Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w91 10/15 tsamba 3-4
  • Ngozi—Kodi Nzoikidwiratu Kapena Zochitika Zamwadzidzidzi?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ngozi—Kodi Nzoikidwiratu Kapena Zochitika Zamwadzidzidzi?
  • Nsanja ya Olonda—1991
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Baibulo Limaphunzitsa za Kukhulupirira Choikidwiratu?
    Nsanja ya Olonda—1996
  • Kodi N’chikonzero cha Mulungu Kapena Zangochitika?
    Galamukani!—1999
  • Kodi Kukhulupirira Kuikidwiratu Kumalamulira Moyo Wanu?
    Nsanja ya Olonda​—1990
  • Kufunafuna Tsogolo la Munthu
    Galamukani!—1999
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1991
w91 10/15 tsamba 3-4

Ngozi​—Kodi Nzoikidwiratu Kapena Zochitika Zamwadzidzidzi?

PAMENE Cristina, msungwana wokongola wochita mpikisano wamafashoni, anali kudutsa msewu wa Nove de Julho wotanganitsidwa ku São Paulo, Brazil, sanawone basi yomayandikira. Woyendetsayo anayesa mosaphula kanthu kuimitsa galimoto lake, koma kunali m’mbuyo mwalendo. Cristina anapondedwa ndi kuphedwa.

Ngozi yaikulu imeneyi inafalitsidwa patsamba loyamba m’nyuzipepala ya ku Brazil O Estado de S. Paulo. (July 29, 1990) Komabe inali kokha imodzi ya ngozi zopha anthu za pamsewu 50,000 zimene zimachitika chaka chirichonse mu Brazil. Ndipo pamene kuli kwakuti zikwizikwi zowonjezereka zimalemala ndi ngozi zotero, ena amapulumuka osavulala. Pamenepa, kodi nchifukwa ninji msungwanayu sanapulumuke? Kodi iye anaikidwiratu kufa pa tsikulo?

Anthu osaŵerengeka akalingalira kuti ziri choncho kumene. Iwo amakhulupirira m’choikidwiratu, kuti zochitika zazikulu, zonga ngati nthaŵi ya imfa ya munthuyo nzolinganizidwiratu. Chikhulupiriro chimenechi chadzutsa mawu onga ngati “Palibe amene angalimbane motsutsana ndi choikidwiratu,” “Nthaŵi yake yakwana,” kapena “Zidzakhala monga mmene zidzakhalira.” Kodi mawu ofala oterowo ali owona? Kodi ife tiri kokha akapolo a choikidwiratu?

Choikidwiratu, kapena chiphunzitso chakuti zochitika zonse zimalinganizidwa pasadakhale, chinawanda pakati pa Agiriki ndi Aroma amakedzana. Ngakhale lerolino, lingalirolo likali lolimba m’zipembedzo zambiri. Mwachitsanzo, Chisilamu chimakhulupirira mawu a Koran awa: “Palibe moyo umene ungafe konse kusiyapo mwachilolezo cha Allah ndi panthaŵi yoikika.” Chikhulupiriro m’choikidwiratu chirinso chofala m’Chikristu Chadziko ndipo chachirikizidwa ndi chiphunzitso cha cholinganizidwiratu, chophunzitsidwa ndi John Calvin. Chotero, kuli kofala kwa atsogoleri achipembedzo kuuza achibale oferedwa kuti ngozi yakutiyakuti inali “chifuniro cha Mulungu.”

Komabe, lingaliro lakuti ngozi ziri chotulukapo cha choikidwiratu, nlotsutsana ndi chibadwa, chidziŵitso chapapitapo, ndi kulingalira. M’chenicheni, ngozi za galimoto sizingakhale konse chotulukapo cha kulowerera kwa Mulungu, popeza kuti kaŵirikaŵiri kupenda kosamalitsa kudzavumbula chochititsa chenicheni cha ngoziyo. Ndiponso, kufufuza kumasonyeza mowonekera bwino kuti kulabadira malangizo oyenera​—onga ngati kumanga lamba lamgalimoto​—kumachepetsa kwakukulukulu kuthekera kwa ngozi yakupha. Kodi malangizo achisungiko alionse angalepheretsedi chifuniro cholinganizidwiratu cha Mulungu?

Komabe, chikhulupiriro m’choikidwiratu chimayambukira moipa wokhulupirirayo. Kodi sichimalimbikitsa machitachita opusa, onga ngati kunyalanyaza malire akuthamanga kwa galimoto ndi zizindikiro za pamsewu kapena kuyendetsa galimoto mutaledzera ndi zoledzeretsa kapena mankhwala ogodomalitsa? Choipa koposa, nchakuti chikhulupiriro m’choikidwiratu chimasonkhezera anthu ena kuimba Mulungu mlandu pamene ngozi iwayambukira. Pokhala okwiya ndi opanda chithandizo, ndipo otsimikizira kuti Mulungu ali wosadera nkhaŵa, iwo angatayedi chikhulupiriro. Emerson wolemba ndakatulo ananena moyenerera kuti: “Mbali yoipitsitsa yovuta m’moyo ndiyo chikhulupiriro mu Choikidwiratu chankhanza kapena Cholinganizidwiratu.”

Koma kodi Baibulo limanenanji za masoka ndi ngozi? Kodi ilo limaphunzitsadi kuti zimenezi ziri zochititsidwa ndi choikidwiratu? Ndiponso, kodi limanenanji za ziyembekezo zathu za chipulumutso? Kodi tiri ndi chosankha chirichonse m’nkhaniyi?

[Mawu Otsindika patsamba 4]

“Mbali yoipitsitsa yovuta m’moyo ndiyo chikhulupiriro mu Choikidwiratu chankhanza kapena Cholinganizidwiratu.”​—Ralph Waldo Emerson

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena