Idzani ku Msonkhano Wachigawo Wakuti “Chinenero Choyera”
KUSIYANA chinenero kwakhala magwero ogawanitsa chiyambire pa Babele. Konko Yehova anasokoneza chinenero cha anthu ndi kulepheretsa cholinga cha anthu cha ‘kumanga nsanja ndi kudzipangira dzina lotchuka.’ (Genesis 11:4) Mmene kusiyana chinenero kungakhalire kogaŵanitsa kukuwonedwa m’zimene zinachitika m’Belgium. Zaka zingapo zapitazo, Yunivesite Yachikatolika pa Louvain inagawanika pakati mwa zinenero.
Chinenero chiri chimodzi chokha cha zifukwa za kugaŵanika pakati pa anthu. Zina ndizo utundu, ufuko, maphunziro, ndi mkhalidwe wa zachuma. Koma Mboni za Yehova zalaka zochititsa kugawanikana zonsezi ndipo ziridi zogwirizana.
Dzinja lathali linawona kusonyezedwa kochititsa nthumanzi kwa umodzi umenewu m’mizinda ya Chorzów (pafupi ndi Katowice), Poznan, ndi Warsaw m’Poland. Mboni, zolankhula zinenero zoposa 16 zosiyanasiyana, zidaalipo kuchokera kumaiko 37. Komabe, umodzi wochititsa nthumanzi unasonyezedwa ndi onse. Kodi nchiyani chomwe chidachititsa zimenezi? Onsewo adalankhula “chinenero choyera” cha chowonadi Chamalemba. Zimenezi zinanenedweratu molosera pa Zefaniya 3:9, NW: “Pamenepo ine [Yehova Mulungu] ndidzasinthira anthu kuchinenero choyera, ndi cholinga chakuti iwo onsewo aitanire pa dzina la Yehova, kuti amtumikire phewa ndi phewa.”
Chotero, pali chifukwa chabwino, kuti misonkhano yachigawo ya 1990 idzakhala ndi mutu wakuti “Chinenero Choyera.” Chifukwa cha kupanda ungwiro kwa anthu, zikhoterero zochokera kudziko loipa la Satana, ndi machitachita amachenjera a Mdyerekezi ndi ziŵanda zake, kulankhula “chinenero choyera” sikumachitika mosavuta. Nthaŵi zonse tifunikira kukhala paulonda motsutsana ndi zikhoterero zadyera zimene zingatigaŵanitse.
Kodi nchifukwa ninji Mulungu watipatsa chinenero choyera chimenechi? Kuchitira kuti tonsefe tikhoze kutumikira Yehova “phewa ndi phewa.” Matembenuzidwe ena amasonyeza kuti ichi chimatanthauza kutumikira “pansi pa goli limodzimodzi” (The Jerusalem Bible); “ndi chimvano chimodzi” (Moffatt); “ncholinga chimodzi” (An American Translation); ndi “kugwirizana muutumiki wake.”—Byington.
Kupyolera m’nkhani, zitsanzo, zokumana nazo, nkhani zosiyirana, ndi madrama a Baibulo pamisonkhano imeneyi, tidzalimbikitsidwa ndi kusonkhezeredwa kulankhula chinenero choyera mwamyaa koposerapo. Zidzatisonkhezeranso kutumikira limodzi ndi abale athu mogwira mtima kwambiri ndi mogwirizana.
Misonkhano imeneyi idzayamba pa Lachinayi mwamsanga pambuyo pa 8:00 a.m. ndipo idzamalizidwa chifupifupi pa 4:00 p.m. pa Sande. Pangani makonzedwe tsopano akupezekapo panyimbo yotsegulira ndi kupezeka pamaprogramu onse kufikira pemphero lomaliza pa Sande masana.
Bwerani ndi Mabaibulo anu ndi mabukhu anyimbo, ndipo khalani wokonzekera kulemba manotsi. Fikanipo muli ndi njala yauzimu, ndipo mudzachoka muli wokonzekeretsedwa mokwanira bwino kulankhula chinenero choyera ndi kutumikira Yehova.