Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w95 4/15 tsamba 2-6
  • Kodi Choonadi cha Chipembedzo Chingapezeke?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Choonadi cha Chipembedzo Chingapezeke?
  • Nsanja ya Olonda—1995
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Filosofi ndi Choonadi
  • Kodi Vumbulutso la Choonadi Likufunika?
  • Chipembedzo ndi Choonadi
  • ‘Tirigu ndi Namsongole’
  • Akristu Amalambira Mumzimu ndi M’choonadi
    Nsanja ya Olonda—2002
  • Kodi Nkufuniranji Choonadi?
    Nsanja ya Olonda—1995
  • Kutsanzira Mulungu wa Choonadi
    Nsanja ya Olonda—2003
  • “Choonadi Chidzakumasulani”
    Nsanja ya Olonda—1998
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1995
w95 4/15 tsamba 2-6

Kodi Choonadi cha Chipembedzo Chingapezeke?

MU Sweden mwamuna wina wofunitsitsa kudziŵa zachipembedzo wa mu mzinda wa Uppsala mmene muli yunivesite, anaganiza za kupenda zikhulupiriro za zipembedzo zosiyanasiyana za mu mzinda wake, ndipo anafikadi pamalo awo olambirira. Iye anamvetsera pamene atsogoleri awo achipembedzo anali kuphunzitsa, ndipo anafunsira kwa ziŵalo zina. Koma anaona kuti Mboni za Yehova zokha ndi zimene zinaoneka kukhala zokhutira kuti “zinapeza choonadi.” Poganiza za malingaliro osiyanasiyana a zipembedzo omwe alipo, iye anazizwa chimene chinachititsa Mboni kunena zimenezo.

Kodi inuyo mukuganiza kuti nkotheka kupeza choonadi cha chipembedzo? Kodi nkotheka ngakhale kudziŵa chabe chimene chingatchedwe choonadi chenicheni?

Filosofi ndi Choonadi

Amene amaphunzira filosofi akhala ndi lingaliro lakuti choonadi chenicheni sichingapezeke mwa kufunafuna kwa anthu. Mwina mukudziŵa kuti filosofi yatanthauziridwa kukhala “sayansi imene imayesa kulongosola chiyambi cha kukhalapo ndi moyo.” Komabe, choonadi nchakuti ndi mwakamodzikamodzi chabe pamene iyo yafika pamenepo. M’buku lakuti Filosofins Historia (Mbiri ya Filosofi), mlembi wa ku Sweden Alf Ahlberg analemba kuti: “Mafunso ambiri a filosofi ali a mtundu wakuti nkovuta kupereka mayankho ake otsimikizirika. . . . Anthu ambiri ali ndi lingaliro lakuti mafunso onse onena za filosofi ya chilengedwe [ya malamulo oyambirira a zinthu] ali a mtundu . . . umenewu.”

Chifukwa chake, amene amayesa kupeza mayankho m’filosofi pa mafunso ofunika a moyo kaŵirikaŵiri akhala osakhutira kapena kugwiritsidwa mwala. M’buku lake lakuti Tankelinjer och trosformer (Kalingaliridwe ndi Chikhulupiriro cha Chipembedzo), mlembi wa ku Sweden Gunnar Aspelin anati: “Chimene timaona nchakuti chilengedwe sichimakondweranso ndi munthu koma ndi gulugufe ndi udzudzu . . . Tili opanda mphamvu, tilibiretu mpang’ono pomwe, kwa zimphamvu zimene zimachita ntchito zake kuthambo ndi m’dziko lathu. Aka ndiko kapenyedwe ka moyo kamene kaoneka kaŵirikaŵiri m’mabuku chakumapeto kwa zaka za zana limene anthu aika chikhulupiriro pa kupita patsogolo nalota mtsogolo mwabwinopo.”

Kodi Vumbulutso la Choonadi Likufunika?

Nkoonekeratu kuti anthu pa okha alephera kupeza choonadi chonena za moyo, ndipo kukuoneka kuti sadzatero konse. Motero, pali chifukwa chomveka choganizira kuti vumbulutso laumulungu nlofunika. Chimene ambiri amatcha buku la chilengedwe chili ndi vumbulutso limenelo. Ngakhale kuti icho sichimalongosola zonse ponena za chiyambi cha moyo, chimasonyeza kuti pali malongosoledwe ena okhutiritsa kwambiri kuposa a zinthu zoonedwa. Udzu umene umakula umatsatira malamulo osiyana ndi aja amene amachitisa miyala kugwa m’dzenje limene likugumuka. Zinthu zamoyo m’chilengedwe zimakula ndi kulinganizika m’njira imene zopanda moyo sizingakhoze. Motero, wophunzira malamulo ndi chipembedzo wina wotchuka anali ndi chifukwa chonenera kuti: “Pakuti chilengedwere dziko lapansi zaoneka bwino zosaoneka zake [za Mulungu] . . . popeza zazindikirika ndi zinthu zolengedwa.”​—Aroma 1:20.

Koma kuti tidziŵe amene amatheketsa makulidwe ndi kulinganizika konseku, tifunikira vumbulutso linanso. Kodi sitiyenera kuganiza kuti vumbulutso loterolo lilipo? Kodi sikukakhala kwanzeru kuganiza kuti Iye amene anapanga zamoyo za padziko lapansi ayenera kudzidziŵikitsa mwini kwa zolengedwa zake?

Baibulo limanena kuti ilo ndilo vumbulutso limenelo. M’magazini ano kaŵirikaŵiri tapereka zifukwa zomveka zokhulupirira mawu amenewo, ndipo anthu oganiza ambiri atero. Kufunitsitsa kwa olemba Baibulo kwa kumveketsa bwino lomwe kuti zimene analemba sizinali zochokera kwa iwo kuli kokondweretsa. Timapeza kuti aneneri a Baibulo anagwiritsira ntchito mawu akuti, “Atero Yehova,” kwa nthaŵi zoposa 300. (Yesaya 37:33; Yeremiya 2:2; Nahumu 1:12) Mwinamwake mukudziŵa kuti amuna ndi akazi amene amalemba mabuku kapena nkhani kaŵirikaŵiri amafuna kwambiri kuikapo dzina lawo. Komabe, amene analemba Baibulo sanadzidziŵitse; nthaŵi zina kumakhala kovuta kudziŵa amene analemba mbali zina za Baibulo.

Mbali ina ya Baibulo imene mungaione kukhala yofunika ndiyo kugwirizana kwa nkhani zake. Zimenezi nzodabwitsadi, poona kuti mabuku 66 a Baibulo analembedwa pa nyengo ya zaka 1,600. Tinene kuti mwapita ku laibulale ya onse ndi kusankha mabuku achipembedzo 66 amene analembedwa kwa nyengo ya zaka mazana 16. Ndiyeno musonkhanitsa pamodzi mabukuwo kupanga buku limodzi. Kodi mungayembekezere bukulo kukhala ndi mutu wankhani umodzi ndi uthenga wogwirizana? Kutalitali. Zimenezo zikafuna chozizwitsa. Talingalirani izi: Mabuku a Baibulo ali ndi mutu wankhani umodzi, ndipo amagwirizana. Izi zimasonyeza kuti payenera kukhala wina wolinganiza, kapena woyambitsa, amene anatsogolera zimene alembi a Baibulo analemba.

Komabe, mudzapeza chinthu china chimene chimatsimikizira kuposa china chilichonse kuti Baibulo nlochokera kwa Mulungu. Maulosi​—chidziŵitso cholembedwa pasadakhale chonena za zimene zikachitikadi mtsogolo. Mawu onga akuti, “padzakhala tsiku lomwelo” ndi akuti, “padzakhala masiku otsiriza” amapezeka m’Baibulo mokha. (Yesaya 2:2; 11:10, 11; 23:15; Ezekieli 38:18; Hoseya 2:21-23; Zekariya 13:2-4) Zaka mazana ambiri Yesu Kristu asanaonekere padziko lapansi, maulosi a m’Malemba Achihebri analongosola za moyo wake​—kuyambira kubadwa kwake mpaka imfa yake. Palibe lingaliro lanzeru lina limene tingapeze loposa lakuti Baibulo ndilo magwero a choonadi chonena za moyo. Yesu mwiniyo akutsimikizira zimenezi ndi mawu akuti: “Mawu anu ndi choonadi.”​—Yohane 17:17.

Chipembedzo ndi Choonadi

Ngakhale ambiri amene amati amakhulupirira Baibulo amakhulupirira kuti choonadi chenicheni sichikhoza kupezeka. Mtsogoleri wachipembedzo wa ku United States John S. Spong anathirira ndemanga kuti: “Tiyenera . . . kuleka kulingalira kuti tili ndi choonadi ndi kuti ena ayenera kuvomereza lingaliro lathulo, koma tizindikire kuti tonsefe sititha kuchidziŵa choonadi chenicheni.” Mlembi wa Roma Katolika, Christopher Derrick, akupereka chimodzi cha zifukwa zochititsa malingaliro amenewo otsutsa kupezeka kwa choonadi: “Kutchula ‘choonadi’ cha chipembedzo kulikonse kumatanthauza kusonyeza kudziŵa . . . Mumatanthauza kuti winawake angakhale wolakwa; ndipo zimenezo nzosatheka konse.”

Komabe, monga munthu woganiza, mungachite bwino kupenda mafunso ofunikira. Ngati choonadi chili chosapezeka, kodi nchifukwa ninji Yesu Kristu ananena kuti: “Mudzazindikira choonadi, ndipo choonadi chidzakumasulani”? Ndipo kodi mmodzi wa atumwi a Yesu ananeneranji kuti chifuniro cha Mulungu ndicho chakuti “anthu onse apulumuke, nafike pozindikira choonadi”? Kodi nchifukwa ninji liwu lakuti “choonadi” likupezeka kwa nthaŵi zoposa zana limodzi m’Malemba Achigiriki Achikristu ponena za chikhulupiriro? Inde, nchifukwa ninji ziri choncho, ngati choonadi chili chosapezeka?​—Yohane 8:32; 1 Timoteo 2:3, 4.

Kwenikweni, Yesu sanangotchula kuti choonadi chikhoza kupezeka komanso anasonyeza kuti kuchipeza nkofunika ngati tifuna kuti kulambira kwathu kulandiridwe ndi Mulungu. Pamene mkazi Wachisamariya anafuna kudziŵa chimene chinali kulambira koona​—kulambira kochitidwa ndi Ayuda ku Yerusalemu kapena kochitidwa ndi Asamariya m’phiri la Gerizimu​—Yesu sanayankhe kuti choonadi chinali chosapezeka. M’malo mwake, anati: “Olambira oona adzalambira Atate mumzimu ndi m’choonadi; pakuti Atate afuna otere akhale olambira ake. Mulungu ndiye mzimu; ndipo omlambira iye ayenera kumlambira mumzimu ndi m’choonadi.”​—Yohane 4:23, 24.

Anthu ambiri amati, ‘Baibulo lingamasuliridwe m’njira zosiyanasiyana, motero munthu sangakhale wotsimikiza za chimene chili choonadi.’ Koma kodi Baibulo linalembedwadi m’njira yotero yosamveka bwino kwakuti munthu sangatsimikizire mmene ayenera kulimvetsa? Inde, mawu ena aulosi ndi maphiphiritso ngovuta kumva. Mwachitsanzo, Mulungu anauza mneneri Danieli kuti buku lake, lokhala ndi malankhulidwe ambiri aulosi, silikamveka mokwanira kufikira “nthaŵi ya chitsiriziro.” (Danieli 12:9) Ndipo nkoonekeratu kuti mafanizo ena ndi zizindikiro zimafuna kumasulira.

Komabe, nkoonekeratunso kuti ponena za ziphunzitso zoyambirira za Chikristu ndi makhalidwe abwino ofunika pa kulambira Mulungu m’choonadi, Baibulo silipita m’mbali. Silimachititsa mamasuliridwe owombana. M’kalata yolembedwa kwa Aefeso, chikhulupiriro cha Chikristu chimanenedwa kukhala “chimodzi,” kusonyeza kuti sipanayenera kukhala zikhulupiriro zambiri. (Aefeso 4:4-6) Mwinamwake mungadabwe kuti, ‘Ngati sikuli koyenera kumasulira Baibulo m’njira zambiri zosiyanasiyana, nchifukwa ninji pali zipembedzo zambirimbiri za “Chikristu”?’ Timapeza yankho ngati tiyang’ana kumbuyo patapita nthaŵi pang’ono pambuyo pa imfa ya atumwi a Yesu ndi pamene mpatuko pa chikhulupiriro choona cha Chikristu unabuka.

‘Tirigu ndi Namsongole’

Yesu ananeneratu za mpatuko umenewu m’fanizo lake la tirigu ndi namsongole. Yesu mwiniyo analongosola kuti “tirigu” amaimira Akristu oona; “namsongole” amaimira Akristu onyenga, kapena ampatuko. “Mmene anthu analikugona,” anatero Yesu, “mdani” akafesa namsongole m’munda wa tirigu. Kufesa kumeneku kunayamba pambuyo pa kugona mu imfa kwa atumwi. Fanizolo limasonyeza kuti kusokonekera kumeneku pakati pa Akristu oona ndi onyenga kukapitiriza kufikira “chimaliziro cha nthaŵi ya pansi pano.” Chifukwa chake, m’zaka mazana onsewo, Chikristu choona chaphimbika chifukwa chakuti malo achipembedzo adzazidwa ndi Akristu a dzina lokha. Komabe, pa “chimaliziro cha nthaŵi ya pansi pano,” padzakhala kusintha. “Mwana wa munthu adzatuma angelo ake” kuti adzalekanitse Akristu onyenga ndi Akristu oona. Izi zinatanthauza kuti tsopano mpingo Wachikristu ukadziŵika mosavuta, pokhala ndi mkhalidwe umene unalipo m’nthaŵi ya atumwi.​—Mateyu 13:24-30, 36-43.

Maulosi onse aŵiri, wa Yesaya ndi wa Mika amaneneratu za kusonkhanitsa alambiri oona kumeneko mu “masiku otsiriza.” Yesaya amati: “Ndipo padzakhala masiku otsiriza, kuti phiri la nyumba ya Yehova lidzakhazikika pa nsonga ya mapiri, ndipo lidzakwezedwa pamwamba pa zitunda; mitundu yonse idzasonkhana kumeneko. Ndipo anthu ambiri adzamka, nati, Tiyeni tikwere kumka ku phiri la Yehova, ku nyumba ya Mulungu wa Yakobo; ndipo iye adzatiphunzitsa za njira zake, ndipo tidzayenda m’mayendedwe ake.” Kuyang’anitsitsa zochitika kumasonyeza kuti ulosi wa Yesaya ukukwaniritsidwa m’nthaŵi yathu.​—Yesaya 2:2, 3; Mika 4:1-3.

Komabe, kukula kwa mpingo Wachikristu sikukuchitidwa ndi mphamvu yaumunthu. Yesu ananeneratu kuti “adzatumiza angelo ake” kudzachita ntchito yosonkhanitsa. Iye anasonyezanso chifuno chapadera kwambiri chochitira zimenezo: “Pomwepo olungamawo adzaŵalitsa monga dzuŵa, mu ufumu wa Atate wawo.” (Mateyu 13:43) Izi zikusonyeza kuti ntchito yotsegula maso, kapena yophunzitsa ikachitidwa padziko lonse ndi mpingo Wachikristu.

Mboni za Yehova zikuona kukwaniritsidwa kwa maulosi onseŵa m’ntchito yophunzitsa imene zikuchita m’maiko 232 lerolino. Poyerekezera, zikhulupiriro za Mboni, miyezo ya khalidwe, ndi kakonzedwe kawo malinga ndi zimene Baibulo limanena, anthu osasinjirira angaone bwino lomwe kuti zinthu zimenezi nzofanana ndi zija za mpingo Wachikristu wa m’zaka za zana loyamba. Mboni zimanena kuti chikhulupiriro chawo ndicho “choonadi” koma osati mwakungolingalira modzikweza. M’malo mwake, izo zimatero chifukwa chakuti zaphunzira mozama Mawu a Mulungu, Baibulo, ndipo zimalitsatira monga muyeso wokha woyeserapo chipembedzo.

Akristu oyambirira anati chikhulupiriro chawo chinali “choonadi.” (1 Timoteo 3:15; 2 Petro 2:2; 2 Yohane 1) Chimene chinali choonadi kwa iwo chiyenera kukhalanso choonadi kwa ife lerolino. Mboni za Yehova zikupempha aliyense kudzionera yekha zimenezo mwa kuphunzira Baibulo. Tikhulupirira kuti mwa kuchita zimenezo nanunso mudzapeza chisangalalo chimene chimadza si kokha ndi kupeza chipembedzo chimene chimapambana zinazo komanso chimadza ndi kupeza choonadi!

[Bokosi patsamba 5]

MAFILOSOFI ENA OTSUTSANA NDI CHOONADI

POSITIVISM: Lingaliro lakuti malingaliro onse a zachipembedzo ali osatsimikizirika ndi opanda pake ndi kuti cholinga cha filosofi ndicho kugwirizanitsa masayansi abwino kuti akhale chinthu chimodzi.

EXISTENTIALISM: Ochirikiza ake anasonkhezeredwa kwambiri ndi mantha a Nkhondo Yadziko II ndipo motero anadzakhala ndi lingaliro la kusumika maganizo pa zoipa za moyo. Imagogomezera kupenda nsautso ya munthu poyang’anizana ndi imfa ndi kupanda pake kwa moyo. Mlembi wochirikiza existentialism Jean-Paul Sartre ananena kuti, popeza kuti kulibe Mulungu, munthu ali payekha ndipo akukhala m’chilengedwe chosasamala za munthu.

SKEPTICISM: Imaphunzitsa kuti nkosatheka kupeza chidziŵitso chenicheni​—choonadi chilichonse​—ponena za kukhalako, mwa kupenda zinthu ndi kulingalira.

PRAGMATISM: Imaona choonadi kukhala chinthu chimene chimatikhutiritsa, makamaka chifukwa cha phindu la chinthucho pa zofuna munthu, monga ngati kuwongolera maphunziro, makhalidwe, ndi ndale. Siimaona kuti choonadi chili ndi phindu lililonse mwa icho chokha.

[Mawu a Chithunzi patsamba 2]

Page 3: Second from left: Courtesy of The British Museum; Right: Sung Kyun Kwan University, Seoul, Korea

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena