Kodi Muli ndi Mzimu Wodzimana?
1 Kuyamikira zimene Yesu Kristu mopanda dyera anachitira mtundu wa anthu kuyenera kutisonkhezera tonsefe kugwiritsa ntchito maluso athu, mphamvu zathu, ndi nyonga zathu modzimana. Malemba amapempha kuti: “Mupereke matupi anu nsembe yamoyo, yoyera, yolandirika kwa Mulungu, ndiyo utumiki wopatulika.” (Aroma 12:1, NW) Kudzipenda nthaŵi ndi nthaŵi kudzakuthandizani kuona ngati mukusonyeza mzimu umenewu mokwanira mmene mikhalidwe yanu ingalolere.
2 Pofuna Chidziŵitso cha Baibulo: Kodi mwapatula nthaŵi yoti muziŵerenga ndi kuphunzira Baibulo nthaŵi zonse? Kodi mumatsatira ndandandayo? Kodi n’chizoloŵezi chanu kukonzekera bwino misonkhano yampingo? Ngati ndinu mutu wabanja, kodi nthaŵi zonse mumachita phunziro la Baibulo ndi banja lanu? Kuchita zimenezi kungafune kudzimana nthaŵi yoonera TV kapena kompyuta ngakhalenso m’ntchito zina. Komabe, kumenekutu n’kudzimana kochepa zedi, popeza mukudziŵa kuti kuthera nthaŵi pa Mawu a Mulungu kudzakutsogolerani kumoyo wosatha!—Yoh. 17:3.
3 Pophunzitsa Ana Anu: Nthaŵi yabwino yoyamba kuphunzira kudzimana ndi ku ubwana. Aphunzitseni ana anu kuti pamene kuli kwakuti pali nthaŵi yoseŵera, payeneranso kukhala nthaŵi yogwira ntchito ndi yochita zinthu za teokalase. (Aef. 6:4) Apatseni ntchito zina zapakhomo. Ikani ndandanda yokhazikika yopita nawo limodzi muutumiki. Khomerezani malangizo anu mwa chitsanzo chanu chabwino.
4 M’ntchito za Mpingo: Mpingo umapindula pamene aliyense mumpingomo akudzimana kuti achite zinthu zokomera onse. (Aheb. 13:16) Kodi n’kotheka kwa inu kuthera nthaŵi yambiri m’ntchito yolalikira Ufumu ndi kupanga ophunzira? Kodi mungadzipereke kuthandiza odwala kapena okalamba, mwina mwakuwathandiza kuwatengera kumisonkhano?
5 Asanapereke nsembe yomaliza yamoyo wake waumunthu, Yesu analangiza ophunzira ake kuti ayenera kuika maganizo awo pazinthu za Ufumu. Zina zonse m’moyo zikhale pambuyo. (Mat. 6:33) Kukhala ndi mzimu wodzimana umenewu kudzatipatsa chimwemwe chochuluka pamene tikupitiriza kutumikira Yehova mosangalala.