Mboni za Yehova Padziko Lonse—Thailand
“DZIKO la mfulu.” Limenelo ndilo tanthauzo la dzinalo Thailand. Nzika zake zoposa 57,000,000 zogwira ntchito zolimba ndi zaulemuzo zili ndi zikhulupiriro zosiyanasiyana zachipembedzo. Ngakhale kuti Chibuddha ndicho chimene chili chachikulu, zipembedzo za Dziko Lachikristu zimachitidwanso m’dziko limeneli la kummwera chakummaŵa la Asia. Anthu onseŵa afunika kumva mbiri yabwino ya Ufumu wa Mulungu.—Mateyu 24:14.a
Othaŵa Kwawo Amva Mbiri Yabwino
M’misasa yoponyanaponyana m’mapiri monse mu Thailand m’mbali mwa malire a Myanmar, choonadi cha Baibulo chikupeza malo kumeneko pakati pa othaŵa kwawo 10,000 a fuko la Karen. Ziŵalo za banja lina la fuko la Karen zokhala m’dera limenelo ndizo Mboni za Yehova. Izo zakhala zikufalitsa mbiri yabwino pakati pa othaŵa kwawo amenewo. Kodi ntchito yawo inayamba motani?
Zaka zingapo kalelo mnyamata wina analeka kupita ku Tchalitchi cha Anglican ndi kukhala mmodzi wa Mboni za Yehova. Atasonkhezeredwa ndi mbusa wawo, abale ake anamtsutsa. Komabe, iye anapirira moleza mtima, ndipo chitsutso cha m’banja mwake chinazirala mwapang’onopang’ono. Atsogoleri achipembedzo a Tchalitchi cha Anglican anapitirizabe kutonza kwawo kufikira pafupifupi zaka ziŵiri zapitazo pamene anathamangitsidwa pamalo awo antchito chifukwa cha khalidwe la chisembwere. Popeza kuti tchalitchicho panthaŵiyo chinalibe mbusa, a m’banja la Mboniyo ndi achibale ena ananyansidwa ndi kuthedwa nzeru. Khumi ndi mmodzi a iwo anatuluka m’tchalitchicho ndi kupempha Mboni kuphunzira nawo Baibulo.
Phunziro limeneli linapita patsogolo bwino kwambiri, othaŵa kwawo ena akumatenga nawo mbali. Choonadicho chinawanda mofulumira, chikumachititsa Mboni zatsopano 17 kubatizidwa mu mtsinje wodutsa mumsasa wa othaŵa. Kunali kokondweretsa chotani nanga kuona agogo aakazi azaka 88 zakubadwa akumizidwa limodzi nazo!
Vidiyo Iyambitsa Chikondwerero
Kuthekera kwa chifutukuko n’kwakukulu pa othaŵa kwawo amenewo. Mu 1993 pa Chikumbutso, panadza anthu 57. Mkati mwa kuchezera kwa woyang’anira woyendayenda m’May wa chaka chimenecho, anthu 67 anasonkhano pa imodzi ya nkhani zake. Ndipo anthu pafupifupi 250 anasonkhana kudzaonerera vidiyo ya Watchtower Society yotchedwa Jehovah’s Witnesses—The Organization Behind the Name.
Mkazi wa pasitala wa Baptist mumsasa wa othaŵa kwawo mmenemo anafika pa nkhani yapoyera ya Baibulo yoperekedwa ndi Mboni ndi kulemba mavesi a Baibulo amene anafotokozedwa. Iye anauza mwamuna wake za mmene analiri wosakhutiritsidwa ndi maulaliki obwerezedwabwerezedwa amene anamva ku tchalitchi chawo. Mwamunayo anatsutsa, akumanena kuti ngati adzapita kumisonkhano ya Mboni za Yehova, anthu onse a m’tchalitchi adzachita mofananamo. Pamene mkaziyo anapitanso kumisonkhano, mwamuna wake anamthamangitsa ndi mpeni ndi kutentha manotsi ake a pamsonkhano ndi zofalitsa zofotokoza Baibulo. Mosasamala kanthu za zimenezo, pamene vidiyo inasonyezedwa, mkaziyo anafikaponso. Pambuyo pake mkaziyu anauza mwamuna wake zimene anaona. Atasintha mtima, mwamunayo anafuna kukaona vidiyo imeneyo ndipo anali wachisoni kuti anatentha manotsi a mkazi wake ndi zofalitsa za Baibulo.
Chotero anthu akumva mbiri yabwino ku Thailand. Motero iwo akupeza ufulu wauzimu mu “dziko la mfulu.”—Yohane 8:32.
[Mawu a M’munsi]
a Kaamba ka chidziŵitso chowonjezereka, onani Kalenda ya Mboni za Yehova ya 1994.
[Bokosi patsamba 24]
ZIŴERENGERO ZA DZIKOLO Chaka Chautumiki cha 1993
CHIŴERENGERO CHAPAMWAMBA CHA OCHITIRA UMBONI: 1,434
KUGAŴA Mboni 1 pa anthu 40,299
OFIKA PACHIKUMBUTSO: 3,342
AVAREJI YA OFALITSA AUPAINIYA: 232
AVAREJI YA MAPHUNZIRO A BAIBULO: 1,489
CHIŴERENGERO CHA OBATIZIDWA: 92
CHIŴERENGERO CHA MIPINGO: 39
OFESI YA NTHAMBI: BANGKOK
[Chithunzi patsamba 25]
Olengeza Ufumu alalikira mbiri yabwino mokangalika
[Chithunzi patsamba 25]
Ofesi ya nthambi yoyamba, 1947
[Chithunzi patsamba 25]
Banja la Beteli kumaso kwa ofesi ya nthambi yatsopano mu Bangkok, yopatuliridwa pa February 8, 1992