Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w95 2/15 tsamba 32
  • Idzani ku Msonkhano Wachigawo wa “Atamandi Achimwemwe”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Idzani ku Msonkhano Wachigawo wa “Atamandi Achimwemwe”
  • Nsanja ya Olonda—1995
  • Nkhani Yofanana
  • Idzani ku Msonkhano Wachigawo wa “Mantha Aumulungu”
    Nsanja ya Olonda—1994
  • Tikulandirani ku Misonkhano Yachigawo ya “Onyamula Kuunika”
    Nsanja ya Olonda—1992
  • Msonkhano Wachigawo wa Mboni za Yehova wa 2003 Wakuti “Patsani Mulungu Ulemerero”
    Nsanja ya Olonda—2003
  • Mukuitanidwa ku Msonkhano Wachigawo wa “Okonda Ufulu”
    Nsanja ya Olonda—1991
Nsanja ya Olonda—1995
w95 2/15 tsamba 32

Idzani ku Msonkhano Wachigawo wa “Atamandi Achimwemwe”

HA, ndi mutu wabwino chotani nanga umene wasankhidwa wa misonkhano yachigawo ya 1995: “Atamandi Achimwemwe”! Umu ndi mmenedi Mboni za Yehova zilili. Atamandi ayani? Si a Yehova Mulungu!

Yehova alibe wofanana naye, ali wosayerekezereka, wapadera m’njira zambiri. Iye ali mwini mphamvu, mwini nzeru, wangwiro m’chilugamo, ndi chitsanzo changwiro cha chikondi. Ali woyenera kulambiridwa ndi kutamandidwa kuposa wina aliyense.

Ndithudi, ife timafuna kukhala atamandi ake achimwemwe! Kuti atithandize kukhala otero, Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova lakonza programu yabwino ya masiku atatu, kuyambira m’chisanu cha 1995. Masiku atatu ameneŵa adzakhaladi achisangalalo, ndipo Mboni iliyonse ya Yehova idzayenera kuchita zonse zomwe ingathe kuti ikakhalepo kuyambira pa nyimbo yoyamba pa Lachisanu mmaŵa mpaka pa nyimbo yomaliza ndi pemphero pa Sande madzulo.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena