Olengeza Ufumu Akusimba
“Sanaleka”
CHIYAMBIRE masiku a Yesu Kristu ndi atumwi ake, atsogoleri achipembedzo achita zambiri poyesayesa kudodometsa kulalikidwa kwa uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. Akuluakulu a mu Yerusalemu ‘adawalamulira’ atumwi mobwerezabwereza ‘kusalankhula kutchula dzina la Yesu.’ (Machitidwe 5:27, 28, 40) Komabe, nkhani ya m’Baibuloyo imati “mawu a Mulungu anakula; ndipo chiŵerengero cha akuphunzira chidachulukatu ku Yerusalemu.”—Machitidwe 6:7.
Zaka zikwi ziŵiri pambuyo pake tikupezabe atsogoleri achipembedzo ku Israel amene akusonkhezera akuluakulu aboma kupinga ntchito ya Akristu oona m’dzikolo. Poumirizidwa ndi anthu achipembedzo otengeka maganizo, mu November 1987, akuluakulu aboma mu Tel Aviv, ku Israel, analamula Mboni kuleka kuchita misonkhano Yachikristu mu Nyumba Yaufumu yokhala pa ofesi ya nthambi ya Watch Tower Society. Lamulolo linayamba kugwira ntchito mu October 1989. Pochita mogwirizana nalo, Mbonizo zinkasonkhana m’malo alendi m’deralo kwa zaka zitatu pamene Nyumba yawo Yaufumuyo inangokhala yosagwiritsiridwa ntchito.
Izi zidakali choncho, nkhaniyo inatengeredwa ku High Court of Justice ya Israel. Ofesi ya loya wa boma inapenda dandaulo limene linaperekedwa ndi Mbonizo ndi kunena kuti panalibe choziletsa kuchita apilo chifukwa cha tsankhu loipalo lachipembedzo. Motero, akuluakulu abomawo anasoŵa chochita koma kungobweza chosankha chawocho, ndipo mwachimwemwe Mboni za Yehova zinabwereranso ku Nyumba yawo Yaufumu.
Kodi ntchito ya kulalikira choonadi cha Baibulo inabwerera m’mbuyo mkati mwa zaka zimenezo? Kutalitali! Panthaŵi ya kutsekedwa kwa Nyumba Yaufumuyo, mu Tel Aviv munali mipingo iŵiri ndi kagulu kapadera ka phunziro la Baibulo m’tauni ina yapafupi ya Lod. Zaka zitatu pambuyo pake, pamene Nyumba Yaufumuyo inatsegulidwanso, Mboni za Yehova zinali zitawonjezereka kukhala mipingo inayi, ndipo kagulu kena ka phunziro la Baibulo katsopano kanali kusonkhana ku Beersheba.
Chiwonjezekocho mu Israel sichinali kokha pakati pa anthu azinenero zazikulu, Chiluya ndi Chihebri. Namtindi wa anthu wasamuka kuchokera ku yemwe kale anali Soviet Union, chotero Mboni za Yehova zolankhula Chirasha tsopano zagwirizana nawo mokangalika kuuza ena uthenga wabwino. Misonkhano ya chinenero cha Chirasha ikuchitidwa m’mipingo itatu; anthu oposa zana limodzi anasonkhana posachedwapa pa msonkhano wadera Wachirasha.
Mosakayikira, anthu achipembedzo atsankhu adzapitirizabe kulimbana ndi kulambira koona. Koma olengeza Ufumu akupitiriza kutsanzira Akristu a m’zaka za zana loyamba amene, mosasamala kanthu za chitsutso, “sanaleka kuphunzitsa ndi kulalikira Kristu Yesu.”—Machitidwe 5:42.