Mbiri Yabwino Mtsogolo!
TONSEFE timachita chisoni pamene tilandira mbiri yoipa yotikhudza. Komanso, timasangalala pamene mbiri yabwino ifika—uthenga wathu wokondweretsa kapena wa okondedwa athu. Koma pamene mbiri yoipa iyambukira ena ndipo osati ife, kaŵirikaŵiri anthu amakhala ndi chidwi cha kudziŵa zambiri; ena amakondadi kufuna kudziŵa za tsoka la ena. Mwapang’ono zimenezi zimasonyeza chifukwa chake anthu amagula kwambiri nkhani za mbiri yoipa!
Kuchiyambi cha Nkhondo Yadziko II, panali chitsanzo champhamvu cha chidwi choipa pa tsoka limene anthu ena ali nalo. Sitima yapamadzi yonyamula zida zankhondo yaliŵiro ya matani 10,000, Graf Spee, inali imodzi ya sitima zankhondo za Ajeremani zonyaditsa mu 1939. Kwa milungu yambiri sitima yankhondo imeneyi inaononga sitima zamalonda za Magulu Ankhondo Ogwirizana ku nyanja za South Atlantic ndi Indian. Potsirizira pake, ngalaŵa zitatu zaliŵiro za Britain zinafunafuna ndi kuukira Graf Spee, zikumapha anthu ambiri ndi kuumiriza sitimayo kukakocheza kudoko la Uruguay la Montevideo kuti ikakonzedwe. Boma la Uruguay linalamula kuti sitima yankhondoyo ibwerere kunyanja komweko nthaŵi yomweyo, apo phuluzi lidzailanda. Chotero nkhondo yothira mdani inali yotsimikizirika.
Pomva zimenezi, gulu lina la anthu achuma la ku United States linahaya ndege, pamtengo wa $2,500 munthu aliyense, kuuluka kumka ku Uruguay kukaonerera nkhondo yosakazayo. Mowagwiritsa mwala, nkhondoyo sinachitike. Adolf Hitler anapereka lamulo lakuti Graf Spee ayiboole ndi kuimiza. Oonerera zikwi zambiri amene anafika padokopo akumayembekezera kuonerera chochitika cha nkhondo yowopsa yapanyanja, m’malo mwake anaona ndi kumva kuphulika kogonthetsa m’kutu kumene kunamiza Graf Spee, itabooledwa ndi amalinyero ake. Mtsogoleri wake anadzipha mwa kudziombera mfuti m’mutu.
Ngakhale kuti anthu ena ali ndi chidwi choipa pa ena, ochuluka angavomereze kuti amakonda mbiri yabwino m’malo mwa mbiri yoipa. Kodi simumalingalira mofananamo? Nangano nchifukwa ninji m’mbiri mwalembedwa mbiri yoipa yochuluka ndipo mbiri yabwino yochepa yokha? Kodi mkhalidwewo ungasinthidwe?
Zochititsa Mbiri Yoipa Yonse
Baibulo limasimba za nthaŵi ina pamene kunali mbiri yabwino yokhayokha. Mbiri yoipa inali chinthu chosadziŵika, chosamvedwa. Pamene Yehova Mulungu anamaliza ntchito zake za kulenga, pulaneti la Dziko Lapansi linali lokonzekera kulandira munthu ndi nyama kuti zisangalale. Nkhani ya Genesis imatiuza kuti: “Anaziona Mulungu zonse zimene adazipanga, ndipo, taonani, zinali zabwino ndithu.”—Genesis 1:31.
Kusakhalako kwa mbiri yoipa sikunakhalitse munthu atalengedwa. Mwana aliyense asanabadwe kwa Adamu ndi Hava, kunamveka mbiri yoipa ya kupandukira Mulungu ndi makonzedwe ake abwino a chilengedwe chadongosolo. Mwana wina wauzimu wa malo aakulu anapanduka pamalo ake ndipo anatha kupandutsa anthu aŵiri oyamba kuti agwirizane naye m’njira yake yachipanduko ndi yonyenga.—Genesis 3:1-6.
Kuchuluka kwa mbiri yoipa imene anthu amva kunayambira pamenepo. Mposadabwitsa kuti chiŵembu, chinyengo, mabodza, kunama, ndi kudyerekeza zasonyezedwa kwambiri m’mbiri yoipa imene yadzaza dziko lonse kuyambira pamenepo. Yesu Kristu mosapita m’mbali anaika liwongo lake pa Satana Mdyerekezi monga woyambitsa wa mbiri yoipa, akumauza atsogoleri achipembedzo a m’tsiku Lake kuti: “Inu muli ochokera mwa atate wanu Mdyerekezi, ndipo zolakalaka zake za atate wanu mufuna kuchita. Iyeyu anali wambanda kuyambira pachiyambi, ndipo sanaima m’choonadi, pakuti mwa iye mulibe choonadi. Pamene alankhula bodza, alankhula za mwini wake; pakuti ali wabodza, ndi atate wake wa bodza.”—Yohane 8:44.
Pamene anthu anawonjezereka m’chiŵerengero, mbiri yoipa inawonjezerekanso. Ndithudi, zimenezi sizimatanthauza kuti panalibe nthaŵi za kukondwera ndi za chimwemwe, pakuti panali zinthu zambiri m’moyo zimene zinachititsa chimwemwe. Komabe, mkhalidwe wa mavuto ndi chisoni wakhala woonekera m’mibadwo yonse ya anthu kufikira tsopano.
Pali chochititsa chinanso chachikulu cha mkhalidwe umenewu wachisoni. Chimenecho ndicho chikhoterero chathu cha choloŵa pa cholakwa ndi tsoka. Yehova mwiniyo amasonyeza chochititsa chosapeŵeka chimenechi cha mbiri yoipa mwa kunena kuti: “Ndingaliro ya mtima wa munthu ili yoipa kuyambira pa unyamata wake.”—Genesis 8:21.
Kodi Nchifukwa Ninji Pali Kufalikira kwa Mbiri Yoipa?
Komabe, pali chifukwa chake mbiri yoipa yafalikira m’zaka za zana la 20 zino. Chifukwa chimenechi chimafotokozedwa bwino kwambiri m’Baibulo, limene linaneneratu kuti anthu m’zaka za zana la 20 adzaloŵa m’nyengo yapadera yodziŵika kuti “masiku otsiriza” kapena “nthaŵi ya chimaliziro.” (2 Timoteo 3:1; Danieli 12:4) Ulosi wa Baibulo ndi kuŵerengera zaka kwa m’Baibulo zimadziŵikitsa “nyengo yamapeto,” imene inayamba mu 1914. Kaamba ka umboni wa m’Malemba watsatanetsatane wa zimenezi, chonde onani mutu 11 wa buku la Knowledge That Leads to Everlasting Life, lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.
Masiku otsiriza anali kudzayamba ndi chochitika chimene mosavuta chikachititsa mbiri yoipa kufalikira padziko lapansi. Kodi chimenecho chinali chiyani? Chinali kuponyedwa pansi kwa Satana Mdyerekezi ndi magulu ake a ziŵanda kuchokera kumwamba. Mungaŵerenge mafotokozedwe ake amphamvu ameneŵa a kuwonjezereka kwa mbiri yoipa yosapeŵeka pa Chivumbulutso 12:9, 12: “Chinaponyedwa pansi chinjoka chachikulu, njoka yokalambayo, iye wotchedwa Mdyerekezi ndi Satana, wonyenga wa dziko lonse; chinaponyedwa pansi kudziko, ndi angelo ake anaponyedwa naye pamodzi. . . . Tsoka mtunda ndi nyanja, chifukwa Mdyerekezi watsikira kwa inu, wokhala nawo udani waukulu, podziŵa kuti kamtsalira kanthaŵi.”
Chotero nthaŵi iliyonse imene yatsala kufikira pamene masiku otsirizawa afika pamapeto ake, tiyenera kuyembekezera mbiri yoipa kupitiriza ndipo ngakhale kuwonjezereka pa kuchuluka ndi ukulu wake.
Sizidzakhala Choncho Nthaŵi Zonse
Mosangalatsa kwa nzika za dziko lapansi, mkhalidwe wosautsa umene ukuchititsa mliri wa mbiri yoipa lerolino sudzakhalako kwa nthaŵi yonse. Kwenikweni, tingathe kunena ndi chidaliro kuti masiku a mbiri yoipa yopitiriza ayandikira mapeto ake. Mkhalidwewo suli wotayitsa mtima, ngakhale kuti ungaoneke monga wotero. Mapeto a mbiri yoipa yonse ayandikira ndipo adzafikadi mosalephera panthaŵi yake ya Mulungu.
Tingakhulupirire zimenezi chifukwa chakuti masiku otsiriza analoseredwa kuti adzafika pamapeto ake ndi chiwonongeko cha Mulungu ndi kuchotsedwa kwa zochititsa mbiri yoipa zonse. Adzachotsa anthu oipa osonkhezera nkhondo amene amakana kusintha ndi kutembenuka panjira yawo yoipa. Zimenezi zidzathera m’nkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu Wamphamvuyonse, yodziŵika kwambiri kukhala nkhondo ya Armagedo. (Chivumbulutso 16:16) Zimenezo zitangochitika, Satana Mdyerekezi ndi magulu ake a ziŵanda adzalandidwa mphamvu. Chivumbulutso 20:1-3 chimafotokoza za kumangidwa kwa Satana, woyambitsa mbiri yoipa yonse kuti: “Ndinaona mngelo anatsika kumwamba, nakhala nacho chifungulo cha phompho, ndi unyolo waukulu m’dzanja lake. Ndipo anagwira chinjoka, njoka yakaleyo, ndiye Mdyerekezi ndi Satana, nammanga iye zaka chikwi, namponya kuphompho, natsekapo, nasindikizapo chizindikiro pamwamba pake, kuti asanyengenso amitundu.”
Pambuyo pa zochitika zazikulu zimenezi, nthaŵi ya mbiri yabwino yatsopano idzafika padziko lapansi ndi nzika zake. Nzika zimenezi zidzaphatikizapo mamiliyoni ambiri amene adzapulumuka nkhondo yomaliza ya Armagedo ndi mabiliyoni amene adzauka kutulo tawo ta imfa kumanda. Mbiri yabwino koposa imeneyi yalongosoledwa m’buku lomaliza la Baibulo kuti: “Chihema cha Mulungu chili mwa anthu; ndipo adzakhalitsa nawo, ndi iwo adzakhala anthu ake, ndi Mulungu yekha adzakhala nawo, Mulungu wawo; ndipo adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena choŵaŵitsa; zoyambazo zapita.”—Chivumbulutso 21:3, 4.
Kodi mungaganizire za nthaŵi yachimwemwe imeneyo? Mtsogolo mwaulemererodi mmene simudzakhalanso mbiri yoipa. Inde, mbiri yoipa yonse idzakhala itatha ndipo sidzamvekanso. Pamenepo mbiri yabwino idzafala, ndipo idzachuluka kumka kuumuyaya.