Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w93 9/1 tsamba 4-7
  • Kodi Chitetezo Chenicheni Nchotheka?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Chitetezo Chenicheni Nchotheka?
  • Nsanja ya Olonda—1993
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Mtundu wa Kulambira Mafano
  • Msampha wa Kukhulupirira Mphamvu Zamatsenga
  • Kumasuka ku Kukhulupirira Malaulo
  • Kupeza Chitetezo cha Mulungu
  • Kodi Zithumwa za Mwaŵi Zingakutetezereni?
    Nsanja ya Olonda—1993
  • Kodi Pali Vuto Ngati Nditachitako Chidwi Pang’ono Ndi Zamatsenga?
    Galamukani!—2002
  • Kukhulupirira Malaulo Kungatsogolere ku Kupanda Chimwemwe
    Mbiri Yabwino Yokusangalatsani
  • Kodi Anthu Ochita Zamatsenga Mphamvu Zake Amazitenga Kuti?
    Galamukani!—2011
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1993
w93 9/1 tsamba 4-7

Kodi Chitetezo Chenicheni Nchotheka?

WOLEMBA nkhani, Ralph Waldo Emerson panthaŵi ina ananena kuti: “Anthu opanda chidziŵitso chakuya amakhulupirira mwaŵi . . . Anthu achidziŵitso amakhulupirira chochititsa ndi chotulukapo cha zinthu.” Inde, munthu amene amaika chikhulupiriro m’mphamvu ya njirisi zamatsenga ndi zithumwa za mwaŵi amapereka moyo wake kulamulidwa ndi mphamvu zosaoneka. Iye amataya nzeru zonse ndi kulingalira nagonjera mantha opanda pake, a malaulo.

Komabe, Baibulo likhoza kumasula munthu pamantha oterowo. Limasonyeza kuti njirisi ndi zithumwa nzopanda mphamvu. Motani? Eya, malinga nkunena kwa The New Encyclopædia Britannica, “njirisi zimalingaliridwa kuti zimatenga mphamvu zake mwakugwirizana kwawo [pakati pa zinthu zina] ndi mphamvu zachilengedwe.” Mphamvu zimenezi zingakhale ‘mizimu ya akufa’ kapena ‘mphamvu ya mwaŵi.’ Koma Baibulo limasonyeza mowonekera bwino kuti “akufa sadziŵa kanthu bi.” (Mlaliki 9:5) Chotero, palibe mizimu ya akufa imene ingathandize kapena kuvulaza amoyo; ndiponso palibe mphamvu yosaoneka yonga mwaŵi imene ingakuchitireni kanthu kena.

M’nthaŵi za m’Baibulo, Mulungu anatsutsa awo amene anamsiya, amene anaiŵala phiri lake loyera, iwo amene anali “kukonzera mulungu wamwaŵi gome, ndi kudzazira mulungu waimfa zikho za vinyo wosanganiza.” Mmalo molandira chitetezo, ochilikiza mwaŵiwo anaperekedwa kuchiwonongeko. “Ndidzasankhiratu inu kulupanga,” anatero Yehova Mulungu.​—Yesaya 65:11, 12.

Mwakuchita matsenga, mtundu wakale wa Babulo mofananamo unaika chikhulupiriro m’mphamvu zotetezera zachinsinsi. Komatu Babulo anakumana ndi tsoka. “Taumirira m’malodza ako ndi matsenga ako owopsa,” anatokosa motero mneneri Yesaya. “Mwinamwake ungapeze chithandizo kuchokera kwa iwo . . . Koma ayi! mosasamala kanthu za machenjera ako ochuluka ndiwe wopanda mphamvu.” (Yesaya 47:12, 13, The New English Bible) M’kupita kwanthaŵi mtunduwo unalekeratu kukhalako. Kukhulupirira matsenga kunatsimikizira kukhala kosaphula kanthu. Mofananamo, palibe njirisi yamatsenga, chithumwa, kapena zango limene lingachite kanthu kukuthandizani kapena kukutetezerani.

Mtundu wa Kulambira Mafano

Komabe, ena sangaone chivulazo m’kunyamula krustalo, phazi la kalulu, kapena chifanizo chachipembedzo. Kodi zinthuzi nzipangizo zosavulaza? Osati malinga nkunena kwa Baibulo. Ilo limanena kuti zinthu zamatsenga nzovulazadi.

Kugwiritsira ntchito njirisi kuli mtundu wa kulambira mafano​—chinthu china chimene chimatsutsidwa momvekera bwino m’Mawu a Mulungu. (Eksodo 20:4, 5) Zowona, munthu sangaganize kuti akulambira mwachindunji njirisi kapena zango. Koma kodi sikumasonyeza ulemu, ndi mkhalidwe wamaganizo wakupembedza mphamvu zamatsenga zosaoneka ngati munthu akhala ndi zinthu zimenezo? Ndipo kodi sizowona kuti kachitidwe kakulambira (monga ngati kupsompsona) kaŵirikaŵiri kumachitidwa kwa zithumwazo? Komatu Baibulo, pa 1 Yohane 5:21, limalangiza Akristu kuti: “Dzisungireni nokha kupeŵa mafano.” Kodi chilangizo chimenechi sichikaphatikizapo zinthu zimene zimaonedwa monga zithumwa kapena njirisi?

Msampha wa Kukhulupirira Mphamvu Zamatsenga

Mwakugwiritsira ntchito njirisi, anthu ambiri amatcheredwanso msampha ndi kukhulupirira matsenga. Zowona, ena anganyamule krustalo kapena chinthu chamatsenga chifukwa cha mwambo osati chifukwa cha kukhulupirira zinthuzo. Koma monga momwedi kuseŵera ndi mkazi wadama kungachititse munthu kutenga nthenda ya AIDS, kuseŵera ndi zinthu zamatsenga kungakhalenso ndi zotulukapo zoipa. Panali chifukwa chabwino pamene Mulungu analetsa Aisrayeli kuchita matsenga, malaulo, ndi kupenduza. Baibulo limachenjeza kuti: “Aliyense wakuchita izi Yehova anyansidwa naye.”​—Deuteronomo 18:10-14.

Kodi nchifukwa ninji panali chiletso champhamvuchi? Chifukwa chakuti mphamvu zosaoneka zimene zimasonkhezera machitachita amenewo sizili mizimu ya akufa kapena mphamvu ya mwaŵi koma ali Satana Mdyerekezi ndi ziŵanda zake.a Ndipo kugwiritsira ntchito njirisi kuli kogwirizana mwachindunji ndi kulambira ziŵanda. Vine’s Expository Dictionary of Old and New Testament Words imanena kuti: “M’nyanga, kugwiritsira ntchito mankhwala, kaya opanda mphamvu kapena amphamvu, kaŵirikaŵiri kunali kutsagana ndi dzoma ndi kuchonderera mphamvu zamatsenga, limodzi ndi zithumwa, njirisi zosiyanasiyana, ndi zina zotero.”

Chotero munthu amene ali ndi chithumwa chamatsenga akuseŵera ndi kukhulupirira mizimu. Iye akudziika paupandu wa kukhala pansi pa chisonkhezero choipa ndi ulamuliro wa “mulungu wa nthaŵi ya pansi pano”​—Satana Mdyerekezi. (2 Akorinto 4:4) Pamenepo, pali chifukwa chabwino chimene Baibulo limatilamulira kupeŵa mitundu yonse ya kukhulupirira mizimu.​—Agalatiya 5:19-21.

Kumasuka ku Kukhulupirira Malaulo

The World Book Encyclopedia ikunenabe kuti: “Mwinamwake kukhulupirira malaulo kudzapitirizabe kukhala mbali ya moyo malinga ngati anthu adzapitiriza kuwopana ndi kukhala osatsimikiza ponena za mtsogolo.” Koma Mboni za Yehova zikuthandiza anthu ambiri kudzimasula ku kukhulupirira malaulo kovulaza. Mkazi wina wa ku South Africa akukumbukira motere: “Ndinali kuvutitsidwa ndi mizimu yoipa, ndipo nyumba yanga inali yodzaza ndi muti wonditetezera kwa mizimuyo.” Mboni za Yehova zinamthandiza kuwona kuwopsa kwa kuseŵera ndi matsenga. Kodi anachita chiyani? “Ndinayamba kutaya chilichonse chimene ndinali nacho chimene chinali chokhudza kulambira mizimu,” iye akutero. “Thanzi langa linawongokera. Ndinapatulira moyo wanga kutumikira Yehova ndipo ndinabatizidwa.” Tsopano ngwomasuka pakukhulupirira malaulo ndi kukhulupirira mizimu.

Talingaliraninso za munthu wamankhwala wa ku Nigeria amene anali kuphatikiza kulambira mizimu m’ntchito yake yochiritsa. Kaŵirikaŵiri anali kuthamangitsa Mboni za Yehova zikafika panyumba pake akumaziwopseza ndi kuzitemberera. Panthaŵi ina anakonza mankhwala apadera, nanenerera mawu ake amatsenga, nawathira kumaso kwa Mboni ina! Iye anafuula nati: “Udzafa m’masiku asanu ndi aŵiri!” Masiku asanu ndi aŵiri pambuyo pake Mboniyo inabwerera, ikumachititsa wamankhwalayo kutulukira kunja mofulumira kuti adzaione, akumakhulupirira kuti waona mzukwa! Matsenga ake atavumbulidwa kukhala opanda pake, iye anavomereza phunziro la Baibulo ndipo pambuyo pake anakhala Mboni.

Nanunso mukhoza kumasuka m’nsinga za mantha ndi kukhulupirira malaulo. Zowona, zimenezi zingakhale zovuta. Mwinamwake munakulira kumalo kumene kugwiritsira ntchito njirisi ndi zithumwa kuli kofala. Akristu a mu Efeso wakale anali ndi vuto lotero. Iwo anali m’malo amene anali kusonkhezeredwa mwamphamvu ndi kukhulupirira mizimu. Kodi anachitanji pamene anaphunzira chowonadi cha Mawu a Mulungu? Baibulo limati: “Ambiri a iwo akuchita zamatsenga anasonkhanitsa mabuku awo, nawatentha pamaso pa onse; ndipo anaŵerenga mtengo wake, napeza ndalama zasiliva zikwi makumi asanu.”​—Machitidwe 19:19.

Kupeza Chitetezo cha Mulungu

Ngati mutaya zinthu zonse zogwirizana ndi matsenga, kodi mudzasiyidwa popanda chitetezo? Kutalitali, “Mulungu ndiye pothaŵirapo pathu ndi mphamvu yathu, thandizo lopezekeratu m’masautso.” (Salmo 46:1) Chitetezo cha Mulungu chidzaoneka makamaka pamene adzawononga dongosolo ili la zinthu loipa. “Ambuye adziŵa kupulumutsa opembedza poyesedwa iwo, ndi kusunga osalungama kufikira tsiku loweruza akalangidwe.”​—2 Petro 2:9; yerekezerani ndi Salmo 37:40.

Pakali pano, ‘nthaŵi ndi zochitika zosadziŵika zimatigwera tonsefe.’ (Mlaliki 9:11, NW) Mulungu samalonjeza kuti atumiki ake adzakhala ndi moyo “wotetezeredwa” kapena kuti adzawachinjiriza kuchivulazo chilichonse. Komabe, iye amalonjeza kuti adzatetezera mkhalidwe wathu wauzimu ndi unansi wathu ndi iye. (Salmo 91:1-9) Motani? Choyamba, iye amatipatsa malamulo ndi malamulo amkhalidwe amene angatipindulitse ndi kutitetezera kuchisonkhezero choipitsa cha Satana. (Yesaya 48:17) Mwakudziŵa kwathu njira za Yehova, ‘kulingalira kudzatidikira, kuzindikira kudzatichinjiriza’​—mwachitsanzo, kudzatichinjiriza kuntchito zosapindulitsa kapena zovulaza.​—Miyambo 2:11.

Njira ina imene Mulungu amatitetezera nayo ndiyo mwakupereka “ukulu woposa wamphamvu” m’nthaŵi za chiyeso. (2 Akorinto 4:7) Ndipo pamene mikhalidwe iwopseza kugonjetsa Mkristu, Iye amapereka “mtendere wa Mulungu wakupambana chidziŵitso chonse” umene umachinjiriza mitima ndi maganizo athu. (Afilipi 4:7) Inde, Mkristu ali wokonzeka “kuchilimika pokana machenjerero a Mdyerekezi.”​—Aefeso 6:11-13.

Kodi mungapeze motani chitetezo chimenecho? Yambani mwakudziŵa Yehova ndi Mwana wake, Yesu Kristu. (Yohane 17:3) Mboni za Yehova zingachite zambiri kukuthandizani m’zimenezi. Pamene mukulitsa unansi wabwino ndi Yehova, mudzayamba kuona chitetezo chake chokoma mtima. Mulungu akuti, monga momwe tikuŵerengera pa Salmo 91:14 kuti: “Popeza andikondadi ndidzampulumutsa; ndidzamkweza m’mwamba, popeza adziŵa dzina langa.”

Ndithudi, ngati muli wokhulupirika kwa iye, m’kupita kwanthaŵi Mulungu adzakudalitsani ndi moyo wosatha m’dziko latsopano likudzalo. Yehova akutsimikiza izi ponena za awo amene adzakhala ndi moyo m’nthaŵi imeneyo: “Sipadzakhala wakuwawopsa; pakuti pakamwa pa Yehova wa makamu padanena.” (Mika 4:4) Matenda ndi imfa sizidzakhalakonso. (Chivumbulutso 21:4) Komabe, ngakhale tsopano, mukhoza kukhala ndi chisungiko china​—ngati mukulitsa unansi wathithithi ndi Yehova. Mofanana ndi wamasalmo, mukhoza kunena kuti: “Thandizo langa lidzera kwa Yehova. Wakulenga zakumwamba ndi dziko lapansi.”​—Salmo 121:2.

[Mawu a M’munsi]

a Kuti mupeze chidziŵitso chowonjezereka, onani brosha la Mizimu ya Akufa​—Kodi Ingakuthandizeni Kapena Kukuvulazani? Kodi Iyo Ilikodi? lofalitsidwa ndi Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania.

[Chithunzi patsamba 6]

Akristu a ku Efeso anataya zinthu zonse zokhudza matsenga

[Chithunzi patsamba 7]

Mu Ufumu wa Mulungu, mantha sadzakhalakonso

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena