Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w92 2/1 tsamba 25-28
  • Khalani ndi Mzimu Wakudzimana!

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Khalani ndi Mzimu Wakudzimana!
  • Nsanja ya Olonda—1992
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Chiyeneretso cha Baibulo
  • Madalitso Otuluka m’Kudzimana
  • Njira Zokhalira Wodzimana
  • Kutumikira Yehova ndi Mzimu Wodzimana
    Nsanja ya Olonda—1993
  • N’kukhaliranji Wodzimana?
    Nsanja ya Olonda—2000
  • Kodi Muli ndi Mzimu Wodzimana?
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2000
  • Nsembe Zotamanda Zimene Zimakondweretsa Yehova
    Nsanja ya Olonda—2000
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1992
w92 2/1 tsamba 25-28

Khalani ndi Mzimu Wakudzimana!

ROLFa anali wantchito wodalirika. Pamene anasankha kupeza ntchito yaganyu kotero kuti awonjezere phande lake muuminisitala Wachikristu, womlemba ntchito anavomereza mosavuta. Chotero Rolf anali wokhoza kuchita upainiya kwazaka zambiri. Komabe, tsiku lina mkhalidwe wantchito unasintha. Rolf anasonyeza kukhala waluso kwambiri pantchito yake kwakuti anapatsidwa udindo wa manijala wamalonda wa kampaniyo. Ntchitoyo inaphatikizapo malipiro abwino ndi ziyembekezo zabwino zamtsogolo za kukwezedwa kowonjezereka. Komabe, sikukakhalanso kotheka kuchita ntchito yaganyu.

Rolf anali ndi mkazi ndi ana aŵiri owasamalira, ndipo ndalama zowonjezerekazo zikanakhala zothandiza. Komabe, iye anakana mwaŵiwo nafunsira ntchito ina, imene ikamlola kukwaniritsa mathayo ake ponse paŵiri auzimu ndi azandalama. Wolemba ntchito wa Rolf anadabwa ndi chosankhachi. Pozindikira kuti ngakhale malipiro aakulu koposa akakhala osaphula kanthu, mkulu wantchitoyo anati: “Ndawona kuti sindingapikisane ndi kutsimikiza kwako.”

Inde, Rolf anali wotsimikiza. Koma analinso ndi mkhalidwe wina​—mzimu wakudzimana. Mzimu umenewo ngwosoŵa m’dziko lathu lokonda kudzikondweretsa. Koma ungachititse njira yamoyo yopindulitsa ndi yokhutiritsa. Kodi mzimu wakudzimana ndiwo chiyani? Kodi umaloŵetsamonji? Ndipo kodi tiyenera kuchitanji kuti tiusunge?

Chiyeneretso cha Baibulo

Kudzimana kumatanthauza kuleka kapena kulepa chinachake chamtengo waukulu. Kudzimana kwakhala mbali ya kulambira koyera kuyambira pamene mboni yokhulupirika yoyamba, Abele, inapereka nsembe kwa Mulungu ‘mwana woyamba wa nkhosa zake.’ (Genesis 4:4) Anthu achikhulupiriro monga Nowa ndi Yakobo, anamtsanzira. (Genesis 8:20; 31:54) Nsembe zanyama zinalinso mbali yofunika ya Chilamulo cha Mose. (Levitiko 1:2-4) Komabe, pansi pa Chilamulocho olambira anapemphedwa kupereka zabwino koposa. Iwo sanaloledwe kupereka nyama yopunduka iriyonse monga nsembe. (Levitiko 22:19, 20; Deuteronomo 15:21) Pamene Aisrayeli ampatuko analakwira lamuloli, Mulungu anawadzudzula, akumati: ‘Pamene mupereka yodwala [kuti ikhale nsembe, mukuti], Palibe choipa! Kaiperekeni kwa kazembe wanu, mudzamkomera kodi? Kapena adzakuvomerezani kodi? . . . Kodi ndiyenera kuilandira ku dzanja lanu?’​—Malaki 1:8, 13.

Lamulo lakupereka nsembe linapitirizidwa m’kulambira Kwachikristu. Komabe, popeza kuti Kristu anapereka mtengo wonse wa dipo, nsembe zanyama sizirinso zolandiridwa kwa Mulungu. Chotero, kodi nchiyani chimene Akristu angapereke nsembe molandirika? Paulo analemba pa Aroma 12:1 kuti: ‘Chifukwa chake ndikupempheni inu, abale, mwa zifundo za Mulungu, kuti mupereke matupi anu nsembe yamoyo, yopatulika, yokondweretsa Mulungu, ndiko kupembedza kwanu koyenera.’ Ndikusintha kodabwitsa kotani nanga! Mmalo mopereka nyama zakufa, Akristu anayenera kudzipereka iwo eni monga nsembe yamoyo​—nyonga yawo, chuma, ndi maluso. Ndipo monga momwe zinaliri mu Israyeli, Yehova sadzalandira nsembe “zodwala,” kapena zamtima wogaŵanika. Iye amafuna kuti olambira ake ampatse zabwino koposa, kuti amtumikire ndi mtima wawo wonse, moyo, nzeru, ndi mphamvu.​—Marko 12:30.

Mzimu wakudzimana umaloŵetsamo zoposa kungomamatira ku ndandanda ya misonkhano ndi kugwira ntchito muuminisitala Wachikristu. Kumatanthauza kutsimikiza mtima kuchita chifuniro cha Mulungu mosasamala kanthu zoloŵetsedwamo. Kumatanthauza kukhala okonzeka kukumana ndi zovuta ndi zododometsa. Yesu anati: ‘Ngati munthu afuna kudza pambuyo panga, adzikane yekha, natenge [mtengo wake wozunzirapo, NW], nanditsate ine.’ (Mateyu 16:24) Mkristu samapanga zokhumba zaumwini kapena zonulirapo zakuthupi kukhala nkhaŵa yake yaikulu. Moyo wake umazikidwa pa kufuna choyamba Ufumu wa Mulungu ndi chilungamo Chake. (Mateyu 6:33) Ngati kuli kotheka, iye amakhala wokonzekera ‘kutenga mtengo wake wozunzirapo,’ kuzunzidwa, kunyazitsidwa, kapena ngakhale kufa!

Madalitso Otuluka m’Kudzimana

Poyang’anizana ndi zinthu zothekera kutichitikira zimenezi, wina angakaikire ngati kudzimana kulidi koyenerera. Kwa amene amakonda Yehova Mulungu ndipo amafuna kulemekeza dzina lake, kudzimana kulidi koyenerera. (Mateyu 22:37) Talingalirani chitsanzo changwiro chosonyezedwa ndi Yesu Kristu. Asanabwere padziko lapansi, iye anali ndi udindo wokwezeka kumwamba monga cholengedwa chauzimu. Komabe, monga momwe anawauzira ophunzira ake, iye ‘sanatsate chifuniro chake, koma cha iye womtuma.’ (Yohane 5:30) Chotero mofunitsitsa ‘anadzikhuthula yekha, natenga mawonekedwe a kapolo, nakhala m’mafanizidwe a anthu; ndipo popezedwa m’mawonekedwe ngati munthu, anadzichepetsa yekha, nakhala womvera kufikira imfa, ndiyo imfa ya [pamtengo wozunzirapo, NW].’​—Afilipi 2:7, 8.

Nsembe zoterozo sizinali zopanda phindu. Popeza kuti Yesu anali wofunitsitsa ‘kutaya moyo wake chifukwa cha abwenzi ake,’ iye anakhoza kulipira mtengo wa dipo, kutheketsa anthu opanda ungwiro kupeza moyo wosakhoza kufa kumwamba, kapena moyo wosatha padziko lapansi. (Yohane 3:16; 15:13; 1 Yohane 2:2) Mwakusunga mosamalitsa umphumphu wake, anachititsa dzina la Yehova kutamandidwa mokulira. (Miyambo 27:11) Nkosadabwitsa kuti Yehova anamdalitsa chifukwa cha kudzimana kumeneko! ‘Mulungu anamkwezetsa iye, nampatsa dzina limene liposa maina onse.’​—Afilipi 2:9.

Ndithudi, Yesu anali Mwana wobadwa yekha wa Mulungu. Kodi Mulungu amafupanso ena amene amadzimana motero kaamba ka iye? Inde, ndipo ichi chasonyezedwa ndi zitsanzo zambiri ponse paŵiri m’nthaŵi zakale ndi zamakono. Talingalirani cholembedwa cha Baibulo cha Rute Mmoabu. Kukuwonekera kuti iye anaphunzira za Yehova kupyolera mwa mwamuna wake Mwisrayeli. Pamene mwamunayo anamwalira, iye anafunikira kupanga chosankha. Kodi akakhalabe m’dziko lachikunja limene anabadwiramo, kapena kodi akapita ku Dziko Lolonjezedwa ndi apongozi ake okalamba, Naomi? Rute anasankha kumka, ngakhale kuti zinatanthauza kudzimana mayanjano ndi makolo ake ndipo mwina ngakhale chiyembekezo cha kukwatiwanso. Komabe, Rute anadziŵa Yehova, ndipo chikhumbo chakumlambira iye pakati pa anthu ake osankhidwa chinampangitsa kumamatira kwa Naomi.

Kodi Rute anafupidwa kaamba ka kudzimana koteroko? Iye anaterodi! M’kupita kwa nthaŵi, mwinimunda wotchedwa Boazi anamtenga iye kukhala mkazi wake, ndipo Rute anabala mwana wamwamuna wotchedwa Obedi, zimene zinampangitsa kukhala kholo lalikazi la Yesu Kristu.​—Mateyu 1:5, 16.

Mofananamo atumiki odzimana a Mulungu amakono akhala ndi madalitso. Mwachitsanzo, mu 1923, William R. Brown, wodziŵika bwino monga “Bible” Brown, anachoka kwawo ku West Indies kukayamba ntchito yolalikira Kumadzulo kwa Afirika. Iye anatsagana ndi mkazi wake ndi mwana wamkazi. Pomalizira pake anasamukira ku Nigeria, kumene ntchito yolalikira inkayamba kumene kubala zipatso. Pamodzi ndi nzika yachikuda ya ku Amereka yotchedwa Vincent Samuels ndi Mboni ina ya ku West Indies yotchedwa Claude Brown, “Bible” Brown anachita mbali yofunika m’mbali zoyambirira za ntchitoyo Kumadzulo kwa Afirika.

Lerolino ofalitsa oposa 187,000 akutumikira ku Sierra Leone, Liberia, Ghana, ndi Nigeria, magawo omwe anatsegulidwa ndi “Bible” Brown ndi mabwenzi ake. Asanamwalire mu 1967, “Bible” Brown anati: “Kuli kosangalatsa chotani nanga kuwona amuna ndi akazi akumvera mbiri yabwino ya Ufumu wa Mulungu!” Inde, iye anadalitsidwa molemera kaamba ka kudzimana kwake.

Njira Zokhalira Wodzimana

Kodi pali njira zina zotani zimene tingasonyezere mzimu wofananawo lerolino? Njira imodzi ndiyo kukhala ndi phande mokhazikika muuminisitala wakunyumba ndi nyumba. (Machitidwe 20:20) Kuchita zimenezo, makamaka pambuyo pa mlungu wa ntchito yakuthupi yotopetsa, sikungakhale kosavuta. Kungafunikire kudzilamulira ndi kumamatira kundandanda yabwino. Koma madalitso otulukapo amaposa kuwavutikira kochitidwako. Inde, mungakhale ndi mwaŵi wapadera wakuthandiza munthu wina kukhala ‘kalata wa Kristu . . . wosalembedwa ndi kapezi iyayi, koma mzimu wa Mulungu wamoyo; wosati m’magome amiyala, koma m’magome a mitima yathupi.’​—2 Akorinto 3:3.

‘Mwakuiombola nthaŵi’ mosamalitsa, kaya kuntchito yakuthupi kapena zosangulutsa, ena awonjezera phande lawo m’ntchito yolalikira. (Aefeso 5:16, NW) Ambiri amakonza ndandanda yawo kotero kuti achiteko upainiya wothandiza pafupifupi kamodzi pachaka. Ena ali okhoza kuchita upainiya wothandiza mosalekeza kapena kutumikira monga apainiya okhazikika. Kudzimana kwina kumene tingakulingalire ndiko kusamukira kumadera kumene kukufunikira ofalitsa Ufumu owonjezereka. Kaŵirikaŵiri izi zimaloŵetsamo kusintha njira yamoyo, kulimbana ndi zovuta, kutengera miyambo ndi makhalidwe atsopano. Koma madalitso akukhala ndi phande lokulira m’kuthandiza ena kupeza moyo amakupanga kudzimana koteroko kukhala koyenerera.

John Cutforth wobadwira ku Canada anazindikira zimenezi. Pambuyo pa kumaliza kwake maphunziro pa Sukulu ya Gileadi ya Baibulo ya Watchtower, anagaŵiridwa monga mishonale ku Australia. “Ndi mtunda wautali wotani nanga kuchokera kunyumba!” anakumbukira motero Mbale Cutforth. “Kodi ndidzabwereranso kuno ku Canada kudzawona makolo anga ndi mabwenzi Armagedo isanakanthe? Njira yokha yodziŵira zimenezi inali kupita.” Mbale Cutforth anapita, ndipo sanamve chisoni kuti anachita kudzimana koteroko. M’zaka zapambuyo pake anayambitsa ntchito yochitira umboni ku Papua New Guinea, kumene akutumikirabe mwachangu, ndipo wamaliza zaka 50 muutumiki wanthaŵi zonse. Panthaŵi ina anati: “Kufunafuna chitsogozo cha Yehova nthaŵi zonse, kulandira asainimenti iriyonse imene aiwona kukhala yoyenera kutipatsa, kumabweretsa chisangalalo, chimwemwe, chikhutiro, ndi mabwenzi osaŵerengeka.”

Ndithudi, mikhalidwe yonga thanzi, ndalama, ndi mathayo abanja ingachepetse zimene mungachite; sionse amene angatumikire monga apainiya ndi amishonale. Komabe, khalani otsimikiza mtima kukhala ndi phande lokwanira monga momwe mungathere pamisonkhano ndi muutumiki wakumunda, osalola zododometsa zazing’ono, monga kusacha bwino kwa tsikulo, kukulepheretsani. (Ahebri 10:24, 25) Mungakhozenso kupereka nthaŵi yanu yochulukira kuphunzira Mawu a Mulungu. Mabanja ena amachita zimenezo mwakuchepetsa nthaŵi yowonongedwa kupenyerera maprogramu a TV, mwinamwake kukhala ndi usiku umodzi pamlungu “wosapenyerera TV” kapena kusakhala nayo komwe TV. Mwachiwonekere, mwakupeza nthaŵi ya phunziro laumwini, “nsembe yakuyamika” imene ‘mumavomereza nayo dzina lake’ pamisonkhano ndi muutumiki wakumunda idzakhala nsembe yamtengo wake.​—Ahebri 13:15.

Kumbukirani kuti, ntchito yolalikira tsopano iri m’mbali zake zomalizira. Posachedwapa Mulungu adzabweretsa chiweruzo padziko laumbombo ndi lokonda kudzikondweretsa. (Zefaniya 2:3) Kuti tikhalebe ndi chiyanjo cha Mulungu, sitiyenera kudzimvera chisoni. Tiyenera ‘kupereka matupi athu nsembe yamoyo, yopatulika, yokondweretsa Mulungu.’ (Aroma 12:1) Mzimu woterowo udzabweretsa chimwemwe chachikulu ndi chikhutiro. Udzatithandiza kupeza chimwemwe chokulirapo muuminisitala wathu. Ndipo udzakondweretsa mtima wa Yehova Mulungu!​—Miyambo 27:11.

Choncho khalani ndi mzimu wakudzimana! Musazengereze kudzipereka kaamba ka ena ndi kuchilikiza zabwino za Ufumu. Paulo anafulumiza kuti: ‘Musaiŵale kuchitira chokoma ndi kugaŵira ena; pakuti nsembe zotere Mulungu akondwera nazo.’​—Ahebri 13:16.

[Mawu a M’munsi]

a Dzina lasinthidwa.

[Chithunzi patsamba 26]

Kupeza nthaŵi ya phunziro laumwini ndi utumiki wakumunda kungaloŵetsemo kudzimana, koma kumafupa

[Chithunzi patsamba 28]

W. R. Brown ndi John Cutforth anadalitsidwa molemera chifukwa cha kudzimana kwawo

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena