Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w95 10/15 tsamba 18-23
  • Kodi Mudzaima Motani ku Mpando wa Chiweruzo?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mudzaima Motani ku Mpando wa Chiweruzo?
  • Nsanja ya Olonda—1995
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Yehova Monga Woweruza Wamkulu
  • Malo a Yesu
  • Kodi Fanizolo Limati Chiyani?
  • Kodi Nkhosazo ndi Mbuzizo Zili ndi Mtsogolo Motani?
    Nsanja ya Olonda—1995
  • Chilungamo Kaamba ka Onse ndi Woweruza Woikidwa ndi Mulungu
    Nsanja ya Olonda—1989
  • Kulekanitsidwa kwa Anthu pa Mkangano Waufumu
    Kupulumuka Kuloŵa m’Dziko Lapansi Latsopano
  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
    Nsanja ya Olonda—1997
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1995
w95 10/15 tsamba 18-23

Kodi Mudzaima Motani ku Mpando wa Chiweruzo?

“Pamene Mwana wa munthu adzadza mu ulemerero wake, ndi angelo onse pamodzi naye, pomwepo iye adzakhala pa chimpando cha kuŵala kwake.”​—MATEYU 25:31.

1-3. Kodi tili ndi chifukwa chotani chokhalira ndi chiyembekezo chabwino ponena za chilungamo?

‘KODI ALI NDI MLANDU KAPENA ALIBE MLANDU?’ Ambiri amadzifunsa motero akamva za mlandu wa m’khoti. Oweruza ndi ogamula mlandu amayesa kukhala oona mtima, koma kodi chilungamo chimakhalapo nthaŵi zonse? Kodi simunamvepo za chisalungamo ndi kukondera poweruza mlandu? Chisalungamo chotero si chalero ayi, monga momwe tikuonera m’fanizo la Yesu lopezeka pa Luka 18:1-8.

2 Mulimonse mmene mwachidziŵira chilungamo chaumunthu, tamverani mawu omalizira a Yesu: “Kodi Mulungu sadzachitira chilungamo osankhidwa ake akumuitana usana ndi usiku . . . ? Ndinena ndi inu, adzawachitira chilungamo posachedwa. Koma Mwana wa munthu pakudza iye, adzapeza chikhulupiriro pa dziko lapansi kodi?”

3 Inde, Yehova adzatsimikiza kuti atumiki ake potsirizira pake achitidwa molungama. Nayenso Yesu alimo ndi mbali, makamaka tsopano popeza kuti tikukhala mu “masiku otsiriza” a dongosolo loipa lilipoli. Posachedwa Yehova adzagwiritsira ntchito Mwana wake wamphamvuyo kusesa kuipa pa dziko lapansi. (2 Timoteo 3:1; 2 Atesalonika 1:7, 8; Chivumbulutso 19:11-16) Tingadziŵe bwino za mbali ya Yesu mwa kupenda limodzi la mafanizo omalizira amene iye anapereka, limene kambiri limatchedwa fanizo la nkhosa ndi mbuzi.

4. Kodi takhala ndi kamvedwe kotani ponena za nthaŵi ya kukwaniritsidwa kwa fanizo la nkhosa ndi mbuzi, koma nchifukwa ninji tidzasumika maganizo pa fanizolo tsopano? (Miyambo 4:18)

4 Nthaŵi yaitali tadziŵa kuti fanizolo limatanthauza kukhala kwa Yesu pa mpando monga Mfumu mu 1914 ndi kuti chiyambire nthaŵiyo wakhala akuweruza​—moyo wosatha kwa anthu onga nkhosa, imfa yachikhalire kwa mbuzi. Koma kupendanso fanizolo kumasonyeza kusintha kwa kamvedwe kathu ponena za nthaŵi ya kukwaniritsidwa kwake ndi zimene limaimira. Kamvedwe kowongoleredwa kameneka kamasonyeza kufunika kwake kwa ntchito yathu yolalikira ndi kuti anthu ayenera kuchitapo kanthu. Kuti tipeze maziko a kamvedwe kakuya kwambiri kameneka ka fanizolo, tiyeni tipende zimene Baibulo limasonyeza ponena za Yehova ndi Yesu, onse aŵiri monga Mafumu ndi Oweruza.

Yehova Monga Woweruza Wamkulu

5, 6. Kodi nchifukwa ninji kuli koyenera kuona Yehova monga Mfumu ndiponso Woweruza?

5 Yehova akulamulira chilengedwe chonse ndi mphamvu pa zonse. Pokhala wopanda chiyambi ndi mapeto, iye ndi “Mfumu yosatha.” (1 Timoteo 1:17; Salmo 90:2, 4; Chivumbulutso 15:3) Ali ndi ulamuliro wa kupanga malamulo ndi kuwasungitsa. Koma ulamuliro wake umaphatikizapo kukhala kwake Woweruza. Yesaya 33:22 amati: “Yehova ndiye Woweruza wathu, Yehova ndiye Wotipatsa malamulo, Yehova ndiye Mfumu yathu; iye adzatipulumutsa.”

6 Kwa nthaŵi yaitali atumiki a Mulungu azindikira kuti Yehova ndiye Woweruza milandu ndi nkhani. Mwachitsanzo, “Woweruza wa dziko lonse lapansi” atapenda umboni wonena za kuipa kwa Sodomu ndi Gomora, anaweruza kuti nzika zake ziwonongedwe ndiponso anapereka chiweruzo cholungama chimenecho. (Genesis 18:20-33; Yobu 34:10-12) Zimatilimbikitsa chotani nanga kudziŵa kuti Yehova ali Woweruza wolungama amene amachita ziweruzo zake nthaŵi zonse!

7. Kodi Yehova anachita motani monga Woweruza pochita ndi Israyeli?

7 Mu Israyeli wakale, Yehova nthaŵi zina anapereka chiweruzo mwachindunji. Kodi sizikanakukondweretsani kalelo kudziŵa kuti Woweruza wangwiro ndiye anali kuweruza milandu? (Levitiko 24:10-16; Numeri 15:32-36; 27:1-11) Mulungu anaperekanso “maweruzo” omwe anali abwino onse monga miyezo yoweruzira. (Levitiko 25:18, 19; Nehemiya 9:13; Salmo 19:9, 10; 119:7, 75, 164; 147:19, 20) Ndiye “Woweruza wa [dziko lonse lapansi, NW],” choncho tonsefe tikukhudzidwa.​—Ahebri 12:23.

8. Kodi ndi masomphenya otani oyenera amene Danieli anaona?

8 Tili ndi umboni woperekedwa ndi “mboni yoona ndi maso” pankhaniyi. Mneneri Danieli anasonyezedwa masomphenya a zilombo zolusa zomwe zinaimira maboma kapena maufumu. (Danieli 7:1-8, 17) Anawonjezera kuti: “Anaikapo mipando yachifumu, nikhalapo Nkhalamba ya Kale Lomwe, zovala zake zinali za mbu ngati chipale chofeŵa.” (Danieli 7:9) Onani kuti Danieli anaona mipando yachifumu “nikhalapo Nkhalamba ya Kale Lomwe [Yehova].” Tsono dzifunseni, ‘Kodi Danieli panopa anali kuona Mulungu akukhala Mfumu?’

9. Kodi tanthauzo lina la ‘kukhala’ pa mpando wachifumu nlotani? Perekani zitsanzo.

9 Chabwino, pamene tiŵerenga kuti wina ‘anakhala’ pa mpando wachifumu, tingaganize za kukhala kwake mfumu, pakuti Baibulo nthaŵi zina limagwiritsira ntchito mawu amenewo. Mwachitsanzo: “Ataloŵa ufumu [Zimri] nakhala pa mpando wachifumu wake, . . . ” (1 Mafumu 16:11; 2 Mafumu 10:30; 15:12; Yeremiya 33:17) Ulosi wa Mesiya unati: “Adzakhala ndi kulamulira pa mpando wachifumu wake.” Chotero, ‘kukhala pa mpando wachifumu’ kungatanthauzedi kukhala mfumu. (Zekariya 6:12, 13) Yehova akunenedwa kukhala Mfumu imene imakhala pa mpando wachifumu. (1 Mafumu 22:19; Yesaya 6:1; Chivumbulutso 4:1-3) Iye ndiye “Mfumu yosatha.” Komabe, pamene anayamba kuchita ulamuliro watsopano, ananenedwa kuti wakhala Mfumu, ngati kuti wakhalanso pa mpando wake wachifumu.​—1 Mbiri 16:1, 31; Yesaya 52:7; Chivumbulutso 11:15-17; 15:3; 19:1, 2, 6.

10. Kodi ntchito yaikulu ya mafumu a Israyeli inali yotani? Perekani chitsanzo.

10 Koma nayi mfundo yofunika: Ntchito yaikulu ya mafumu akale inali ija ya kuzenga milandu ndi kugamula ziweruzo. (Miyambo 29:14) Kumbukirani chiweruzo cha nzeru cha Solomo pamene aliyense wa akazi aŵiriwo anati khanda limodzimodzilo ndi lake. (1 Mafumu 3:16-28; 2 Mbiri 9:8) Imodzi ya nyumba zake zaboma inali “Khumbi la Mpando Wachifumu loweruziramo iye,” lotchedwanso “khumbi la milandu.” (1 Mafumu 7:7) Yerusalemu anatchedwa malo kumene “anaika mipando ya chiweruzo.” (Salmo 122:5) Mwachionekere, ‘kukhala pa mpando wachifumu’ kungatanthauzenso kuweruza.​—Eksodo 18:13; Miyambo 20:8.

11, 12. (a) Kodi kukhala pa mpando kwa Yehova, kotchulidwa m’Danieli chaputala 7 kunatanthauzanji? (b) Kodi malemba ena amatsimikiza motani kuti Yehova amakhala pa mpando kuweruza?

11 Tsopano tiyeni tibwerere kuja kumene Danieli anaona ‘Nkhalamba ya Kale Lomwe ikukhala.’ Danieli 7:10 amawonjezera kuti: “Woweruza mlandu anakhalapo, ndi mabuku anatsegulidwa.” Inde, Nkhalamba ya Kale Lomwe inali kukhala pansi kuti ipereke chiweruzo chokhudza kulamulira dziko ndi kuweruza Mwana wa munthu kukhala woyenera kulamulira. (Danieli 7:13, 14) Ndiyeno timaŵerenga kuti “inadza Nkhalamba ya Kale Lomwe; ndi mlandu unakomera opatulika,” aja oweruzidwa kukhala oyenera kulamulira ndi Mwana wa munthu. (Danieli 7:21, 22) Potsirizira pake ‘Woweruza mlandu anakhalako’ ndi kupereka chiweruzo chowopsa pa ulamuliro womaliza wa padziko lonse.​—Danieli 7:26.a

12 Chotero, pamene Danieli anaona Mulungu ‘akukhala pa mpando wachifumu’ zinatanthauza kuti Iye anafika kudzapereka chiweruzo. Poyambirira Davide anaimba kuti: “[Yehova] mwandiweruzira mlandu wanga; mwakhala pa mpando wachifumu, woweruza wolungama.” (Salmo 9:4, 7) Ndipo Yoweli analemba kuti: “Agalamuke amitundu, nakwerere ku chigwa cha Yosafati; pakuti [ine Yehova] ndidzakhala komweko kuweruza amitundu onse.” (Yoweli 3:12; yerekezerani ndi Yesaya 16:5.) Onse aŵiri Yesu ndi Paulo anakhalapo pamlandu umene munthu anakhala pansi akumazenga mlandu ndi kupereka chiweruzo.b​—Yohane 19:12-16; Machitidwe 23:3; 25:6.

Malo a Yesu

13, 14. (a) Kodi ndi chitsimikizo chiti chimene anthu a Mulungu anali nacho chakuti Yesu adzakhala Mfumu? (b) Kodi Yesu anakhala liti pa mpando wake wachifumu, ndipo analamulira kuyambira mu 33 C.E. ndi mtsogolo mwake m’lingaliro lotani?

13 Yehova ali ponse paŵiri Mfumu ndi Woweruza. Bwanji nanga za Yesu? Mngelo wolengeza kubadwa kwake anati: “Ambuye Mulungu adzampatsa iye mpando wachifumu wa Davide atate wake: . . . ndipo ufumu wake sudzatha.” (Luka 1:32, 33) Yesu adzakhala woloŵa nyumba wachikhalire wa ufumu wa Davide. (2 Samueli 7:12-16) Adzalamulira ali kumwamba, pakuti Davide anati: “Yehova ananena kwa Ambuye wanga [Yesu], Khalani pa dzanja lamanja langa, kufikira nditaika adani anu chopondapo mapazi anu. Yehova adzatumiza ndodo ya mphamvu yanu kuchokera ku Ziyoni; Chitani ufumu pakati pa adani anu.”​—Salmo 110:1-4.

14 Kodi zimenezo zinali kudzachitika liti? Yesu sanalamulire monga Mfumu pamene anali munthu. (Yohane 18:33-37) Mu 33 C.E., iye anamwalira, anaukitsidwa, nakwera kumwamba. Ahebri 10:12 amati: “Adapereka nsembe imodzi chifukwa cha machimo, anakhala pa dzanja lamanja la Mulungu.” Kodi Yesu anali ndi ulamuliro wotani? “[Mulungu] namkhazikitsa pa dzanja lake lamanja m’zakumwamba, pamwamba pa ukulu wonse, ndi ulamuliro, ndi mphamvu, ndi ufumu . . . nampatsa iye akhale mutu pamtu pa zonse, kwa Eklesia.” (Aefeso 1:20-23) Chifukwa chakuti Yesu nthaŵiyo anali ndi ulamuliro waufumu pa Akristu, Paulo anakhoza kulemba kuti Yehova “anatilanditsa ife ku ulamuliro wa mdima, natisunthitsa kutiloŵetsa mu ufumu wa Mwana wa chikondi chake.”​—Akolose 1:13; 3:1.

15, 16. (a) Kodi nchifukwa ninji tikuti Yesu sanakhale Mfumu ya Ufumu wa Mulungu mu 33 C.E.? (b) Kodi Yesu anayamba liti kulamulira mu Ufumu wa Mulungu?

15 Komabe, nthaŵiyo Yesu sanakhale Mfumu ndi Woweruza pa amitundu. Anakhala pafupi ndi Mulungu, akumayembekezera nthaŵi ya kukhala Mfumu ya Ufumu wa Mulungu. Paulo analemba ponena za iye kuti: “Za mngelo uti anati nthaŵi iliyonse, Khala pa dzanja lamanja langa, kufikira ndikaika adani ako mpando wa ku mapazi ako?”​—Ahebri 1:13.

16 Mboni za Yehova zafalitsa umboni wochuluka wakuti nyengo ya kuyembekeza kwa Yesu inatha mu 1914, pamene iye anakhala wolamulira wa Ufumu wa Mulungu m’miyamba yosaoneka. Chivumbulutso 11:15, 18 chimati: “Ufumu wa dziko lapansi wayamba kukhala wa Ambuye wathu, ndi wa Kristu wake: ndipo adzachita ufumu kufikira nthaŵi za nthaŵi.” “Ndipo amitundu anakwiya, ndipo unadza mkwiyo wanu.” Inde, amitundu anakwiyirana pa Nkhondo Yadziko I. (Luka 21:24) Nkhondo, zivomezi, miliri, njala, ndi zina zotero, zimene taona chiyambire 1914 zimatsimikiza kuti Yesu tsopano akulamulira mu Ufumu wa Mulungu, ndi kuti mapeto a dzikoli ali pafupi.​—Mateyu 24:3-14.

17. Kodi ndi mfundo zofunika ziti zimene tapeza kufikira pano?

17 Nawa malongosoledwe achidule: Mulungu anganenedwe kuti wakhala pa mpando wachifumu monga Mfumu, koma m’lingaliro lina iye angakhale pa mpando wake wachifumu kuweruza. Mu 33 C.E., Yesu anakhala kudzanja lamanja la Mulungu, ndipo tsopano ndi Mfumu ya Ufumuwo. Koma kodi Yesu, amene akulamulira monga Mfumu tsopano, alinso Woweruza? Ndipo nchifukwa ninji zimenezi zili zofunika kwa ife, makamaka nthaŵi inoyi?

18. Kodi pali umboni wotani wakuti Yesu adzakhalanso Woweruza?

18 Yehova, amene ali ndi mphamvu ya kuika oweruza, anasankha Yesu monga Woweruza wokwaniritsa miyezo Yake. Yesu anasonyeza zimenezi polankhula zakuti anthu adzakhala amoyo mwauzimu: “Atate saweruza munthu aliyense, koma anapereka kuweruza konse kwa Mwana.” (Yohane 5:22) Komabe, mbali ya Yesu ya kuweruza imaposa pamenepo, pakuti alinso woweruza wa amoyo ndi akufa. (Machitidwe 10:42; 2 Timoteo 4:1) Nthaŵi ina Paulo anati: “[Mulungu] anapangira tsiku limene adzaweruza dziko lokhalamo anthu m’chilungamo, ndi munthu [Yesu] amene anamuikiratu, napatsa anthu chitsimikizo, pamene anamuukitsa iye.”​—Machitidwe 17:31; Salmo 72:2-7.

19. Kodi nchifukwa ninji kuli kolondola kunena kuti Yesu amakhala pa mpando monga Woweruza?

19 Kodi tili ndi chifukwa chomveka chonenera kuti Yesu amakhala pa chimpando cha ulemerero wake pantchito yeniyeni ya Woweruza? Inde. Yesu anauza atumwi kuti: “Inu amene munanditsata ine, m’kubadwanso, pamene Mwana wa munthu adzakhala pa chimpando cha ulemerero wake, inunso, mudzakhala pa mipando khumi ndi iŵiri, kuweruza mafuko khumi ndi aŵiri a Israyeli.” (Mateyu 19:28) Ngakhale kuti Yesu tsopano ndi Mfumu ya Ufumuwo, ntchito yake ina yotchulidwa pa Mateyu 19:28 idzaphatikizapo kukhala pa mpando wachifumu kuweruza mkati mwa Zaka Chikwi. Panthaŵiyo adzaweruza anthu onse, olungama ndi osalungama. (Machitidwe 24:15) Kuli kothandiza kukumbukira zimenezi pamene tisumika maganizo athu pa limodzi la mafanizo a Yesu limene limakhudza nthaŵi yathu ndi miyoyo yathu.

Kodi Fanizolo Limati Chiyani?

20, 21. Kodi atumwi a Yesu anafunsa za chiyani chimene chimakhudza nthaŵi yathu, chikumabutsa funso lotani?

20 Imfa ya Yesu itayandikira, atumwi ake anamfunsa kuti: “Zija zidzaoneka liti? Ndipo chizindikiro cha [kukhalapo, NW] kwanu nchiyani, ndi cha mathedwe a nthaŵi ya pansi pano?” (Mateyu 24:3) Yesu analosera zochitika zazikulu zimene zidzakhalako pa dziko lapansi ‘mathedwe asanadze.’ Mapetowo atakhala pafupi, mitundu ‘idzapenya Mwana wa munthu alinkudza pa mitambo ya kumwamba, ndi mphamvu ndi ulemerero waukulu.’​—Mateyu 24:14, 29, 30.

21 Koma kodi anthu a mitunduwo zinthu zidzawakhalira bwanji pamene Mwana wa munthu adza ndi ulemerero wake? Tiyeni tipeze yankho lake m’fanizo la nkhosa ndi mbuzi, limene limayamba ndi mawu aŵa: “Koma pamene Mwana wa munthu adzadza mu ulemerero wake, ndi angelo onse pamodzi naye, pomwepo iye adzakhala pa chimpando cha kuŵala kwake: ndipo adzasonkhanidwa pamaso pake anthu a mitundu yonse.”​—Mateyu 25:31, 32.

22, 23. Kodi ndi mfundo ziti zimene zikusonyeza kuti fanizo la nkhosa ndi mbuzi silinayambe kukwaniritsidwa mu 1914?

22 Kodi fanizo limeneli limanena za nthaŵi pamene Yesu anakhala pa mpando m’mphamvu yachifumu mu 1914, malinga ndi zimene tadziŵa nthaŵi yaitali? Eya, Mateyu 25:34 amanenadi kuti iye ndi Mfumu, choncho fanizolo moyenerera liyamba kugwira ntchito Yesu atakhala Mfumu mu 1914. Koma kodi ndi kuweruza kotani kumene anachita mwamsanga pambuyo pake? Sikunali kuweruza “mitundu yonse.” M’malo mwake, anasumika maganizo ake pa aja omwe amati ndiwo “nyumba ya Mulungu.” (1 Petro 4:17) Mogwirizana ndi Malaki 3:1-3, Yesu, monga mthenga wa Yehova, anayang’anira mwa chiweruzo Akristu odzozedwa otsala pa dziko lapansi. Inalinso nthaŵi ya kupereka chiweruzo pa Dziko Lachikristu, limene monama linati ndilo “nyumba ya Mulungu.”c (Chivumbulutso 17:1, 2; 18:4-8) Komabe palibe chimene chikusonyeza kuti panthaŵiyo, kapena chiyambire nthaŵiyo, Yesu anakhala pa mpando kuweruza anthu a mitundu yonse komaliza monga nkhosa kapena mbuzi.

23 Tikapenda zochita za Yesu m’fanizolo, tikumuona iye akuweruza mitundu yonse komaliza. Fanizolo silikusonyeza kuti kuweruzako kudzapitiriza kwa nyengo ya zaka zambiri, ngati kuti anthu onse amene afa zaka zakumbuyoku aweruzidwira ku imfa yosatha kapena ku moyo wosatha. Zikuoneka kuti unyinji wa awo amene amwalira zaka zaposachedwapa apita kumanda a anthu onse. (Chivumbulutso 6:8; 20:13) Koma, fanizolo likusonyeza nthaŵi pamene Yesu akuweruza anthu a “mitundu yonse” amene ali amoyo panthaŵiyo ndipo akuyang’anizana ndi chilango cha chiweruzo chake.

24. Kodi fanizo la nkhosa ndi mbuzi lidzakwaniritsidwa liti?

24 M’mawu ena, fanizolo likusonya mtsogolo pamene Mwana wa munthu adzadza mu ulemerero wake. Adzakhala pa mpando kuweruza anthu amoyo panthaŵiyo. Chiweruzo chake chidzazikidwa pa umunthu wawo umene asonyeza. Nthaŵiyo “wolungama ndi woipa” adzakhala atazindikiridwa bwino. (Malaki 3:18) Kupereka chiweruzocho ndi chilango chake kudzachitika panthaŵi yaifupi. Yesu adzapereka ziweruzo zolungama zozikidwa pa mkhalidwe umene munthu yense adzakhala atasonyeza.​—Onaninso 2 Akorinto 5:10.

25. Kodi Mateyu 25:31 akusonyezanji mwa kunena kuti Mwana wa munthu wakhala pa chimpando choŵala?

25 Chotero, zimenezi zikutanthauza kuti ‘kukhala kwa Yesu pa chimpando cha kuŵala kwake’ kwa chiweruzo, kotchulidwa pa Mateyu 25:31, kumanena za nthaŵi ya mtsogolo pamene Mfumu yamphamvu imeneyi idzakhala pa mpando kupereka chiweruzo ndi chilango pa mitundu. Inde, nkhani ya chiweruzo imene ikunena za Yesu pa Mateyu 25:31-33, 46 njofanana ndi nkhani ya pa Danieli chaputala 7, pamene Mfumu yolamulira, Nkhalamba ya Kale Lomwe, inakhala pa mpando kuchita ntchito yake ya Woweruza.

26. Kodi ndi kafotokozedwe kotani katsopano kamene kakhalapo?

26 Kulimva mwa njira imeneyi fanizo la nkhosa ndi mbuzi kumasonyeza kuti chiweruzo pa nkhosa ndi mbuzi chidzaperekedwa mtsogolo. Chidzachitika “masauko” [“chisautso,” NW] otchulidwa pa Mateyu 24:29, 30 atayamba ndipo Mwana wa munthu ‘adza ndi ulemerero.’ (Yerekezerani ndi Marko 13:24-26.) Ndiyeno, pokhala dongosolo lonse loipa lidzakhala litafika pamapeto ake, Yesu adzakhala pabwalo la milandu ndi kupereka chiweruzo ndi chilango.​—Yohane 5:30; 2 Atesalonika 1:7-10.

27. Kodi tiyenera kufuna kudziŵa chiyani ponena za fanizo la Yesu lomaliza?

27 Zimenezi zikuwongolera kamvedwe kathu ka nthaŵi ya kukwaniritsidwa kwa fanizo la Yesu, kamene kakusonyeza pamene nkhosa ndi mbuzi zidzaweruzidwa. Koma kodi zimatikhudza motani ife amene tikulalikira mwachangu uthenga wabwino wa Ufumu? (Mateyu 24:14) Kodi zikuchititsa ntchito yathu kukhala yosafunika kwenikweni, kapena kodi zikutipatsa thayo lolemera kwambiri? Tiyeni tione m’nkhani yotsatira mmene zikutikhudzira.

[Mawu a M’munsi]

a Liwu lomasulidwa “Woweruza mlandu” pa Danieli 7:10, 26 limapezekanso pa Ezara 7:26 ndi Danieli 4:37; 7:22.

b Ponena za kuperekana ku khoti kwa Akristu, Paulo anafunsa kuti: “Kodi muweruzitsa [kwenikweni “kukhazika pa mpando”] iwo amene ayesedwa achabe mumpingo?”​—1 Akorinto 6:4.

c Onani Revelation​—Its Grand Climax At Hand!, masamba 56, 73, 235-45, 260, lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.

Kodi Mukukumbukira?

◻ Kodi Yehova amatumikira motani monga Mfumu ndiponso Woweruza?

◻ Kodi ‘kukhala pa mpando wachifumu’ kungakhale ndi matanthauzo aŵiri ati?

◻ Kodi kumbuyoku tinanenanji za nthaŵi ya kukwaniritsidwa kwa Mateyu 25:31, koma kodi pali maziko otani a lingaliro latsopano?

◻ Kodi ndiliti pamene Mwana wa munthu akhala pa mpando wake wachifumu, malinga ndi zimene Mateyu 25:31 akusonyeza?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena