Yehova Anatisamalira Pansi pa Chiletso—Gawo 3
PANALI pa March 14, 1990. Patsiku losaiŵalikalo, ndinali pakati pa amene anapezekapo pamene nduna yaikulu ya boma ya Unduna wa Nkhani Zachipembedzo ku Berlin Wakum’maŵa inatipatsa chikalata chopereka chilolezo chalamulo pa Mboni za Yehova m’dziko limene kale linkatchedwa German Democratic Republic, kapena Jeremani Wakum’maŵa. Mkati mwa chochitikacho patsikulo, ndinakumbukira nthaŵi imene ndinakhala Mboni ndi kulingalira za nthaŵi zovuta zimene tinakumana nazo.
Chapakati pa ma 1950, pamene Margarete, wantchito mnzanga yemwe anali Mboni, analankhula nane kwa nthaŵi yoyamba za zikhulupiriro zake zozikidwa pa Baibulo, chizunzo pa Mboni za Yehova mu Jeremani Wakum’maŵa chinali chowopsa. Posakhalitsa, mkaziyo anapita kukagwira ntchito kwinakwake, ndipo ndinayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni ina. Ndinabatizidwa mu 1956, ndipo Margarete ndi ineyo tinakwatirana m’chaka chimenecho. Tinali mu Mpingo wa Lichtenberg ku Berlin. Unali ndi ofalitsa Ufumu okwanira pafupifupi 60 okhala ndi phande m’ntchito yolalikira.
Zaka ziŵiri pambuyo pa ubatizo wanga, nduna za boma zinafika panyumba ya yemwe anali wotsogoza mumpingo wathu. Anafuna kumgwira, koma anali kuntchito ku Berlin Wakumadzulo. Banja lake linamdziŵitsa kuti akhalebe kumeneko, ndipo pambuyo pa miyezi ingapo linapita kukakhala naye Kumadzulo. Ngakhale kuti ndinali ndi zaka 24 zokha, ndinapatsidwa mathayo aakulu mumpingo. Ndikuthokoza Yehova kuti amapereka nzeru ndi nyonga yofunikira kusamalirira ntchito zoterozo.—2 Akorinto 4:7.
Kupereka Chakudya Chauzimu
Pamene Khoma la Berlin linamangidwa mu August 1961, Mboni za Yehova Kum’maŵa zinalekanitsidwa mwadzidzidzi ndi abale awo Kumadzulo. Motero inayamba nyengo imene tinkapanga makope a mabuku athu, poyamba ndi taipi, ndiyeno ndi makina ojambulira osiyanasiyana. Kuyambira 1963, ndinatha zaka ziŵiri ndikumanga chipinda chobisika chosindikira m’nyumba mwathu. Nditamaliza ntchito ya masana yosula ziŵiya, usiku ndinkasindikiza makope a Nsanja ya Olonda mothandizidwa ndi abale ena. Akuluakulu a boma anali ofunitsitsa kutulukira gulu lathu losindikiza, koma Yehova anatithandiza kotero kuti chakudya chathu, monga momwe tinkachitchera, chinafika panthaŵi yake.
Kutulutsa makope okwanira a magazini athu kunafuna mapepala ochuluka, ndipo kupeza unyinjiwo kunali kovuta. Ngati tikadagula mapepala ochuluka nthaŵi zonse, tikadakopa chidwi cha akuluakulu a boma. Chotero tinagaŵira Mboni imodzi ndi imodzi ntchito yogula mapepala muunyinji wochepa ndi kuwabweretsa kukagulu kathu ka phunziro Labaibulo. Ndiyeno anatengedwa kupita kumene tinkasindikizira magazini. Kenako Mboni zina zinagaŵira magazini omalizidwawo.
Popeza kuti nduna za boma zinaganiza kuti ndinaloŵetsedwa m’kusindikiza mabuku, zinkandilondalonda. Chakumapeto kwa 1965, ndinawawona akunditsata nthaŵi zambiri ndipo ndinawona kuti anapangana kuchita kanthu kena. Mwadzidzidzi, ndinakumana nawo m’maŵamaŵa tsiku lina.
Kupulumukira Mwaŵi
Ndinali kupita kuntchito m’maŵa m’nyengo yachisanu. Dzuŵa linali lisanatuluke, ndipo ndinalimbana ndi kuzizira kwadzawoneni. Poyenda, ndinawona mitu ya amuna anayi pamwamba pa mpanda. Amunawo anatembenuka pamphambano nabwera mbali yakumene ndinali panjirayo. Ndinachita mantha powazindikira kuti anali nduna za boma. Kodi ndikatani?
Chipale chofeŵa chochuluka chinakankhidwira kumbali kusiya kanjira kopapatiza. Ndinapitirizabe kuyenda. Nditazolika, ndinasumika maso anga pansi. Ndinapemphera mofulumira monong’ona. Amunawo anayandikirabe. Kodi anandizindikira? Pamene tinayandikana kwambiri ndiyeno nkupambana pakanjira kopapatizako, sindinathe kukhulupirira zimene zinali kuchitika. Ndinapitirizabe kuyenda mofulumira. “Inu!” anafuula motero mmodzi wa iwo, “ndiuja akupita paja. Ima iwe!”
Ndinalikumba liŵiro lowopsa. Nditakhota mofulumira pamphambano, ndinalumpha mpanda wa nyumba ya mnansi ndi kuloŵa mumpanda wathu kumbuyo. Nditadelukira m’nyumba, ndinatseka ndi kumanga chitseko. “Ukani nonse!” ndinafuula tero. “Adza kudzandigwira.”
M’kamphindi Margarete anali m’chipinda chapansi naima pambali pa chitseko. Mosataya nthaŵi ndinali m’kachipinda kapansi kusonkheza chitofu. Ndinakwatula zolembedwa zonse za mpingo zomwe ndinali nazo ndi kuziponya pamoto.
“Tsegulani!” amunawo anafuula. “Tsegulani chitseko! Ndife aloya a boma.”
Margarete sanakatsegule pamene ndinali kutentha kotheratu kalikonse. Ndiyeno ndinapita kwa Margarete ndi kumkodola ndi mutu kuti atsegule chitseko. Amunawo analoŵa.
“Nchifukwa ninji unathaŵa?” anafunsa tero.
Posapita nthaŵi nduna zina za boma zinafika, ndipo nyumba yonse inafufuzidwa. Ndinada nkhaŵa kwambiri kaamba ka chipinda chobisika chosindikizira kumene kunali makina osindikizira ndi mapepala okwanira 40,000. Koma poloŵera pake pobisika sipanapezedwe. Ngakhale kuti anandifunsa mafunso kwa nthaŵi yaitali, Yehova anandithandiza kukhala wodekha. Chokumana nacho chimenecho chinatiyandikitsa kwambiri kwa Atate wathu wakumwamba ndi kutilimbitsa kuti tipirire.
Mu Ndende Koma Omasuka
Chakumapeto kwa ma 1960, ndinaitanidwa kukagwira ntchito yausirikali. Chifukwa chakuti chikumbumtima changa sichinandilole kutumikira, ndinakakamizidwa kukhala m’ndende ndi mumsasa wachibalo kwa miyezi isanu ndi iŵiri. Mumsasa wa ku Cottbus, kum’mwera koma chakum’maŵa kwa Berlin, tinalimo Mboni zokwanira 15. Tonsefe tinali m’menemo chifukwa cha uchete wathu Wachikristu. (Yesaya 2:2-4; Yohane 17:16) Masiku athu ogwira ntchito anali aatali ndipo ntchitoyo inali yakalavulagaga. Tinkadzuka ndi 4:15 a.m. ndi kutengeredwa kunja kwa msasa kukagwira ntchito yokonza njanje. Komabe, ngakhale kuti tinali m’ndende, tinali nayo mipata yakuuza ena za Ufumu wa Yehova.
Mwachitsanzo, tinali ndi owombeza ula aŵiri ku Cottbus. Tsiku lina ndinamva kuti wamng’ono pa aŵiriwo anafunitsitsa kulankhula nane. Kodi akafunanji? Anandiululira zonse. Agogo ake aakazi anali owombeza ula, ndipo iye anapeza mphamvu zotero pambuyo poŵerenga mabuku awo. Ngakhale kuti mwamunayo anafuna kwambiri kuwonjoka ku mphamvu zomwe zinkamlamulira, anawopa kulangidwa. Analira momvetsa chisoni. Koma kodi zimenezo zinandikhudza bwanji?
M’kukambitsirana kwathu, anafotokoza kuti mphamvu zake zoneneratu za mtsogolo zinalephera pamene anakhala pamodzi ndi Mboni za Yehova. Ndinamfotokozera kuti kuli mizimu yoipa, kapena ziŵanda, ndi yabwino, kapena angelo olungama. Ndikumagwiritsira ntchito chitsanzo cha amene anakhala Akristu ku Efeso wakale, ndinagogomezera kufunika kwa kutaya zinthu zonse zochita ndi kuwombeza ula kapena kusiya machitachita aliwonse akukhulupirira mizimu. (Machitidwe 19:17-20) “Ndiyeno ukafikire Mboni,” ndinamuuza tero. “Mboni zimapezeka kulikonse.”
Mnyamatayo anachoka mumsasawo pambuyo pa masiku angapo, ndipo sindinamve kalikonse ponena za iye. Koma kukumana kwanga ndi mwamuna wamanthayo ndi wosatonthozeka yemwe analakalaka ufulu kunazamitsa chikondi changa pa Yehova. Mbonife zokwanira 15 tinali mumsasa chifukwa cha chikhulupiriro chathu, koma tinali omasuka m’lingaliro lauzimu. Mnyamatayo anamasulidwa m’ndende, koma anakhalabe muukapolo kwa “mulungu” amene anamuwopsa. (2 Akorinto 4:4) Ha, Mbonife tiyenera kuuwona kukhala wamtengo wapatali chotani nanga ufulu wathu wauzimu!
Ana Athu Ayesedwa
Sanali achikulire okha amene anachirimika kuchirikiza zikhulupiriro zawo zozikidwa pa Baibulo komanso ndiachichepere omwe. Ankakakamizidwa kulolera molakwa ponse paŵiri kusukulu ndi kuntchito. Ana athu anayi onse anafunikira kuchirimika kuchirikiza zikhulupiriro zawo.
Dzoma lopereka sawatcha ku mbendera linkachitika kusukulu pa Lolemba lirilonse. Ana ankaloŵa m’bwalo alimumzere, kuimba nyimbo, ndi kupereka suluti ya Thälmann pamene mbendera inali kukwezedwa. Ernst Thälmann anali Mjeremani wochirikiza Chikomyunizimu yemwe anaphedwa ndi a SS a Nazi mu 1944. Nkhondo yachiŵiri ya dziko itatha, Thälmann anakhala ngwazi m’Jeremani Wakum’maŵa. Chifukwa cha chikhulupiriro chathu chozikidwa pa Baibulo chakuti utumiki wopatulika uyenera kuperekedwa kokha kwa Yehova Mulungu, mkazi wanga ndi ineyo tinalangiza ana athu kuimirira mwaulemu padzoma lotero popanda kutengamo mbali.
Ana asukulu anaphunzitsidwanso nyimbo Zachikomyunizimu. Margarete ndi ineyo tinapita kusukulu kwa ana athu ndi kufotokoza chifukwa chake sakaimba nyimbo zandale. Komabe, tinafotokoza kuti akakhala ofunitsitsa kuphunzira nyimbo zina. Motero, pausinkhu wochepa, ana athu anaphunzira kuchirimika ndi kukhala osiyana ndi ausinkhu wawo.
Chakumapeto kwa ma 1970, mwana wathu wamkazi wamkulu anafuna kukaphunzirira pantchito ya muofesi. Komabe, aliyense wofuna kuphunzirira pantchito anafunikira kuphunzira zoyambirira zankhondo kwa masiku 14. Popeza kuti chikumbumtima cha Renate sichinamlole kutenga mbali m’zimenezo, anachirimika ndipo potsirizira thayo lakuphunzira zimenezo linachotsedwa pa iye.
Mkati mwa kuphunzirira kwake pantchito, Renate anapezeka m’kalasi kumene anaitanidwa kupezekapo pakuyeseza kuwombera mfuti. “Renate, nawenso udzapita nafe kukayeseza kuwombera mfuti,” anatero mphunzitsi. Kukana kwake sikunamveke kwa mphunzitsiyo. “Sudzawomberako mfuti,” analonjeza motero. “Udzangosamalira zakumwa.”
Madzulowo, tinakambitsirana monga banja. Tinalingalira kuti kukakhala kolakwa kuti Renate akapezekepo pakuyeseza kuwombera mfuti, ngakhale ngati iye sakatengamo mbali mwachindunji. Atalimbitsidwa mwakukambitsirana nafe ndi pemphero, sanalole aliyense kumuwopsa. Tinalimbikitsidwa chotani nanga kuwona mwana wathu wamkazi wachichepere akutenga kaimidwe kake kuchirikiza malamulo olungama amakhalidwe!
Kuwonjezera Ntchito Yathu Yakulalikira Poyera
Pamene kutsutsidwa kwa ntchito yathu kunachepekera chakumapeto kwa ma 1970, zofalitsidwa zathu Zachikristu zochuluka zinayamba kubwera kuchokera Kumadzulo. Ngakhale kuti imeneyi inali ntchito yowopsa, abale olimba mtima anaichita modzifunira. Tinayamikira kwambiri kukhala ndi mabuku owonjezereka amenewo ndi zoyesayesa za amene anawatheketsa. Pamene chizunzo chinali chowopsa m’zaka zoyambirira za chiletso, ntchito yolalikira kunyumba ndi nyumba inali yovuta kwenikweni. Kunena zowona, kuwopa kulangidwa ndi boma kunachititsa ena kuipeŵa. Koma m’kupita kwa nthaŵi ntchito yathu yakulalikira poyera inawonjezereka mofulumira. M’ma 1960, kokha ofalitsa Ufumu okwanira pafupifupi 25 peresenti ankatenga mbali muutumiki wakunyumba ndi nyumba mokhazikika. Komabe, chiŵerengero cha okhala ndi phande mokhazikika m’mbali imeneyo ya uminisitala chinawonjezereka kufika 66 peresenti podzafika chakumapeto kwa ma 1980! Panthaŵiyo akuluakulu aboma sanaikeko nzeru kwambiri ku ntchito yathu yakulalikira poyera.
Panthaŵi ina mbale yemwe ndinali kugwira naye ntchito muuminisitala anadza ndi mwana wake wamkazi wachichepere. Pochita chidwi ndi kukhalapo kwa msungwanayo, dona wachikulire yemwe tinakambitsirana naye anatiuza kuloŵa m’nyumba yake. Anayamikira ulaliki wathu wa m’Malemba nativomereza kumfikiranso. Pambuyo pake ndinauza mkazi wanga kuti azipitako, ndipo mwamsanga anayamba kuchititsa phunziro Labaibulo kwa mkaziyo. Mosasamala kanthu ndi ukalamba ndi kudwaladwala, donayo anakhala mlongo wathu ndipo ali wokangalikabe muutumiki wa Yehova.
Kupanga Masinthidwe Pamene Ufulu Unayandikira
Yehova anatikonzekeretsa kaamba ka nthaŵi imene tikakhala ndi ufulu wokulirapo. Mwachitsanzo: Kutangotsala pang’ono kuti chiletso chichotsedwe, tinauzidwa kusintha njira imene tinkaitanirana pamisonkhano. Powopa kugwidwa, tinkaitanana ndi maina athu oyamba. Ambiri amene anadziŵana kwa zaka zambiri sanadziŵe dzina lachiŵiri la wokhulupirira mnzawo. Komabe, pokonzekera kulandira okondwerera owonjezereka pamisonkhano, tinalimbikitsidwa kumagwiritsira ntchito dzina lachiŵiri. Kwa ena zimenezi zinawoneka kukhala zosayenera, koma amene anatsatira uphunguwo anapanga masinthidwe mosavuta pambuyo pake pamene tinapeza ufulu.
Tinalimbikitsidwanso kuyamba misonkhano yathu ndi nyimbo. Motero tinazoloŵera njira yotsatiridwa ndi mipingo yakwina. Masinthidwe ena anakhudza ukulu wa timagulu tathu tamaphunziro abukhu. Mwapang’onopang’ono tinawonjezereka kuchoka pa anthu anayi kufika pa anthu asanu ndi atatu m’ma 1950. Pambuyo pake tinawonjezeredwa kufika pa anthu 10 ndipo potsirizira anthu 12. Ndiponso, kupenda kunachitidwa kutsimikizira kuti malo osonkhanira a mpingo uliwonse akhale pakati kaamba ka Mboni zambiri.
Nthaŵi zina nzeru ya kusinthako inawoneka pambuyo pa kupangidwa kwa masinthidwe operekedwawo. Ha, Yehova anadzisonyeza kaŵirikaŵiri kukhala Atate wanzeru ndi wodera nkhaŵa chotani nanga! Mwapang’onopang’ono, anatithandiza kugwirizana ndi gulu lake lonse la padziko lapansi, ndipo mowonjezereka tinadzimva kukhala mbali ya ubale wadziko lonse wa anthu ake. Ndithudi, Yehova Mulungu mwachikondi anatetezera anthu ake m’zaka zonse zokwanira pafupifupi 40 zimene iwo anagwiriramo ntchito pansi pa chiletso ku Jeremani Wakum’maŵa. Ndife achimwemwe chotani nanga tsopano kukhala ololedwa mwalamulo!
Lerolino, muli Mboni za Yehova zokwanira 22,000 kapena kuposapo m’dziko limene kale linali Jeremani Wakum’maŵa. Ziri umboni wa chitsogozo chanzeru ndi chisamaliro chachikondi cha Yehova Mulungu. Chichirikizo chake m’zaka zomwe tinali pansi pa chiletso chimasonyeza kuti akhoza kulamulira mkhalidwe uliwonse. Kaya chida chosulidwira anthu ake chikhale chotani, sichidzapambana. Nthaŵi zonse Yehova amasamalira bwino amene amamdalira. (Yesaya 54:17; Yeremiya 17:7, 8)—Monga momwe yasimbidwira ndi Horst Schleussner.
[Chithunzi patsamba 31]
Horst ndi Margarete Schleussner kumalo a Sosaite ku Berlin Wakum’maŵa