Umodzi wa Dziko Lonse—Kodi Udzafika Motani?
MONGA nyumba yowonongeka imene inasakazidwa ndi alendi osasamala, dongosolo la dziko lilipoli lingofunika chinthu chimodzi basi—kuphwasulidwa ndi kubweretsa dongosolo lina. Limeneli si lingaliro wamba la anthu olosera za chiwonongeko. Malinga nkunena kwa Baibulo, ndi lingaliro lokhalo lolondola. Chifukwa ninji?
Maziko a dongosolo la dziko lilipoli ngosalimba. Dziko lonse ladyedwa ndi chiswe ndipo lavunda. Mizati yake yachitsulo ikuchita dzimbiri. Zipupa zochirikizira zafooka. Denga lake likugwa. Mipope yake ya madzi ikuchucha. Magetsi ake sakugwira bwino ntchito ndiponso angachititse ngozi. Okhalamo ake amangokhalira kumenyana ndi kusakaza kotheratu nyumba yonse. Nyumba yonse imeneyo ndi malo ozungulira zadzala ndi tizilombo toluma ndipo tingaphe kapena kuvulaza anthu.
“Kutsetserekera Kudzenje la Manda”
Chifukwa cha mikangano yosatha ya ndale, umbombo, kuukirana, ndiponso udani waukulu wa mitundu ndi mafuko, “mtundu wonse wa anthu uli kutsetserekera kudzenje la manda,” monga momwe ananenera Gwynne Dyer. Kuzungulira dziko lonse, magulu ouma khosi—magulu opereka chisonkhezero, omenyera ufulu, magulu achifwamba, magulu aupandu padziko lonse, ndi ena—akufuna kukwaniritsa zolinga zawo zadyera ndipo aonetsa kuti angasokoneze mtendere uliwonse umene ungakhale padziko lapansi monga momwe akufunira. Monga alendi osasamala, iwo angavutitse munthu aliyense.
Komabe, malinga nkunena kwa othirira ndemanga ambiri, magulu ampatuko kapena anthu osayeruzika si okhawo amene amalepheretsa umodzi wadziko lonse. Cholepheretsa chachikulu ndicho maiko enieniwo. Maiko odzilamulira, akutero wolemba zankhondo S. B. Payne, Jr., akukhala “mumkhalidwe wosayeruzika wa dziko lonse.” Iwo amachita zilizonse zimene zimagwirizana ndi zofuna za dziko lawo basi, akumasamala pang’ono za zofuna za ena ngati amasamala nkomwe. Chotsatirapo chake, kuyambira kalekale ‘wina wapweteka mnzake pomlamulira.’—Mlaliki 8:9.
Ndithudi, maboma a maiko ena ayesa kuthetsa ukatangale ndi kuponderezana m’maiko awo, ndipo pamlingo wina, m’maiko enanso. Ayesa kukhazikitsa umodzi ndi maiko ena nthaŵi ndi nthaŵi. Koma ngakhale pamene maiko ena agwirizana ncholinga cholimbana ndi dziko lina loukira, pamakhala chikayikiro chakuti mwina anachita zimenezo ndi zikhumbo zadyera osati ncholinga chothandizanadi ayi. Zenizeni nzakuti maboma a anthu alibe njira yoti angathetseretu kusagwirizana kwa dziko. Gwynne Dyer akuti: “Lingaliro lakuti maiko onse a padziko lapansi ayenera kugwirizana poletsa kapena kulanga dziko lina loukira lodzigangira ndi lingaliro labwinodi, koma kodi ndani adzanena kuti dziko loukira ndi ili, ndiponso ndani adzataya ndalama ndi miyoyo pofuna kuletsa dzikolo?”
Ndithudi, dziko lina lingathe kuukira dziko linzake kokha ngati nzika zake zambiri zikugwirizana ndi kuukirako. Zochitika m’mbiri zimasonyeza mobwerezabwereza kuti si “dziko lodzigangira” lokha limene nzika zake zachirikiza atsogoleri ake, kaya alakwe kapena asalakwe. Zoonadi, anthu ochuluka padziko lapansi achita zimenezi. Iwo atsatira mwaumbuli “bodza, zinenezo ndi nkhani zachiwembu,” zofalitsidwa ndi atsogoleri ambiri a ndale ndi achipembedzo, malinga nkunena kwa magazini ya Time.
Utundu waipitsa malingaliro a anthu abwino ndi achifundo ndipo wawasonkhezera kuchita upandu wankhanza kwa amuna, akazi ndi ana a mtundu wina. Mwachitsanzo, ponena za Nkhondo Yadziko I, wolemba mbiri J. M. Roberts akufotokoza kuti: “China mwa zinthu zodabwitsa kwambiri zochitika mu 1914 nchakuti m’dziko lililonse anthu ambiri, a zipani zosiyanasiyana, zikhulupiriro ndi mafuko, modabwitsa, akuoneka kuti anapita kunkhondo mofunitsitsa ndi mwachimwemwe.” Kodi anthu asintha zochita zawo kuyambira nthaŵiyo? Ayi! Kuipa kwa “utundu wochita mwakhungu,” monga momwe mtolankhani Rod Usher anautchera, kukupitirizabe kusokoneza chiyembekezo chilichonse chakuti kungakhale umodzi wadziko lonse.
Zisonkhezero Zochokera Kwina Zikugwira Ntchito
Komabe, pali chinthu chachikulu cholepheretsa umodzi wadziko lonse. Baibulo limavumbula kuti pali zisonkhezero zochokera kwina zimene zikuchititsa zimenezi. Ameneŵa amadziŵika kuti ndi Satana Mdyerekezi ndi atumiki ake, ziŵanda. Malinga nkunena kwa Baibulo, Satana ndiye ‘mulungu wa nthaŵi ino ya pansi pano amene wachititsa khungu maganizo awo a osakhulupirira,’ kuti “chiwalitsiro cha Uthenga Wabwino wa ulemerero wa Kristu” chisawawalire.—2 Akorinto 4:4; Chivumbulutso 12:9.
Komabe, zimenezi sizimatanthauza kuti anthu alibe mlandu pa zochita zawo. Koma zimafotokoza chifukwa chake maboma a anthu sangakhazikitse dziko la umodzi weniweni. Malinga ngati Satana Mdyerekezi akhalapobe, iye adzasonkhezerabe amuna ndi akazi kukulitsa zimene Baibulo limatcha “ntchito zathupi,” zophatikizapo ‘madano, ndewu, zotetana.’—Agalatiya 5:19-21.
Boma la Dziko Lonse
Nanga tsono chothetsera vutoli nchiyani? Zaka mazana asanu ndi aŵiri zapitazo, Mtaliyana wina wandakatulo ndi wafilosofi Dante anafotokoza yankho lake. Iye anagogomezera kuti ndi boma la dziko lonse lokha limene lingadzetse mtendere ndi umodzi wa mtundu wa anthu. Anthu ambiri amaona kuti kuyembekezera mtundu uliwonse wa boma la dziko lonse ndiko kungodzinyenga chabe, si chinthu chakuti ungachidalire kwenikweni. “Boma la dziko lonse,” akumaliza motero Payne, wolemba wotchulidwa poyambirira, “nlosatheka lerolino.” Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti boma la dziko lonse limene lingakhazikitsidwe lingafunikire kutsimikiza kuthetsa zinthu ziŵiri zimene zimaoneka ngati sizingathetsedwe nkomwe ndi anthu, zomwe zili zakuti “boma la dziko lonse lidzayenera kuthetseratu nkhondo ndiponso silidzafunikira kukhala boma lopondereza la padziko lonse.”
Nzachidziŵikire kuti palibe boma la anthu limene lidzachita zimenezo. Komabe, Ufumu wa Mulungu wolamuliridwa ndi Yesu Kristu, ungathetse ndipo udzathetsa nkhondo. (Salmo 46:9, 10; Mateyu 6:10) Zoonadi, udzachotsa onse amene amayambitsa nkhondo. Mneneri Danieli akufotokoza kuti pamapeto a nthaŵi yoikidwiratu ndi Mulungu yakuti anthu alamulire dziko lapansi, maulamuliro a anthu ‘adzakhala ogaŵanika’ monga “chitsulo chosanganizika ndi dongo.” (Danieli 2:41-43) Zotsatirapo zake ndizo kusiyana maganizo m’zandale ndi mikangano yosatha. Komabe, Danieli akunena kuti Ufumu wa Mulungu “udzaphwanya ndi kutha maufumu awo onse [autundu ndi osagwirizana],” kapena maboma, nudzakhazikitsa Ufumu umene takhala tikuuyembekezera kwa nthaŵi yaitali wolamuliridwa ndi Yesu Kristu.—Danieli 2:44.
Sikungakhale kwanzeru kupanga malo abwino okhala anthu ngati anthu okhalira kupweteka ndi kusautsa anzawo apitirizabe kukhala padziko lapansi. Komabe, “ochita zoipa adzadulidwa.” (Salmo 37:1, 2, 9, 38; Miyambo 2:22) Choncho, Kristu adzachotsa onse amene amakana dala malamulo a Mulungu kapena amene amathandiza atsogoleri a dziko osokoneza. Adzawononga onse amene akuipitsa pulanetili. Mulungu akulonjeza “kuwononga iwo akuwononga dziko.”—Chivumbulutso 11:18.
Umenewu sudzakhala ulamuliro wopondereza wa padziko lonse. Yesu Kristu adzachita zonse “kaamba ka choonadi ndi chifatso ndi chilungamo” pamene alekanitsa abwino ndi oipa. (Salmo 45:3, 4; Mateyu 25:31-33) Ndiponso kuchita zimenezi sikuipa mtima kapena kungowononga, kugwiritsira ntchito ulamuliro mwankhanza. Ayi! Sizili monga nyumba yokongola yakalekale imene womangitsa nyumba zatsopano wadyera akufuna kuigwetsa. Zidzafanana ndi kugwetsa nyumba zosakazika kosaneneka ncholinga chomangapo nyumba zina zooneka bwino ndi zosamalika.
Koma bwanji nanga za zisonkhezero zochokera kwina zimene zinali kupangitsa kusagwirizana kumeneku kumbuyoku? Kodi izo zidzakhala ndi ufulu woloŵereranso m’dongosolo latsopano limeneli kotero kuti okhalamo ake adzayambiranso machitachita awo osakaza, kumenyana ndi anzawo amene akukhala nawo ndi kuvutitsa aliyense? Kutalitali. Kuchotsa ndi kukonzanso kumeneku kudzakhala komaliza ndi kotheratu. “Nsautso siidzauka kaŵiri.”—Nahumu 1:9.
Baibulo limayerekezera kuwonongedwa kotheratu kwa Satana ndi kutentha zinyalala. Limanena kuti “Mdyerekezi wakuwasokeretsa [anthu okhala padziko lapansi] anaponyedwa m’nyanja ya moto ndi sulfure.” (Chivumbulutso 20:10) Ndi fanizo lamphamvu chotani nanga! Talingalirani, chiwonongeko choyerekezeredwa osati ndi chotenthera china chaching’ono chochepa mphamvu koma chiwonongeko chofanana ndi nyanja yonse yamoto, yotha kutentha ndi kuwonongeratu chilichonse choipa ndi chodetsedwa. Palibe aliyense, kaya ndi munthu kapena chiŵanda, amene adzaloledwa kupitirizabe kuchita zinthu zosokoneza dongosolo la dziko lonse, amene amanyalanyaza malamulo a Mulungu osiyanitsa chabwino ndi choipa, kapena amene amavutitsa anthu anzawo. Onse osokoneza umodzi adzatha psiti!—Salmo 21:9-11; Zefaniya 1:18; 3:8.
Anthu Ogwirizana Ochokera m’Mitundu Yonse
Opulumuka kuyeretsa kwakukulu kumeneku adzakhala a “khamu lalikulu . . . ochokera mwa mtundu uliwonse, ndi mafuko ndi anthu ndi manenedwe.” (Chivumbulutso 7:9) Kusiyana kwa mitundu ndi mafuko sikudzawagaŵanitsa. Adzakhala ataphunzira kukhala pamodzi mogwirizana ndi mwamtendere. (Yesaya 2:2-4) Ndipo chosangalatsa kwambiri nchakuti, ameneŵa adzakhala pamodzi ndi anthu amene anali pa pulanetili kalekale amene adzabwezeretsedwa m’dziko lapansi loyera mwa makonzedwe odabwitsa a chiukiriro.—Yohane 5:28, 29.
Kodi mukufuna kudzakhala m’dziko lotero? Okhawo amene amachita mogwirizana ndi zifuno za Mulungu ndiwo amene adzakhalamo, ndipo zifuno zakezo zinafotokozedwa bwino lomwe m’Baibulo. (Yohane 17:3; Machitidwe 2:38-42) Mboni za Yehova zidzakhala zokondwa kukuthandizani kuphunzira zimene Mulungu amafuna kotero kuti mukhale ndi chiyembekezo cha kusangalala ndi moyo kosatha m’dziko lapansi la umodzi weniweni.
[Chithunzi patsamba 7]
Boma lolamuliridwa ndi Yesu Kristu lidzadzetsa dziko laumodzi