Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w96 5/15 tsamba 29-31
  • Kodi Ndinu Mpainiya Wolinganiza Zinthu?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Ndinu Mpainiya Wolinganiza Zinthu?
  • Nsanja ya Olonda—1996
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Khalani Olimba Mwauzimu!
  • Kulinganiza Mathayo a Banja
  • Kulinganiza Zachuma
  • Apainiya Olinganiza Zinthu Ndiwo Dalitso Lenileni
  • Madalitso a Utumiki Waupainiya
    Nsanja ya Olonda—1997
  • Apainiya Amapereka ndi Kulandira Madalitso
    Nsanja ya Olonda—1994
  • Upainiya Umalimbitsa Ubwenzi Wathu Ndi Mulungu
    Nsanja ya Olonda—2013
  • Limbikirani Muutumiki Waupainiya
    Nsanja ya Olonda—1993
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1996
w96 5/15 tsamba 29-31

Kodi Ndinu Mpainiya Wolinganiza Zinthu?

NKHOPE ya tate ili ngwee kukondwa atatambasula manja pamene akuyembekezera kuti mwana wake wamkazi amene akuphunzira kuyenda anyamule mwendo wake nthaŵi yoyamba. Mwanayo atagwa, iye akumlimbikitsa kuyesanso. Akudziŵa kuti posapita nthaŵi adzaimirira ndi kulimba.

Momwemonso, mtumiki mpainiya watsopano amafunikira nthaŵi ndi chilimbikitso kuti apeze mkhalidwe wolinganiza zinthu wofunika kuti apambane monga mlaliki wa Ufumu wanthaŵi zonse. Apainiya ambiri amapitiriza kutumikira mwachimwemwe zaka zambiri. Oŵerengeka amaleka kulinganiza kwawo bwino zinthu chifukwa cha kusintha kwa mikhalidwe yawo kumene sanayembekezere. Ena amataya ngakhale chimwemwe chawo. M’dziko lina, 20 peresenti ya amene amayamba upainiya amasiya m’zaka ziŵiri zoyambirira za utumiki wawo wanthaŵi zonse. Kodi nchiyani chimene chingachotse mpainiya pa utumiki wake wosangalatsa koposawo? Kodi pali zimene angachite kupeŵa kubwevuka kumeneku?

Ngakhale kuti matenda, kusoŵa ndalama, ndi mathayo a banja zingachititse ena kusiya utumiki wanthaŵi zonse, chimene chakhumudwitsa ena ndicho kulephera kukhalabe olinganiza bwino mathayo awo osiyanasiyana achikristu. Kulingana kwa zinthu kumatanthauza “mkhalidwe pamene mbali ina kapena mphamvu siiposa inayo kapena siisiyana ndi zinazo.”

Yesu Kristu anasonyeza ophunzira ake mmene akanachitira ntchito yolalikira ndi kupanga ophunzira. Mu utumiki wake, anasonyezanso mmene pangakhalirebe kulinganiza zinthu. Yesu anasonyeza kuti atsogoleri achiyuda sanali kulinganiza zinthu, akumawauza kuti: “Mupereka limodzi la magawo khumi la timbewu tonunkhira, ndi katsabola, ndi la chitowe, nimusiya zolemera za Chilamulo, ndizo kuweruza kolungama, ndi kuchitira chifundo, ndi chikhulupiriro; koma zijazo munayenera kuzichita, osasiya izi zomwe.”​—Mateyu 23:23.

Choonadi chimenechi chimagwiranso ntchito mofananamo lerolino, makamaka pa utumiki waupainiya. Posonkhezeredwa ndi changu ndi cholinga chabwino, ena ayamba upainiya popanda kukonzekera mokwanira kapena kupenda zonse zophatikizidwamo. (Luka 14:27, 28) Enanso, utumiki wakumunda wawatanganitsa kwambiri kwakuti anyalanyaza mbali zina zofunika zachikristu. Kodi angathe bwanji kulinganiza zinthu ndi kukhalabe otero?

Khalani Olimba Mwauzimu!

Yesu sananyalanyaze mkhalidwe wake wauzimu. Ngakhale kuti makamu amene anadza kudzamva iye ndi kuchiritsidwa anafuna nthaŵi yake yochuluka, iye anapatula nthaŵi ya kupemphera mosinkhasinkha. (Marko 1:35; Luka 6:12) Lerolino kuchita upainiya molinganiza zinthu kumafunanso kugwiritsira ntchito mokwanira makonzedwe onse ofunika kuti tikhale olimba mwauzimu. Paulo anati: “Ndiwe tsono wakuphunzitsa wina, kodi ulibe kudziphunzitsa mwini?” (Aroma 2:21) Kungakhale kulakwa kwambiri kuwonongera nthaŵi yako yonse ukulalikira kwa ena pamene ukunyalanyaza kupatula nthaŵi ya phunziro laumwini lokwanira ndi ya kupemphera nthaŵi zonse.

Kumiko wakhala mpainiya zaka makumi aŵiri. Ngakhale kuti ali ndi ana atatu ndi mwamuna wosakhulupirira, iye m’kupita kwa zaka wapeza kuti nthaŵi yake yabwino koposa ya kuŵerenga ndi kuphunzira Baibulo imakhala asanapite kukagona. Pamene akuphunzira, amasamalira makamaka mfundo zimene angagwiritsire ntchito mu utumiki wakumunda kotero kuti utumiki wake wa tsiku ndi tsiku uzikhala watsopano ndi wosangalatsa. Apainiya ena achipambano amayambirira kudzuka ena onse m’banja asanadzuke kuti apezenso nyonga yauzimu m’maola abata mmaŵa. Mungapatule nthaŵi zina zoyenera kuti muzikonzekera misonkhano ndi kuyendera limodzi ndi zofalitsa zatsopano zachikristu. Ngati mukufuna kukhalabe ndi chimwemwe mu utumiki, simuyenera kufulumiza kapena kunyalanyaza phunziro laumwini.

Kulinganiza Mathayo a Banja

Makolo ochita upainiya afunikiranso kukumbukira kuti mbali yaikulu ya “chifuniro cha Yehova” kwa iwo imaphatikizapo kusamalira zofuna za banja lawo zakuthupi, za mtima, ndi zauzimu. (Aefeso 5:17, NW; 6:1-4; 1 Timoteo 5:8) Nthaŵi zina ngakhale mwamuna wokhulupirira ndi ena m’banja amawopa kuti sadzakhala akulandira chisamaliro ndi chichirikizo kwa mkazi wake ndi mayi wawo iye atayamba upainiya. Maganizo otero amawapangitsa kuchita mphwayi ndi chikhumbo chake cha kukhala mpainiya. Komabe, mwa kukonzekera bwino ndi kulingalirapo pasadakhale, kulinganiza zinthu kungakhalepobe.

Apainiya ambiri amayesetsa kuchita ntchito yawo yonse ya kulalikira pamene apabanja sali panyumba. Kumiko, wotchulidwa poyamba, amakhala ndi banja lake pakudya mfisulo, amatsazikana ndi mwamuna wake ndi ana mmaŵa, ndipo amafika panyumba iwo asanabwere. Lolemba iye amaphikiratu chakudya chochuluka kotero kuti azipuma ndi kudya chakudya limodzi ndi banja lake m’malo mwa kudzitangwanitsa m’khichini. Kuchita ntchito zingapo nthaŵi imodzi, monga ntchito zina zapanyumba pamene akuphika, kumamthandizanso. Mwa njira imeneyo, Kumiko amapeza ndi nthaŵi ya kuitanira mabwenzi a ana ake ndi kuwakonzera zabwino.

Pamene ana akukula kukhala achinyamata, iwo nthaŵi zambiri amafuna chisamaliro chochuluka kuchokera kwa makolo awo kuti alimbane ndi malingaliro atsopano, zikhumbo, zikayikiro, ndi nkhaŵa zowathetsa nzeru. Zimenezi zimafuna kuti kholo mpainiya likhale latcheru ndi kusintha ndandanda yake. Talingalirani za Hisako, mayi wa ana atatu wochita upainiya. Kodi anachita chiyani pamene mwana wake wamkazi wamkulu pa onse anayamba kusonyeza kusakondwa ndi mphwayi kaamba ka misonkhano yachikristu ndi utumiki wakumunda chifukwa cha chisonkhezero cha mabwenzi akudziko akusukulu? Chimene mwana wake wamkaziyo anafunikira kwenikweni ndicho kupanga choonadi kukhala chakechake ndi kutsimikizadi kuti kulekana ndi dziko ndiko njira yabwino koposa.​—Yakobo 4:4.

Hisako akunena kuti: “Ndinasankha kuphunziranso naye ziphunzitso zoyambirira m’buku la Kukhala ndi Moyo Kosatha tsiku ndi tsiku. Poyamba tinali kungophunzira mphindi zoŵerengeka, nthaŵi zambiri mwana wanga akumadandaula kuti m’mimba ndi mutu zikupweteka kwambiri itakwana nthaŵi ya kuphunzira. Koma ndinachititsa phunzirolo nthaŵi zonse. Patapita miyezi yoŵerengeka, mzimu wake unawongokera kwambiri, kwakuti panthaŵi yaifupi chabe anadzipatulira nabatizidwa.” Tsopano Hisako akusangalala ndi utumiki wake wanthaŵi zonse limodzi ndi mwana wake wamkazi.

Atate ochita upainiya afunikanso kusamala kuti sakutanganitsidwa kwambiri ndi kusamalira okondwerera m’munda ndi mathayo awo a mumpingo kwakuti alephera kusonyeza chikondi kwa ana awo omakula ndi kuwapatsa chitsogozo chimene afunikira. Izi si zinthu zimene mwamuna ayenera kutulira mkazi wake. Mkulu wotanganitsidwa wachikristu amene wakhala mpainiya nthaŵi yaitali amenenso ali ndi bizinesi amapatula nthaŵi ya kuphunzira ndi aliyense wa ana ake anayi mmodzi ndi mmodzi. (Aefeso 6:4) Ndiponso, amakonzekera misonkhano ya mlungu ndi mlungu pamodzi ndi banja lake. Apainiya olinganiza zinthu samanyalanyaza mabanja awo pa zinthu zakuthupi ndi zauzimu.

Kulinganiza Zachuma

Kaonedwe koyenera ka zofunika za tsiku ndi tsiku kalinso mbali ina imene apainiya ayenera kuyesetsa kukhala olinganiza zinthu. Panonso, tingaphunzire zambiri pa chitsanzo chabwino cha Yesu ndi uphungu wake. Anatsutsa kuda nkhaŵa kopambanitsa ndi zinthu zakuthupi. M’malo mwake, analimbikitsa ophunzira ake kuika Ufumu patsogolo, akumalonjeza kuti Mulungu adzawasamalira monga momwe amachitira ndi zolengedwa zake zina. (Mateyu 6:25-34) Mwa kutsatira uphungu wabwino umenewu, apainiya ambiri akhalabe mu utumiki wanthaŵi zonse zaka zambiri, ndipo Yehova wadalitsa kuyesayesa kwawo kupeza ‘chakudya cha tsiku ndi tsiku.’​—Mateyu 6:11.

Mtumwi Paulo analangiza Akristu anzake kuti ‘kulolera kwawo kudziŵike kwa anthu onse.’ (Afilipi 4:5, NW) Ndithudi, kulolera kudzafuna kuti tisamalire bwino thanzi lathu. Apainiya olinganiza zinthu amalimbikira kusonyeza kulolera m’moyo wawo ndi m’maganizo awo kulinga ku zinthu zakuthupi, podziŵa kuti ena amaona khalidwe lawo.​—Yerekezerani ndi 1 Akorinto 4:9.

Achichepere amene amayamba utumiki waupainiya ayenera kupeŵa kudyerera kupatsa kwa makolo awo. Ngati akukhala panyumba ya makolo, angakhale akupereka umboni wa kulinganiza zinthu kwawo ndi chiyamikiro mwa kugwirako ntchito zapanyumba ndi kupeza ntchito yamaola ochepa imene ingawatheketse kuthandizira kusamalira zapanyumba.​—2 Atesalonika 3:10.

Apainiya Olinganiza Zinthu Ndiwo Dalitso Lenileni

Mwina ndinu mpainiya amene akuyesetsa kukhalabe wolinganiza zinthu bwino. Khalani ndi chidaliro. Monga momwe mwana wamng’ono amafunikira nthaŵi yakuti aphunzire kuimirira ndi kuyenda, apainiya ambiri okhwima amanena kuti kunawatengera nthaŵi kuti akhale olinganiza zinthu posamalira mathayo awo onse.

Kuchita phunziro laumwini, kusamalira apabanja, ndi kudzipezera zofunika zawo zakuthupi zili zina za zinthu pa zimene apainiya amayesa kukhala olinganiza zinthu. Malipoti akusonyeza kuti apainiya ambiri amakwaniritsa mathayo awo m’njira yapadera. Iwo ndi dalitso kwa anthu ndipo amapereka thamo kwa Yehova ndi gulu lake.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena