Dziko Lopanda Nkhondo—Lidzafika Liti?
TCHATA cha United Nations chinayamba kugwira ntchito pa October 24, 1945. Ndicho njira yaikulu koposa yobweretsera mtendere wa dziko imene sinalinganizidwepo ndi anthu. Pokhala ndi Maiko 51 monga mamembala ake oyamba, United Nations inakhala gulu lapadziko lonse lalikulu koposa m’mbiri ya dziko. Ndiponso, kwa nthaŵi yoyamba, gulu lapadziko lonselo linali lokhoza kukhala ndi gulu lankhondo lochirikizira mtendere ndi chisungiko ndi kubweretsa dziko lopanda nkhondo.
Lerolino, pokhala ndi Maiko 185 monga mamembala ake, United Nations njamphamvu kuposa kale. Nangano, kodi nchifukwa ninji gulu lamphamvu koposalo padziko lonse m’mbiri ya anthu lalephera kukwaniritsa zolinga zake zonse zabwinozo?
Chipembedzo—Chododometsa Chachikulu
Chinthu chachikulu chimodzi chosokoneza ndicho mbali imene chipembedzo chikuchita m’nkhani za dziko. Zoonadi, chiyambire pamene United Nations inakhalako, zipembedzo zazikulu za m’dzikoli zalonjeza kuchirikiza gulu limenelo. Potchula za deti la kukumbukira chaka chake cha 50, Papa John Paul II anafotokoza za United Nations kukhala “chiŵiya chabwino koposa chochirikizira ndi kutetezera mtendere.” Mawu akewo amavomerezedwa ndi gulu lonse la atsogoleri achipembedzo a padziko. Koma mgwirizano wamachenjera umenewu pakati pa chipembedzo ndi boma sungabise choonadi chakuti chipembedzo chakhala chododometsa ndi chonyong’onya kwa United Nations.
Kwa zaka mazana ambiri chipembedzo chachita mbali yaikulu popititsa patsogolo kapena pochirikiza udani wautundu, nkhondo, ndi kupulula anthu. M’zaka zaposachedwapa, podzizimbaitsa ndi changu chachipembedzo, anthu achinansi aphana. Liwu lakuti “kuyeretsa fuko” lagwiritsiridwa ntchito kwambiri mogwirizana ndi nkhondo za kumadera a Balkan. Komabe, udani wachiwawa umene ambiri kumeneko ali nawo kwa wina ndi mnzake wazikidwa pa zipembedzo zawo osati pa fuko lawo, popeza kuti ambiri a iwo achokera mu fuko lofanana. Inde, chipembedzo chiyenera kuvomera mbali yaikulu ya mlandu wa kukhetsa mwaziwo mu yemwe kale anali Yugoslavia, ndipo United Nations yalephera kuletsa zimenezi kuchitika.
Moyenerera, posachedwapa profesa wina wachipembedzo wa pakoleji ananena kuti “m’nyengo ya pambuyo pa nkhondo ya mawu mmene nkhondo zachipembedzo zomawonjezereka, kupenda chipembedzo ndi kupulula anthu kungakhale chimodzi cha zinthu zoyambirira zofunika kuchitidwa msanga, ngakhale kuti kungadzetse mavuto.” Nkwachionekere tsopano kuti anthu akudziŵa mmene chipembedzo chikusokonezera zoyesayesa zobweretsa mtendere wa dziko.
Chosankha cha mu 1981 cha United Nations chinati: “Podera nkhaŵa za maumboni a kusalekererana ndi kukhalapo kwa kusankhana chifukwa cha nkhani za chipembedzo kapena za chikhulupiriro kumene kukuonekabe m’mbali zina za dziko, Tasankha kugwiritsira ntchito njira zonse zofunika kuti tithetse msanga kusalekererana kumeneko kwa mtundu uliwonse ndi maumboni ake ndi kutetezera ndiponso kulimbana ndi kusankhana chifukwa cha chipembedzo kapena chikhulupiriro.”
Mogwirizana ndi chosankha chawo, United Nations yalengeza 1995 kukhala Chaka cha Kulekererana. Komabe, kuti tinene zoona, kodi kupeza mtendere ndi chisungiko kudzathekadi m’dziko logaŵanika ndi chipembedzoli?
Mtsogolo mwa Chipembedzo
Ulosi umene uli m’buku la Baibulo la Chivumbulutso umapereka yankho. Umafotokoza za “mkazi wachigololo wamkulu” wophiphiritsira amene akhala monga “mfumu” ndipo “akuchita ufumu pa mafumu a dziko.” Mkazi wachigololo ameneyu amakhala ndi moyo wa ‘kudyerera’ ndipo amachita chigololo ndi maboma adziko. Maboma ameneŵa akusonyezedwa kukhala ngati “chilombo chofiiritsa,” chimene mkazi wachigogolo wakwera mwachimwemwe. (Chivumbulutso 17:1-5, 18; 18:7) Pokhala wodziŵika kuti “Babulo Wamkulu,” mkazi waulamuliro wambiri ndi woipa ameneyu dzina lake lachokera ku Babulo wakale, magwero a chipembedzo cha mafano. Moyenerera, lerolino mkazi wachigololo amaimira zipembedzo zonse za dziko, zimene zazisakaniza ndi zochitika za maboma.
Nkhaniyo imapitiriza kuti, potsirizira pake, Mulungu adzasonkhezera mtima magulu ankhondo a chilombocho kuti amuukire. Ameneŵa “[a]dzadana ndi mkazi wachigololoyo, n[a]dzamkhalitsa wabwinja wausiŵa, n[a]dzadya nyama yake, n[a]dzampsereza ndi moto.” (Chivumbulutso 17:16)a Motero Yehova Mulungu mwiniyo adzachitapo kanthu mwa kugwiritsira ntchito mitundu yamphamvu kuchita mkupiti wa kuchotsa chipembedzo chonyenga. Dongosolo la padziko lonse lachipembedzo, ndi matchalitchi ake okongola ndi akachisi, zidzawonongedweratu. Kudodometsa kwa chipembedzo pa mtendere ndi chisungiko panthaŵiyo kudzachotsedwa. Komabe ngakhale panthaŵiyo, kodi padzakhaladi mtendere weniweni ndi chisungiko pa dziko lapansi?
Chibadwa cha Anthu Opanda Ungwiro
Kodi pali chitsimikiziro chilichonse chakuti kuchotsa chipembedzo kudzatseguliradi njira dziko lopanda nkhondo? Ayi. United Nations idzakumanabe ndi mkhalidwe wosayembekezereka wosiyana ndi zimenezo. Komanso, anthu akufuna mtendere ndi chisungiko. Chikhalirechobe, anthuwo ndiwo amene amasokoneza kwambiri mtendere ndi chisungiko. Udani, kunyada, kudzitukumula, dyera, ndi umbuli ndiyo mikhalidwe yaumunthu yochititsa mikangano ndi nkhondo zonse.—Yakobo 4:1-4.
Baibulo linaneneratu kuti m’tsiku lathu anthu adzakhala “odzikonda okha, okonda ndalama, odzitamandira, odzikuza, amwano, osamvera akuwabala, osayamika, osayera mtima, opanda chikondi chachibadwidwe, osayanjanitsika, akudyerekeza, osakhoza kudziletsa, aukali, osakonda abwino, achiŵembu, aliuma olimbirira, otukumuka mtima.”—2 Timoteo 3:1-4.
Mlembi Wamkulu Boutros Boutros-Ghali anavomereza kuti “dzikoli likuvutika ndi chipwirikiti cha chitaganya ndi makhalidwe, chimene chili chachikulu koposa m’maiko ambiri.” Makambitsirano ochuluka sangathetse mikhalidwe yoipa ya chibadwa cha munthu wopanda ungwiro.—Yerekezerani ndi Genesis 8:21; Yeremiya 17:9.
Yesu Kristu—Kalonga wa Mtendere
Mwachionekere, United Nations singathe kudzetsa mtendere wa dziko. Mamembala ake ndi ochirikiza ake onse ali anthu opanda ungwiro, mosasamala kanthu za zonulirapo zawo zapamwambazo. Baibulo limanena kuti “njira ya munthu siili mwa iye mwini; sikuli kwa munthu woyenda kulongosola mapazi ake.” (Yeremiya 10:23) Ndiponso, Mulungu amachenjeza kuti: “Musamakhulupirira zinduna, kapena mwana wa munthu, amene mulibe chipulumutso mwa iye.”—Salmo 146:3.
Baibulo limaneneratu zimene Yehova adzachita kupyolera mwa Mwana wake, “Kalonga wa Mtendere.” Yesaya 9:6, 7 amati: “Kwa ife mwana wakhanda wabadwa, kwa ife mwana wamwamuna wapatsidwa; ndipo ulamuliro udzakhala pa pheŵa lake, ndipo adzamutcha dzina lake Wodabwitsa, Wauphungu, Mulungu wamphamvu, Atate Wosatha, Kalonga wa mtendere. Za kuenjezera ulamuliro wake, ndi za mtendere sizidzatha.”
Mitundu ya dziko yatopetsedwa ndi zaka 50 za kuyesayesa kosaphula kanthu. Posachedwapa idzawononga magulu achipembedzo onga mkazi wachigololowo. Ndiyeno Yesu Kristu, “Mfumu ya mafumu ndi Mbuye wa ambuye,” ndi gulu lake la ankhondo akumwamba adzawononga maboma onse a anthu ndi kupha onse amene amakana ulamuliro wa Mulungu. (Chivumbulutso 19:11-21; yerekezerani ndi Danieli 2:44.) Mwa njira imeneyi Yehova Mulungu adzabweretsa dziko lopanda nkhondo.
[Mawu a M’munsi]
a Kuti mudziŵe zochuluka za ulosi wa Chivumbulutso wonena za Babulo Wamkulu, onani mitu 33 mpaka 37 ya buku lakuti Revelation—Its Grand Climax At Hand!, lofalitsidwa mu 1988 ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.
[Bokosi patsamba 7]
LINGALIRO LACHIKRISTU PA UNITED NATIONS
Mu ulosi wa Baibulo, maboma a anthu kaŵirikaŵiri amaimiridwa ndi zilombo. (Danieli 7:6, 12, 23; 8:20-22) Chifukwa chake, kwa zaka makumi ambiri magazini a Nsanja ya Olonda asonyeza kuti zilombo za m’Chivumbulutso machaputala 13 ndi 17 ndi maboma adziko amakono. Zimenezi zimaphatikizapo United Nations, imene imasonyezedwa m’Chivumbulutso chaputala 17 monga chilombo chofiiritsa chokhala ndi mitu isanu ndi iŵiri ndi nyanga khumi.
Komabe, kaonedwe kameneka ka Malemba sikamaloleza konse kuchitira chipongwe maboma kapena akuluakulu ake. Baibulo limafotokoza mwachimvekere kuti: “Anthu onse amvere maulamuliro aakulu; pakuti palibe ulamuliro wina koma wochokera kwa Mulungu; ndipo iwo amene alipo aikidwa ndi Mulungu. Kotero kuti iye amene atsutsana nawo ulamuliro, akaniza choikika ndi Mulungu; ndipo iwo akukaniza, adzadzitengera kulanga.”—Aroma 13:1, 2.
Chifukwa cha zimenezo, Mboni za Yehova, zimene sizimaloŵa konse m’ndale, sizimadodometsa maboma a anthu. Sizimasonkhezera chipanduko kapena kugwirizana nawo m’zochitika za kukana kumvera boma. M’malo mwake amazindikira kuti pamafunikira boma kuti anthu asunge malamulo.—Aroma 13:1-7; Tito 3:1.
Mboni za Yehova zimaona gulu la United Nations monga momwe zimaonera magulu ena a boma a dzikoli. Amadziŵa kuti United Nations ikupitiriza kukhalako chifukwa cha chilolezo cha Mulungu. Mogwirizana ndi Baibulo, Mboni za Yehova zimapereka ulemu woyenera ku maboma onse ndi kuwamvera malinga ngati kumvera kumeneko kuli kosawachititsa kuchimwira Mulungu.—Machitidwe 5:29.