Nkhani Yaikuluyo—Kodi Njotani?
KODI ndinkhani yaikulu iti imene aliyense wa ife akuyang’anizana nayo? Kodi ndiyo kukwera kwa madzi a m’nyanja ndi mphepo yoipa yopangitsidwa ndi kutentha kwa dziko lonse? Kodi ndiyo kuchepekera kwa chiphimba thambo, kochititsa kuvumbulidwa kowopsa ku cheza chovulaza cha ultraviolet? Kodi ndiyo kuchulukitsitsa kwa anthu, kumene kukukulitsa mavuto ena adziko lonse, monga ngati umphaŵi ndi upandu? Kapena kodi ndiyo chiyembekezo cha kupululutsidwa kwa mamiliyoni osaneneka m’nkhondo ya nyukliya, ndi opulumuka chipiyoyocho akumafa m’kupita kwa nthaŵi m’nsautso ya kuzizira, njala, kapena cheza?
Pambuyo pokambitsirana nkhani zimenezi ndi zina, magazini a Scientific American anatsimikiza motere mu 1989: “Kuthekera kwa nkhondo ya nyukliya mosakaikira kumapereka ngozi yowopsa koposa yothekera ku . . . kupulumuka.” Pamenepo, kodi nkhondo ya nyukliya ndiyo nkhani yaikulu yomwe tikuyang’anizana nayo?
Nkhani Yaikuluyo
Pokhala ndi masinthidwe andale zadziko ochitika chiyambire 1989, nkhondo ya nyukliya ingawoneke kukhala yosatheka kwenikweni. Ngakhale zinthu ziri choncho, malinga ngati zida za nyukliya zidzakhalapobe, izo zidzapereka chiwopsezo chachikulu kwa anthu. Komabe, chidziŵitso chopezeka mu 1990 Britannica Book of the Year chikusonya kunkhani ina yovuta. Mogwirizana ndi bukhu lazilozero limeneli, anthu oposa 230 miliyoni apadziko lapansi samakhulupirira Mulungu. Magwero ena akusonyeza kuti mamiliyoni owonjezereka asonkhezeredwa ndi nthanthi za Kum’mawa zimene zimavomereza lingaliro lakuti kulibeko Mlengi. Kuwonjezerapo, pamene kuli kwakuti mamiliyoni mazana ambiri amakhulupirira Mlengi, malingaliro awo onena za iye amasiyana kotheratu. Ndipo m’nkhani zambiri, zochita zawo zimabweretsa chitonzo chachikulu pa Uyo amene amati amamlambira.—2 Petro 2:1, 2.
Ngati Mulungu alikodi—ndipo iye ndithudi aliko—pamenepo ndithudi nkhani yaikulu koposa lerolino iyenera kuphatikizapo iye. Kodi anawalengeranji anthu? Kodi tiri ndi thayo lotani kulinga kwa iye? Kodi adzachita motani ndi mmene anthu akuwonongera dziko lapansi? Ndipo kodi adzayankha motani ku chitokoso choperekedwa mwakukana kukhulupirira ndi kugonjera ku chifuniro chake kochitidwa ndi ambiri? Kwenikweni, nkhani yaikulu imene aliyense wa ife akuyang’anizana nayo njakuti kaya tidzavomereza kapena kukana ufumu wa Mulungu, “amene dzina lake lokha ndilo YEHOVA.”—Salmo 83:18, King James Version.
Chiyambi cha Chilengedwe Chonse
Ndithudi, kwa anthu amene samakhulupirira Mulungu, thayo lathu kulinga kwa iye sinkhani konse. Koma munthu aliyense amene amayang’ana mowona mtima pa luso ndi kukongola kwa kapangidwe ka mudzi wathu wadziko lapansi amakakamizika kuvomereza kuti payenera kukhala Wolinganiza wamkulu. Nzowona kuti poyesayesa kufotokoza zozizwitsa zachilengedwe zotizinga, asayansi ambiri samalingalilapo Mulungu. Mwachitsanzo, ambiri amati chilengedwe chonse chinafika paukulu womwe chiripowu kuchokera ku dontho laling’ono kwambiri kuposa mutu wa phini, kuti zonsezo zinachitika “mwachibadwa,” mwamwaŵi, popanda kufunikira Mlengi. Komabe, pambuyo polongosola nthanthi yatsopano yotchuka yonena za mmene chilengedwe chinayambira, katswiri wa physics, Hanbury Brown, m’bukhu lake lakuti The Wisdom of Science, akuvomereza kuti: “Kwa anthu ambiri, ndikulingalira kuti zimenezo zikawoneka monga chinyengo mmalo mwa kulongosola.” Profesa Brown akutsimikiza kuti “chiyambi ndi chifuno cha dziko nzinsinsi zazikulu” zimene sayansi ikuwoneka kukhala yosakhoza kuzimasulira.
Asayansi asonyeza kuti zinthu ndi mphamvu nzolingana kwenikweni ndikuti zinthu zingasinthidwe kukhala mphamvu ndipo mphamvu zingasinthidwe kukhala zinthu. Monga momwe zawonedwera m’kuphulika kwa nyukliya, kanthu kakang’ono kamapanga mphamvu yaikulu. Pamenepo, kodi nkuti komwe kuli magwero a mphamvu zonse zokhala m’nyenyezi mamiliyoni 100,000 za m’mlalang’amba wathu, limodzinso ndi milalang’amba yoposa 1,000 miliyoni imene imapanga chilengedwe chowoneka ndi maso?
Baibulo limati: ‘Kwezani maso anu kumwamba, muone amene analenga izo, amene atulutsa khamu lawo ndi kuziŵerenga; azitcha zonse maina awo, ndi mphamvu zake zazikulu, ndi popeza ali wolimba mphamvu, palibe imodzi isoweka.’ Kodi Ameneyo ndani? Baibulo liri ndi yankho iri: “Ine ndine Yehova; dzina langa ndi lomweli; ndipo ulemerero wanga Ine sindidzapereka kwa wina.”—Yesaya 40:26; 42:5, 8.
Kulingalira kwakuti dziko lapansi ndi chilengedwe chonse zinakhalako mwamwaŵi kumachotsa ulemerero woyenera kumka kwa Mlengiyo, Yehova Mulungu. (Chibvumbulutso 4:11) Kumachotsanso chisonkhezero champhamvu chakuchita zinthu mwathayo kulinga ku dziko lapansi. Ngati anthu akadazindikira kuti ali oŵerengera kwa Mulungu kaamba ka zimene amachitira chilengedwe chake, mwinamwake iwo akanakhala osamala kwambiri m’nkhani zonga ngati kuipitsa, kuwononga chiphimba thambo, ndi kutentha kwa dziko lonse.
Chiyambi cha Moyo
Talingaliraninso funso ili: Kodi moyo unayamba motani? Anthu aphunzitsidwa kuti moyo unayamba wokha popanda kuloŵereramo kwa Mulungu. Komatu zimenezi zimasemphana ndi lamulo lokhazikitsidwa bwino la sayansi. Panthaŵi ina anthu ankakhulupirira kuti akafaluvu ankachokera ku ndoŵe za ng’ombe, nyongolotsi kuchokera ku mnofu wovunda, ndipo makoswe kuchokera m’matope. Ngakhale m’zaka za zana lapita, asayansi ankaphunzitsa kuti tizilombo tating’ono timachokera ku zinthu zopanda moyo. Koma malingaliro ameneŵa anatsutsidwa ndi Redi, Pasteur, ndi asayansi ena. The World Book Encyclopedia (kope la mu 1990) ikufotokoza kuti: “Pambuyo pa kufufuza kwa Pasteur, akatswiri a zamoyo ambiri analivomereza lingaliro lakuti zamoyo zonse zimachokera ku zinthu zamoyo zomwe zilipo kale.”
Komabe, asayansi amapanga nthanthi yakuti nthaŵi zakale, zinthu zinali zosiyanako. Iwo amati zamoyo za selo imodzi zoyambirira zinakhalako mwamwaŵi kuchokera ku msanganizo wopanda moyo umene amautcha primeval soup, womwe unali ndi zinthu zofunikira kaamba ka moyo. “Mwaŵi, mwaŵi wokha ndiwo unachita zonsezo, kuchokera ku primeval soup nkukhala munthu,” akulengeza motero Christian de Duve m’bukhu lakuti A Guided Tour of the Living Cell.
Polankhula za Mulungu, Baibulo likuti: ‘Chitsime cha moyo chiri ndi inu.’ (Salmo 36:9) Ndemanga imeneyi njogwirizanadi ndi zimene zawonedwa—kuti moyo ungachokere ku moyo womwe ulipo kale. Komabe, popeza kuti sayansi yotchuka imakonda kulingalira mphatso imodzi yabwino koposa yochokera kwa Mulungu, moyo, kukhala chinachake chomwe chinangochitika, anthu ambiri amalingalira kuti alibe thayo lirilonse kulinga kwa Mulungu kaamba ka mmene amagwiritsirira ntchito miyoyo yawo. Chotero, iwo amaswa malamulo a Mulungu, kutsenderezana, kuberana, kuphana, ndikuwononga ndalama zambiri, nthaŵi, ndi luso m’kupanga zida zakupha mowopsa ndi kusakaza kwambiri.
Kuthetsa Nkhaniyo
Pambali pa osakhulupirira Mulungu ndi okhulupirira zamakono, anthu ena osaŵerengeka amakana ufumu wa Mulungu. Anthu ambiri lerolino amati amakhulupirira Mulungu, ndipo oposa mamiliyoni 1,700 amadzitcha Akristu. Kwa zaka mazana ambiri matchalitchi a Chikristu Chadziko atamanda Mulungu mwapoyera m’mautumiki awo. Koma kodi ambiri a anthu 1,700 miliyoni ameneŵa aimadi pati m’nkhani ya ufumu wa Mulungu?
Ponse paŵiri munthu aliyense payekha ndi maiko asonyeza kusaulingalira kwawo mwakuchita zinthu mosemphana ndi malamulo achindunji a Mulungu. Maiko odzitcha kukhala Achikristu achilikiza machitachita opanda umulungu a chiwawa, kuphatikizapo nkhondo zoipitsitsa ziŵiri m’mbiri ya anthu—ndipo atsogoleri achipembedzo “Achikristu” kumbali zonse ziŵirizo anadalitsa nkhondo zimenezo! Mwa chinyengo chimenecho, iwo amuimira moipa kwambiri Mulungu. Monga momwe Baibulo likulongosolera kuti: ‘Avomereza kuti adziŵa Mulungu, koma ndi ntchito zawo amkana iye.’—Tito 1:16.
Komabe, Mulungu “sakhoza kudzikana yekha.” (2 Timoteo 2:13) Nthaŵi iyenera kufika pamene iye adzathetseratu mbali zonse za nkhani ya ufumu imeneyi mogwirizana ndi chifuno chake cholongosoledwa ichi: “Adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.” (Ezekieli 38:23) Koma kodi nchifukwa ninji watenga nthaŵi yaitali chotero? Kodi pomalizira pake nkhaniyo idzathetsedwa motani? Ndipo kodi mungapange motani zosankha zolondola m’nkhani yofunika koposa imeneyi?
[Mawu a Chithunzi patsamba 2]
Chithunzi chakumbuyo chapachikuto: U.S. Naval Observatory photo
[Mawu a Chithunzi patsamba 3]
Kumbuyo: U.S. Naval Observatory photo