Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w93 10/1 tsamba 29-30
  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
  • Nsanja ya Olonda—1993
  • Nkhani Yofanana
  • Musamangidwe M’goli ndi Osakhulupirira
    Nsanja ya Olonda—1989
  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
    Nsanja ya Olonda—2004
  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
    Nsanja ya Olonda—2002
  • Bwanji Ngati Ndikondana ndi Wosakhulupirira?
    Galamukani!—1994
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1993
w93 10/1 tsamba 29-30

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Kodi kukakhala koyenera kwa Mkristu kuchita bizinesi mogwirizana ndi wosakhulupirira, pamene kuli kwakuti Baibulo limatiuza kuti: “Musakhale omangidwa m’goli ndi osakhulupira”?

Timapeza uphunguwo pa 2 Akorinto 6:14-16: “Musakhale omangidwa m’goli ndi osakhulupira osiyana; pakuti chilungamo chigaŵana bwanji ndi chosalungama? Kapena kuunika kuyanjana bwanji ndi mdima? Ndipo Kristu avomerezana bwanji ndi Beliyali? Kapena wokhulupira ali nalo gawo lanji pamodzi ndi wosakhulupira? Ndipo chiphatikizo chake nchanji ndi kachisi wa Mulungu ndi wa mafano?”

Palibe chifukwa cha kukhulupirira kuti mtumwi Paulo anapereka uphungu umenewu ali ncholinga cha kukhazikitsa ziletso zakutizakuti, monga ngati zimene zimatsutsa Mkristu kuchita bizinesi ndi munthu wosakhulupirira. Komabe, uphunguwu umakhudza zimenezo, ndi mbali zinanso za moyo.

Paulo analembera uphungu umenewo abale ake Achikristu mu Korinto wakale. Pokhala mumzinda umene unali woipa kwambiri, iwo tsiku lililonse anafunikira kulimbana ndi maupandu a khalidwe ndi auzimu. Kokha ngati anali osamala, kukhala m’malo a ziyambukiro zoipa kukanafooketsa pang’onopang’ono chitsimikizo chawo cha kukhala anthu apadera, “mbadwa yosankhika, ansembe achifumu, mtundu woyera mtima, anthu a mwini wake.”​—1 Petro 2:9.

Asanalembe zimene zili pa 2 Akorinto 6:14-16, Paulo anali atathetsa vuto lina lalikulu pakati pa abale ake a ku Korinto. Iwo anali atalola munthu wa chisembwere choipitsitsa kukhala pakati pawo, chotero Paulo analamula za kuthamangitsa, kapena kuchotsa, wochimwa wosalapayo. (1 Akorinto 5:1) Cholakwa cha munthuyo chinasonyeza kuti mayanjano oipa kapena kudziloŵetsa kosasamala mumkhalidwe wa dzikoli kungayambukire Akristu.

Akristu a ku Korinto anafunikira kupeŵa kuyanjana ndi munthu wothamangitsidwayo, koma kodi zimenezi zinatanthauza kuti anafunikira kudzilekanitsa kotheratu ndi osakhulupirira? Kodi iwo anafunikira kupeŵa kuonana kulikonse kapena zochita ndi osakhala Akristu, akumakhala kagulu ka mpatuko kodzipatula, mofanana ndi Ayuda amene anadzipatula kukakhala ku Qumran pafupi ndi Nyanja Yakufa? Tiyeni tilole Paulo ayankhe: “Ndinalembera inu m’kalata uja, kuti musayanjane ndi achigololo; sikonsekonse ndi achigololo a dziko lino lapansi . . . pakuti nkutero mukatuluke m’dziko lapansi.”​—1 Akorinto 5:9, 10.

Lingaliro la mawu amenewo nlomveka. Paulo anazindikira kuti Akristu anali chikhalirebe papulaneti lino, akumakhala pakati pa osapembedza amene makhalidwe awo anali oluluza ndi amene miyezo yawo inali yosiyana ndi yawo akumachita nawo zinthu pafupifupi tsiku lililonse. Popeza kuti zimenezo kwakukulukulu zinali zosapeŵeka, Akristu anayenera kukhala maso pangozi za kuchita ndi anthu otero.

Tsopano tiyeni tilingalirenso za kalata yachiŵiri ya Paulo kwa Akorinto. Iye anasonyeza kuti Akristu odzozedwa ngoyenerera kukhala atumiki a Mulungu, nthumwi zoimira Kristu. Iye anawauza kukhala maso pachokhumudwitsa chilichonse chimene chingaipitse utumiki wawo. (2 Akorinto 4:1–6:3) Paulo anafulumiza mwachindunji abale ake a ku Korinto, amene anali ngati ana ake auzimu, kukulitsa chikondi chawo. (2 Akorinto 6:13) Pambuyo pake iye anawafulumiza kuti: “Musakhale omangidwa m’goli ndi osakhulupira osiyana.” Iye anagwiritsira ntchito mpambo wa mafunso osafuna mayankho kuti agogomezere mfundoyo.

Mawu apatsogolo ndi apambuyo amasonyeza kuti Paulo sanali kunena za mbali imodzi ya moyo, monga ngati m’bizinesi kapena ntchito, ndi kukhazikitsa lamulo loti liperekedwe pankhaniyi. Mmalomwake, anali kupereka uphungu wochita ndi mikhalidwe yonse, wolama, ndi wothandiza kwa abale amene anawakonda kwambiri.

Mwachitsanzo, kodi uphungu umenewu ungagwire ntchito pankhani ya Mkristu amene akufuna kuloŵa muukwati? Ndithudi. M’kalata yake yoyamba, mtumwiyo analangiza Akorinto amene anafuna kuloŵa muukwati kuti achite motero “mwa Ambuye.” (1 Akorinto 7:39) Iye anagogomezera nzeru ya mawu amenewo ndi zimene analemba pambuyo pake, monga momwe ananenera pa 2 Akorinto 6:14-18. Ngati Mkristu alingalira za kukwatirana ndi munthu wina amene sali mtumiki wa Yehova ndi amene sali wotsatira Kristu, iye akakhala akulingalira za kugwirizana ndi wosakhulupirira. (Yerekezerani ndi Levitiko 19:19; Deuteronomo 22:10.) Mwachionekere, kusiyana kwa ziyambi kungabweretse mavuto, kuphatikizapo auzimu. Mwachitsanzo, wosakhulupirirayo angakhale akulambira mulungu wonyenga panthaŵi ino kapena mtsogolo. Paulo anafunsa modzutsa maganizo kuti: “Kristu avomerezana bwanji ndi Beliyali?”

Komabe, bwanji za mbali ina ya moyo​—kuloŵa m’bizinesi ndi munthu wosakhulupirira? M’zochitika zina Mkristu angalingalire kuti, kuti akhale ndi moyo ndi kusamalira banja lake afunikira kuloŵa muunansi wa bizinesi ndi munthu amene sali Mkristu mnzake. (1 Timoteo 5:8) Lingalirani zitsanzo wamba izi:

Mkristu angafune kuyamba bizinesi yogulitsa katundu, komano njira yokha ikakhala ya kuvomereza kuchitira zinthu pamodzi ndi munthu amene angapeze katundu wofunikayo kapena ndalama. Mkristu wina angafune kuchita ulimi (kapena kuŵeta ziŵeto); komabe, nasoŵa malo, chotero afunikira kuchita zimenezi mogwirizana ndi munthu amene ali wofunitsitsa kumbwereka munda woti adzigaŵana naye phindu. Kapena Mkristu wina sangathe kuyamba bizinesi yokonza mipope chifukwa chakuti Kaisara amangopereka malaisensi oŵerengeka chabe, ndipo malaisensiwo atha; njira yokha imene angachite ndiyo kugwirizana ndi wachibale wosakhulupirira amene ali ndi laisensiyo.​—Marko 12:17.

Izi nzitsanzo chabe. Sitikuyesa kunena za kuthekera konse, kapena kunena mawu ovomereza kapena kusavomereza. Koma polingalira zitsanzo zimenezi, kodi mungathe kuona chifukwa chake uphungu wa pa 2 Akorinto 6:14-18 suyenera kunyalanyazidwa?

Mkristu amene agwirizana m’kuchita bizinesi ndi wosakhulupirira, kaya akhale wachibale kapena ayi, angakumane ndi mavuto ndi ziyeso zosayembekezereka. Mwinamwake mnzakeyo anganene kuti njira yopangira phindu ndiyo kulemba geni yochepa kapena kuloŵetsa antchito amene sanalembedwe m’buku mwalamulo, ngakhale ngati zimenezo zingaswe malamulo aboma. Angakhale wofunitsitsa kupatsa chiwongola dzanja chamtseri kwa anthu opereka katundu chifukwa cha kubweretsa katundu amene sanalembedwe painivoisi yantchito. Kodi Mkristu akakhala ndi mbali iliyonse m’kusaona mtima kotero? Ndipo kodi nchiyani chimene Mkristuyo akachita pamene nthaŵi yakuti onsewo asaine zikalata za msonkho ifika kapena zikalata zina za lamulo zonena za mmene bizinesi yawo ikuyendera?​—Eksodo 23:1; Aroma 13:1, 7.

Kapena wogwirizana naye m’bizinesi wosakhulupirirayo angafune kuoda zinthu zogwirizana ndi maholide achikunja, kutumiza makadi amafuno abwino a paholide m’dzina la kampaniyo, ndi kukongoletsa malo a bizinesi kaamba ka maholide achipembedzo. Paulo anafunsa kuti: “Chiphatikizo chake nchanji ndi kachisi wa Mulungu ndi wa mafano? Pakuti ife ndife kachisi wa Mulungu wamoyo.” Ndimawu oyenerera chotani nanga akuti: “Chifukwa chake, Tulukani pakati pawo, ndipo patukani, ati [Yehova NW], ndipo musakhudza kanthu kosakonzeka; ndipo ine ndidzalandira inu”! (2 Akorinto 6:16, 17) Pogwiritsira ntchito uphungu wanzeru umenewo, Akristu ambiri asankha mitundu ya ntchito zakudziko imene singawapatse mavuto ambiri monga momwe kungathekere.​—Ahebri 13:5, 6, 18.

Mpingo sukulangizidwa kulonda kapena kufufuza zonse zimene Akristu amachita m’ntchito yawo yakudziko, kaya monga olembedwa ntchito kapena eni mabizinesi. Zowonadi, ngati kudziŵika kuti Mkristu akugwirizana m’kuchita chinthu cholakwa, monga ngati kuchilikiza kulambira konyenga kapena mpangidwe wina wa kunama kapena kuba, mpingo uyenera kutenga njira yochilikizira miyezo ya Yehova.

Komabe, mfundo yaikulu njakuti, uphungu wa Paulo wouziridwawo wakuti, “Musakhale omangidwa m’goli ndi osakhulupira osiyana,” ungathandize Akristu kupeŵa mavuto ndi mchitidwe uliwonse wofunika wa chiweruzo. Akristu anzeru adzasunga uphunguwo ndi kupeŵa kuloŵa m’mikhalidwe imene idzawachititsa kukhala pansi pa chitsenderezo chowonjezereka cha kulolera molakwa malamulo a Baibulo a mkhalidwe. Ngati munthu alingalira kuti ayenera kuchita bizinesi mogwirizana ndi wosakhulupirira, ena sayenera kufulumira kuweruza kapena kumsuliza, akumazindikira kuti iye adzafunikira kusenza thayo la chosankha chakecho. Kwakukulukulu, Paulo sanali kuika lamulo lamphamvu loletsa kuchita bizinesi mogwirizana ndi wosakhulupirira. Komabe, uphungu wake suyenera kunyalanyazidwa. Mulungu anauzira uphungu umenewo ndi kuupangitsa kulembedwa m’Baibulo kaamba ka phindu lathu. Tingakhale anzeru ngati tiulabadira.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena