Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
◼ Kodi Nkoyenera kwa Mkristu Kukasaka Kapena Kukasodza?
Machitidwe osiyanasiyana onena za kusaka kaŵirikaŵiri amaphatikizapo maganizo okaikitsa. Motero nkwabwino kwa Mkristu kuyesayesa kumvetsetsa ndi kugwiritsira ntchito malingaliro a Yehova Mulungu pankhaniyi monga momwe ikupezekera m’Baibulo.
Mulungu anapatsa anthu ulamuliro pa zonse ziŵiri “nyama zakuthengo” ndi “zoweta.” Poyamba, anthu sanaloledwe ndi Mlengi, ndiponso panalibe chifuno chirichonse chakuthupi, cha kuphera nyama kuti zikhale chakudya. (Genesis 1:24, 29, 30) Kunali kokha pambuyo pa Chigumula kuti Mulungu anapatsa anthu kuyenerera kwa kudya mnofu wa nyama zimene zinachotsedwamo “moyo wake—mwazi wake” (Genesis 9:3, 4) Imeneyo ikakhala kaya nyama ya zoŵeta kapena yakuthengo.
Aisrayeli anaŵeta nyama, zonga nkhosa ndi ng’ombe, zimene zikanaphedwa kaamba ka chakudya atakhumba nyama. Iwo anasakanso ndi kusodza kuti apeze chakudya. (Deuteronomo 12:20-24; 14:4-20) Izi zikugwirizana ndi mawu ophiphiritsira a Mulungu akuti iye ‘akatumiza asodzi ambiri kukasodza anthu ake ndi osaka ambiri kukawasaka.’ (Yeremiya 16:16) Pambuyo pake, Yesu anaphatikizapo asodzi pakati pa atumwi ake ndipo anatsogoza ntchito yeniyeni ya kusodza.—Mateyu 4:18-22; 17:27; Luka 5:2-6; Yohane 21:4-7.
Pamene kholo lokalambalo Isake linapempha chakudya cha nyama yokoma, mwana wake wamwamuna Yakobo anali wofunitsitsa kupha mbuzi zazing’ono ziŵiri kumpangira chakudya. Komabe, Esau, anakasaka nyama yamphongo kuti apeze nyama ya kudya atate wake. Tawonani kuti ngakhale kuti nyama zoŵeta zinalipo, Isake anapempha nyama yakuthengo. Wonaninso, kuti ana onse aŵiriwo anapha nyama zimene zikakhala chakudya, osati kaamba ka iwo eni, koma kaamba ka winawake.—Genisis 27:1-19.
Nyama zingaphedwe kaamba ka zifukwa zina zosakhala nyama. Zikopa zake zingapangidwe kukhala zovala. (2 Mafumu 1:8; Marko 1:6; Ahebri 11:37) Zofunda zotetezera ndi zipangizo zinapangidwanso kuchokera ku zikopa zanyama, ngakhale zanyama zimene zinali zodetsedwa ndi zimene Aisrayeli sanadye.—Eksodo 39:33, 34; Numeri 24:7; Oweruza 4:19; Salmo 56:8.
Chofunika cha Mulungu chakuti mwazi wa nyama yophedwa ufotseredwe pansi chiyenera kukumbutsa osaka kuti moyo wanyama ngwochokera kwa iye ndipo chotero uyenera kuchitidwa mwaulemu, osati kuphedwa mwanjiru. (Levitiko 17:13) Mwachiwonekere Nimrode anapha nyama ndipo mwinamwake anadzitukumula kaamba ka luso lake losaka, kukula kapena kuchuluka kwa nyama zimene anapha, kapena zikumbukiro za chipambano zomwe zingakhale zitapangidwa kuchokera ku izo. Iye anali ‘mpalu wamphamvu motsutsana ndi Yehova.’—Genesis 10:9.
Chisangalalo chotero m’kusaka kapena kupha nyama, kapena m’kugwira nsomba, chingayambike mwa m’Kristu. Kaŵirikaŵiri wosaka kapena wosodza nsomba amene wafufuza mtima wake mosamalitsa wapeza kuti iye anayambukiridwa ndi ‘kuphera chisangalalo.’ Chisangalalo choterocho chimamkera limodzi ndi kuphera njiru kwa moyo wa nyama. Motero pamene kuli kwakuti sikulakwa kusaka kapena kusodza (pamene nyamayo kapena nsombazo zidzagwiritsiridwa ntchito ndi munthu wina monga chakudya kapena chifuno china choyenerera), kukakhala kosayenera kutero ngati Mkristu anali ndi mkhalidwe wofanana ndi wa Nimrode. Koma palinso ngozi zina kuwonjezera pa kupeza chisangalalo m’kuthamangitsa, kupha, kapena kupeza zikumbukiro za chipambano.
Nsanja ya Olonda ya January 1, 1984, inafotokoza chifukwa chimene Akristu owona samanyamulira kapena kusungira mfuti kaamba ka kuzigwiritsira ntchito motsutsana ndi anthu kapena kudzitetezera kwa iwo. (Masamba 19-24) Kusinkhasinkha pa uphungu umenewu kwatsogolera Mboni zina kupendanso ngakhale kukhala ndi mfuti zosakira. Ambiri asankha kungotaya mfuti zawo kapena kupeŵa kuziwonetsera ndi kupezeka mosavuta kuzigwiritsira ntchito. Chotero Akristu amenewa sakasonyeza lingaliro la kunyadira zida kapena kuzidalira. Ndiponso, kusakhala ndi mfuti zosakira, kapena kusakhala nazo pafupi, kungapeŵetse ngozi. Zida zakuphazo sizingapezeke kwa ana amene mwangozi angavulaze kapena kupha winawake, ndiponso sipakakhala mfuti pafupi pamene winawake anawopsezedwa kwambiri kapena kuchita tondovi.—Yerekezerani ndi Miyambo 22:3.
Akristu ena angakonde fungo la nyama yamthengo yakutiyakuti kapena nsomba, ndipo njira yogwira ntchito kwambiri yopezera zakudya zoterozo ndiyo mwakusaka kapena kusodza. Ena amasangalala ndi mpweya ndi maseŵera olimbitsa thupi ogwirizanitsidwa ndi kusaka m’nkhalango, kapena amapeza kuti maora a kukhala chete posodza ngotsitsimula. Baibulo silimatsutsa zimenezi, motero palibe kufunika kwa kuweruza ena kuti kaya amasangalala ndi zinthu zotero kapena ayi. Ndipo chitsanzo cha Isake ndi ana ake aamuna aŵiri chimasonyeza kuti palibe chifuno cha kukanganira amene adzadya nyama yakuthengo kapena nsombazo.—Mateyu 7:1-5; Aroma 14:4.
Mwachiwonekere mtumwi Petro anaphatikizidwa kwambiri m’kusodza. Powona nsomba ziri mbwe pafupi nawo, Yesu woukitsidwayo anamthandiza kupenda malingaliro ake ponena za nsomba kapena bizinesi yosodzayo. Yesu anafunsa kuti: “Simoni mwana wa Yona, kodi umandikonda ine kuposa izi?”—Yohane 21:1-3, 9-15; wonani Nsanja ya Olonda, November 1, 1988, tsamba 31.
Mofananamo, Mkristu amene mwachikumbumtima chabwino asankha kukasaka kapena kukasodza ayenera kudziŵa bwino lomwe zinthu zake zoyambirira. Mwachitsanzo, ngati nyengo yosaka kapena yosodza iyambika panthaŵi imene misonkhano ya mpingo inalinganizidwa, kodi iye akachitanji? Kapena kodi zokamba zake zimasonyeza kuti amanyada ndi luso lake la kulimba mtima posaka kapena kusodza? Kukakhala kwabwino chotani nanga pamene Mkristu wachikulire amene, nthaŵi zina, amasankha kusaka kapena kusodza anganene mokhutira maganizo kuti: “Inde, Ambuye, mudziŵa kuti ndikukondani [kuposa zolondoledwa zimenezi].”—Yohane 21:16.