Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
Kodi kungakhale bwino kwa Mkristu kukaonana ndi sing’anga wa nthenda zamaganizo?
Malipoti ochokera ku maiko ena akusonyeza kuti pali kuwonjezereka kwa matenda a maganizo ndi mtima mu “masiku otsiriza” ano. (2 Timoteo 3:1) Akristu amamva chisoni chachikulu pamene okhulupirira anzawo agwidwa nawo, koma amadziŵa kuti aliyense ayenera kudzisankhira kuti kaya ayenera kufunafuna machiritso a matenda ake, ndipo ngati zili choncho, kuti ndi mtundu wanji wa machiritsowo.a “Yense adzasenza katundu wake wa iye mwini.” (Agalatiya 6:5) Ena, amene amadwala kwambiri schizophrenia, kusemphana kwa mphamvu za m’minyewa, kuchita tondovi kwambiri, kuvutitsidwa maganizo ndi zinthu zosadziŵika, kudzivulaza ndi matenda ena ovutitsa a m’maganizo, atha kukhala ndi moyo wabwino pambuyo pa kupeza chithandizo choyenera cha akatswiri.
M’malo ena kufunafuna machiritso kwakhala kofala. M’zochitika zambiri wodwalayo samakhala ndi vuto lalikulu lamaganizo koma amakhala ndi vuto pa kulimbana ndi mkhalidwe wina wake m’moyo. Komabe, Baibulo ndilo limapereka thandizo labwino koposa pa kusamalira mavuto a moyo. (Salmo 119:28, 143) Kupyolera mu Baibulo, Yehova amapereka nzeru, kulingalira, ndi chidziŵitso chenicheni—zinthu zimene zimatilimbitsa m’maganizo ndi mumtima. (Miyambo 2:1-11; Ahebri 13:6) Atumiki okhulupirika a Mulungu angalankhule mwasontho nthaŵi zina chifukwa cha kuvutika mtima kwakukulu. (Yobu 6:2, 3) Yakobo 5:13-16 amalimbikitsa otero kuitana akulu kaamba ka thandizo ndi uphungu. Mkristu angakhale wodwala mwauzimu, kapena angakhale wovutitsidwa maganizo ndi mkhalidwe wina wosasinthika kapena ndi zipsinjo zazikulu, kapena mwinamwake angamve kukhala wochitiridwa chisalungamo. (Mlaliki 7:7; Yesaya 32:2; 2 Akorinto 12:7-10) Munthu wotero angapeze thandizo kwa akulu, amene ‘adzamdzoza ndi mafuta’—ndiko kuti, kumpatsa mwaluso uphungu wa Baibulo wotonthoza—ndiponso ‘kumpempherera.’ Chotulukapo chake? “Pemphero la chikhulupiriro lidzapulumutsa wodwalayo, ndipo Ambuye adzamuukitsa [pa kuchita kwake tondovi kapena pa kumva kwake kukhala wosiyidwa ndi Mulungu].”
Komabe, bwanji ngati kupsinjika ndi kusokonezeka maganizo kwa munthu kupitiriza mosasamala kanthu za chithandizo chaluso cha abusa auzimu? Ena amene ali mumkhalidwe umenewu asankha kukapimidwa m’thupi mosamalitsa. (Yerekezerani ndi Miyambo 14:30; 16:24; 1 Akorinto 12:26.) Mwinamwake vuto lakuthupi lingakhale chochititsa kupsinjika mtima kapena maganizo. Kuthetsa vutolo m’zochitika zina kwapereka mpumulo kwa munthu wodwala maganizoyo.b Ngati palibe vuto lakuthupi limene lapezedwa, sing’angayo, atapemphedwa, angavomereze kuti wodwalayo akaonane ndi sing’anga wa nthenda zamaganizo. Ndiyeno muyenera kuchitanji? Monga momwe tanenera kale, ichi nchosankha chimene munthu aliyense ayenera kudzipangira. Ena sayenera kusuliza kapena kugamula.—Aroma 14:4.
Ngakhale zili choncho, nzeru yeniyeni iyenera kugwiritsiridwa ntchito ndipo muyenera kusamala kuti simukuiŵala mapulinsipulo a Baibulo. (Miyambo 3:21; Mlaliki 12:13) Ponena za matenda akuthupi, odwala amayang’anizana ndi machiritso osiyanasiyana amene angasankhepo, kuyambira pamankhwala odziŵika kale ndi kale kufikira pamachiritso onga naturopathy, acupuncture, ndi homeopathy. Palinso mitundu yosiyanasiyana ya asing’anga a nthenda zamaganizo. Pakati pawo pali ochiritsa mwa kupima maganizo ndi enanso, amene amasanthula umoyo wakale wa wodwala kuti ayese kupeza zifukwa za kusinthasintha kakhalidwe kapena malingaliro opweteka. Ochiritsa mwa kupima maganizo mwa kakhalidwe amayesa kuthandiza wodwalayo kuphunzira kakhalidwe katsopano. Ena odziŵa za thanzi lamaganizo amakhulupirira kuti matenda ambiri amaganizo ayenera kuchiritsidwa ndi mankhwala.c Zamveka kuti ena amavomereza zakudya zakutizakuti ndi mavitameni.
Odwala ndi mabanja awo ayenera kusamala polingalira zosankha zimenezi. (Miyambo 14:15) Chotero, Profesa Paul McHugh, woyang’anira Department of Psychiatry and Behavioral Sciences pa Johns Hopkins University School of Medicine, ananena kuti using’anga wa nthenda zamaganizo “uli luso lazamankhwala losatsatirika bwino. Ulibe njira yosavuta yopezera umboni wa kupima ndi kuchiritsa kwake ngakhale pamene uchitidwa pa kusokonezeka kwa mbali zocholowana koposa za moyo wa munthu—malingaliro ndi kakhalidwe.” Mkhalidwe umenewu umasiya mpata wa njira zachilendo ndi chinyengo, limodzinso ndi machiritso a zolinga zabwino amene angachititse chivulazo chachikulu m’malo mwa kuchiritsa.
Tiyenera kutchulanso kuti, pamene kuli kwakuti akatswiri a nthenda zamaganizo ndi akatswiri a zamaganizo ali ndi madigirii aukatswiri a sukulu zapamwamba, ena ambiri opanda ziyeneretso zaukatswiri amakhala monga aphungu kapena ochiritsa popanda uyang’aniro. Anthu ena ataya ndalama zambiri akumapita kwa anthu opanda ziyeneretso ameneŵa.
Ngakhale kwa sing’anga wa nthenda zamaganizo wophunzitsidwa ndi woyeneretsedwa, pali zinthu zofunika kuzilingalira. Posankha dokotala wa zamankhwala kapena wa opaleshoni, tiyenera kutsimikizira kuti adzalemekeza malingaliro athu ozikidwa pa Baibulo. Mofananamo, kungakhale kwangozi kukaonana ndi sing’anga wa nthenda zamaganizo amene salemekeza malingaliro athu achipembedzo ndi a makhalidwe abwino. Akristu ambiri akulimbikira, mosasamala kanthu za mavuto a maganizo ndi mtima, kukhala ndi “mkhalidwe umodzimodziwo wa maganizo umene Kristu Yesu anali nawo.” (Aroma 15:5, NW) Ameneŵa amadera nkhaŵa moyenerera ponena za maganizo a aliyense amene angayambukire malingaliro kapena kakhalidwe kawo. Asing’anga ena amaona ziletso zilizonse zoikidwa ndi zikhulupiriro za m’Malemba monga zosafunikira ndipo zovulaza kwambiri thanzi lamaganizo. Iwo angavomereze, machitidwe otsutsidwa m’Baibulo, monga umathanyula kapena kusakhulupirika kwa muukwati.
Malingaliro ameneŵa akuphatikizidwa pa zimene mtumwi Paulo anatcha kuti “zotsutsana za ichi chitchedwa chizindikiritso konama.” (1 Timoteo 6:20) Amatsutsana ndi choonadi chonena za Kristu ndipo ali mbali ya ‘nzeru ndi chinyengo chopanda pake’ cha dziko lino. (Akolose 2:8) Muyezo wa Baibulo ngomveka: “Kulibe nzeru ngakhale luntha ngakhale uphungu wotsutsana ndi Yehova.” (Miyambo 21:30) Asing’anga a nthenda zamaganizo amene amanena kuti ‘zoipa nzabwino, ndipo zabwino nzoipa’ ali “mayanjano oipa.” M’malo mwa kuthandiza kuchiritsa maganizo ovutika, iwo ‘amaipsa makhalidwe okoma.’—Yesaya 5:20; 1 Akorinto 15:33.
Chotero Mkristu amene akuona kuti nkofunika kuonana ndi sing’anga wa nthenda zamaganizo ayenera kufufuza ziyeneretso, maganizo, ndi mbiri ya wochiritsayo ndi zotulukapo zimene zingakhalepo za machiritso alionse amene akuvomerezedwa. Ngati Mkristu wopsinjika maganizo sangachite zimenezi yekha, mwinamwake bwenzi lokhwima ndi lapafupi kapena wachibale angathe kuthandiza. Mkristu amene saali wotsimikizira ponena za nzeru ya machiritso akutiakuti angapeze kuti kulankhula ndi akulu mumpingo nkothandiza—ngakhale kuti chosankha chomalizira nchake (kapena cha makolo ake, kapena chosankha chogwirizana cha mwamuna ndi mkazi wake).d
Sayansi ingachite zambiri lerolino pa kuchotsa kuvutika kuposa kale. Chikhalirechobe, pali matenda ambiri—akuthupi ndi amaganizo omwe—amene ali osachiritsika panthaŵi ino ndipo tiyenera kuwapirira kupyola dongosolo ili la zinthu. (Yakobo 5:11) Pakali pano “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru,” akulu, ndi ena onse mumpingo amasonyeza chifundo ndi kupereka chichirikizo kwa odwala. Ndipo Yehova iye mwini amawalimbitsa kuti apirire mpaka nthaŵi yaulemereroyo pamene sikudzakhalanso kudwala.—Mateyu 24:45; Salmo 41:1-3; Yesaya 33:24.
[Mawu a M’munsi]
a Nthaŵi zina munthu angapemphedwe kufufuzidwa maganizo, mwinamwake pamene akufuna kuloŵa ntchito yapamwamba. Kaya munthuyo alola kufufuzidwa kumeneku kapena ayi nchosankha chaumwini, koma ziyenera kudziŵidwa kuti kufufuza maganizo sindiko kuchiritsa maganizo.
b Onani “Kupambana Nkhondo Yolimbana ndi Kuchita Tondovi,” m’kope la March 1, 1990 la Nsanja ya Olonda.
c Matenda ena amaganizo amaoneka kuti amamva mankhwala oyenera. Koma mankhwala ameneŵa ayenera kugwiritsiridwa ntchito mosamala moyang’aniridwa ndi asing’anga kapena akatswiri a nthenda zamaganizo aluso ndi achidziŵitso amene amagwiritsira ntchito mankhwala, popeza pangakhale zotulukapo zina zoipa kwambiri ngati saperekedwa pamlingo woyenera.
d Onani nkhani yakuti “Nsautso ya Maganizo—Pamene Yakantha Mkristu” m’kope la Nsanja ya Olonda ya October 15, 1988.