Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w97 7/1 tsamba 30-31
  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
  • Nsanja ya Olonda—1997
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Nkhosazo ndi Mbuzizo Zili ndi Mtsogolo Motani?
    Nsanja ya Olonda—1995
  • Kodi Mudzaima Motani ku Mpando wa Chiweruzo?
    Nsanja ya Olonda—1995
  • Khristu Akadzayamba Kulamulira Adzaweruza Nkhosa ndi Mbuzi
    Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
  • Tizithandiza Abale a Khristu Mokhulupirika
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1997
w97 7/1 tsamba 30-31

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Tinasangalala ndi phunziro lathu la fanizo la Yesu la nkhosa ndi mbuzi. Malinga ndi chidziŵitso chatsopano chofotokozedwa mu Nsanja ya Olonda ya October 15, 1995, kodi tinganenebe kuti Mboni za Yehova lerolino zikuchitako ntchito yolekanitsa?

Inde. Ndi chifukwa chabwino, ambiri aganiza zimenezi chifukwa Mateyu 25:31, 32 amati: “Pamene Mwana wa munthu adzadza mu ulemerero wake, ndi angelo onse pamodzi naye, pomwepo iye adzakhala pa chimpando cha kuŵala kwake: ndipo adzasonkhanidwa pamaso pake anthu a mitundu yonse; ndipo iye adzalekanitsa iwo wina ndi mnzake, monga mbusa alekanitsa nkhosa ndi mbuzi.” Nsanja ya Olonda ya October 15, 1995, inasonyeza chifukwa chake mavesiwa adzakwaniritsidwa chisautso chachikulu chitayamba. Yesu adzadza ndi ulemerero wake ndi angelo ake, nadzakhala pa mpando wake wachiweruzo. Ndipo adzalekanitsa anthu. Motani? Adzagamula mlandu malinga ndi zimene anthu anachita kapena zimene sanachite nthaŵiyo isanafike.

Tingayerekezere zimenezi ndi kuzenga mlandu kumene kumafika pa kupereka chiweruzo pamlandu wa m’khoti. Umboni umapezeka panyengo yaitali khoti lisanagamule ndi kupereka chilango. Umboni wakuti kaya anthu amene ali ndi moyo tsopano adzakhala nkhosa kapena mbuzi wakhala ukupezeka kwa nthaŵi yaitali. Ndipo ukali kubwera. Koma pamene Yesu akhala pa chimpando chake, mlanduwo udzakhala utatha. Adzakhala wokonzeka kupereka chiweruzo. Adzalekanitsa anthu ku kudulidwa kosatha kapena ku moyo wosatha.

Komabe, ngakhale kuti kulekanitsa anthu ku moyo kapena ku imfa kotchulidwa pa Mateyu 25:32 kuli mtsogolo, sikuti sipadzakhala kulekanitsa, kapena kugaŵa, nthaŵiyo isanafike. Baibulo, pa Mateyu chaputala 13, limatchula ntchito ina yolekanitsa yoyambirira. Nzosangalatsa kuti buku la Ogwirizana m’Kulambiridwa kwa Mulungu Yekha Wowona, masamba 179-80, limafotokoza ntchitoyi pamutu wakuti “Kulekanitsidwa kwa Anthu”.a Bukulo limati: “Palinso zochitika zina zapadera zimene Yesu anazigwirizanitsa kwambiri ndi mapeto a dongosolo la zinthu. Chimodzi cha izi ndicho kulekanitsa ‘ana a ufumu’ kwa ‘ana a woipayo.’ Yesu analankhula za ichi m’fanizo lake la munda wa tirigu umene mdani anabzalamo namsongole wambiri.”

Bukulo linali kunena za fanizo la Yesu lopezeka pa Mateyu 13:24-30 ndipo lomasulidwa m’mavesi 36-43. Onani m’vesi 38 kuti mbewu yabwino ya tirigu imaimira ana a Ufumu, koma namsongole amaimira ana a woipayo. Mavesi 39 ndi 40 akusonyeza kuti pa “chimaliziro cha nthaŵi ya pansi pano”​—nthaŵi imene tikukhalamo tsopano​—namsongoleyo akusonkhanitsidwa. Kulekanitsidwa ndi kumtentha pomaliza pake, kumuwononga.

Fanizo limeneli likunena za Akristu odzozedwa (amene m’fanizo la nkhosa ndi mbuzi akutchedwa abale a Yesu). Komabe, mfundo njomveka yakuti ntchito yofunika kwambiri yolekanitsa ikuchitikadi nthaŵi zino, odzozedwa akulekanitsidwa kwa aja odzitcha Akristu komanso amene amasonyeza kuti ali “ana a woipayo.”

Yesu anapereka zitsanzo zina za anthu akuwagaŵa, kapena kuwalekanitsa. Kumbukirani kuti anati za njira yotakata yomka nayo kuchiwonongeko: ‘Ali ambiri amene aloŵa pa icho.’ (Mateyu 7:13) Mawu amenewo samangonena zimene zidzachitika pomaliza pake. Amanena zimene zinali kuchitika, monga zilili tsopano kuti ali oŵerengeka omwe akupeza njira yopapatiza yomka nayo kumoyo. Kumbukiraninso kuti potumiza atumwi ake, Yesu anatero kuti iwo adzapeza ena oyenera. Ena sadzakhala oyenera, ndipo atumwiwo anayenera kusansa fumbi la mapazi awo “likhale mboni ya paiwo.” (Luka 9:5) Kodi si zoona kuti zonga zimenezo zimachitika pamene Akristu akuchita utumiki wawo wapoyera lerolino? Ena amalabadira, pamene ena amakana uthenga wa Mulungu umene timawaperekera.

Nkhani za mu Nsanja ya Olonda zonena za nkhosa ndi mbuzi zinati: “Pamene chiweruzo chofotokozedwa m’fanizolo chili patsogolopa, ngakhale tsopano lino kanthu kena kofunika kwambiri kakuchitika. Ife Akristu tikuchita ntchito yopulumutsa moyo ya kulengeza uthenga wogaŵanitsa anthu. (Mateyu 10:32-39).” M’lemba limenelo la Mateyu chaputala 10, timaŵerenga kuti Yesu ananena kuti kumtsatira kudzachititsa magaŵano​—atate ndi mwana, mwana wamkazi ndi amake.

Pomaliza, abale odzozedwa a Kristu apititsa patsogolo ntchito yolalikira uthenga wa Ufumu padziko lonse lapansi. Pamene anthu aumva ndi kuchitapo kanthu, kuulandira kapena kuukana, amakhala akudzisonyeza okha mmene alili. Ife anthu sitingathe, ndipo sitiyenera, kunena kuti, ‘Munthu uyu ndi nkhosa; uja ndi mbuzi,’ m’lingaliro la Mateyu chaputala 25. Chikhalirechobe, kusonyeza kwathu anthu uthenga wabwino kumawapatsa mwaŵi wosonyeza kumene aima​—chimene ali ndi mmene amachitira ndi abale a Yesu. Chotero, monga umboni umene ukuchuluka pamlandu wa m’khoti, kulekanitsa amene akuchirikiza abale a Yesu ndi amene akukana kuwachirikiza kukuonekera. (Malaki 3:18) Monga momwe Nsanja ya Olonda inasonyezera, posachedwapa Yesu adzakhala pa chimpando chake ndi kupereka chilango, akumalekanitsa anthu mwachiweruzo m’lingaliro lake lonse, ku moyo kapena ku kudulidwa.

[Mawu a M’munsi]

a Lofalitsidwa mu 1983 ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena