Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w89 6/1 tsamba 24
  • Kufunafuna Kaamba ka Chowonadi cha Baibulo Kufupidwa mu Israyeli

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kufunafuna Kaamba ka Chowonadi cha Baibulo Kufupidwa mu Israyeli
  • Nsanja ya Olonda—1989
  • Nkhani Yofanana
  • “Sanaleka”
    Nsanja ya Olonda—1995
  • Kodi Ndani Ayenera Kutchedwa Kuti Rabi?
    Nsanja ya Olonda—1996
  • Kuumirira mu Ntchito Yawo ya Umulungu
    Nsanja ya Olonda—1988
Nsanja ya Olonda—1989
w89 6/1 tsamba 24

Ripoti la Olengeza Ufumu

Kufunafuna Kaamba ka Chowonadi cha Baibulo Kufupidwa mu Israyeli

ANTHU owonjezerekawonjezereka mu Israyeli mofanana ndi kwina kulikonse akuwona kupusa kwa zoyesayesa za munthu za kubweretsa mtendere wosatha ndi kupereka chiyembekezo kaamba ka mtsogolo. Mboni za Yehova 370 m’dziko lokongola, la mumbiri limenelo zikubweretsa chiyembekezo chopatsa moyo kwa awo ofunafuna Mulungu. (Yesaya 55:2, 3) Maripoti otsatiraŵa ochokera ku ofesi ya nthambi ya Watch Tower Society mu Tel Aviv akusonyeza kuti Mulungu amafupa awo amene amafunafuna chowonadi cha Baibulo.

“Zisokonezo zopangidwa ndi okhulupirira opanda maziko a chipembedzo amwano zazimiririka, ndipo zoyesayesa zawo zapapitapo za kusokoneza misonkhano yathu zikupitiriza kuwatembenukira. Mwachitsanzo, okwatirana aŵiri achikulire a ku Russia anali kuyanjana ndi gulu la Adventist koma sanakhutiritsidwe ndi zimene iwo anali kuphunzira. Iwo sanawone umboni uliwonse wa zizunzo zimene zinaloseredwa kuzindikiritsa Chikristu chowona. Kenaka tsiku lina iwo anapeza magazini ya nkhani yakale, yotayidwa ya chinenero cha ku Romania yomwe inali ndi ripoti lonena za kuwukira kwa gulu komwe kunachitidwa kumbuyoko mu 1985 pa chimango cha ofesi ya nthambi ya Sosaite ndi pa Nyumba ya Ufumu mu Tel Aviv. Ndi chikondwerero chawo chitadzutsidwa, iwo anapita ku Tel Aviv ndi kuyenda mozungulirazungulira kwa maora anayi kufikira anapeza chimango cholongosoledwa mu nkhani ya nyuzipepalayo. Iwo anasangalala kulandira mayankho ku ena a mafunso awo ndi kukhala kaamba ka msonkhano wa madzulo, kumene iwo anali achimwemwe kukumana ndi zina za Mboni zolankhula Chirussia. Kuyambira pamenepo, phunziro la Baibulo lokhazikika lakhala likuchitidwa ndi iwo. Kuchulukira kumene iwo amaphunzira, kumakhalanso kuchulukira kumene amakhutiritsidwa kuti apeza kokha chimene anali kufunafuna​—chowonadi!

“M’chochitika china, mbale anachitira umboni kwa mwamuna wachichepere wokhala ndi banja yemwe sanavomerezane ndi zina za nsonga zimene anayesera kulongosola ndipo chotero sanapitirize kuyang’ana mu uthenga wa Ufumu. Zaka zingapo pambuyo pake, mwana wamkazi wa mwamuna ameneyu anadwala, ndipo anawuzidwa ndi mabwenzi okhulupirira malaulo kuti vutolo mwachidziŵikire linali logwirizana ndi mezuzah yomangiriridwa pamphuthu panyumba yake. Iwo anayamikira kuti anayenera kulola rabi kuifufuza iyo. Anagamulapo kuchita chimenechi. Pa nthaŵi imodzimodziyo, iye anapemphera mowona mtima kwa Mulungu kaamba ka chitsogozo m’kupeza chowonadi.

“Pa ulendo wake wopita kunyumba kwa rabi, mwamunayo mwadzidzidzi anagamulapo zopita kukatenga cholembera cha mankhwala ku chipatala chaching’ono cha zaumoyo. Pamene anafika, ndani amene iye anayenera kupeza kumeneko kuposa Mboni yomwe inalalikira kwa iye zaka zingapo kumbuyoko! Mbaleyo akulongosola kuti analibe makonzedwe a kupita ku chipatala chaching’onocho madzulo amenewo kufikira pamene mwadzidzidzi anakumbukira chinachake chimene anachifuna. Mbaleyo ndi mwamunayo anakhala pansi ndi kulankhula kwa maora angapo madzulo amenewo, ndipo phunziro la Baibulo linakonzedwa ndi mwamuna wachichepereyo. Iye anayamba kupezeka pa misonkhano, kupita patsogolo kwake kunali kokhazikika, ndipo analoŵa mu Sukulu ya Utumiki Wateokratiki. Mwamsanga anayamba kupita mu utumiki wa m’munda, ndipo iye tsopano ali mbale wobatizidwa. Iye sanafike konse kunyumba ya rabi!”

Kufunafuna chowonadi cha Baibulo kwa anthu amenewa kunafupidwa molemerera, apeza kuti anapeza chuma chamtengo wake kuposa golidi.​—Miyambo 3:13-18.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena