Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w95 8/15 tsamba 3-4
  • Kodi Mungakhale ndi Moyo Motani m’Malo Owopsa?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mungakhale ndi Moyo Motani m’Malo Owopsa?
  • Nsanja ya Olonda—1995
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kusunga Mkhalidwe Wabwino
  • Kulimbana ndi Upandu Kukulephereka
    Galamukani!—1998
  • Pamene Kunalibe Upandu
    Galamukani!—1998
  • N’chifukwa Chiyani Anthu Ambiri Amakhala Mwamantha?
    Galamukani!—2005
  • Kuyesayesa Kuthetsa Upandu
    Galamukani!—1996
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1995
w95 8/15 tsamba 3-4

Kodi Mungakhale ndi Moyo Motani m’Malo Owopsa?

“NDINALI ndi mantha nthaŵi zonse. Ndinali kuwopa m’chikepi. Ndinali kuwopa m’galimoto langa. Ndinali kuwopa m’nyumba mwanga. Paliponse panali upandu. Nthaŵi zonse anthu anali kuberedwa,” akutero Maria. Kodi mumamva monga mkazi wa ku Brazil ameneyu, kuwopa m’malo amene mumakhala, makamaka mu mdima wa usiku?

Kuŵerenga nkhani za matekitivi kungakhale kosangalatsa, koma ngati zichitikadi kaŵirikaŵiri sizimatha bwino. Upandu wina sungathetsedwe. Kapena munthu wina ataphedwa, munthu wina amakhala wopanda mwamuna wake, atate, kapena mwana wamwamuna, wopanda mkazi, amayi, kapena mwana wamkazi. Kodi chiwawa chikuwonjezereka m’dera lanu? Kodi mumakhumba malo abata kumene banja lanu lingakhale lotetezereka? Kapena ngati muumirizika kulera ana anu m’dera lodzala ndi upandu, kodi mungachitenji kuti mupitirize kukhala ndi moyo?

Zoona, pakali mizinda mmene upandu uli wochepa. M’maiko ambiri, anthu akukhalabe kumadera akumidzi a bata. Koma zinthu zikusintha mofulumira ngakhale m’madera amene kale analingaliridwa kukhala opanda upandu. Mwachitsanzo, ku Brazil zaka 50 zapitazo, 70 peresenti ya chiŵerengero chake cha anthu anali kukhala kumidzi. Tsopano 70 peresenti amakhala m’mizinda. Mavuto a m’mizinda, onga ngati upandu ndi chiwawa, adza pamodzi ndi kusoŵa kwa ntchito. Kaya mukukhala m’dera lowopsa kapena ayi, inu mufunikirabe kupita kuntchito kapena kusukulu ndi kuchita zinthu zina zambiri muli kwina.

Povomereza “mkhalidwe wamantha” umene ulipo, mkulu wina wa polisi ku Rio de Janeiro akutchula za kupanda chilungamo kwa anthu ndi magulu aupandu kukhala zochititsa zake. Iye akulingaliranso kuti manyuzipepala ndi wailesi yakanema zimawanditsa mantha kwa anthu onse, “zikumalefulitsa mitima ya anthu ndi nkhani zatsoka.” Kumwerekera ndi anamgoneka, kusweka kwa mabanja, ndi maphunziro olakwika a chipembedzo zimachititsanso kuwonjezereka kwa kusaweruzika. Ndipo kodi mtsogolo muzadzetsanji? Kodi zochitika zachiwawa zosatha, zosonyezedwa m’mabuku ndi m’mafilimu monga zosangulutsa chabe, zidzachititsa anthu kukhala ouma mtima kwa ena? Kodi mbali zimene zimalingaliridwa kukhala zopanda upandu nazonso zidzakhala zowopsa?

Popeza kuti chiwawa chili chosakondweretsa kwa woukiridwa, timafuna kwambiri kukhala otetezereka. Mposadabwitsa kuti nzika za nkhaŵa zimafuna maofesala apolisi ambiri m’misewu ndi zilango zandende zokhwimirapo kapena ngakhale chilango cha imfa! Ngakhale kuti ndi zangozi, ena amagula mfuti zodzitetezera nazo, pamene kuli kwakuti ena amafuna kuti boma lichepetse kugulitsidwa kwa mfuti. Koma ngakhale kuti pali mbiri yoipa yakuti upandu ukuchuluka, palibe chifukwa cha kutayira mtima. Kwenikweni, nzika zambiri za mizinda yonga Johannesburg, Mexico City, New York, Rio de Janeiro, ndi São Paulo sizinaberedwepo. Tiyeni tione mmene anthu okhala m’malo owopsa amachitira.

Kusunga Mkhalidwe Wabwino

Ponena za dera lodzala ndi upandu, wolemba nkhani wina akunena za “luntha ndi kupirira kwa anthu a ku Brazil ambiri amene akhoza kukhala mwa ulemu ndi moyenera m’mikhalidwe yoipa kwambiri.” Pambuyo pa zaka 38 mu Rio de Janeiro, Jorge akuti: “Ndimapeŵa misewu ndi madera ena ndipo sindimasonyeza kunyumwa kulikonse. Ndimapeŵanso kuyenda mumsewu usiku ndipo sindimasonyeza kuwopa kwambiri. Ngakhale kuti ndine wosamala, ndimaona anthu monga ngati kuti ali oona mtima, kuwachitira ulemu.”

Inde, peŵani mavuto osayenera. Samalani za inu mwini. Musanyalanyaze mfundo yakuti mantha aakulu angakhwethemule munthu, akumapangitsa ngakhale anthu aulemu wawo kuchita mopanda nzeru. Ponena za ntchito yake m’madera owopsa, Odair akuti: “Ndimayesa kulingalira bwino, osalola maganizo anga kuchita mantha ndi zoipa zimene zingachitike chifukwa zimenezi zimachititsa munthu kumangika ndi kutekeseka kosafunikira. Ndimayesa kuchitira ulemu anthu onse.” Kuwonjezera pa kukhala maso ndi kutalikirana ndi anthu okayikitsa, akuwonjezaponso chinthu china chothandiza cholamulirira malingaliro a munthu: “Pazonsezo, ndimakulitsa chidaliro mwa Yehova Mulungu, ndikumakumbukira kuti palibe chinthu chimene samaona ndipo zonse zimene zimachitika zimaloledwa ndi iye.”

Komabe, palibe munthu amene amafuna kukhala m’mantha osatha. Ndiponso, kodi ndani amene angakane kuti mantha ambiri ndi kutsenderezeka ndizo zinthu zovulaza malingaliro ndi thanzi? Chifukwa chake, kodi nchiyembekezo chotani chimene chilipo kwa awo amene amawopa kuti angaukiridwe panthaŵi iliyonse? Popeza kuti ambiri akuwopa kuti kutsogoloku kuli upandu woipitsitsa, kodi tidzaonadi mapeto a chiwawa? Tikukupemphani kuti muŵerenge nkhani yotsatira yakuti, “Kodi Mantha Adzatha Liti?”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena