Misonkhano Yachigawo ya “Chilungamo Chaumulungu”
NDI kuvutika kokulira chotani nanga kumene kulipo m’dziko chifukwa cha kusoweka kwa chilungamo! Kugwiritsira ntchito molakwika kwa mphamvu kofala kumbali ya atsogoleri ena andale kwatulukamo m’kuvutika kopanda chilungamo. Zikondwerero zadyera za chuma zimatsendereza anthu, kutulukapo m’kuvutika kwambiri. Kenaka pali chitsenderezo cha atsogoleri a chipembedzo lerolino omwe ali monga ofanana ndi anzawo a m’tsiku la Yesu, ndipo za amene iye ananena kuti: “Amanga katundu wolemera ndi wosautsa ponyamula, nawasenza pa mapewa a anthu; koma iwo eni okha safuna kuwasuntha amenewo ndi chala chawo.” (Mateyu 23:4) Pali kugwiritsira ntchito mphamvu molakwika kochuluka ndi kutulukapo kwa kupanda chilungamo mkati mwa banja.
Mbiri yakale imasonyeza kuti chidzakhala chopanda phindu kuyang’ana kwa anthu opanda ungwiro, mosasamala kanthu kuti iwo angakhale owona mtima motani, kulungamitsa zinthu zoterozo. Koma alipo kumwamba wokhalako Wamkulukulu ndi Woweruza, Yehova. Iye ali Mulungu wa chilungamo. Moyenerera, Mose analemba kuti: “Thanthwe, ntchito yake ndi yangwiro, pakuti njira zake zonse ndi chilungamo. Mulungu wokhulupirika ndi wopanda chisalungamo; iye ndiye wolungama ndi wolunjika.”—Deuteronomo 32:4, NW.
Yehova walekerera kwa nthaŵi yaitali kupanda chilungamo kwa dzikoli, koma iye sadzachita tero kwa nthaŵi zonse. Pali nthaŵi yoikika kaamba ka iye kuchitapo kanthu ndipo kenaka ulosi wopezeka pa Yesaya 14:4-7 udzakwaniritsidwa, womwe umalonjeza kuti mtundu wonse wa nkhalwe udzasiya ndipo ‘dziko lonse lapansi lidzakhala m’mpumulo.’
Chifukwa cha chikhulupiriro chawo cholimba m’malonjezo a ulosi amenewa, Mboni za Yehova zimasangalala kulengeza kutali ndi mofalikira kuti posachedwapa Yehova adzabweretsa kumapeto zitsenderezo zonse, kusawongoka, ndi kupanda chilungamo mwa kubweretsamo ulamuliro wotheratu wa Ufumu. Kenaka palibe wina aliyense adzavulaza kapena kusakaza, popeza ‘dziko lonse lapansi lidzadzala ndi odziŵa Yehova, monga madzi adzaza nyanja.’—Yesaya 11:9.
Kuti tilimbikitse chikhulupiriro chathu mwa ziweruzo zolungama za Yehova, misonkhano yachigawo ya 1988 idzakhala ndi mutu wakuti “Chilungamo Chaumulungu.” Kugogomezera mutu umenewo sikudzatisonkhezera ife kokha m’kudziŵikitsa chiyembekezo chathu kaamba ka chilungamo chaumulungu komanso kudzatilimbikitsa ife kuchita m’chigwirizano ndi chilungamo chaumulungu m’zochita zathu zonse.
Monga atumiki a Yehova, tonsefe tikudziŵa kuti chifukwa cha kulakwa kwa makolo athu oyambirira, zikhoterero zathu ziri kulinga ku dyera, kulinga ku kupanda chilungamo. Chotero tidzayamikira chidziŵitso choyenera chomwe tidzalandira kupyolera mwa nkhani za Baibulo, zisonyezero, kufunsidwa, ndi zitsanzo zomwe zidzamveketsa chifuno cha kusungirira chilungamo chaumulungu. Ichi chiri m’chigwirizano ndi lamulo la pa Mika 6:8, ‘kuchita cholungama ndi kukonda chifundo ndi kuyenda modzichepetsa ndi Mulungu wathu.’ Ichi chimatheketsa kugwirizana, kukhutiritsidwa, ndi chimwemwe; chimathandizanso kuwonjezera kulalikira mbiri yabwino kudziko lonse lapansi.
Mbali yowonekera kwambiri ya misonkhano imeneyi idzakhala ija yakuti chiŵerengero cha mizinda ingapo idzalumikizidwa pa lamya kaamba ka nkhani zapadera zoperekedwa ndi ziwalo za Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova. Ndiponso kaamba ka misonkhano imeneyi amishonale kuzungulira dziko lonse lapansi adzapatsidwa zoyendera kaamba ka iwo ichi chidzawatheketsa iwo kuchezera mabanja awo kachiŵirinso.
Ngati Yehova alola, Misonkhano ya Chigawo ya “Chilungamo Chaumulungu” idzayamba pa Lachinayi pa 1:30 p.m. ndi kutha pa 4:00 p.m. pa Sande. Lolani kuti tikonze zochita zathu kudzakhalapo pamene programu idzayamba ndi kukonzekera kukhala kufikira nyimbo yomaliza ndi pemphero lothera tsiku lirilonse. Idzani ndi chilakolako chabwino chauzimu ndipo okonzekera kulemba nsonga. Khalani otsimikiziridwa kuti Yehova watisungira “phwando” la zinthu zabwino lomwe lidzalimbikitsa ndi kutitsitsimula ife kaamba ka ntchito yomwe iri kutsogolo.—Yesaya 25:6; Nyimbo ya Solomo 2:4.
Inde, lolani aliyense abwere wogamulapo kudzatenga dalitso lokulira lauzimu monga momwe kungathekere kuchokera ku Msonkhano wa Chigawo wa “Chilungamo Chaumulungu.”
Ndandanda ya Malo a Misonkhano ya Chigawo ya 1988 ya “Chilungamo Chaumulungu” mu Zambia
August 18-21: Sesheke, Lundazi, Chipata, Kafue, Mufulira, Luanshya, Kitwe (A), Kitwe (B), Chingola, Solwezi, Manyinga
August 25-28: Choma, Nyanje, Lusaka (A), Lusaka (B), Lusaka (C), Lusaka (English), Ndola (A), Ndola (B), Mongu, Kaoma, Mumbwa
September 1-4: Kabwe, Mununga, Kazembe, Senga Hill, Kasama, Serenje
September 8-11: Mansa, Samfya, Mpika, Kalungu, Kapiri Mposhi