Yehova Anatisamalira Pansi pa Chiletso—Gawo 1
Kwa zaka makumi ambiri Mboni za Yehova zakhala zofunitsitsa kudziŵa za abale awo m’maiko amene analetsa ntchito yawo Yachikristu. Ndife okondwa kutulutsa nkhani yoyamba mwa zitatu zovumbula zinthu zina zomwe zinachitika. Zimenezi nzolembedwa zaumwini za Akristu okhulupirika m’dziko lomwe kale linkatchedwa Jeremani wa Kum’maŵa.
MU 1944, ndinali wandende Wachijeremani wogwidwa m’nkhondo, wogwira ntchito monga mnthumwantumwa wa chipatala mu Msasa wa Cumnock, pafupi ndi Ayr, Scotland. Ndinkaloledwa kutulukira kunja kwa msasa, ngakhale kuti kudziŵana ndi anthu akumaloko kunaletsedwa. Ndikumawongola miyendo pa Sande ina, ndinakumana ndi mwamuna yemwe anayesayesa mwakhama kundifotokozera zinthu za m’Baibulo. Zimenezo zitachitika ndinkawongolera miyendo pamodzi naye nthaŵi zambiri.
Mkupita kwa nthaŵi anandiitanira kumsonkhano m’nyumba ina. Zimenezi zinamuika paupandu, chifukwa ndinali nzika ya dziko la adani. Panthaŵiyo sindinadziŵe kuti anali mmodzi wa Mboni za Yehova—mwachiwonekere msonkhanowo unali umodzi wa maphunziro Abaibulo atimagulu tating’ono. Ngakhale kuti sindinamvetsetse zambiri, ndimakumbukira bwino lomwe chithunzithunzi cha mwana wovala mkanjo woyera wautali, pamodzi ndi mkango ndi mwana wa nkhosa. Chithunzithunzi chimenechi cha dziko latsopano, cholongosoledwa m’bukhu la Baibulo la Yesaya, chinandikopa kwambiri.
Mu December 1947, ndinamasulidwa m’ndende. Nditabwerera kwathu ku Jeremani, ndinakwatira Margit, yemwe ndinamdziŵa isanayambe nkhondo. Tinakhala ku Zittau, pafupi ndi kumene dziko lathu limagaŵana malire ndi Poland ndi Chekosolovakiya. M’masiku angapo okha, mmodzi wa Mboni za Yehova anagogoda pachitseko chathu. Ndinauza mkazi wanga kuti: “Ngati ameneyu ndimmodzi wa gulu limene ndinakumana nalo ku Scotland, pamenepo tidzaphatikana nawo.” Mlungu umodzimodziwo, tinapezeka pamsonkhano wathu woyamba ndi Mbonizo.
Tinaphunzira m’Baibulo za kufunika kwa kupezeka pamisonkhano Yachikristu nthaŵi zonse ndi kukhala ndi phande m’ntchito yolalikira. Kunena zowona, zimene Mbonizo zinaphunzitsa kuchokera m’Baibulo mosataya nthaŵi zinakhala zinthu zofunika koposa m’miyoyo yathu. Mkupita kwa nthaŵi ndinayamba kuchititsa phunziro Labaibulo la kagulu. Ndiyeno, mu February 1950, oyang’anira oyendayenda Achikristu aŵiri anatifunsa nati: “Kodi simufuna kumizidwa?” Masana amenewo Margit ndi ineyo tinaphiphiritsira kudzipatulira kwathu kwa Mulungu mwa ubatizo.
Kuyamba kwa Mavuto
Zittau anali m’dera la Jeremani lolamulidwa ndi Soviet Union, ndipo zoyesayesa zovutitsa Mboni za Yehova zinali zitayamba mu 1949. Tinapeza malo aang’ono a msonkhano ku Bautzen pambuyo pakuyesayesa kwambiri. Ndiyeno, m’chilimwe, masitima apadera opita kumsonkhano wachigawo waukulu ku Berlin zinaletsedwa mwadzidzidzi. Komabe zikwi zambiri zinapezekako.
Ndiponso misonkhano yampingo inadodometsedwa. Anthu achipongwe anangopezekapo chabe kuti azifuula ndi kuimba malikwere. Pachochitika china tinatsala pang’ono kukakamizika kuimitsa nkhani ya woyang’anira woyendayenda. Oulutsa nkhani anatitcha aneneri a chiweruzo. Nkhani za m’nyuzipepala zinanena kuti tinasonkhana pamwamba pa mapiri poyembekezera kutengedwa m’mitambo. Ndiponso mapepalawo anagwira mawu asungwana ena kukhala akunena kuti Mboni zinayesa kuchita nawo chisembwere. Kalongosoledwe kakuti ‘amene adzipatulira kwa Yehova akalandira moyo wosatha’ kanapotozedwa kunena kuti amene anagonana ndi Mboni akapeza moyo wosatha.
Pambuyo pake tinaimbidwa mlandu wakukhala osonkhezera nkhondo. Zimene tinkanena za nkhondo ya Mulungu ya Armagedo zinatengedwa molakwa kukhala zikutanthauza kuti tinalimbikitsa mpikisano wa zida ndi nkhondo. Zinali zopanda pake chotani nanga! Komabe, mu August 1950, pamene ndinapita kuntchito yausiku pakampani yosindikiza nyuzipepala yomwe ndinkagwirako ntchito yosindikiza, ndinaimitsidwa pachipata. “Wachotsedwa ntchito,” anatero mlonda, yemwe anali ndi wapolisi. “Anthu inu mukuchirikiza nkhondo.”
Nditabwerera kunyumba, Margit anakondwera. “Sudzagwiranso ntchito usiku wonse,” iye anatero. Sitinadere nkhaŵa. Posapita nthaŵi ndinapeza ntchito ina. Tinadalira mwa Mulungu kuti akatisamalira, ndipo anatero.
Ntchito Yathu Iletsedwa
Pa August 31, 1950, ntchito ya Mboni za Yehova mu German Democratic Republic inaletsedwa. Ambiri anagwidwa. Mboni zinazengedwa mlandu, zina zikumalandira chilango chokhala m’ndendende kwa moyo wonse. Ziŵiri za ku Zittau, zomwe zinavutika m’misasa yachibalo ya Anazi, zinamangidwa ndi ochirikiza Chikomyunizimu.
Woyang’anira mpingo wathu anagwidwa pamodzi ndi mkazi wake. Amene anawagwira anasiya ana aang’ono aŵiri m’nyumba kuti adzisamalire okha. Agogo akuchikazi anatenga anawo, ndipo lerolino asungwana aŵiriwo ali achangu kuuza ena za Ufumu wa Mulungu.
Amtengatenga a m’mipingo ya ku Jeremani wa Kum’maŵa anayenda ulendo kupita ku Berlin kukatenga mabuku pamalo olinganizidwa m’chigawo chomasuka chakumadzulo ndi kubwera. Ambiri mwa amtengatenga olimba mtima ameneŵa anagwidwa, kuzengedwa mlandu, ndi kuweruzidwa kupita kundende.
Tsiku lina apolisi anabwera m’maŵamaŵa kudzafufuza nyumba yathu. Tinadziŵa kuti adzabwera, choncho ndidaika zolembedwa zonse za mpingo, zimene ndinkasunga, m’nkhokwe yathu, pafupi ndi chisa cha mavu. Tizilomboto sitinandivutepo, koma pamene amunawo anayamba kufufuza malowo, mwadzidzidzi anakutidwa kwadzawoneni ndi mavu. Amunawo analikumba liŵiro lakuthaŵa!
Yehova anali atatikonzekeretsa kuyang’anizana ndi chiletsocho kupyolera m’misonkhano yochitidwa mu 1949. Programuyo inatilimbikitsa kuwonjezera phunziro laumwini, kupezeka pamisonkhano, ndi ntchito yathu yakulalikira, ndiponso kudalirana wina ndi mnzake kaamba ka chichirikizo ndi chilimbikitso. Zimenezi zinatithandiza kwambiri kukhalabe okhulupirika. Chifukwa chake, ngakhale kuti anthu anatisuliza ndi kutitemberera, sitinalefulidwe mpang’ono pomwe.
Kuchita Misonkhano Pansi pa Chiletso
Chiletsocho chitalengezedwa, ndinakumana ndi Mboni zina ziŵiri kukambitsirana mmene tikapitirizira kuchita misonkhano yathu yampingo. Kupezekapo kunali kwaupandu, chifukwa chakuti utagwidwa uli pamsonkhano ukaweruzidwa kupita kundende. Tinafikira Mboni za m’dera lathu. Zina zinachita mantha, koma kunali kolimbikitsa kuti iriyonse inazindikira kufunika kwa kupezeka pamisonkhano.
Mwamuna wokondwerera yemwe anali ndi nkhokwe anaipereka kuti tiigwiritsire ntchito monga malo osonkhanira. Ngakhale kuti inali m’munda, yowoneka kwa onse, nkhokweyo inali ndi chitseko chakumbuyo chomwe chinkatsegukira kukamkwaso kobisika ndi zitsamba. Choncho kubwera kwathu ndi kupita sikunazindikiridwe. M’nyengo yonse yachisanu nkhokwe yakaleyo inakhala malo a misonkhano yathu yochitika mounikiridwa ndi makandulo, ndi opezekapo okwanira pafupifupi 20. Tinkakumana mlungu ndi mlungu kaamba ka phunziro lathu la magazini a Nsanja ya Olonda ndi Msonkhano Wautumiki. Programuyo inagwirizanitsidwa ndi mkhalidwe wathu, ikumagogomezera kuti tinafunikira kukhala achangu mwauzimu. Posapita nthaŵi tinasangalala kulandira mwamuna wokondwererayo monga mbale wathu watsopano m’chowonadi.
Chapakati pa ma 1950, ziweruzo za makhoti zinakhala zofeŵako, ndipo abale ena anamasulidwa m’ndende. Ambiri anatumizidwa ku Jeremani wa Kumadzulo. Koma kwa ine, zinthu zinasintha mwadzidzidzi pambuyo pochezeredwa ndi mbale wochokera ku Jeremani wa Kumadzulo.
Ntchito Yanga Yaikulu Yoyamba
Mbaleyo anati ndi Hans. Titakambitsirana, ndinapemphedwa kufika pakeyala yakutiyakuti ku Berlin. Nditazindikira dzina lobisika pabelu lapachitseko, ndinauzidwa kuloŵa. Anthu aŵiri anatsagana nane nandiloŵetsa m’kukambitsirana kwabwino koma kwawamba. Ndiyeno anandifunsa zimene anafuna nati: “Ngati ungapatsidwe ntchito yapadera, kodi ungailandire?”
“Inde ndithu,” ndinayankha motero.
“Chabwino,” iwo anatero, “tinafuna kudziŵa zimenezo. Pitani bwino.”
Pambuyo pa milungu itatu ndinapemphedwanso kubwerera ku Berlin ndipo ndinalinso m’chipinda chomwe chija. Akumandipatsa mapu a dera lozungulira Zittau, abalewo anatchula mfundo yeniyeni. “Sitinazifikire Mboni m’derali. Kodi ungazifikire mmalo mwathu?”
“Ndithudi ndidzatero,” ndinayankha tero mosataya nthaŵi. Deralo linali lalikulu, loposa makilomita 100 m’litali, kuchokera ku Riesa mpaka ku Zittau, ndi pafupifupi makilomita 50 m’bwambi. Ndipo ine ndinali ndi njinga yokha. Pamene Mboni zonse zinafikiridwa, iriyonse inaikidwa mumpingo wakewake, umene nthaŵi zonse unatumiza wouimira ku Berlin kukanyamula mabuku ndi malangizo. Kugwira ntchito mwanjira imeneyi kunaletsa kuika paupandu mipingo ina pamene boma linkazunza mpingo umodzi uliwonse.
Khulupirirani mwa Yehova
Mosasamala kanthu za chizunzo, pomvera malangizo a Baibulo, sitinasiye konse kupita kunyumba ndi nyumba ndi uthenga wathu wonena za Ufumu wa Mulungu. (Mateyu 24:14; 28:19, 20; Machitidwe 20:20) Tinafikira makeyala movomerezedwa ndi anthu omwe tinawadziŵa kale, ndipo tinasangalala ndi zokumana nazo zabwino koposa. Nthaŵi zina ngakhale zophophonya zathu zinakhala madalitso, monga momwe zotsatira zikusonyezera.
Mkazi wanga ndi ineyo tinapatsidwa keyala yoti tikapiteko, koma tinapita panyumba yolakwika. Pamene chitseko chinatseguka, tinawona yunifomu ya wapolisi yokoloŵekedwa kukhoma. Nkhope ya Margit inasintha; mtima wanga unagunda kwabasi. Zimenezi zingatanthauze kuponyedwa m’ndende. Ndinapemphera mofulumira.
“Kodi ndinu yani?” anafunsa tero mwamunayo mwaukali. Tinakhala chete.
“Ndikhulupirira ndinakuwonani kwinakwake,” anatero Margit, “koma sindingathe kukumbukira. Eya, ndinu wapolisi. Ndiganiza ndinakuwonani muli pantchito.”
Zimenezi zinamtonthoza mtima, ndipo anafunsa mwaubwenzi nati: “Kodi ndinu a Yehova?”
“Inde,” ndinayankha tero, “ndife amene, ndipo mwawona kuti kuli kulimba mtima kumene kwatipangitsa kugogoda pachitseko chanu. Ndife okondweretsedwa ndi inu panokha.”
Anatiuza kuloŵa m’nyumba mwake. Tinamchezera nthaŵi zambiri ndipo tinayamba phunziro Labaibulo. Mkupita kwa nthaŵi mwamunayu anakhala mbale wathu Wachikristu. Chokumana nacho chimenecho chinalimbitsa chikhulupiriro chathu mwa Yehova chotani nanga!
Kaŵirikaŵiri alongo ankagwira ntchito monga amtengatenga, ntchito imene inafuna kuti iwo aike chikhulupiriro chawo chonse mwa Yehova. Zimenezo zinachitika nthaŵi ina pamene Margit anapita ku Berlin kukanyamula mabuku. Kunali mabuku ochuluka amene sanayembekezere. Nsambo yoyanikira zovala inagwiritsiridwa ntchito kumangira sutukesi yolemera yodzalayo. Zonse zinali bwino kufikira pamene Margit anakwera sitima. Ndiyeno ofisala wowona pa katundu woloŵa ndi kutuluka m’dzikolo anabwera.
“Kodi katundu uyu ngwayani, ndipo muli chiyani?” anafunsa tero, ataloza chala sutukesiyo.
“Ndizovala zanga,” Margit anayankha tero.
Pokhala wokaikira, anamlamula kuitsegula. Mwapang’onopang’ono ndi mwadala, Margit anayamba kumasula nsambo imeneyo kusutukesi, akumamasula mfundo imodzi imodzi. Popeza kuti ntchito ya ofisala wowona pa katundu woloŵa ndi kutuluka m’dziko inafuna kuti iye ayende pasitima pamtunda wakutiwakuti ndiyeno kutsika ndi kukwera sitima ina paulendo wobwerera, anatekeseka kwambiri. Pomalizira pake, kutangotsala mfundo zitatu, anataya mtima. “Tuluka munomo, ndipo tenga zovala zako!” anafuula motero.
Mmene Yehova Anadisamalirira pa Ine Ndekha
Kaŵirikaŵiri sindinathe kugona tulo kwa maola anayi usiku uliwonse, chifukwa chakuti nthaŵi zambiri ndinkasamalira zinthu za mpingo nthaŵi yausiku. Tsiku lina m’maŵamaŵa pambuyo pogwira ntchito yotero usiku apolisi anagogoda pachitseko chathu. Anadza kudzafufuza. Panalibe nthaŵi yobisa kalikonse.
Apolisiwo anathera m’maŵa wonse akufufuza malowo kotheratu, ngakhale m’chimbudzi momwe kuti mwina munabisidwa kalikonse. Palibe yemwe anaganiza zakusanthula jekete langa lomwe linakoloŵekedwa kukhoma. Ndinali nditaika zikalata mofulumira m’matumba ake ochuluka. Matumbawo anali otundumuka ndi zimene apolisiwo anali kufuna, koma anapita chimanjamanja.
Panthaŵi ina, mu August 1961, ndinali ku Berlin. Umenewo unakhala ulendo wanga womalizira wonyamula mabuku Linga la Berlin linasamangidwe. Pasitesheni ya sitima ya ku Berlin panali anthu ochuluka pamene ndinakonzekera kubwerera ku Zittau. Sitimayo inafika, ndipo aliyense anathamangira kupulatifomu kukakwera. Ndikumayendera pamodzi ndi khamulo, ndinapezeka mwadzidzidzi m’mbali ya sitima yopanda anthu. Nditangoloŵa m’sitimayo mlonda anatsekera zitseko kunja. Ndinaima ndekha m’chigawo chimodzi cha sitima, pamene kuli kwakuti okwera ena analoŵa m’mbali zina za sitimayo.
Tinauyamba ulendowo kupita ku Zittau. Kwa nthaŵi yakutiyakuti ndinali ndekha m’ngolomo. Ndiyeno sitima inaima, ndipo zitseko za chigawo changa zinatsegulidwa. Asirikali ambiri a Soviet Union analoŵa. Panthaŵiyo mpamene ndinadziŵa kuti ndinakwera m’chigawo chosungidwira asirikali a Soviet Union. Ndinalakalaka kuti nthaka itseguke ndi kundimeza. Komabe, asirikaliwo sanawone kalikonse kachilendo.
Tinayambanso ulendo wopita ku Zittau, kumene zitseko za chigawo chathu zinatsegulidwa, ndipo asirikaliwo analumphira pabwalo. Anayamba kufufuza okwera onse pasiteshenipo. Koma ine ndekha ndinapita popanda kuimitsidwa. Asirikali ambiri anandichitiradi perete, poganiza kuti ndinali nduna yaikulu.
Tinazindikira pambuyo pake mmene mabukuwo analiri ofunika, pakuti kumangidwa kwa Linga la Berlin kunadodometsa mwakanthaŵi njira yathu yonyamulira mtokoma. Komabe, mabukuwo anakhoza kukhutiritsa zosoŵa zathu kwa miyezi ingapo. M’nthaŵi yonseyo, makonzedwe akuti tizifikiridwa akapangidwa.
Kumangidwa kwa Linga la Berlin mu 1961 kunadzetsa masinthidwe kwa ife ku Jeremani wa Kum’maŵa. Koma Yehova, monga mwanthaŵi zonse, anali patsogolo pa zochitika. Anapitirizabe kutisamalira pansi pa chiletso.—Monga yasimbidwira ndi Hermann Laube.
[Chithunzi patsamba 27]
Tinakhala ndi msonkhano waung’ono ku Bautzen