Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w90 1/1 tsamba 7
  • “Achangu mu Mzimu” mu Mexico

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Achangu mu Mzimu” mu Mexico
  • Nsanja ya Olonda​—1990
  • Nkhani Yofanana
  • Kuchokera ku Tondovi Kumka ku Chimwemwe
    Nsanja ya Olonda​—1990
  • Zimene Mungachite Mwana Akabadwa
    Banja Lanu Likhoza Kukhala Losangalala
  • “Mawu a Mulungu Anakula”
    Nsanja ya Olonda—1996
  • Kuvomereza Mbiri Yabwino m’Belgium
    Nsanja ya Olonda​—1990
Nsanja ya Olonda​—1990
w90 1/1 tsamba 7

Ripoti la Olengeza Ufumu

“Achangu mu Mzimu” mu Mexico

“DZIKO lonse likuwoneka kukhala lachangu ndipo likugwedera ndi zochitika.” Inalemba tero ofesi yanthambi ya Watch Tower Society mu Mexico, ndipo ndemanga imeneyo yakhala yowona chotani nanga! Ntchito yopita patsogolo ya m’dziko limenelo ikutsimikiziridwa m’chakuti mu August, munali chiŵerengero chapamwamba chapamwezi chotsatizana cha 70, chikumathera ndi ofalitsa 277,436. Kuwonjezerapo, maphunziro Abaibulo oposa 400,000 anachitiridwa ripoti, ndipo opezekapo pa Chikumbutso chaka chatha anafika 1,046,291. Ndi maziko otani nanga kaamba ka kukula kwa mtsogolo!

Mfundo yaikulu ya 1989 inali kusintha kwa kaimidwe ka Mboni za Yehova mu Mexico. Monga chotulukapo, Baibulo likakhoza kugwiritsiridwa ntchito m’ntchito yolalikira ya kunyumba ndi nyumba kwa nthaŵi yoyamba, ndipo misonkhano ikakhoza kutsegulidwa ndi pemphero. Izi zinali ndi chotulukapo cha mwamsanga. M’miyezi iŵiri, chiŵerengero cha ofalitsa chinakula kufika ku 17,000.

Chisangalalo cha abale pa kakulidwe chikuwoneka m’ndemanga zawo. Wina analemba kuti: “Pamene kalatayo inaŵerengedwa mu mpingo, inasokonezedwa kaŵiri ndi kuwomba m’manja kwachisangalalo. Chinalidi chosangalatsa!” Winanso ananena kuti: “Sitikanatha kusalira ndi chisangalalo. Zotulukapo zawoneka m’kufika pamsonkhano nthaŵi idakalipo. Aliyense amafuna kukhalapo kaamba ka pemphero lotsegulira.”

“M’gawo lathu,” inatero Mboni ina, “mkazi amene ali wokangalika m’programu ya phunziro la Baibulo wa Tchalitchi Chakatolika anathira ndemanga kuti: ‘Ngati kalelo ndemanga zawo zokha ndi magazine, [za Mbonizo] zinatisiya opanda mawu, popeza tsopano akutsegula Baibulo pa makomo, tatayikiratu!’”

Mboni za Yehova mu Mexico zimagogomezeranso kuchitira umboni wa mwamwaŵi ndi Baibulo. Mlongo wina anafikira mkazi amene anafunsa zimene anaganiza ponena za kuchotsa mimba. Mboniyo inayankha kuti: “Zimene ndimaganiza sizofunika kuposa zimene Baibulo limanena.” Pambuyo poŵerenga malemba angapo, mlongoyo analingalira kuti: “Kwa Mlengi moyo uli wofunika kwambiri, ngakhale moyo wa awo amene sanabadwebe.”

Kenaka mkaziyo anawulula kuti anali kuyembekezera kukhala ndi mwana woyamba, koma kufufuza kwa m’chipatala kunavumbula kuti mwanayo akakhala wopunduka. Dokotala wake analingalira kuti achotse mimbayo, ndipo mwamuna wake anavomereza, koma mkaziyo sanali wotsimikiza. Wofalitsayo analingalira naye kuchokera m’Baibulo, kumpatsa dzina lake, ndipo kenaka analekana.

Zaka zisanu pambuyo pake pa msonkhano wachigawo, okwatirana aŵiriwo ndi mwana wawo wa zaka zinayi zakubadwa anafuna kuwona mlongoyo ndi mwamuna wake. Anali mkazi mmodzimodziyo! Kodi chinachitika nchiyani? Pambuyo pa kukambitsirana kwake ndi Mboniyo, mkaziyo anasankha kukhala ndi mwana. Dokotala wake anakana kuwonana nayenso, ndipo mwamuna wake anawopsyeza kuti adzamusiya ngati mwanayo akabadwa wopunduka. Pamene nthaŵi ya kubadwa kwa mwanayo inafika, anangopita kukawonana ndi dokotala woyamba amene anapeza.

Mwamsanga mwanayo atabadwa, dokotalayo ananena kuti: “Mwagwira ntchito, mayi! Muli ndi msungwana wamng’ono wokongola.” Posakhulupirira zimene anamva, anapempha dokotalayo kufufuza mwanayo mosamalitsa. Kenaka anamuwuza nkhani yake. Dokotalayo anangonena kuti: “Izi nzozizwitsa.” Mkaziyo anali wosangalatsidwa kuti anali ndi kulimba mtima kwa kulemekeza lingaliro la Yehova pa kupatulika kwa moyo, ndipo anatcha mwana wake wokongola, waumoyo dzina la mlongoyo. Mwamsanga pamene anali wamphamvu, iye anafunafuna Mboni ndi kuyamba kuphunzira Baibulo ndi izo. Chisanakwane chaka chimodzi, iye ndi mwamuna wake anabatizidwa.

Mtumwi Paulo anafulumiza kuti: “Khalani achangu mu mzimu, tumikirani [Yehova, NW].” (Aroma 12:11) Mboni za Yehova mu Mexico, mofanana ndi Akristu owona kwina kulikonse, zikuvomereza ku chenjezo limeneli ndi mtima wawo wonse. Chimenecho ndicho chifukwa chake dziko lonselo liri lachangu ndipo likupita patsogolo ndi ntchito yauzimu. Yehova amadalitsa motani nanga okhulupirika ake!

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena