Kodi Chakudya Ichi Chingakhale ndi Tanthauzo kwa Inu?
MWEZI wandendende ngwowalira padziko lonselo. M’chipinda chapamwamba chochezera m’Yerusalemu wakale, amuna 12 asonkhana mokweteza gome. Khumi ndi mmodzi akumvetsera mwatcheru pamene Mphunzitsi wawo akuyambitsa phwando lofunika kwambiri ndipo akulankhula mawu a tanthauzo lalikulu. Cholembedwa china chimati:
‘Yesu [Kristu] anatenga mkate, nadalitsa, naunyema; ndipo mmene anapatsa kwa ophunzira, anati, Tengani, idyani; ichi ndi thupi langa. Ndipo pamene anatenga chikho, anayamika, napatsa iwo, nanena, Mumwere ichi inu nonse, pakuti ichi ndicho mwazi wanga wa pangano, wothiridwa chifukwa cha anthu ambiri ku kuchotsa machimo. Ndipo ndinena kwa inu, sindidzamwanso chipatso ichi cha mpesa, kufikira tsiku limene ndidzamwa chatsopano, pamodzi ndi inu, mu Ufumu wa Atate wanga. Ndipo pamene anaimba nyimbo, anatuluka kumka ku phiri la Azitona.’—Mateyu 26:26-30.
Ichi chinachitika pambuyo pakuloŵa kwa dzuŵa pa tsiku la 14 la mwezi Wachiyuda wa Nisani m’chaka cha 33 cha Nyengo Yathu. Yesu ndi atumwi ake anali atangotha kumene kuchita phwando la Paskha kukumbukira kulanditsidwa kwa Aisrayeli ku ukapolo wa Igupto m’zaka za zana la 16 B.C.E. Kristu anali atatulutsa Yudase Iskariote, amene anali pafupi kumpereka. Chifukwa chake, Yesu yekha ndi atumwi ake 11 okhulupirika analipo.
Mgonero umenewu sunali kupitirizidwa kwa Paskha Wachiyuda. Unali kanthu kena katsopano kamene kanatchedwa Mgonero wa Ambuye. Ponena za phwando ili, Yesu analamula otsatira ake kuti: ‘Chitani ichi chikumbukiro changa.’ (Luka 22:19, 20; 1 Akorinto 11:24-26) Kodi nchifukwa ninji iye ananena izi? Ndipo kodi ndimotani mmene chochitika cha zaka mazana ambiri zapitazo chingakhalire ndi tanthauzo kwa inu?