kaamba ka kuyanjana ndi anthu amene iwo amawalingalira kukhala osayenera. Iwo akung’ung’udza kuti: “Uyu alandira anthu ochimwa, nadya nawo.” Zimenezo nzoluluzitsa chotani nanga kwa iwo! Afarisi ndi alembi amachitira anthu wamba mofanana ndi fumbi lapansi pamapanzi awo. Kunena zowona, iwo amagwiritsira ntchito liwu Lachihebrilo ‛am ha·’aʹrets, ‘anthu adziko [dziko lapansi],’ kusonyeza kunyansidwa kumene ali nako kaamba ka oterowo.
Kumbali ina, Yesu akuchitira aliyense mwaulemu, mokoma mtima, mwachifundo. Monga chotulukapo, ambiri a odzichepetsa ameneŵa, kuphatikizapo anthu amene ali odziŵika bwino lomwe kukhala ochita zolakwa, ali ofunitsitsa kumumvetsera. Koma bwanji ponena za chisulizo cha Afarisi pa Yesu cha kupanga zoyesayesa pa anthu amene iwo amaŵalingalira kukhala osayenera?
Yesu akuyankha chitsutso chawo mwa kugwiritsira ntchito fanizo. Iye akulankhula mwa lingaliro la Afarisi iwo eniwo, monga ngati kuti ngolungama ndipo ngotetezereka m’gulu la nkhosa la Mulungu, pamene ‛am ha·’aʹrets oluluzikawo asokera ndipo ali mumkhalidwe wotayika. Tamverani pamene akufunsa kuti:
“Munthu ndani wa inu ali nazo nkhosa makumi khumi, ndipo pakutayika imodzi ya izo, sasiya nanga m’chipululu zinazo makumi asanu ndi anayi mphambu zisanu ndi zinayi, nalondola yatayikayo kufikira aipeza? Ndipo pamene adaipeza, ayisenza pa pamapeŵa ake wokondwera. Ndipo pakufika kunyumba kwake amema abwenzi ake ndi anansi ake, nanena nawo, Kondwerani ndi ine, chifukwa ndinapeza nkhosa yanga yotayikayo.”
Pamenepo Yesu akugwiritsira ntchito mawu a fanizo lake, kufotokoza kuti: “Ndinena kwa inu, kotero kudzakhala chimwemwe kumwamba chifukwa cha wochimwa mmodzi wotembenuka mtima, koposa anthu olungama makumi asanu ndi anayi mphambu asanu ndi anayi, amene alibe kusoŵa kutembenuka mtima.”
Afarisi amadzilingalira kukhala olungama motero safunikira kulapa. Pamene ena a iwo anasuliza Yesu zaka ziŵiri zapitazo chifukwa cha kudya ndi osonkhetsa msonkho ndi ochimwa, iye anawauza kuti: “Sindinadza kudzaitana olungama, koma ochimwa.” Afarisi odzilungamitsa amene akulephera kuwona kufunikira kwawo kwa kulapa, sakubweretsa chisangalalo kumwamba. Koma ndithudi ochimwa olapawo akutero.
Kulimbikitsa mwamphamvu kwambiri mfundo yakuti kubwezeretsedwa kwa ochimwa otayika kumachititsa chikondwerero chachikulu, Yesu akusimba fanizo lina. Iye akuti: “Kapena mkazi wanji ali nazo ndalama zasiliva khumi, ngati itayika imodzi, sayatsa nyali, nasesa m’nyumba yake, nafunafuna chisamalire kufikira akaipeza? Ndipo mmene aipeza amema abwenzi ake ndi anansi ake, nanena, Kondwerani ndi ine, chifukwa ndinapeza ndalama ndidatayayo.”
Pamenepo Yesu akupanga kugwiritsira ntchito kofananako. Iye akupitirizabe kunena kuti: “Chomwecho, ndinena kwa inu, kuli chimwemwe pamaso pa angelo a Mulungu chifukwa cha munthu wochimwa mmodzi amene atembenuka mtima.”
Nkochititsa chidwi chotani nanga kudera nkhaŵa kwachikondi kumeneku kwa angelo a Mulungu kaamba ka kubwezeretsedwa kwa ochimwa otayika! Izi ziri makamaka choncho popeza kuti amene poyamba anali odzichepetsa ameneŵa ‛am ha·’aʹrets onyozedwa potsirizira pake akuloŵa mumzera wa kukhala ziŵalo Muufumu wakumwamba wa Mulungu. Monga chotulukapo, iwo amadzipezera malo apamwamba kumwamba oposa a angelo enieniwo! Koma mmalo mwa kuchita nsanje kapena kunyoza, angelowo modzichepetsa amazindikira kuti anthu ochimwa amenewa ayang’anizana ndi kugonjetsa mikhalidwe m’moyo imene idzawakonzekeretsa kutumikira monga mafumu akumwamba ndi ansembe omvera chifundo ndi okoma mtima. Luka 15:1-10; Mateyu 9:13; 1 Akorinto 6:2, 3; Chivumbulutso 20:6.
▪ Kodi nchifukwa ninji Yesu akuyanjana ndi ochimwa odziŵika, ndipo kodi ndichisulizo chotani chimene iye akusonyeza kuchokera kwa Afarisi?
▪ Kodi ndimotani mmene Afarisi amawonera anthu wamba?
▪ Kodi ndimafanizo otani amene Yesu akugwiritsira ntchito, ndipo ife tingaphunzirenji mu ameneŵa?
▪ Kodi nchifukwa ninji kukondwera kwa angelo kuli kochititsa chidwi?