Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w91 7/1 tsamba 28-30
  • Kukhala Otanganitsidwa Kwambiri ndi Mbiri Yabwino

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kukhala Otanganitsidwa Kwambiri ndi Mbiri Yabwino
  • Nsanja ya Olonda—1991
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Chitsanzo Chathu Lerolino
  • Kodi Mukuchita Mbali Yanu?
  • Mphotho za Uminisitala Wolinganizika
  • Dziperekeni Nokha!
  • ‘Tanganidwani Kwambiri’ ndi Utumiki Wanu
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2001
  • ‘Pitiriza Kulankhula, Usakhale Chete’
    ‘Kuchitira Umboni Mokwanira za Ufumu wa Mulungu’
  • Kodi Pali Uminisitala Umene Mungachite?
    Nsanja ya Olonda—1991
  • Kodi Mukukwaniritsa Mbali Zonse za Utumiki Wanu?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2019
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1991
w91 7/1 tsamba 28-30

Kukhala Otanganitsidwa Kwambiri ndi Mbiri Yabwino

MTUMWI Paulo adali m’vuto lodziŵika kwa Mboni za Yehova zomwe ndiaminisitala anthaŵi zonse​—iye anali wopereŵera m’zandalama. Chotero m’Korinto iye anayamba ntchito yotsika yopanga mahema imene anaiphunzira pamene adali wachichepere. Ntchitoyo inali yovuta, ndipo panthaŵi zina mwina manja ake anakha mwazi chifukwa chogwira nsalu zahema zokakala. Ndalama zopezedwa zinangompezera chakudya ndi chofunda, koma iye anali wokhutira, popeza kuti pamene ntchito yake yakuthupi inatha tsiku lirilonse, anaika ziŵiya za ntchito yake ndi kuchita chinthu chachikulu chimene anabwerera ku Korinto​—analalikira mbiri yabwino!​—Afilipi 4:11, 12.

Pasabata, Paulo ankapita ku sunagoge. Zowona, Paulo poyamba analankhula kwa omvetsera ake a ku Korinto “mofoka ndi m’mantha, ndi monthunthumira mwambiri.” (1 Akorinto 2:1, 3) Koma posonkhezeredwa ndi mmene ena analabadirira uthenga wake, Paulo anapitirizabe ‘kufotokozera m’sunagoge masabata onse, nakopa Ayuda ndi Ahelene.’​—Machitidwe 18:1-4.

Komabe, kwa nthaŵi yakutiyakuti, Paulo ankangolalikira mochepekera. Ndiyeno kunabwera Sila ndi Timoteo kuchokera ku Makedoniya ndi chopereka chowoloŵa manja chimene ‘chinakwaniritsa kusoŵa kwake.’ (2 Akorinto 11:9; Afilipi 4:15) Cholimbikitsanso, chinali uthenga wakuti abale ku Tesalonika anali ochirimika mosasamala kanthu za chizunzo.​—1 Atesonika 3:6.

Kodi zimenezi zinamyambukira motani Paulo? ‘Paulo anayamba kukhala wotanganitsidwa kwambiri ndi mawuwo [“anapereka nthaŵi yake yonse kukulalikira,” The Jerusalem Bible; Today’s English Version], akulalikira kwa Ayuda nachitira umboni wakuti Yesu ndiye Kristuyo.’ (Machitidwe 18:5, NW) Pokhala atawonjoledwa ku mavuto a zandalama kwakanthaŵi, Paulo sanakhale pansi mpaka anabwerera ku ulaliki wa nthaŵi zonse. Iye anabwerera ku ntchito yake ali ndi changu chokangalika, osati kungolalikira kwa Ayuda koma ngakhale kupatula nthaŵi yakulemba yoyamba ya makalata ake ouziridwa​—kalata yomka kwa Atesalonika!

Chitsanzo Chathu Lerolino

Cholembedwa cha ntchito yaikulu ya Paulo m’Korinto chinasungidwa kotero kuti chilimbikitse Akristu onse kukhala otanganitsidwa kwambiri ndi mbiri yabwino. Paulo anazindikira kuti Ambuye Yesu iyemwiniyo anapereka kwa ophunzira ake ulemu waukulu wokhala “kuunika kwa dziko lapansi.” Iwo sanafunikire kukubisa kuunika kumeneku. Yesu anawauza kuti: ‘Muwalitse inu kuunika kwanu pamaso pa anthu, kuti pakuwona ntchito zanu zabwino, alemekeze Atate wanu wakumwamba.’ (Mateyu 5:14-16) Ichi chinatanthauza kukhala ndi phande lokwanira m’kulalikira konenedweratu ndi Yesu. (Mateyu 24:14; 28:19, 20; Machitidwe 1:6-8) Kulalikidwa kwa mbiri yabwino ya Ufumu imeneyi kunali chifukwa chachikulu chimene mpingo Wachikristu unakhalirako.

Akristu oyambirira, mofanana ndi Paulo, anaiwona ntchito yolalikira imeneyi kukhala yofunika kwambiri. Chotero, pamene adani a Mulungu analingalira kuti anazima kuunika kwenikweni mwakumupha mwankhanza “Mkulu wa moyo,” otsatira ake anapitirizabe kukhala kuunika kwa dziko lapansi, akumalalikira mokangalika. (Machitidwe 3:15) Ngakhale chizunzo sichinaletse kuyesayesa kwawo. Cholembedwa cha Baibulo chimati: ‘Masiku onse m’kachisi ndi m’nyumba sanaleka kuphunzitsa ndi kulalikira Kristu Yesu.’ (Machitidwe 5:42) Palibe chimene chinakhoza kuwaletsa!

M’nthaŵi zamakono, Akristu mofananamo akhala otanganitsidwa kwambiri ndi ntchito yochitira umboni. Chakumapeto kwa zaka za zana la 19, ophunzira a Mawu a Mulungu osonkhezeredwa ndi chikumbumtima anayamba kuwona kufunika kwa kugaŵana chowonadi cha Baibulo ndi ena. Zion’s Watch Tower Tract Society​—gulu limene lakula kukhala lamitundu yonse​—linapangidwa kukhala lalamulo mu 1884. Ophunzira Baibulo ameneŵa, otchedwa Mboni za Yehova kuyambira mu 1931, adzaza kwenikweni dziko lapansi ndi chidziŵitso cha Mawu a Mulungu. Ntchito yawo yaikulu yatulukapo khamu lalikulu la anthu oposa mamiliyoni anayi! Ndipo mosakaikira chiŵerengero chawo chidzapitirizabe kumakula pansi pa chitsogozo cha Yehova.​—Yesaya 60:22.

Kodi Mukuchita Mbali Yanu?

Yesu anati: ‘Zotuta zichulukadi koma antchito ali oŵerengeka.’ (Mateyu 9:37, 38) Mu 1990 pafupifupi anthu okwanira mamiliyoni khumi anapezeka pa Chikumbutso cha imfa ya Kristu. Ndikuthekera kotani nanga kumene kulipo kwa kututa kwa padziko lonse! Koma pamene tikusangalala ndi kufutukuka kopitirizabe kumeneku, aliyense ayenera kudzifunsa kuti, ‘Kodi ineyo ndikukhala ndi phande lalikulu motani m’ntchito yaikulu imeneyi? Kodi ndimatero mokhazikika​—mlungu uliwonse ngati kuli kotheka?’

Akulu ayenera kutsogolera m’ntchito imeneyi monga “zitsanzo za gululo.” (1 Petro 5:3) Zowonadi, akulu ambiri ali ndi ntchito zakuthupi. Analinso wotero mtumwi Paulo pamene anali m’Korinto. Komabe, iye anapatula nthaŵi kaamba ka ntchito yokhazikika ya kulalikira. Akulu ambiri lerolinonso ngotanganitsidwa kwambiri ndi ntchito zauzimu kumapeto a mlungu. Ichi chikhoza kukhala ndi chiyambukiro champhamvu ndi cholimbikitsa kwa onse mumpingo. M’miyezi ina pamene kuyesayesa kwapadera kwachitidwa, mipingo yochulukirapo yakhala ndi ambiri a ofalitsa ake akuloŵa muutumiki waupainiya. Kodi chinsinsi pamenepa nchiyani? Nchakuti akulu amatsogolera ponse paŵiri m’kulalikira ndi m’kulinganiza makonzedwe autumiki wakumunda.

Atumiki otumikira mofanamo akhoza kukhala chisonkhezero chabwino ku mpingo ngati amakhala ndi phande mokhazikika muutumiki wakumunda. Kumbukirani, Malemba amafuna kuti iwo akhale “olemekezeka, . . . akutumikira bwino.” (1 Timoteo 3:8, 13) Kukhulupirika muutumiki wakumunda nkofunika kuti mbale ayeneretsedwe monga mkulu kapena mtumiki wotumikira.​—Tito 1:8, 9.

Mofanana ndi Paulo, ena amakhoza kuchepetsako ntchito yawo yakuthupi ndiyeno kuchita upainiya. Chiŵerengero cha apainiya okhazikika, othandiza, ndi apadera chinawonjezereka kuchokera pa 137,861 m’zaka khumi zokha zapitazo kufika pa 536,508 mu 1990. Ndithudi, dalitso ndi chivomerezo cha Yehova ndizo zokha zikachititsa zimenezi. Komabe, apainiya ayenera kusamala kugwiritsira ntchito nthaŵi mwanzeru, osati kungofuna kupanga lipoti labwino mwakupeza maola ambiri. Apainiyanu, kodi ndinu okonzekera bwino lomwe ndi ogwira mtima muuminisitala? Kodi mumakalamira kupanga kuwongokera kopitirizabe kotero kuti uminisitala wanu ukhaledi wobala zipatso?

Mphotho za Uminisitala Wolinganizika

Kodi mumayamikira chidziŵitso chosungitsa moyo choperekedwa mwezi uliwonse mu Nsanja ya Olonda ndi magazini anzake, Galamukani!? Mosakaikira mumatero. Kodi chiyamikiro chanu chakusonkhezerani kukhala ndi phande m’kuwagaŵira magazini ameneŵa? Mlongo wina mu Botswana anatero. Iye kale anali wotsutsa chowonadi, koma mwamuna wake anamuŵerengera magaziniwo. M’kupita kwanthaŵi anasintha mtima ndi kukhala Mboni. Chinkana kuti satha kuŵerenga, iye ngwachipambano kwambiri m’kugaŵira magazini, mwakumati, “Sinditha kuŵerenga, koma mwamuna wanga amandiŵerengera magaziniŵa. Ndimasangalala nawo, ndipo ndikhulupirira kuti nanunso mudzatero.”

Kodi bwanji osakhala ndi phande kwa mlungu ndi mlungu m’ntchito yopulumutsa moyo imeneyi? Mutangokhala ndi ziyeneretso zauzimu, mpingo Wachikristu udzakhala wokondwa kukuthandizani kuyamba. Komabe, kugaŵira magazini ndimbali imodzi yokha ya utumikiwo. Aliyense wotanganitsidwa kwambiri ndi mbiri yabwino amayesayesa kukhala ndi uminisitala wolinganizika. Mwachitsanzo, Watch Tower Society imafalitsa mamiliyoni a mabuku achikuto cholimba, ndipo ameneŵa amagaŵiridwa kwa anthu monga magwero okhalitsa kwambiri a chakudya chauzimu. Kodi mwakhala ndi luso lokwanira lakugaŵira mabuku muuminisitala wanu, monga Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi?

Ndipo bwanji ponena za anthu amene amasonyeza chikondwerero? Kodi mumasunga cholembedwa chabwino kuti mupange maulendo obwereza kwa iwo? Maulendo oterowo angatsogolere ku mbali ya utumiki imene imadzetsa chisangalalo chabwino koposa​—ntchito ya phunziro Labaibulo lapanyumba. Kumbukirani, Yesu anatilamula pa Mateyu 28:19, 20 ‘kupanga ophunzira, kuwabatiza.’ Ichi chimatanthauza kuphunzira nawo Baibulo. Zowonadi, kuyamba phunziro kaŵirikaŵiri kumafuna kuumirira. Mboni ina inakumana ndi okwatirana okalamba omwe anavomera phunziro Labaibulo ndi mtima wonse. Koma iwo anasinthira kutsogolo phunzirolo motsatizana kwa milungu itatu. Mkupita kwanthaŵi phunzirolo linayambidwa. Kenaka, kwakanthaŵi, okwatiranawo anadumpha phunzirolo pafupifupi pambuyo pa mlungu uliwonse. Komabe, potsirizira pake, mkaziyo anapita patsogolo mpaka kubatizidwa. “Pambuyo pobatizidwa,” mbaleyo akukumbukira motero, “maso ake ananjerama ndi misozi yachisangalalo, chimene chinachititsa misozi ya chisangalalo kwa mkazi wanga ndi ine.” Inde, kukhala wotanganitsidwa ndi mbiri yabwino kumadzetsa chisangalalo chosaneneka!

Dziperekeni Nokha!

Yesu Kristu ndi mtumwi Paulo anatikhazikitsira zitsanzo zakuti tizitsanzire. Ndipo tiri nazo zitsanzo zazikulu pakati pa Mboni za Yehova m’nthaŵi zamakono. Ino ndiyo nthaŵi yakuti onse odziŵa mbiri yabwino akhale okangalika mokwanira m’kuidziŵikitsa kwa ena. Baibulo limatitsimikizira kuti ntchito yonseyo ‘siiri chabe.’​—1 Akorinto 15:58.

Mofanana ndi Paulo, ambiri ali ndi mathayo a zandalama oti awakwaniritse. Chifukwa cha chimenechi, ambiri sangakhoze kuchita upainiya. Koma ndi chithandizo cha Yehova, onse angatsatire uphungu wabwino woperekedwa pa Aroma 12:11 wakuti: ‘Musakhale aulesi m’machitidwe anu; khalani achangu mumzimu, tumikirani [Yehova, NW].’ Ndipo ngati mikhalidwe isintha kulola nthaŵi yowonjezereka yoithera muutumiki wa Yehova, aliyense yemwe amakondadi Yehova, adzautenga mwaŵiwo, mofanana ndi Paulo. Khalani otanganitsidwa kwambiri ndi mbiri yabwino! Kuteroko sikudzangodzetsa madalitso tsopano koma mtsogolo mudzabweretsa moyo wamuyaya wokhala ndi chimwemwe chosatha ndi chisangalalo!​—Mateyu 19:28, 29.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena