Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w89 2/15 tsamba 30-31
  • Msonkhano Wachigawo wa “Kudzipereka Kwaumulungu”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Msonkhano Wachigawo wa “Kudzipereka Kwaumulungu”
  • Nsanja ya Olonda—1989
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Ndandanda ya Malo a Misonkhano ya Chigawo ya 1989 ya “Kudzipereka Kwaumulungu” mu Zambia
  • Idzani ku Msonkhano Wachigawo Wakuti “Chinenero Choyera”
    Nsanja ya Olonda​—1990
  • Mukuitanidwa ku Msonkhano Wachigawo wa “Okonda Ufulu”
    Nsanja ya Olonda—1991
  • Pezekanipo pa Msonkhano Wachigawo wa 1987 wa “Khulupirirani mwa Yehova”
    Nsanja ya Olonda—1987
  • Tikulandirani ku Misonkhano Yachigawo ya “Onyamula Kuunika”
    Nsanja ya Olonda—1992
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1989
w89 2/15 tsamba 30-31

Msonkhano Wachigawo wa “Kudzipereka Kwaumulungu”

MTUMWI Paulo analemba kuti: “Masiku otsiriza zidzafika nthaŵi zowawitsa. Pakuti anthu adzakhala . . . okonda zokondweretsa munthu osati okonda Mulungu, akukhala nawo mawonekedwe a [kudzipereka kwaumulungu, NW] koma mphamvu yake adaikana.”​—2 Timoteo 3:1-5.

Ndi molongosoka chotani nanga mmene mawu amenewo amalongosolera unyinji wokulira wa awo odzinenera kukhala Akristu! Molingana ndi mtsogoleri wachipembedzo mmodzi, “lerolino matchalitchi ochuluka kwambiri akhala . . . malo a pakati a zosangalatsa.” Mosiyana kwambiri, atsatiri owona a Kristu ali anthu “achangu pa ntchito zokoma.” (Tito 2:14) Atsatiri a Yesu ali “mchere wa dziko lapansi” ndi “kuwunika kwa dziko.”​—Mateyu 5:13, 14.

Misonkhano yathu ya pa chaka, yachigawo, ya mtundu, ndi ya mitundu yonse, iri mbali zina za kulambira kwathu zimene zimatikhalitsa apadera. Mutu weniweni wa misonkhano yathu yachigawo ya 1989, “Kudzipereka Kwaumulungu,” umaloza ku mkhalidwe wa kulambira kwathu umene umatipanga kuwoneka osiyana.

Malemba amagogomezera kufunika kwa kudzipereka kwaumulungu. Msonkhanowu udzakhala mwaŵi wowonjezereka wa “kudzizoloŵeretsa [kudzipereka kwaumulungu, NW]. Pakuti chizoloŵezi cha thupi chipindula pang’ono; koma [kudzipereka kwaumulungu, NW] kupindula zonse, popeza [ku]khala nalo lonjezano la kumoyo uno ndi la moyo ulinkudza.” (1 Timoteo 4:7, 8) Ndipo 1 Timoteo 6:6 mowonjezereka imalongosola kuti: “Koma [kudzipereka kwaumulungu, NW] pamodzi ndi kudekha, zipindulitsa kwakukulu.” Yesu Kristu ali kalongosoledwe kokwanira ka kudzipereka kwaumulungu.​—1 Timoteo 3:16.

Liwu la Chigriki lotembenuzidwa “kudzipereka kwaumulungu” liri eu·seʹbei·a. Kwa Akristu kuli “mtundu wapamwamba koposa wa kudzipereka kwa Mulungu.” Kudzipereka kuli “kuwona mtima ndi changu m’kachitidwe ka ntchito za chipembedzo.” Kudzipereka kwaumulungu kuli kuvomereza kwa mtima kumene kudzasonkhezera winawake kukhala m’njira imene imakondweretsa Mulungu. Kumatanthauza kukhala wokhoterera kwa Mulungu. Tiyenera kukhala osamala motani nanga kuti pamene tiri m’dziko, tisakhale mbali yake! Mantha aumulungu adzatichotsa ku kuchita chimene chiri choipa, koma kudzipereka kwaumulungu kumatisonkhezera kuchita chimene chiri chokondweretsa kwa Mulungu. Molimbikitsa, pa 2 Petro 2:9 tikutsimikiziridwa kuti “[Yehova, NW] adziŵa kupulumutsa [odzipereka mwaumulungu, NW] poyesedwa iwo.”

Kuti tipeze kudzipereka kwaumulungu timafunikira kuwona Mulungu ndi Mawu ake mosamalitsa. Kuti achite kudzipereka kwaumulungu, munthu afunikira kudziŵa Mulungu molongosoka ndipo kenaka kuchita mogwirizana ndi chidziŵitsocho. Kumaitanira kukhala wozindikira za zosowa zauzimu. Chifukwa cha kufunika kwa kuchita kwathu kudzipereka kwaumulungu, tifunikira thandizo lonse limene tingapeze mothekera. Misonkhano yathu yachigawo idzachita zochuluka kutipatsa thandizolo. Kupyolera mu nkhani, zisonyezero, ndi kufunsana, tidzaphunzitsidwa mmene tingachitire kudzipereka kwaumulungu m’mbali zonse za miyoyo yathu.

Ife tikufuna kukhala Akristu enieni ndipo mwakutero kuwoneka osiyana ndi dziko. Chotero bwerani ku misonkhanoyi ndi chilakolako chabwino chauzimu. Chipangeni kukhala chonulirapo kupezekapo kaamba ka nyimbo yotsegulira pa Lachisanu m’mawa, ndipo khalanibe kufikira nyimbo ndi pemphero lothera pa Sande madzulo. Sumikani chisamaliro chanu pa pulatiformu ku utali wonse kufikira programu itha. Kanizani chiyeso kapena chikhoterero cha kuchezera ena mkati mwa magawo. Bwerani okonzekera kudzalemba nsonga. Mwa kupereka chisamaliro chabwino ku programu, mudzakhala kuposa ndi kale lonse okonzekera mokwanira kuchita kudzipereka kwaumulungu m’mbali zonse za moyo: m’chomangira cha banja, mu mpingo, ndi kulinga kwa akunja.

Ndandanda ya Malo a Misonkhano ya Chigawo ya 1989 ya “Kudzipereka Kwaumulungu” mu Zambia

August 18-20:

Sesheke, Lundazi, Chipata, Kafue, Mufulira, Luanshya, Kitwe A.

(Buchi), Kitwe B. (Chamboli), Chingola, Solwezi, Manyinga, Chate

August 25-27:

Nyimba, Choma, Nyanje, Ndola A. (Chifubu), Ndola

B. (Mushili), Ndola (English), Mongu, Kaoma, Mumbwa

September 1-3:

Chansa, Kabwe, Mununga, Kazembe, Senga Hill, Kasama, Serenje,

Lusaka A. (Matero), Lusaka B. (Woodlands), Lusaka C. (Chingwere),

Lusaka D. (Chelstone)

September 8-10:

Mansa, Samfya, Mpika, Kalungu, Kapiri Mposhi

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena