Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w95 7/1 tsamba 31
  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
  • Nsanja ya Olonda—1995
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Ndi Ndani Akutsogolera Anthu a Mulungu Masiku Ano?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2017
  • Kodi Bungwe Lolamulira Limagwira Ntchito Bwanji Masiku Ano?
    Kodi Ndani Akuchita Chifuniro cha Yehova Masiku Ano?
  • Kugwirizana ndi Bungwe Lolamulira Lerolino
    Nsanja ya Olonda​—1990
  • Kodi “Kapolo Wokhulupirika Komanso Wanzeru” Ndi Ndani, Nanga Amachita Zotani?
    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1995
w95 7/1 tsamba 31

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Kodi Mulungu anali kuchita tsankhu posankha amuna a m’bungwe lolamulira loyambirira amene anali a fuko ndi mtundu wofanana​—onse akumakhala Ayuda?

Ayi, sanali kuchita tsankhu konse. Onse amene Yesu anayamba kuitana kukhala ophunzira ake anali Ayuda. Ndiyeno, pa Pentekoste wa 33 C. E., Ayuda ndi otembenuzidwira ku Chiyuda anali oyamba kudzozedwa ndi mzimu woyera kukhala pa mzera wa kulamulira ndi Kristu kumwamba. Panali pambuyo pake pamene Asamariya ndi Akunja osadulidwa anaphatikizidwa. Chifukwa chake, nzomveka kuti bungwe lolamulira panthaŵiyo linapangidwa ndi Ayuda, “atumwi ndi akulu [ku Yerusalemu],” otchulidwa pa Machitidwe 15:2. Ameneŵa anali amuna amene anali ndi maziko akuya a chidziŵitso cha Malemba ndi okhala ndi nzeru kwa zaka zambiri pa kulambira koona, ndipo anali atakhala ndi nthaŵi yochuluka ya kukhala akulu Achikristu okhwima maganizo.​—Yerekezerani ndi Aroma 3:1, 2.

Pofika nthaŵi ya msonkhano wa bungwe lolamulira wosimbidwa m’Machitidwe chaputala 15 umenewo, Akunja ambiri anakhala Akristu. Ameneŵa anaphatikizapo Aafirika, Azungu, ndi anthu akumadera ena. Komabe, palibe cholembedwa chilichonse chosonyeza kuti Akunja otero alionse anawonjezedwa pa bungwe lolamulira kuti Chikristu chikhale chokopa kwa osakhala Ayuda. Pamene kuli kwakuti Akristu Akunja otembenuka chatsopano ameneŵa anali ziŵalo zolingana za “Israyeli wa Mulungu,” ayenera kuti analemekeza kukhwima maganizo ndi chidziŵitso chachikulu cha Akristu Achiyuda, monga ngati atumwi, amene anali mbali ya bungwe lolamulira kalelo. (Agalatiya 6:16) Onani pa Machitidwe 1:21, 22 mmene chidziŵitso chimenecho chinalemekezedwera.​—Ahebri 2:3; 2 Petro 1:18; 1 Yohane 1:1-3.

Kwa zaka mazana ambiri Mulungu anachita mwa njira yapadera ndi mtundu wa Israyeli, umene Yesu anasankhamo atumwi ake. Sikunali kuphonya kapena chisalungamo kuti palibe atumwi amene anachokera kumene tsopano timatcha South America kapena Afirika kapena Far East. M’kupita kwa nthaŵi amuna ndi akazi akumalowo anali kudzakhala ndi mpata wa kulandira mwaŵi waukulu kuposa kukhala mtumwi pa dziko lapansi, kukhala wa bungwe lolamulira la m’zaka za zana loyamba, kapena kuikidwa pa thayo lina lililonse pakati pa anthu a Mulungu lerolino.​—Agalatiya 3:27-29.

Mtumwi wina anasonkhezeredwa kunena kuti “Mulungu alibe tsankhu; koma m’mitundu yonse, wakumuwopa iye ndi wakuchita chilungamo alandiridwa naye.” (Machitidwe 10:34, 35) Inde, mapindu a dipo la Kristu alipo kaamba ka onse, popanda tsankhu. Ndipo anthu ochokera mu fuko ndi manenedwe ndi mtundu uliwonse adzaphatikizidwa mu Ufumu wakumwamba ndi m’khamu lalikulu limene lidzakhala kosatha pa dziko lapansi.

Anthu ambiri amaganiza kwambiri za kusiyana kwa mafuko, zinenero, ndi mitundu. Zimenezi zikusonyezedwa ndi zimene timaŵerenga pa Machitidwe 6:1 ponena za nkhani imene inachititsa kudandaula pakati pa Akristu olankhula Chigiriki ndi aja olankhula Chihebri. Mwinamwake tingakhale titakula ndi mkhalidwe kapena kutengera mkhalidwe wamakono wosakonda chinenero china, fuko, mtundu, kapena miyambo. Popeza kuti zimenezo zikhozadi kuchitika, tingachite bwino kupanga kuyesayesa kwamphamvu kuumba malingaliro athu ndi zochita mogwirizana ndi lingaliro la Mulungu, lakuti anthu onse ali olingana kwa iye, mosasamala kanthu za maonekedwe athu akunja. Pamene Mulungu anachititsa ziyeneretso za akulu ndi atumiki otumikira kulembedwa, iye sanatchule fuko kapena mtundu ayi. Iye anasumika maganizo pa ziyeneretso zauzimu za awo amene angadzipereke kutumikira. Zimenezo zili choncho kwa akulu akumaloko, oyang’anira oyendayenda, ndi oyang’anira nthambi lerolino, monga momwe zinalili ndi bungwe lolamulira m’zaka za zana loyamba.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena