Kuwopa Akufa Nkofalikira
Dzuŵa laloŵa kale. Mukubwerera kunyumba mochedwerapo kuposa mmene mukanafunira. Pamene mukuyenda kudutsa pamanda akumaloko, mtima wanu ukuyamba kugunda mofulumira. Mkhalidwe wachete wa usiku wamdima ukukuchititsani kukhala watcheru pa phokoso lililonse laling’ono. Mwadzidzidzi chapatalipo inu mukumva kulira kochititsa nthumanzi ndi kodabwitsa. Mukuyenda mofulumira—kugunda kwa mtima kwanu kukuwonjezerekanso—pamene mukufulumira kuti mufike kunyumba kaamba ka chitetezo.
KODI munayamba mwakhalapo ndi malingaliro amantha pamene munali kumanda kapena pafupi nawo? Ngati ndi choncho, inu mwina mungakhale mutayambukiridwa ndi lingaliro lachipembedzo limene lili lofala padziko lonse—lakuti mizimu ya akufa ingathandize kapena kuvulaza amoyo.
Miyambo yambiri ya kukhulupirira malaulo yakhalapo chifukwa cha chikhulupiriro chakuti akufa amafuna thandizo la amoyo kapena kuti iwo angavulaze amoyo ngati sakondweretsedwa. Mwachitsanzo, m’maiko ena a ku Latin America, anthu ambiri ali ndi mwambo wa kumanga kanyumba kokhala ndi mtanda pamalo amene munthu waferapo m’ngozi. Anthu amayatsa makandulo ndi kuika maluŵa pamenepo poyesayesa kusonyeza chikondwerero kapena kuthandiza moyo kapena mzimu wa munthu wakufayo. M’zochitika zina, malipoti onena za mayankho “ozizwitsa” a mapemphero amafalitsidwa, kwakuti anthu amayamba kupita kumalo a animita, kanyumba kakang’ono ka moyo kapena mzimu wa munthu wakufayo. Kumeneko iwo amapanga mandas, kapena malonjezo, akuti ngati munthu wakufayo adzawathandiza kuchita kapena kulandira kanthu kena—kapena machiritso ozizwitsa—adzasonyeza chiyamikiro chawo mwanjira yapadera. Komanso, kungasimbidwe kuti moyo wa munthuyo umaonekera mu mdima wa usiku, ukumawopseza awo amene alipo. Kumanenedwa mofala kuti iwo ndiwo penando, osautsa anthu amoyo chifukwa cha zochitika zakale.
M’maiko ambiri anthu amayesayesa kwambiri kutonthoza “mizimu” ya akufa. Mapwando okonzedwa mosamalitsa amachitidwa, nsembe zimaperekedwa, mawu otonthoza amanenedwa—zonsezo poyesayesa kupeŵa chilango chochokera kwa mzimu wa munthu wakufayo. Kumalingaliridwa kuti, kutonthoza mzimuko, kudzadzetsa mfupo ndi madalitso kwa otsalawo.
“Ambiri amakhulupirira kuti palibe chinthu chimene chimachitika ‘mwawamba kapena mwachibadwa,’” likutero lipoti lina la mu Afirika. “Pa chochitika chilichonse—kaya chikhale matenda, tsoka, kusabala ana, mavuto azachuma, kugwa kwa mvula kapena kuŵala kwa dzuŵa kopambanitsa, ngozi, kusagwirizana kwa banja, imfa—amakhulupirira kuti mizimu yosaoneka, yokhala ndi mphamvu zauzimu, ndiyo imene imachititsa zonsezo.” Lipoti lina likuti: “Anthu amakhulupirira kuti mizimu ya makolo awo imakhala m’malo ena kumwamba ndipo nthaŵi zonse imayang’anira otsala awo padziko lapansi. Amakhulupira kuti makolowo ali ndi mphamvu zauzimu, zimene angagwiritsire ntchito kudalitsira ndi kutetezera achibalewo padziko lapansi kapena kuwalanga, zikumadalira ndi mmene achibale awo amalemekezera kapena kunyalanyazira akufa.”
Koma kodi zimenezo zimagwirizana ndi Mawu a Mulungu? Kodi lingaliro lanu nlotani?
[Chithunzi patsamba 4]
“Animita” ku Chile