Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w94 6/1 tsamba 25-27
  • Omaliza Maphunziro a Gileadi Apeza “Chimwemwe Chachikulu m’Kupatsa”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Omaliza Maphunziro a Gileadi Apeza “Chimwemwe Chachikulu m’Kupatsa”
  • Nsanja ya Olonda—1994
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Mawu a Kutsazikana Olangiza
  • Programu Yamasana ya Mbali Zosiyanasiyana
  • Amishonale Owonjezereka Kaamba ka Kututa Kwapadziko Lonse
    Nsanja ya Olonda—1991
  • Sukulu ya Gileadi—Ya Zaka 50 Ndipo Ikupitabe Patsogolo!
    Nsanja ya Olonda—1993
  • Omaliza Maphunziro a Gileadi—“Amishonale Enieni!”
    Nsanja ya Olonda—1995
  • Sekerani mwa Yehova Ndipo Kondwerani
    Nsanja ya Olonda—1999
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1994
w94 6/1 tsamba 25-27

Omaliza Maphunziro a Gileadi Apeza “Chimwemwe Chachikulu m’Kupatsa”

PA SANDE, March 6, 1994, banja la Beteli la pamalikulu apadziko lonse a Mboni za Yehova ndi alendo linasonkhana pachochitika chokondweretsa​—kumaliza maphunziro kwa kalasi la 96 la Sukulu ya Gileadi ya Baibulo ya Watchtower. M’mawu ake oyamba, tcheyamani wa programuyo Karl F. Klein, amene watumikira m’Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova kwa zaka pafupifupi makumi aŵiri, anauza ophunzira 46 kuti: “Yesu anati muli chimwemwe chachikulu m’kupatsa koposa m’kulandira. Chotero zidzakhala motero m’gawo lanu laumishonale​—pamene mupatsa mowonjezereka, ndi pamenenso mudzakhala otero.”​—Machitidwe 20:35, NW.

Mawu a Kutsazikana Olangiza

Panatsatira nkhani zotsatizana zokambidwa kwa ophunzirawo. Leon Weaver, chiŵalo cha Komiti ya Dipatimenti ya Utumiki, anakamba nkhani ya mutu wakuti “Chipiriro Chimalemekeza Yehova.” Tonsefe timakunana ndi mayeso. (2 Akorinto 6:3-5) “Pamene tili pansi pa chitsenderezo,” Mbale Weaver anatero, “nkosavuta kudzidalira.” Komabe, iye anakumbutsa ophunzirawo kuti: “Mayeso alionse aumunthu amene mungakumane nawo, Yehova ali wosamala ponena za iwo. Sadzakulolani kuyesedwa koposa kumene mungathe kupirira.”​—1 Akorinto 10:13.

“Nthaŵi Zonse Samalirani Bwino Gawo Lanu” ndiwo unali mutu wa nkhani yotsatira, yoperekedwa ndi Lyman Swingle wa Bungwe Lolamulira. Aisrayeli sanasankhe nthaŵi zonse kumene akakhala ndi zimene akachita. Fuko lililonse linapatsidwa gawo la dziko, ndipo Alevi anagaŵiridwa ntchito zapadera zoti achite. Mofananamo, ambiri amene ali mu utumiki wapadera wa nthaŵi yonse lerolino​—monga ngati amishonale ndi ziŵalo za banja la Beteli​—samadzisankhira kumene adzakhala ndi ntchito imene adzachita. Bwanji ngati munthu akhala ndi malingaliro osatsimikizira ponena za gawo lake? “Ngati muyang’anitsitsa pa Mkulu wa chikhulupiriro chathu, Yesu, ndi kulingalira chitsanzo chake mosamalitsa, simudzagonja,” Mbale Swingle anatero.​—Ahebri 12:2, 3, NW.

Leonard Pearson, wa Watchtower Farms Committee, anatsatira ndi mutu wakuti “Khalanibe Openya Bwino.” Iye anati: “Mungathe kukhala ndi kamera yabwino koposa, malo okongola kwambiri, mkhalidwe wabwino, ndipo kungotulutsabe zotulukapo zosaoneka bwino​—ngati kamera yanu ili yosalunjikitsidwa bwino.” Mofanana ndi poonera papakulu, kapenyedwe kathu kayenera kuphatikizapo kulalikira kwapadziko lonse kumene kukuchitidwa. Sitiyenera kutaya chinthunzi chonse. “Awo amene amasumika maganizo pa iwo okha adzakhala osakondwa m’magawo awo,” Mbale Pearson anatero. “Awo amene amasumika maganizo pa Yehova ndi ntchito imene wawapatsa kuti achite adzapambana.”

“Pali Zambiri Zokhalira Oyamikira” ndiwo unali mutu wa nkhani yotsatira, yoperekedwa ndi John E. Barr, chiŵalo china cha Bungwe Lolamulira. “Musataye lingaliro lanu la kuyamikira Yehova,” Mbale Barr analangiza ophunzirawo motero. “Ndilo magwero ena aakulu koposa a chikhutiro, mosasamala kanthu za gawo limene muli nalo.” Mkhalidwe wa kuyamikira unasonkhezera Davide kulemba kuti: “Zingwe zandigwera mondikondweretsa; inde chosiyira chokoma ndili nacho.” (Salmo 16:6) “Muli nacho chosiyira chofunika chotero pokhala oyandikana ndi Yehova m’moyo wanu wa tsiku ndi tsiku,” Mbale Barr anatero. “Yehova sadzachotsa unansi umenewo kwa inu malinga ngati mupitirizabe kuuona monga kanthu kena kokoma kwambiri kamene mukuyamikira.”

Mlangizi wa Gileadi Jack Redford anali wokamba nkhani wotsatira, pa mutu wakuti “Kodi Mudzagwiritsira Ntchito Motani Lilime Lanu?” Kalankhulidwe kosasamala kangachititse chiwonongeko chotani nanga! (Miyambo 18:21) Kodi ndi motani mmene lilime lingalamuliridwire? “Choyamba muyenera kuphunzitsa maganizo anu,” Mbale Redford anayankha motero, “chifukwa chakuti lilime limasonyeza zimene zili m’maganizo ndi mu mtima.” (Mateyu 12:34-37) Yesu anapereka chitsanzo chabwino kwambiri; anagwiritsira ntchito lilime lake kulemekeza dzina la Yehova. “Lerolino kuli njala ya kufuna kumva mawu a Yehova,” Mbale Redford anauza kalasilo. “Mumadziŵa mawu amenewo. Inu muli ndi ‘lilime la ophunzira.’ Chotero nthaŵi zonse lolani lilime lanu kutsogozedwa ndi maganizo ndi mtima umene uli wodzipatulira kotheratu kwa Yehova.”​—Yesaya 50:4.

Kufunika kwa pemphero kunagogomezeredwa mu nkhani yakuti “Kodi Mukuyenda Monga Ngati Muli Pamaso pa Yehova?” Ulysses Glass, woyang’anira kaundula wa sukulu, anati: “Ngati atate wina anagwira ntchito zolimba kuti asamalire banja lake komano naleka kulankhula nalo ndipo wosasonyeza chikondi chilichonse, banja lakelo lingafikire pakunena kuti cholinga chake chinali cha kungochita ntchito yosakondweretsayo osati kusonyeza chikondi. Chotero zili chonchonso kwa ife. Tingakhale otanganitsidwa mu utumiki wa Mulungu. Koma ngati sitipemphera, pamenepo tikungodzipatulira pantchitoyo koposa kuchita motero kwa Atate wathu wakumwamba.”

Theodore Jaracz, wa Bungwe Lolamulira, anakamba nkhani ya mutu wakuti “Chifukwa Chake Makamu Akuyanjana ndi Anthu a Mulungu.” Chaka chilichonse zikwi mazana ambiri zimaloŵa m’gulu la Yehova. (Zekariya 8:23) Kodi nchiyani chimene chimadziŵikitsa Mboni za Yehova kukhala anthu a Mulungu? Choyamba, zimavomereza Baibulo lathunthu kukhala Mawu a Mulungu. (2 Timoteo 3:16) Chachiŵiri, zili zauchete pa ndale za dziko. (Yohane 17:16) Chachitatu, zimachitira umboni dzina la Mulungu. (Yohane 17:26) Chachinayi, zimasonyeza chikondi cha kudzimana. (Yohane 13:35; 15:13) Pokhala ndi ziyeneretso zimenezi, tingathe ‘kulalikira zoposazo za iye amene anatiina kutuluka mu mdima, kuloŵa kuunika kwake kodabwitsa.’​—1 Petro 2:9.

Pambuyo pa nkhani zosonkhezera maganizo zimenezi, ophunzira 46 onse analandira madipuloma. Iwo agaŵiridwa ku maiko 16 kuzungulira dziko lonse.

Programu Yamasana ya Mbali Zosiyanasiyana

M’nthaŵi ya masana Phunziro la Nsanja ya Olonda lachidule linachititsidwa ndi Donald Krebs wa Komiti ya Beteli. Ndiyeno omaliza maphunzirowo anapereka programu ya mutu wakuti “Nzeru Ifuula Panja.” (Miyambo 1:20) Anachita zitsanzo za zokumana nazo zofupa zimene anali nazo ponse paŵiri mu umboni wa pa khwalala ndi m’malo azamalonda. Zoonadi, Yehova amadalitsa awo amene amakhala ndi kulimbika mtima kwa kulalikira mwamwaŵi. “Ndimakonda kulingalira kuti ife tili monga mazenga okhala m’manja mwa otuta aungelo,” anatero womaliza maphunziro wina. “Pamene maluso athu ali akuthwa, ndi pamenenso angelo amenewo angatigwiritsire ntchito kuchitira ntchito yowonjezereka.” (Yerekezerani ndi Chivumbulutso 14:6.) Programu ya ophunzirayo inaphatikizaponso kusonyezedwa kwa masilaidi kumene kunatenga omvetserawo paulendo wophunzitsa wa kuona maiko a Bolivia, Malta, ndi Taiwan​—atatu a maiko amene omaliza maphunziro a m’kalasili atumizidwako.

Kenako, Wallace ndi Jane Liverance​—amene akhala amishonale kwa zaka 17​—anafunsidwa. Mu October 1993 anaitanidwa ku Watchtower Farms, kumene Mbale Liverance amatumikira tsopano monga mmodzi wa alangizi a Gileadi.

Chitsanzo cha mbali zinayi, cha mutu wakuti “Kulemekeza Oyenerera m’Zaka Zawo za Ukalamba” chinatsatira. Pamene anthu akalamba, mantha a kukhala osathandiza ndi onyalanyazidwa angachotse chidaliro chawo. (Salmo 71:9) Chitsanzo chosonkhezera maganizo chimenechi chinasonyeza mmene onse mu mpingo angachirikizire okalamba okhulupirika amenewo.

Pambuyo pa nyimbo ndi pemphero lomaliza, omvetsera onse 6,220 pa Jersey City Assembly Hall ndi mu nyumba zina zokhala ndi wailesi zakanema anatsitsimulidwa. Tikupempherera omaliza maphunzirowo m’magawo awo atsopano. Apitirizetu kupeza chimwemwe chimene chimapezeka m’kupatsa.

[Bokosi patsamba 26]

Ziŵerengero za Kalasi

Chiŵerengero cha maiko kumene anachokera: 9

Chiŵerengero cha maiko ogaŵiridwako: 16

Chiŵerengero cha ophunzira: 46

Avareji ya zaka zakubadwa: 33.85

Avareji ya zaka m’choonadi: 16.6

Avareji ya zaka muutumiki wa nthaŵi yonse: 12:2

[Bokosi patsamba 27]

Kusumika Maganizo pa Malta

DZIKO LACHIKRISTU linatsekereza choonadi cha Baibulo ku Malta kwa zaka zambiri. Amishonale omalizira otumizidwako, Frederick Smedley ndi Peter Bridle, anamaliza maphunziro a kalasi lachisanu ndi chitatu kalelo mu 1947. Komabe, anagwidwa ndi kuthamangitsidwa m’Malta mofulumira atangofika. 1948 Yearbook of Jehovah’s Witnesses ikusimba kuti: “Amishonale aŵiri ameneŵa athera nthaŵi yochuluka m’makhoti ndiponso ndi akuluakulu a dzikolo kuposa mmene achitira pantchito yawo yautumiki, chifukwa chabe cha chitsutso cha Bungwe Lolamulira la Roma Katolika. Ansembe akunena kuti Malta ndi wa Akatolika ndipo wina aliyense ayenera kuchoka.” Tsopano, pafupifupi zaka 45 pambuyo pake, amishonale anayi a m’kalasi la 96 la Gileadi agaŵiridwa ku Malta.

[Chithunzi patsamba 26]

Kalasi la 96 la Omaliza Maphunziro a Sukulu ya Gileadi ya Baibulo ya Watchtower

M’ndandanda pansipa, mizera ikuŵerengedwa kuyambira kutsogolo kumka kumbuyo, ndipo maina andandalikidwa kuyambira kulamanzere kumka kulamanja mumzera uliwonse.

(1) Ehlers, P.; Giese, M.; Sellman, S.; Zusperregui, J.; Rowe, S.; Jackson, K.; Scott, T. (2) Liehr, T.; Garcia, I.; Garcia, J.; Fernández, A.; Davidson, L.; Liidemann, P.; Gibson, L.; Juárez, C. (3) Fouts, C.; Pastrana, G.; Claeson, D.; Fernández, L.; Walls, M.; Dressen, M.; Pastrana, F.; Burks, J. (4) Burks, D.; Scott, S.; Jackson, M.; Mauray, H.; Juárez, L.; Zusperregui, A.; Brorsson, C.; Rowe, C. (5) Sellman, K.; Liidemann, P.; Davidson, C.; Mauray, S.; Walls, D.; Dressen, D.; Schaafsma, G.; Liehr, S. (6) Claeson, T.; Gibson, T.; Giese, C.; Ehlers, D.; Fouts, R.; Schaafsma, S.; Brorsson, L.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena