Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w93 10/15 tsamba 4-7
  • Dziko Lopanda Mbala

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Dziko Lopanda Mbala
  • Nsanja ya Olonda—1993
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • “Wakubayo Asabenso”
  • Chisungiko m’Dziko Latsopano la Mulungu
  • Kodi Mantha Adzatha Liti?
    Nsanja ya Olonda—1995
  • Kodi Nchifukwa Ninji Kuba Kukuwonjezerekabe?
    Nsanja ya Olonda—1993
  • Kulaka Upandu m’Dziko Lachipolowe
    Nsanja ya Olonda—1991
  • Kuba—Kulekeranji?
    Galamukani!—1995
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1993
w93 10/15 tsamba 4-7

Dziko Lopanda Mbala

ZINACHITIKA mofulumira kwambiri. Mwamuna wovala bwino anaika mfuti pamutu pa Antônioa kutsogolo kwa nyumba yake mu São Paulo, Brazil, nalamula kupatsidwa mfungulo ndi mapepala ofunika a galimoto lake, nathaŵa mofulumira ndi galimotolo.

Mu Rio de Janeiro, pamaso pa mwana wake wamkazi wa zaka khumi, amuna anayi onyamula zida anaukira mwamuna wotchedwa Paulo. Ndiyeno, atapita ndi galimoto kunyumba kwake, achifwambawo analoŵa ndi kuba zimene anafuna, akumadzaza galimoto ziŵiri za Paulo. Atawopseza kupha mkazi wa Paulo, anatenga mkaziyo ndi wantchito wake monga chikole kupita nawo kusitolo la Paulo la zinthu zamtengo wake, limene anabamo chinthu chilichonse cha mtengo wapatali. Komabe, mosayembekezereka, mbalazo pambuyo pake zinaimba lamya, zikumawadziŵitsa kumene zinasiya galimotozo.

Nzachisoni chotani nanga kuberedwa ndalama ndi katundu zimene munavutikira kwambiri kuzipeza! Ngakhale kuti Antônio kapena Paulo sanachitepo kanthu paokha ndi kusatsatira njira ya lamulo, ena nzimene amachita. Anthu ena amakhaulitsa mbalayo mwakuipha kapena kuivulaza, kapena iwo eni kutaya miyoyo yawo. Mwachitsanzo, pamene mnyamata wina anatsomphola watchi ya mkazi wina wa ku Brazil, mkazi wokwiyayo anasolola mfuti m’chikwama chake ndi kuwombera mbalayo, naipha. Kodi chinatsatirapo nchiyani? O Estado de S. Paulo ikusimba kuti: “Anthu amene anaona chochitikacho anathokoza mkhalidwe wa mkazi wosadziŵikayo, ndipo palibe aliyense amene anafuna kuthandiza apolisi kumdziŵa.” Ngakhale kuti Akristu amalakalaka dziko lopanda mbala, iwo samabwezera monga momwe anachitira mkaziyo. Popeza kuti kubwezera nkwa Mulungu, iwo amalabadira mawu a pa Miyambo 24:19, 20 akuti: “Usavutike mtima chifukwa cha ochita zoipa; ngakhale kuchitira nsanje amphulupulu; pakuti woipayo sadzalandira mphotho.”

Koma ngati mwaukiridwa, kodi mungachitenji? Chochitika cha mu Rio de Janeiro chimasonyeza mmene kulili kofunika kukhala bata. Mkristu wina, Heloísa, anali paulendo wa pa basi kupita kukachititsa phunziro la Baibulo. Amuna aŵiri anayamba kulanda zinthu apaulendowo. Heloísa atafika pamalo omwe anafunikira kutsika, anawauza kuti anali mmodzi wa Mboni za Yehova ndi kuti anali kupita kukachititsa phunziro la Baibulo. Iye anasonyeza Baibulo lake ndi buku lophunziridwa. Popanda kumlanda kanthu, mbalazo zidamlola kutsika. Komabe, wapaulendo wina sanaloledwe kuchoka. Pambuyo pake woyendetsa basiyo anati sanaonepo konse zimenezo.

Regina anakhalanso bata pamene amuna aŵiri onyamula zida anamlamulira kuloŵa m’galimoto lake. Akumawasonyeza kope lake la magazini a Galamukani!, Regina anapereka umboni. Popeza kuti mbalazo zinachita mantha, iye anazipempha kutsegula m’malo ena osungiramo zinthu mmene anaikamo masiwiti. Koma mbalazo zitaona makaseti tepi a Kingdom Melodies, zinayamba kumvetsera nyimbozo. Popeza kuti mkhalidwe unakhala waubwenzi, mbalazo zinaganiza za kusiya Regina pamsewu waukulu popanda kumvulaza, zikumamtsimikiziritsa kuti adzapeza munthu wachifundo amene adzamthandiza. Atayenda kwa mphindi khumi, anapeza nyumba, koma mwininyumbayo sanakhulupirire nkhaniyo, akumati: “Simukuoneka kuti munali mwaukiridwa; muli wabata kwambiri.”

Ngakhale kuti mkhole sungavulazidwe mwakuthupi, chokumana nacho chowopsa choterocho chingakhale ndi ziyambukiro zazikulu. ‘Mkholeyo angakhale wamantha, kuda ziŵalo za banja kapena awo amene amayesayesa kumthandiza, kulephera kudalira ena, kusautsidwa ndi tsatanetsatane wa kulinganiza zinthu, amalingalira kuti dziko lilibe chilungamo,’ ikutero O Estado de S. Paulo. Mosiyana ndi zimenezo, mkhole amene amadalira Yehova Mulungu ali wothekera kwambiri kupyola m’chokumana nacho chotero popanda kuvulala mwakuthupi ndi mwamaganizo. Komabe, kodi simukuvomereza kuti likhoza kukhala dalitso ngati kungakhale kulibe upandu kapena kanthu kalikonse kochititsa mantha?

“Wakubayo Asabenso”

Ngakhale kuti ambiri amakonda mkhalidwe wawo wa moyo wakusirira, Mawu a Mulungu athandiza mbala kusintha zikhumbo zawo ndi maumunthu awo. (Aefeso 4:23) Pokhala ndi chifuno cha moyo chenicheni chozikidwa m’Baibulo, iwo amalabadira mawu akuti: “Zapang’ono, pokhala chilungamo, ziposa phindu lalikulu lopanda chiweruzo.” (Miyambo 16:8) Cláudio akunena kuti: “Pafupifupi aliyense m’banja langa anali Mboni, koma sindinamvetsere zimene anandiuza ponena za Yehova ndi zifuno zake. Pamene ndinali kubwerera paulendo wina wa pafupifupi [makilomita 2,000] ndikumayendetsa galimoto lakuba, ndinafunikira kupyola malo ambiri otsekedwa ndi apolisi. Ndili paulendowo ndinazindikira kuti ndinafunikira kusintha moyo wanga. Ndinali nditayesapo zimenezo kale koma ndinalephera. Panthaŵiyi ndinayamba kulingalira za achibale anga omwe ali Mboni za Yehova ndi mmene aliri osiyana, osangalala, achimwemwe, ndi amtendere.” Chotsatirapo, Cláudio anayamba kuphunzira Mawu a Mulungu, analeka mankhwala oledzeretsa ndi mabwenzi ake akale, nakhala mtumiki Wachikristu.

Enanso tsopano amalabadira mawu akuti: “Musakhulupirire kusautsa, ndipo musatama chifwamba.” (Salmo 62:10) Pambuyo pa chilango cha kukhala m’ndende kaamba koyesa kupha munthu pamene anali kuba, José, womwerekera ndi mankhwala oledzeretsa ndi wogulitsa mankhwalawo, anapindula ndi phunziro la Baibulo pamodzi ndi mlamu wake. Iye analeka mankhwala oledzeretsa ndipo tsopano ali Mboni yachangu.

Komabe, umunthu watsopano sumabwera nthaŵi imodzi kapena mozizwitsa. Oscar, yemwe anali womwerekera kwambiri ndi mankhwala oledzeretsa ndi kuba, akusimba kuti: “Ndinapemphera mwaphamphu kwambiri kwa Yehova kotero kuti kaŵirikaŵiri misozi yanga inachita ngati kadziŵe pansi.” Inde, kuwonjezera pa phunziro lakhama la Mawu a Mulungu, pemphero losalekeza, la mtima wonse nlofunika. Onani nzeru yokhala m’lingaliro loperekedwa mwapemphero ili: “Musandipatse umphaŵi, ngakhale chuma, mundidyetse zakudya zondiyenera; ndingakhute ndi kukukanani, ndi kuti, Yehova ndani? Kapena ndingasauke ndi kuba, ndi kutchula dzina la Mulungu wanga pachabe.”​—Miyambo 30:8, 9.

Dyera liyenera kuloŵedwa m’malo ndi chikondi chenicheni: “Wakubayo asabenso; koma makamaka agwiritse ntchito, nagwire ntchito yokoma ndi manja ake, kuti akhale nacho chakuchereza wosoŵa.” (Aefeso 4:28) Monga momwe anachitira kwa Akristu a m’zaka za zana loyamba omwe poyamba anali ‘mbala kapena osirira,’ Yehova, kupyolera mwa dipo la Yesu Kristu, mwachifundo amakhululukira amene amalapa. (1 Akorinto 6:9-11) Kuli kotonthoza chotani nanga kudziŵa kuti mosasamala kanthu ndi mmene tinaliri kale, tikhoza kusintha mkhalidwe wa moyo wathu ndi kupeza chiyanjo cha Mulungu!​—Yohane 3:16.

Chisungiko m’Dziko Latsopano la Mulungu

Tayerekezerani dziko lapansi lopanda mbala. Simukafunikira chitetezo cha ndalama zambiri cha oweruza, maloya, apolisi, ndi ndende zomwe! Likakhala dziko lachitukuko m’limene aliyense akalemekeza ena ndi chuma chawo! Kodi zimenezo zikumveka kukhala zosakhulupiririka? Kodi Mulungu adzaloŵereradi m’nkhani za anthu ndi kuthetsa kusayeruzika? Tikupemphani kupenda umboni wakuti Baibulo lili Mawu a Mulungu ndi kuti maulosi ake ali odalirika. Mudzapeza maziko olimba okhalira ndi chidaliro chakuti kusintha kuli patsogolopa. Palibe aliyense amene angalepheretse Mulungu kudzetsa mpumulo wolonjezedwa kwa anthu onse okonda chilungamo: “Usavutike mtima chifukwa cha ochita zoipa, usachite nsanje chifukwa cha ochita chosalungama. Pakuti adzawamweta msanga monga udzu, ndipo adzafota monga msipu wauŵisi.” (Salmo 37:1, 2) Mawu amenewo olembedwa kalekale adzakwaniritsidwa kotheratu posachedwa.

Ufumu wa Mulungu udzathetsa kuvutika konse ndi chisalungamo, zimene zimachititsa kuthedwa nzeru ndi kusatsimikizirika kwakukulu. Palibe amene adzasoŵa kanthu, akumakhala ndi chikhumbo cha kufuna kuba. Tikutsimikiziridwa muulosi wakuti: “M’dzikomo mudzakhala dzinthu dzochuluka pamwamba pa mapiri; zipatso zake zidzati waa, ngati za ku Lebano [wakale]: Ndipo iwo a m’mudzi adzaphuka ngati msipu wapansi.” (Salmo 72:16) Ndithudi, m’Paradaiso wobwezeretsedwayo, palibe chimene chidzadodometsa mtendere wa anthu odziŵa ndi kulambira Mulungu wowona.​—Yesaya 32:18.

Zimenezo zidzakhala dalitso lotani nanga kaamba ka kutsutsa njira za dziko lino ladyera! Lemba la Miyambo 11:19 limati: “Wolimbikira chilungamo alandira moyo; koma wolondola zoipa adzipha yekha.” Inde, pambuyo pakuti oipa adulidwa, palibe aliyense amene adzawopa kutaya moyo wake kapena chuma chake. Lemba la Salmo 37:11 limatilonjeza kuti: “Ofatsa adzalandira dziko lapansi; nadzakondwera nawo mtendere wochuluka.”

[Mawu a M’munsi]

a Maina ena asinthidwa.

[Bokosi patsamba 5]

Kuchita ndi Vuto la Kuba

PANYUMBA​—Popeza kuti mbala zikhoza kuthyola nyumba yanu kaya mulipo kapena ayi, zitseko zanu zikhale zotseka ndi zokhoma. Akatswiri amayamikira kukhala ndi maalamu ochenjezera kapena galu wolonda. Dziŵitsani mnansi wodalirika pamene mudzachokapo kupita kutchuthi. Khalani wabata​—achifwamba amachita zinthu mofulumira kwambiri, mosayembekezereka, ndipo akhoza kusintha zolinga zawo mwamsanga ngati achita mantha. Ngati ndinu mmodzi wa Mboni za Yehova, dzidziŵikitseni ndipo yesani kupereka umboni. Mukhoza kuchititsa munthuyo kukhala waubwenzi kapena kumva chifundo. Musakangane naye pokhapo ngati akuukirani mwakuthupi.

PAKATI PA ANTHU​—Khalani maso kuona ngati winawake akukulondolani. Yendani pakati pa kanjira ka oyenda pansi. Peŵani makwalala amdima ndi opanda anthu. Ikani chikwama chanu kapena zinthu zina zamtengo pamalo osungika. Yendani mokangaza monga ngati mukupita kwinakwake. Peŵani kuvala zovala zamtengo kwambiri kapena zinthu zamtengo wake zokopa. Khalani ndi wina pogula zinthu ngati mikhalidwe ilola. Nyamulani ndalama zofunikira zokha, zili zogaŵidwa m’matumba kapena malo osiyanasiyana.

MU GALIMOTO​—Ngati kuba galimoto munthu alimo kuli kowanda m’dera lanulo, musakhalebe m’galimoto lanu lili chiimire. Sinthani njira popita ndi pobwera kuntchito. Dzerani njira yotetezerekapo, ngakhale ngati ili yotalikirapo. Musanaimike galimoto, unguzani kuona ngati pali chinthu chilichonse chokayikiritsa. Peŵani kutsegula malo oikamo katundu pamalo opanda anthu. Musasiye zinthu zamtengo powonekera m’galimoto. Unyolo wokhomera woonekera kapena chipangizo china chochinjirizira kuba chingagwetse ulesi mbala wamba.

[Bokosi patsamba 6]

“Musadzikundikire nokha chuma pa dziko lapansi, pamene njenjete ndi dzimbiri ziwononga; ndi pamene mbala ziboola ndi kuba: koma mudzikundikire nokha chuma m’mwamba, pamene njenjete kapena dzimbiri siziwononga, ndipo mbala siziboola ndi kuba.”​—Mateyu 6:19, 20

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena