Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w92 5/15 tsamba 3
  • Kodi Baibulo Liridi Mphatso Yochokera kwa Mulungu?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Baibulo Liridi Mphatso Yochokera kwa Mulungu?
  • Nsanja ya Olonda—1992
  • Nkhani Yofanana
  • Yehova Amateteza Anthu Ake
    Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2020
  • Anthu Akuphunzira Kwambiri Koma Sakusintha Kwenikweni
    Galamukani!—2002
  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
    Nsanja ya Olonda—1997
  • N’chifukwa Chiyani Mphatso Imene Mulungu Watipatsa Ndi Yamtengo Wapatali?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2017
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1992
w92 5/15 tsamba 3

Kodi Baibulo Liridi Mphatso Yochokera kwa Mulungu?

“NDIKHULUPIRIRA kuti Baibulo ndilo mphatso yabwino koposa imene Mulungu anapatsa anthu.” Ndemanga imeneyo inaperekedwa ndi Abraham Lincoln, prezidenti wa 16 wa United States.a Sindiye yekha amene anayamikira bukhu lakalekale limeneli.

William E. Gladstone yemwe anali nduna ya boma la Briteni ya m’zaka za zana la 19 anati: “Baibulo liri ndi Magwero Apadera, ndipo nlosiyana kotheratu ndi mabuku ena onse.” Kusonyeza malingaliro ofananawo, nduna ya boma la Amereka ya m’zaka za zana la 18 Patrick Henry anati: “Baibulo limaposa mabuku ena onse amene analembedwapo.” Mwachiwonekere kuti anakopeka ndi Malemba, wolamulira wa Falansa Napoléon Bonaparte anathirira ndemanga kuti: “Baibulo sibukhu wamba, koma ‘lamoyo,’ lokhala ndi mphamvu yogonjetsa onse olitsutsa.”

Kwa ena, Baibulo lakhala magwero a chithandizo ndi chitonthozo. Chiŵalo cha Bungwe la Nduna za ku Amereka, kazembe Robert E. Lee, ananena kuti: “M’kuzizwa ndi m’zipsinjo zanga zonse, Baibulo silinalepherepo kundipatsa chidziŵitso ndi nyonga.” Ndipo chifukwa cha chiyamikiro chake cha bukhu limeneli, prezidenti wa United States John Quincy Adams ananena kuti: “Kwazaka zambiri, chakhala chizoloŵezi changa kuŵerenga Baibulo lonse kamodzi pachaka.”

Ngati Wam’mwambamwamba anapatsa anthu Baibulo, payenera kukhala umboni wakuti nlouziridwa mwaumulungu. Liyenera kukhala lofunika kuposa bukhu lirilonse. Ndipo kuti Baibulo likhale magwero owona a chilimbikitso ndi malangizo, liyenera kukhala lodalirika kotheratu. Chotero, funso nlakuti, Kodi Baibulo liridi mphatso yochokera kwa Mulungu? Tiyeni tifune yankho la funsoli m’nkhani yotsatira.

[Mawu a M’munsi]

a Ndithudi, iripo mphatso yaikulu kuposa imeneyo​—Yesu Kristu.​—Yohane 3:16.

[Zithunzi patsamba 3]

William E. Gladstone

[Mawu a Chithunzi]

Chithunzi cha U.S. National Archives

Abraham Lincoln

[Mawu a Chithunzi]

Chithunzi cha U.S. National Archives

Patrick Henry

[Mawu a Chithunzi]

Harper’s U.S. History

Napoléon Bonaparte

[Mawu a Chithunzi]

Wonjambulidwa ndi E. Ronjat

John Quincy Adams

[Mawu a Chithunzi]

Harper’s U.S. History

Robert E. Lee

[Mawu a Chithunzi]

Chithunzi cha U.S. National Archives

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena