Wojambula Wamkulu Waluso—Yehova!
“OJAMBULA aluso amaika utoto kuwala kwa dzuŵa ndi kuloŵa kwa dzuŵa kosaŵerengeka, ndipo ntchito zawo zimagulitsidwa kaamba ka mazana, ngakhale zikwi, za madola. Komabe, Yehova Mulungu, Wojambula Wamkulu Waluso ndi Woyambitsa wa kuloŵa kwa dzuŵa ndi kuwala kwa dzuŵa, amatipatsa ife kumodzi tsiku lirilonse—kwaulere. Zoyambirirazo zimaposa kotheratu makope opangidwa. Kodi chimenecho sichiyenera kutipatsa ife chifukwa cha kuyamikirira iye monga Mlengi?” Analingalira tero woyang’anira woyendayenda wa Mboni za Yehova mu Hawaii mkati mwa imodzi ya nkhani zake ku mpingo.
Mkazi wosakhulupirira kukhalapo kwa Mulungu, akumachezera Nyumba ya Ufumu kwa nthaŵi yoyamba, anali m’gululo. Iye anazindikira kulingalira kwa mtumikiyo, koma zikaikiro zamphamvu ponena za kukhalapo kwa Mulungu zinatsalirabe. Ngakhale kuli tero, pamene iye anali kuyendetsa galimoto kupita kunyumba kuchokera ku ntchito chifupifupi zaka ziŵiri pambuyo pake, iye anagwidwa mu ora la kuchuluka kwa magalimoto odutsa. Ichi chinampangitsa iye kuwona kuloŵa kwa dzuŵa kwapadera kozizwitsa. Malingaliro ake anabwerera ku nkhani ya woyang’anira woyendayenda amene uja.
Iye akusimba kuti: “M’malo mwa kukwiyitsidwa ponena za kugwidwa mu kuchuluka kwa magalimoto odutsa, ndinawona kuloŵa kwa dzuŵa kokongola, ndipo kunandikumbutsa ine za chimene mlankhuliyo ananena ponena za kuyamikira Yehova Mulungu monga Wojambula Waluso ndi Mlengi. Chinandipangitsa ine kulingalira kuti, ‘Mwinamwake chimene iye ananena chiri chowona; mwinamwake palidi Mlengi.’ Ndinalingalira ponena za icho pamene ndinapitiriza kupita kunyumba, ndipo usiku umenewo ndinaitana bwenzi langa lomwe poyambapo linandiitana ine kupita ku Nyumba ya Ufumu. Ndinayamba kuphunzira Baibulo, ndipo tsopano ndimalambira Yehova monga Mulungu wanga ndi Mlengi.”
Mofanana ndi wamasalmo, mkazi ameneyu sanafike kokha ku kuyamikira Yehova monga Wojambula Wamkulu Waluso wa chilengedwe komanso anafika ku kuyimba zitamando zake. Analemba tero wamasalmo: “Lemekezani Yehova kuchokera kumwamba . . . Mlemekezeni, dzuŵa ndi mwezi. Mlemekezeni, nyenyezi zonse zowunikira. . . . Alemekeze dzina la Yehova; popeza analamulira, ndipo zinalengedwa.”—Salmo 148:1-5.