Pezekanipo pa Msonkhano Wachigawo wa 1987 wa “Khulupirirani mwa Yehova”
ULI mutu wabwino chotani kaamba ka misonkhano yathu yachigawo ya 1987: ‘‘Khulupirirani mwa Yehova”! Zoonadi kukhulupirira kwathu mwa Yehova kumatipatula ife kuchokera ku dziko. Ena onse amaika chikhulupiriro chawo mu zinthu zonga ngati chuma chawo, nzeru zawo, mphamvu yawo, kapena olamulira awo ndi atsogoleri awo andale ndi achipembedzo. Posachedwapa onse adzafika ku mapeto okhumudwitsa.—Masalmo 146:3, 4.
Kodi kuika chikhulupiriro chathu mwa wina wake kapena mu china chake kumatanthauzanji? Malinga ndi olemba bukhu lopereka matanthauzo a mawu ofanana, “kukhulupirira kumatanthauza kudalira kotheratu ndi kotsimikizirika pa china chake kapena pa wina wake.”a Inde, ndipo imeneyo ndi njira imene ife timamverera ponena za iko. Ife motheratu ndi motsimikizirika timaika chidaliro chathu mwa Yehova.
Kufunika kwa kudalira mwa Yehova kukubweretsedwa ku chidziwitso chathu mobwerezabwereza mu Mawu a Mulungu. Amasalmo mobwerezabwereza akukamba za kukhulupirira kwawo mwa Yehova: “Koma [ine, NW] ndikhulupirira mwa Yehova.” “Koma ine ndakhulupirira Inu, Yehova.” Zokamba zawo zimatikumbutsa ife mawu a mu nyimbo imodzi ya Nyimbo zathu za Ufumu: “Yehova pothawira, tidalira Mulungu wathu amene . . . Yehova ndiye linga, populumukira kwa olungama onse.”—Masalmo 31:6, 14.
Malemba mobwerezabwereza amatilamula ife kuika chikhulupiriro chathu mwa Mulungu: “Khulupirira Yehova ndipo chita chokoma. “Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, osachirikizika pa luntha lako.” (Masalmo 37:3; Miyambo 3:5) Mawu a Mulungu amatiuzanso ife za atumiki okhulupirika a Yehova omwe anafupidwa chifukwa iwo anaika chikhulupiriro chawo mwa iye mkati mwa nthawi za tsoka lalikulu. Pakati pa amenewa anali Mfumu Hezekiya, Ebedi-Meleki, Ahebri atatu, ndi Danieli.—2 Mafumu 18:5; Yeremiya 39:18; Danieli 3:28; 6:23.
Kodi ndi motani mmene timasonyezera kukhulupirira kwathu mwa Yehova? Njira imodzi ndiyo ya kumudziwa iye ndi kumutenga iye pa Mawu ake. Yesu Kristu anatipatsa ife njira yachifupi kwambiri: “Muthange mwafuna Ufumu wake ndi chilungamo chake, ndipo zonse zimenezo zidzawonjezedwa kwa inu.” Inde, ngati tikhulupirira mwa Yehova ndi mtima wathu wonse, tidzaika zikondwerero za Ufumu choyamba mu miyoyo yathu ndi kutsatira njira ya makhalidwe owongoka.—Mateyu 6:33.
Nchifukwa ninji kukhulupirira kwathu mwa Yehova kumafunikira kukhala kolimba? Chifukwa cha zitsenderezo zomwe zimabweretsedwa motsutsana ndi ife kuchokera ku dzanja liri lonse. Kwa ena chiri chizunzo chapoyera, kwa ena kuyesedwa kuchita zoipa. Komabe ena kukhulupirira kwawo kumayesedwa mwa kufunikira kwa kupirira. Msonkhano wathu wachigawo ukudzawo uli pakati pa zithandizo zambiri zimene Yehova wapereka mu masiku ano amapeto.
Chaka chino msonkhano udzakhala wa masiku atatu athunthu, Lachisanu, Loweruka, ndi Sande. Mwakukonzanso utali wa zigawo, programu mu chenicheni idzakhala ndi kuchuluka kwa nkhani monga momwe inaliri chaka chapita. Cholinga chenicheni cha mbali zonse za programu, tingakhale otsimikizira, chidzakhala kulimbikitsa kukhulupirira kwathu mwa Yehova limodzinso ndi mu gulu lake lowoneka ndi maso limene iye akuligwiritsira ntchito pa nthawi ino.
Chotero lolani mboni iri yonse ya Chikristu ya Yehova kutsimikizira kukapezekapo chifupifupi pa umodzi wa misonkhano imeneyi. Bweretsani ana anu. Khalani pafupi kaamba ka nyimbo yotsegulira ndi pemphero lotsegulira Lachisanu m’mawa ndi kukhala kufikira pa nyimbo yotsekera ndi pemphero lotsekera pa Sande masana. Bwerani okonzekera limodzi ndi Baibulo, bukhu la nyimbo, kabukhu kolembamo nsonga, ndi pensulo. Lowani osagawanika mu mzimu wa zomwe ziri kuperekedwa, kuphatikizapo nyimbo ndi mapemphero. Perekani chisamaliro cheni cheni ku zimene zikuperekedwa. Ndipo tiyeni ife titsimikizire kuti pa nthawi zonse kapesedwe kathu ndi khalidwe lathu zikhale zovomerezeka.
Prinsipulo la Malemba ‘fesani moolowa manja, tutani moolowa manja,’ limagwira ntchito ku kupezekako kwathu pa Msonkhano Wachigawo wa “Khulupirirani mwa Yehova”. Ngati tiri ofunitsitsa kwambiri kutenga programu yonse, tidzatenga madalitso ochulukira kuchokera pa msonkhano, ndipo tidzakhala madalitso okulira kwa ena.—2 Akorinto 9:6.
a Webster’s New Dictionary of Synonyms