‘Tanganidwani Kwambiri’ ndi Utumiki Wanu
1 Tikamaŵerenga kuti mtumwi Paulo ankapanga mahema ali ku Korinto, tingaganize kuti zimenezi sizinam’patse nthaŵi yambiri yolalikira. Koma pa Machitidwe 18:5, NW, pamati: ‘Paulo anatanganidwa kwambiri ndi mawu, akumachitira umboni kwa Ayuda kutsimikizira kuti Yesu ndiye Kristu.’ N’chifukwa chiyani Paulo anatanganidwa kwambiri ndi ntchito yolalikira? Ngakhale kuti anthu ambiri ku Korinto anali atakhulupirira, Ambuye anam’tsimikizira kuti mu mzindawu munali anthu ambiri ofunika kukhala ophunzira. (Mac. 18:8-11) Kodi ifeyo tili nazonso zifukwa zimene tiyenera kukhalira otanganitsidwa kwambiri ndi utumiki wathu? Inde tili nazo. Tikhoza kupeza anthu ambiri amene tingawaphunzitse choonadi.
2 Therani Nthaŵi Yambiri mu Utumiki Mwezi wa April: Ndithudi mwezi uliwonse mumafuna kutanganidwa ndi ntchito yolalikira uthenga wabwino. Komabe pali miyezi ina imene imatipatsa mpata wochuluka ‘wotanganidwa kwambiri’ ndi ntchito imeneyi. Miyezi imeneyo imaphatikizapo April amene m’pachimake pa nyengo ya Chikumbutso. Kodi mungathe kuchita upainiya wothandiza kapena kuchita zambiri mu utumiki? Ofalitsa ambiri amene achita zimenezi adalitsidwa kwambiri. (2 Akor. 9:6) Ngati mukuchita zimene mungathe, dziŵani kuti Yehova amasangalala ndi utumiki wanu wamtima wonse. (Luka 21:2-4) Mulimonse momwe zingakhalire, cholinga chanu chikhale ‘kutanganidwa kwambiri’ ndi utumiki mu April. Musaiŵalenso kupereka malipoti a utumiki mwezi ukatha kuti ntchito yanu iphatikizidwe pamodzi ndi ya anthu ena onse a Yehova.
3 Ayendereni Anthu Atsopano Amene Anabwera pa Chikumbutso: Chaka chatha m’Malaŵi muno, anthu amene anapezeka pa Chikumbutso anali okwanira 150,754. Sitikudziŵa kuti chaka chino tidzakhala angati. Koma malipoti akusonyeza kuti tidzakhala ndi “zotuta” zochuluka. (Mat. 9:37, 38) Chotero, pitani mwamsanga kukawathandiza mwauzimu anthu achidwi amene anabwera pa Chikumbutso. Kuchedwa kupitako kungam’patse mpata ‘woipayo kukwatula mawu a Ufumu ofesedwa m’mitima mwawo.’ (Mat. 13:19) Kupitako mofulumira kudzasonyeza kuti ndinudi ‘wotanganidwa kwambiri’ ndi utumiki wanu.
4 Pitirizani Kuthandiza Anthu Osagwira Ntchito: Mu February tinayamba ntchito yapadera yothandiza anthu osagwira ntchito. Ngati ena sanayenderedwe paulendo wa ubusa, akulu ayendere anthu ameneŵa mwezi wa April usanathe. Akulu aone pomwe pagona vuto la munthu aliyense ndiponso momwe angam’thandizire kuyambiranso kutumikira Yehova mwachangu. Kuwathandiza mwachikondi kotereku kumasonyeza kuti akulu akusamaliradi maudindo awo monga abusa a “gulu la Mulungu.” (1 Pet. 5:2; Mac. 20:28) Nsanja ya Olonda ya September 15, 1993, tsamba 22-3, ili ndi malingaliro abwino kwambiri amene akulu angagwiritse ntchito pothetsa mavuto asanu odziŵika okhudza anthu osagwira ntchito. Kunena zoona, ena angalimbikitsidwe kuyambiranso utumiki wakumunda mu April.
5 Thandizani Anthu Ambiri Kukhala Ofalitsa Osabatizidwa: Kodi ana anu ayeneretsedwa kukhala ofalitsa atsopano a uthenga wabwino? Bwanji ena amene mukuphunzira nawo Baibulo? Ngati akulu anawavomereza anthu ameneŵa, kodi mwezi wa April sungakhale nthaŵi yabwino kuyamba kufalitsa? Ngati munthu akulimbikira ndipo waphunzira bulosha la Mulungu Amafunanji komanso buku la Chidziŵitso, mungapitirize kuphunzira Baibulo m’buku lachiŵiri mogwiritsa ntchito limodzi la mabuku awa, Mawu a Mulungu, Mtendere Weniweni, kapena Ogwirizana m’Kulambiridwa. Cholinga chanu chikhale kuthandiza wophunzira kuchidziŵa bwino choonadi, kuti ayenerere kukhala wofalitsa wosabatizidwa kenako Mboni ya Yehova yodzipatulira ndiponso yobatizidwa.—Aef. 3:17-19; 1 Tim. 1:12; 1 Pet. 3:21.
6 Ngati mukhalabe ndi chidwi chenicheni mwa amene mumaphunzira nawo Baibulo, mudzawathandiza kutenga choonadi kukhala chawochawo. Mboni ina inakumana ndi banja lina lachikulire limene linavomera mosangalala kuphunzira Baibulo. Koma kwa masabata atatu otsatizana banjali linkangoti, tiphunzira mlungu wamaŵa. Kenako anayamba kuphunzira. Ndiye banja lija linayamba kuzemba kuphunzira mlungu uliwonse. Kenako, mkaziyo anayamba kulimbikira mpaka anabatizidwa. “Mayiyu atabatizidwa analira ndi chisangalalo, zimene zinaliritsanso ine ndi mkazi wanga.” Akutero mbaleyo. Inde, ‘kutanganidwa kwambiri’ ndi uthenga wabwino kumadzetsa chimwemwe kwambiri!
7 Ulosi wa m’Baibulo komanso zimene zikuchitika m’dziko zikusonyeza kuti tili m’kati mwenimweni mwa nthaŵi ya mapeto. Ino ndi nthaŵi imene anthu a Mulungu onse akufunika ‘kutanganidwa kwambiri’ kuuza ena uthenga wabwino. Mtumwi Paulo akutitsimikizira kuti kugwira ntchito imeneyi “sikuli chabe mwa Ambuye” ayi.—1 Akor. 15:58.