Mukuitanidwa ku Msonkhano Wachigawo wa “Okonda Ufulu”
CHIYAMBIRE November 1989, nkhani ya ufulu yakhala ikutchuka kuposa ndi kale lonse. Makamaka anthu a kumaiko a Kum’mawa kwa Yuropu akhala akusangalala ndi ufulu wandale wowonjezereka kuposa mmene anachitira kwa zaka zoposa 40.
Koma pali ufulu wofunika koposa kuposa ufulu wina uliwonse wandale. Tingaŵerenge za iwo m’Mawu a Mulungu, Baibulo. Yesu Kristu panthaŵi ina ananena kuti: ‘Mudzazindikira chowonadi, ndipo chowonadi chidzakumasulani.’ (Yohane 8:32) Inde, Akristu odzipereka akhala omasuka ku kuwopa anthu ndi ukapolo ku tchimo ndi imfa, monga momwe tikuŵerengera pa Aroma 6:18, 22. Timaŵerenganso kuti ‘pamene pali mzimu wa Yehova pali ufulu.’ (2 Akorinto 3:17) Kwenikweni, Mawu a Mulungu amapereka chiyembekezo chowala kuti ‘cholengedwa chomwe chimasulidwa ku ukapolo wa chivundi, ndi kuloŵa ufulu wa ulemerero wa ana a Mulungu.’—Aroma 8:21.
Ngati munthu aliyense akufuna kupeza ufulu Wachikristu panthaŵi ino, ayenera kupanga kuyesayesa kwenikweni. Sikuli kungokana kuchita chinthucho. Ndipo kupitiriza kusangalala ndi ufulu umenewu kumafunikira kuyesayesa kowonjezereka, polingalira za mphamvu zimene zimatilanda ufulu: Satana Mdyerekezi, dziko lake loipa, ndi zikhoterero zathu zobadwa nazo zochimwa. Yehova Mulungu wapereka thandizo kupyolera m’Mawu ake ouziridwa, kupyolera mwa mzimu wake woyera, ndi kupyolera m’gulu lake lowoneka ndi maso.—Luka 11:13.
Pofuna kuthandiza okonda ufulu onse kulimbikitsa kugwira kwawo zolimba pa ufuluwo, misonkhano yachigawo ya Mboni za Yehova yachaka chino idzagwirira ntchito pa mutu wakuti “Okonda Ufulu.” Misonkhano imeneyi idzakhala ya masiku atatu, kuyambira Lachisanu mmawa pa 9:20 ndikupitiriza mpaka Sande 4:00 p.m. Anthu onse amene adzabwera adzatsitsimulidwa mwauzimu ndikumangiriridwa ndi nkhani zodzutsa maganizo, kufunsana kosangalatsa, zitsanzo zogwira maganizo, ndi drama yochititsa chidwi yozikidwa pa Baibulo; ndiponso sitifunikira kunyalanyaza chisangalalo chotenthetsa maganizo chakukumana ndi mabwenzi akale ndi atsopano, ndi chisangalalo chakugwirizana ndi zikwi zina zambiri m’kuimba nyimbo Zaufumu, ndikukhalamo ndi phande m’mapemphero apoyera amtima wonse.
Atumiki odzipereka onse a Yehova asalole konse china chirichonse kudodometsa kupezekapo kwawo pa Lachisanu mmawa pamene misonkhano imeneyi idzayamba. Ndipo khalani otsimikiza kubwera osati ndi Baibulo lokha ndi bukhu lanyimbo komanso pensulo ndi bukhu zodzalembera nsonga. Muyeneranso kubwera muli amaso kwenikweni ponena za kusoŵa kwanu kwauzimu monga mbali ya anthu aufulu.—Mateyu 5:3.