Tikulandirani ku Misonkhano Yachigawo ya “Onyamula Kuunika”
PATSIKU loyamba lenileni la masiku akulenga panalengedwa kuunika kwa padziko lapansi. Timaŵerenga kuti Yehova Mulungu anati: “Kukhale kuunika.” Ndipo “pamenepo kuunika kunakhalako.” (Genesis 1:3, NW) Zimenezi zimagwirizana ndi zimene mtumwi Yohane analemba kuti: “Mulungu ndiye kuunika, ndipo mwa Iye monse mulibe mdima.”—1 Yohane 1:5.
Popeza kuti Mwana wa Mulungu ngwogwirizana ndi Atate ŵake, nkosadabwitsa kuti Yesu nthaŵi ina anati: “Ndiri kuunika kwa dziko lapansi.” (Yohane 9:5) Ifeyo tikhoza kutuluka mumdima ndi kuloŵa kuunika mwakuika chikhulupiriro mwa Yehova Mulungu ndi Mwana wake. Yesu ananenanso kuti: “Ndadza Ine kuunika ku dziko lapansi, kuti yense wokhulupirira ine asakhale mumdima.” (Yohane 12:46) Moyenerera, Yesu Kristu anati ponena za otsatira ake owona: ‘Inu ndinu kuunika kwa dziko lapansi. . . . Chomwecho muŵalitse inu kuunika kwanu pamaso pa anthu, kuti pakuwona ntchito zanu zabwino, alemekeze Atate wanu wakumwamba.’—Mateyu 5:14, 16.
Ndidalitso lotani nanga kukhala ndi chowonadi, chidziŵitso cha Mawu a Mulungu omveketsedwa bwino ndi “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru”! (Mateyu 24:45-47) Sitimasokonezedwanso ndi chikhulupiriro cha Utatu; sitimadabwanso ndi chifukwa chimene Mulungu wachikondi ndi wamphamvuyonse walolera kuipa ndi chiwawa; sitimakaikiranso mkhalidwe wa akufa. Kuunika kwatipatsa chiyembekezo, chiyembekezo cha Ufumu. Kwativumbulira mmene Mlengi aliri Mulungu wabwino kwambiri. Kuunika kwa chowonadi kwatipatsa cholinga m’moyo, kuchita chifuno chimene tinalengedwera, kulemekeza Wotipanga, Yehova Mulungu. Timachita zimenezi mwakukhala onyamula kuunika. Kukhala onyamula kuunika ndiko ulemu waukulu ndi mwaŵi, koma kulinso thayo lalikulu. Kuti tiikwaniritse ntchitoyo, tifunikira kugwiritsira ntchito chithandizo chonse choperekedwa ndi Yehova. Choncho nkoyenerera chotani nanga kuti misonkhano yathu yachigawo ya 1992 itchedwe Misonkhano Yachigawo ya “Onyamula Kuunika”!
Kuti tiwongolere maluso athu ndi chiyamikiro kaamba ka ntchito yathu monga onyamula kuunika, tidzafunikira kupezekako kumsonkhano umodzi wa imeneyi, kupezekapo panyimbo yoyamba ndi kukhalapo mpaka pemphero lothera. Ndipo tidzafunikira kutchera khutu ku zonse zimene zidzakambidwa papulatifomu, zikhale nkhani, mbali zakufunsa, zokumana nazo, kapena drama. Kulemba manotsi sikumangotitheketsa kukhala ndi kanthu kotikumbutsa kamene tingalozeko pambuyo pake komanso kumatithandiza kwambiri kusumika maganizo pazimene zikukambidwa. Inde, tonsefe tidzafunikira ‘kuyang’anira mamvedwe athu’ paprogramu ya msonkhanowo.—Luka 8:18.