Kodi Moyo Wanu Umalamuliridwa ndi Choikidwiratu?
“ALA NÒ DON.” Mawu ameneŵa amatanthauza kuti, “Nzochita za Mulungu,” m’chinenero cha Bambara ku Mali, West Africa. Mawu onga ameneŵa ngofala kumbali imeneyo ya dziko. M’chinenero chachiwolofu, mawuwo amati, “Yallah mo ko def” (Mulungu anachita zimenezo). Ndipo m’chinenero china cha Dogoni m’dzikolo, amati, “Ama biray” (Anachititsa ndi Mulungu).
Mawu ofanana ndi ameneŵa amapezeka m’maiko ena. Kaŵirikaŵiri timamva mawu onga akuti, “Nthaŵi yake inali itakwana” ndi, “Chinali chifuniro cha Mulungu” pamene imfa kapena tsoka lichitika. Ku West Africa, mawu onga akuti “Munthu amakonza, Mulungu amawononga” amalembedwa kwambiri pa galimoto zonyamula anthu ndipo amaikidwa pa zikwangwani m’masitolo. Kwa ambiri mawuwo angokhala okuluŵika. Komabe, kaŵirikaŵiri amasonyeza kuti kukhulupirira choikidwiratu nkwakukulu.
Kodi kukhulupirira choikidwiratu nchiyani? The World Book Encyclopedia imati ndi “chikhulupiriro chakuti zochitika zimayambitsidwa ndi mphamvu zimene anthu sangathe kuzilamulira.” Kodi “mphamvu” zimenezi nchiyani? Zaka zikwi zambiri zapitazo, Ababulo anakhulupirira kuti choikidwiratu cha munthu chinasonkhezeredwa mwamphamvu ndi kaimidwe ka nyenyezi pa kubadwa kwake. (Yerekezerani ndi Yesaya 47:13.) Agiriki anakhulupirira kuti choikidwiratu chinalamuliridwa ndi milingu itatu yachikazi yamphamvu imene inapota ulusi wa moyo, kuupima, ndi kuudula. Komabe, akatswiri azaumulungu a Dziko Lachikristu ndiwo amene anadza ndi lingaliro lakuti Mulungu mwiniyo ndiye amene amasankha choikidwiratu cha munthu!
Mwachitsanzo, Augustine “Woyera” anakana “malingaliro onyenga ndi oipa” a openda nyenyezi. Komanso, ananenetsa kuti “kuvomereza kuti Mulungu aliko, ndipo pa nthaŵi imodzimodziyo kukana kuti Iye amadziŵiratu zamtsogolo, ndiko kupusa kwenikweni.” Anati, Mulungu kuti akhaledi wamphamvuyonse, ayenera “kudziŵa zinthu zonse zisanachitike” wosasiya “chinthu chili chosaikidwiratu.” Komabe, Augustine ananenetsa mwamphamvu kuti ngakhale kuti Mulungu amadziŵiratu zinthu zonse zimene zidzachitika, anthu ali ndi ufulu wa kudzisankhira.—The City of God, Buku V, Mitu 7-9.
Zaka mazana ambiri pambuyo pake, katswiri wazaumulungu wachiprotesitanti John Calvin anafutukula nkhani imeneyi, akumatsutsa kuti pamene kuli kwakuti ena “[Mulungu] amawasankhiratu kukhala ana ndi oloŵa nyumba a ufumu wakumwamba,” ena amasankhidwiratu kudzakhala “olandira mkwiyo wake”!
Lerolino, kukhulupirira choikidwiratu kumaonedwa mwamphamvu kumbali zambiri za dziko lapansi. Lingalirani za chokumana nacho cha Ousmane, mnyamata wa ku West Africa. Iyeyo anali mmodzi wa ophunzira okhoza kwambiri kusukulu kwawo, koma pamene analemba mayeso, iyeyo analephera! Zimenezi zinatanthauza osati kungobwereza sukuluyo chaka china komanso kuvutika ndi manyazi pamaso pa a m’banja la kwawo ndi mabwenzi. Bwenzi lake lina linayesa kumtonthoza mwa kunena kuti chinali chifuniro cha Mulungu. Mofananamo amayi ake a Ousmane anaimba mlandu choikidwiratu chifukwa cha kulephera kwake.
Poyamba Ousmane anavomereza mokhutira kuyesayesa kwawo kumtonthoza. Ndi iko komwe, ngatidi kulephera kwake kunali chifuniro cha Mulungu, palibe chilichonse chimene akanachita kuti akuletse. Koma atate wake anaona nkhaniyo m’njira ina. Anauza Ousmane kuti kulephera kwake mayeso anakuchititsa yekha—osati Mulungu. Ousmane analephera kokha chifukwa chakuti ananyalanyaza maphunziro ake.
Kukhulupirira kwake choikidwiratu kutagwedezeka, Ousmane anasankha kudzifufuzira nkhaniyo. Tsopano tikukupemphani kuchita chimodzimodzi mwa kulingalira nkhani yotsatira.