Kodi Mumalakalaka Nthaŵi Pamene . . .
□ mungadzimve kukhala wotetezereka ndi wachisungiko m’nyumba mwanu—mosasamala kanthu kuti ndi nthaŵi yanji?
□ simudzafunikira maloko, mizati, mabelu ochenjeza kuti kwabwera mbala, magalasi osunzumirira alendo, malinga, alonda, agalu olonda, ndi zochinjiriza zina?
□ mungayende m’makwalala muli nokha m’chisungiko changwiro, ngakhale usiku?
□ mankhwala ogodomalitsa ndi mavuto onse ogwirizana nawo adzakhala zinthu zakale?
□ nkhondo zonse zidzaleka, ndipo zida sizidzapangidwa kapena kukundikidwa?
□ simudzafunikira kudandaula ndi chakudya, mpweya, ndi madzi oipitsidwa?
□ uchigaŵenga, kugwidwa ukapolo, ndi ziwopsyezo za mabomba zidzachotsedwa kotheratu?
□ chuma chachilengedwe cha dziko lapansi chidzachinjirizidwa, kusungidwa, ndi kugwiritsiridwa ntchito mwanzeru kaamba ka ubwino wa onse?
□ umbombo ndi dyera zidzaleka kukhala chisonkhezero cha anthu?
□ ana adzasunga kupanda liŵongo kwawo ndikukhala aulemu kwa ena ndi katundu wawo?
□ akazi sadzatsenderezedwa ndi kuvutitsidwa?
□ malamulo ndi mpambo wa zitsogozo udzakhala wabwino ndipo udzaperekedwa mwachilungamo kaamba ka ubwino wa onse?
□ boma lidzapanga zosankha zozikidwa pa zosoŵa zenizeni ndipo osati pa ndale zadziko?
□ ufulu ndi kulingana sikudzanenedwa kokha komanso kuchitidwa?
□ umphaŵi udzatheratu, koma onse adzakhala ndi zonse zofunikira kaamba ka thanzi lawo, umoyo wabwino, ndi chimwemwe?
□ ana adzafunidwa ndi kusamaliridwa ndipo sadzaipsyidwa kapena kutaidwa konse?
□ matenda ndi imfa zidzagonjetsedwa, ndipo sipadzakhalanso miliri yowopsya?
□ aliyense amene mukumana naye adzakhala wachifundo, wothandiza, ndipo wodalirika?
□ moyo wa aliyense udzakhaladi wamtengo wake, ndipo onse angapeze chimwemwe chosatha?
□ chipembedzo sichidzakhalanso mphamvu yogaŵanitsa, yotsogolera ku kudzikweza, udani, ndi nkhondo?
□ onse adzakhala ndi malo okwanira ndi osangalatsa okhalamo, ndipo kupanda pokhala kudzakhala chinthu chakale?
Ngati munganene kuti inde ku lirilonse la mafunso ali pamwambawo, mudzasangalala kuŵerenga nkhani zomwe zikutsatira.