Kodi Mantha Adzatha Liti?
KODI kungakudabwitseni kudziŵa kuti chisungiko chenicheni nchogwirizanitsidwa ndi munthu wina amene anakhalako ndi moyo zaka 2,000 zapitazo? Posonyeza kufunika kwa chikondi, Yesu Kristu anasimba za fanizo lina lochititsa chidwi kuti: “Munthu wina anatsika kuchokera ku Yerusalemu kumka ku Yeriko; ndipo anagwa m’manja a achifwamba amene anamvula zovala, namkwapula, nachoka atamsiya wofuna kufa.” Ngakhale kuti apaulendo ena aŵiri ananyalanyaza munthuyo, Msamariya wina wokoma mtima anasonyeza chifundo. Komabe, kodi ndani lerolino amene amasamala za ochitiridwa chiwawa? Kodi ndi mpumulo wotani umene tingayembekezere pa mantha?—Luka 10:30-37.
Pamene kuli kwakuti amanena kuti amakhulupirira Mulungu, ambiri amaganiza kuti munthu ndiye ayenera kuchititsa munthu mnzake kulemekeza ndi kumvera lamulo. Koma kodi zilango zandende zokakala kapena apolisi ambiri olandira malipiro abwino angathetse upandu wachiwawa? Kodi mumakhulupiriradi kuti magulu osungitsa lamulo, ndi zoyesayesa zoona mtima za kupereka chisungiko china, adzathetsa zinthu zonga anamgoneka, magulu a upandu ndi umphaŵi? Komabe, kumva kwathu njala ndi ludzu la chilungamo sikuyenera kukhala kopanda pake.—Mateyu 5:6.
Salmo 46:1 limati: “Mulungu ndiye pothaŵirapo pathu ndi mphamvu yathu, thandizo lopezekeratu m’masautso.” Tidzaona kuti mawu ameneŵa sali a ndakatulo chabe yosangalatsa.
Monga mukudziŵa, ofalitsa nkhani tsiku lililonse amasimba za kupha kwauchinyama m’nkhondo zachiŵeniŵeni ndi m’kuukira kwa zigaŵenga. Kumbali zina za dziko, kupha achichepere osafunidwa kapena mboni zoona ndi maso za upandu kwakhala kofala. Kodi nchifukwa ninji moyo wakhala wosanunkha kanthu chotero? Ngakhale kuti pangakhale zochititsa zosiyanasiyana za chiwawa chotero, pali chifukwa chimodzi chimene sitiyenera kunyalanyaza.
Malinga ndi kunena kwa Mawu a Mulungu, Baibulo, “dziko lonse lapansi ligona mwa woipayo.” (1 Yohane 5:19) Kwenikweni, Yesu Kristu anadziŵikitsa Satana Mdyerekezi osati kokha monga wabodza komanso monga “wambanda.” (Yohane 8:44) Pokhala akusonkhezera anthu m’njira zosiyanasiyana, cholengedwa chauzimu champhamvu chimenechi chikuchirikiza kuwonjezereka kwa chiwawa kwamakono. “Tsoka mtunda ndi nyanja, chifukwa Mdyerekezi watsikira kwa inu, wokhala nawo udani waukulu, podziŵa kuti kamtsalira kanthaŵi,” Chivumbulutso 12:12 chimatero. Komabe, mwamwaŵi, dongosolo loipali lidzaloŵedwa m’malo ndi “miyamba yatsopano, ndi dziko latsopano mmenemo mukhalitsa chilungamo.”—2 Petro 3:13.
Kuwonjezera pa chiyembekezo chabwino kwambiri chimenechi cha dziko latsopano, kodi tili ndi thandizo lotani tsopano lino?
Tisanapeze yankho lokhutiritsa la funso limeneli, ndi bwino kukumbukira kuti ngakhale Akristu enieni alibe chitsimikizo chakuti adzatetezeredwa pa upandu. Mtumwi Paulo analongosola ngozi zina zimene iye mwiniyo anakumana nazo. Anali kuyenda “mowopsa mwake mwa mitsinje, mowopsa mwake mwa olanda, mowopsa modzera kwa mtundu [wake], mowopsa modzera kwa amitundu, mowopsa m’mudzi, mowopsa m’chipululu, mowopsa m’nyanja.” (2 Akorinto 11:26) Ndipo Paulo anapulumukabe ngozi zimenezi. Zili chimodzimodzi lerolino; mwa kukhala ochenjera, tingapitirize kuchita ntchito zathu mwanthaŵi zonse monga mmene kungathekere. Tiyeni tilingalire zinthu zina zimene zingatithandize.
Ngati munthu akukhala m’malo owopsa, khalidwe labwino lingakhale lotetezera, popeza kuti anthu amapenyetsetsa ena. Ngakhale kuti mbala zimalinganiza ndi kuchita upandu, zambiri zimadziona kukhala monga momwe munthu aliyense alili. Peŵani kusuliza zimene amachita, ndipo musayese kufufuza zimene akuchita. Motero, mungachepetse kuthekera kwa kuukiridwa kwanu. Kumbukirani kuti mbala zimafuna kudziŵa amene wagula kanthu kena katsopano kapena amene akupita kutchuti ndipo motero sadzakhala panyumba, chotero samalani zimene mukuuza ena.
Mboni za Yehova zambiri zapeza kuti mbiri yawo monga atumiki yawapatsa chitetezero china pang’ono. Apandu kaŵirikaŵiri asonyeza kuti amalemekeza Akristu amenewo, amene mosakondera amadzipereka kuti athandize anthu m’chitaganya. Mbonizo sizili zambanda kapena mbala, ndiponso sizili ‘zodudukira m’nkhani za eni,’ nchifukwa chake sizili chiwopsezo.—1 Petro 4:15, NW.
Chisungiko m’Dziko Latsopano la Mulungu
Timaipidwa ndi “kuchuluka kwa kusayeruzika” konenedweratu ndi Yesu Kristu, koma m’malo mwa kukhala odera nkhaŵa mopambanitsa, tingakhale ndi chidaliro chakuti Mulungu adzachotsa dongosolo loipa limeneli posachedwapa. Kuwonjezera pa kuneneratu za kulalikira kwa padziko lonse kwa “uthenga uwu wabwino wa ufumu,” Yesu anakumbutsa otsatira ake kuti: “Iye wakulimbika chilimbikire kufikira kuchimaliziro, yemweyo adzapulumuka.”—Mateyu 24:12-14.
Tingatsimikizire kuti awo amene amaukira ena, nthaŵi zina ndi nkhanza yosakhulupiririka, adzachotsedwa. Miyambo 22:22, 23 imati: “Usalande za waumphaŵi chifukwa ali waumphaŵi, ngakhale kutsendereza wosauka kubwalo. Pakuti Yehova adzanenera mlandu wawo; omwe akwatula zawo iye adzakwatula moyo wawo.” Yehova adzachotsa ochita zoipa, onga mbala, ambanda, ndi okonda chiwerewere. Ndiponso, sadzanyalanyaza ochitiridwa upandu wotero. Adzawabwezera zimene anataya ndi kuwachiritsa mokwanira.
Ndithudi, awo amene ‘amasiyana nacho choipa, nachita chokoma’ adzapeza moyo wosatha mwa kupulumuka pa chisautso chachikulu chimene chikudzacho kapena mwa kuuka kwa akufa. “Olungama adzalandira dziko lapansi, nadzakhala momwemo kosatha.” (Salmo 37:27-29) Mapindu otero adzakhalapo chifukwa cha nsembe ya dipo ya Yesu. (Yohane 3:16) Koma kodi moyo udzakhala wotani m’Paradaiso wobwezeretsedwayo?
Moyo mu Ufumu wa Mulungu udzakhala wokondweretsadi. Yehova akuneneratu kuti: “Anthu anga adzakhala m’malo a mtendere, ndi mokhala mokhulupirika ndi mopuma mwa phe.” (Yesaya 32:18) Onse opeza moyo wosatha adzakhala atasintha umunthu wawo. Palibe amene adzakhala woipa kapena wopanda chilungamo, ndipo palibe amene adzayembekezera kuukiridwa ndi munthu wotero. Mneneri Mika akuti: “Adzakhala munthu yense patsinde pa mpesa wake, ndi patsinde pa mkuyu wake; ndipo sipadzakhala wakuwawopsa.” (Mika 4:4; Ezekieli 34:28) Zimenezo nzosiyana chotani nanga ndi malo okhala owopsa a lerolino!
[Bokosi patsamba 6]
CHENJERANI
Apandu ambiri amagwira ntchitoyo nthaŵi yonse, akumachititsa upandu kukhala ntchito yawo. Angamagwire ntchitoyo m’magulu a aŵiriaŵiri kapena atatuatatu, ngakhale ngati ndi mmodzi yekha amene akulozerani mfuti. Pali umboni wowonjezereka wakuti pamene mpanduyo ali wachichepere, mpamenenso amakhala wowopsa kwambiri. Kodi mungachitenji ngati mukhala woukiridwayo?
Khalani wabata kuti musatekese maganizo a mbalayo—angakupheni chifukwa cha mantha akewo. Ngati muli mmodzi wa Mboni za Yehova, mdziŵitseni zimenezo. Komabe, konzekerani kupereka zimene mbalayo ikufuna. Ngati muchedwa, ngoziyo imawonjezereka. Pambuyo pake, mwina mungaone kukhala kwabwino kupempha kuti akubwezereni ziphaso zanu kapena ndalama zokwerera basi.
Kaŵirikaŵiri simungathe kudziŵa munthu waupandu. Mbala zina nzomwerekera ndi anamgoneka kapena zili apandu aakulu, zina zimangofuna ndalama zogulira chakudya. Mulimonse mmene zingakhalire, musanyamule ndalama zambiri. Peŵani kusonyeza majuwelo, mphete zagolidi, kapena mawatchi okwera mtengo. Yendani mozoloŵereka, mosasonyeza mantha. Musayang’anitsitse munthu monga ngati kuti mukufuna kumuulula. Patakhala kuwomberana mfuti mu msewu, gonani pansi; zovala zingachapidwe pambuyo pake.—Yemwe kale anali wapolisi ku Rio de Janeiro.
[Chithunzi patsamba 5]
Khalani wabata ndi kupereka zimene mbalayo ikufuna. Ngati muchedwa, ngoziyo imawonjezereka