Tikulifuna Dziko Latsopano
BWERERANI kumbuyo ndipo yang’anani mikhalidwe yomwe yakuzingani. Kodi mukuzikonda zimene mukuwona?
Mwinamwake inu mwaumwini muli ndi nyumba yabwino m’malo osangalatsa, osungidwa bwino. Mwinamwakenso muli ndi ntchito ya malipiro abwino imene mumaikonda. Kuwonjezerapo, inu ndi okondedwa anu mungakhale mukusangalala ndi mlingo winawake wa umoyo wabwino. M’zonse, mungaganize kuti ndinu wosungika ndiponso wachimwemwe.
Koma talingalirani za malo oyandikana nawo, mbali zina za dziko limene mumakhalamo, ndi maiko ena. Tayang’anani dziko lonse. Kodi chimene mukuchiona n’chithunzi chokongola? Kodi ichodi n’chokhutiritsa, chamtendere ndi kupita patsogolo?
Mogwirizana ndi zoneneratu zina kuchiyambi kwa zaka za zana lino, sayansi tsono ikadathetsa kale matenda aakulu onse, kupereka chakudya chochuluka kwa onse, kulinganiza ndi kuwongolera malo otizinga, ndikubweretsa nyengo yamtendere. Koma kodi chachitikadi nchiyani?
Sikutofunikira kusanthula kwakukulu kuti tiwone kuti mtendere wanyenga pulaneti lathu. “Chiyambire nthaŵi za Baibulo, anthu akhala akuchenjezedwa kusula malupanga kukhala zolimira,” walemba motero Michael Renner mu State of the World 1990. “Uphungu woterowo sunakhalepo konse woyenerera motero. Kulondola kosalekeza kwa mphamvu yankhondo kungakhale kunabweretsa anthu pamphembenu pa chiwonongeko.”
Pali malipoti ambiri onena za mkangano wapachiweniweni ndi nkhondo zimene zasakaza maiko ambiri kuzungulira dziko lonse. Mogwirizana ndi magwero ena, nkhondo 22 zinkamenyedwabe mu 1988.a Kodi amafa angati m’nkhondozi? Mutapenda chakachi, “chiwonkhetso cha anthu ophedwa m’nkhondo zonse zomwe zinkamenyedwa mu 1988 chinali 4,645,000. Maperesenti makumi asanu ndi aŵiri mphambu zisanu ndi chimodzi za omwe anaphedwa anali anthu wamba,” ikutero St. Louis Post-Dispatch.
Kodi zochitika zadziko za panthaŵi ino zikusonyeza kuti kutsogoloku kuli dziko lamtendere? “Nkhani zikunena kuti Nkhondo Yamawu ikulekeka ndipo mtendere ukupatsidwa mpata. Koma yang’ananinso,” inatero nkhani ina mu San Jose Mercury News ya ku California, U.S.A. “M’Maiko Otukuka Kumene, nkhondo ikuulikabe ndi chiyembekezo chochepa chakuti idzatha. Izi ndi nkhondo zobisika m’dziko. Kwakulukulu izo ziri kulimbana kwa maboma motsutsana ndi anthu awo: kulimbana kwachiweniweni kolimbanirana malo, chipembedzo, kupambadzukana maganizo kwa mwambo ndi fuko, ulamuliro wandale zadziko, ngakhale mankhwala ogodomalitsa. . . . Kuchokera ku Nyanga ya Afirika mpaka Kum’mwera cha kum’mawa kwa Asia, nkhondo yakakamiza anthu mamiliyoni ambiri kuthaŵa kwawo. Mbewu zimazulidwa, zipatala zimawukiridwa, zoŵeta zimawonongedwa, makolo amaphedwa mwankhalwe pamaso pa ana awo, anyamata a zaka 10 zakubadwa amatengedwa kukhala amtengatenga ndipo pambuyo pake kukhala asilikali, asungwana achichepere amagwiriridwa chigololo. M’maiko ameneŵa amene kwakukulukulu aiwalidwa, nkhondo yasiya mkukuluzi wa zosakaza ndi kusokonezeka kwa mayanjano kumene zitaganya zimenezi sizidzachira konse. . . . Kufufuza kukusonyeza kuti ma 1980 awona nkhondo zambiri kuposa zaka khumi zina zirizonse m’mbiri.”
Anthu ambiri amene amakhoza kuthaŵira ku maiko otukuka amapeza mtendere umene amaufunawo utawonongedwa ndi chiwopsyezo cha chiwawa chaupandu. “Chiukiro cha upandu mu [United States] chapitirizabe m’ma 1980 mosasamala kanthu za kuneneratu kwakuti chidzaleka,” ikusimba motero U.S.News & World Report. “Mwachitsanzo m’chaka china: Pamakhala maupandu owopsya 8.1 miliyoni monga mbanda, kufwamba ndi kuthyola nyumba. . . . Choipitsitsa pazonse ndi njira imene kukhetsa mwaziko kwakhalira kolekereredwa ndi kosadziŵika. Kukhala mnkhole ndiko mkhalidwe woipa. U.S. Bureau of Justice Statistics ikuyerekezera kuti 83 peresenti ya ana amene tsopano ali ndi zaka 12 zakubadwa adzakhala minkhole ya chiwawa chenicheni kapena choyeseredwa ngati mlingo wa upandu upitiriza monga mmene uliri. . . . Kupereka chilango kwa olakwa m’chitaganya nkosatsimikizirika kapena kumachitidwa mochedwa. Padziko lonse, apolisi ngwokhoza kuthetsa mlandu umodzi wokha mwa isanu ya milandu yowopsya ya upandu.” Mikhalidwe yofananayo ndiyo ili pa dziko lonse. UN General Assembly ikusimba za “kuwonjezeka ponse paŵiri m’kuchitika ndi kuwopsya kwa upandu m’mbali zambiri zadziko.”
Koma ngakhale ngati nkhondo zonse, zida, ndi upandu zinachotsedwa mwamsanga padziko lapansi, moyo ungawopsyezedwebe. “Umphaŵi wofa nawo, matenda adzawoneni, ndi kusadziŵa kulemba ndi kuŵerenga kochuluka kumazindikiritsa miyoyo ya anthu mazana mamiliyoni ambiri m’maiko otukuka kumene,” yadziŵitsa motero Worldwatch Institute mu lipoti lawo la State of the World 1990. “Anthu onse—olemera kapena osauka, amphamvu mwankhondo kapena ofooka—akuyang’anizana ndi vuto la kusakaza kwa malo otizinga kosayembekezereka.”
Inde, madongosolo enieni ochilikiza moyo pamene anthu onse amadalira ndiwo akunyalanyazidwa. “Dziko lonse lapansi liri mu mkhalidwe woipa [kuposa mu 1970],” walemba motero mkonzi Paul Hoffman m’magazine a Discover. “Zapadzala zikusefukira m’maenje athu. Mpweya wa kutentha kopambanitsa ukutenthetsa chifunga cha dziko. Chifunda thambo cha dziko chikuperepeseka. Zipululu zikufutukuka, ndipo nkhalango zamvula zikuchepekera. Mitundu ya zomera ndi zinyama ikusoloka pa mlingo wa 17 pa ola limodzi.”
Wonjezerani pamenepo ziyambukiro za kuwonongedwa kopitirizabe kwa dziko ndi madzi. M’malo mwake lingalirani za kukwera kwa chiŵerengero cha anthu padziko, chimene chimatulukapo kumangidwa kapena kupangidwa kwa misewu pamalo omwe akanalimidwa, mwakutero kuwonjezera kusoloka kwa mitundu ya zinyama ndi zomera. Talingalirani za kupereŵera kwa madzi abwino ndi vuto la mvula ya asidi. Wonjezeraniko zotulukapo zowopsyeza umoyo za mpweya woipitsidwa kwabasi ndi mavuto a zapadzala zodzetsa matenda. Zonse pamodzi, zimatanthauza tsoka kwa mtundu wa anthu. Kaya ndife ayani kapena kaya timakhala kuti, timafuna mpweya, zakudya, madzi, ndi zinthu zina kuti tikhale ndi moyo. Timazifuna zosaipitsidwa ndiponso zokwanira. Kalekale, “kwa anthu osauka, zaka za m’makumi asanu ndi atatu zakhala tsoka losasimbika, nthaŵi ya zakudya zopereŵera ndi kukwera kwa mlingo wa imfa,” yatero State of the World 1990.
Pokhala ndi mtundu wa anthu ukuwopsyezedwa m’njira zambiri chotero, kodi wina aliyense angakane kuti dziko latsopano likufunika kwambiri? Koma kodi zimenezo zingathekedi? Kodi dziko loterolo likachokera kuti? Kodi ndi zopinga zotani zimene ziyenera kulakidwa pulaneti lathu lisanalingaliridwe kukhaladi lachisungiko ndi lopita patsogolo? Tiyeni tiwone.
[Mawu a M’munsi]
a “Nkhondo” ikulongosoledwa kukhala kulimbana kumene kumaloŵetsamo pafupifupi boma limodzi ndipo kumene anthu pafupifupi 1,000 amaphedwa pachaka.
[Mawu a Chithunzi patsamba 4]
WHO photo by P. Almasy