Umodzi Wa Dziko Lonse—Kodi Udzakhalapodi?
“NGATI tidzapambana m’mibadwo ingapo ikudzayo kusanduliza dziko limene tikukhalamo la maiko odzilamulira okha kuti likhaledi chitaganya chimodzi cha padziko lonse, . . . pamenepo tidzakhala titathetsanso khalidwe lakalekaleli lankhondo . . . Komabe, ngati tidzalephera, mwinamwake kudzakhala . . . kopanda chitukuko.” Akutero wolemba za mbiri yankhondo Gwynne Dyer m’buku lake lakuti War.
Mbiri yolembedwa, akutero Dyer, yadzala ndi nkhani za maiko ndi magulu ena amphamvu amene anathirana nkhondo kuti athetse mikangano yawo. Kusagwirizana kwawo kunatayitsa miyoyo ya anthu mamiliyoni ambiri okhudzidwa. Mawu a Mfumu Solomo a mmene zimenezi zinakhudzira anthu a m’tsiku lake ngoonabe lerolino. Iye analemba kuti: “Ndinabweranso tsono ndi kupenyera nsautso zonse zimachitidwa kunja kuno; ndipo taona, misozi ya otsenderezedwa, koma analibe wakuwatonthoza; ndipo akuwatsendereza anali ndi mphamvu koma iwowa analibe wakuwatonthoza.”—Mlaliki 4:1.
Lerolino, monga momwe wolemba mbiri wotchulidwa pamwambayo akufotokozera, kuwonjezera pa kuchitira chifundo “misozi ya otsenderezedwa,” palinso chifukwa china chofunira kupeza njira ina yosandulizira dzikoli la maiko odzilamulira okha kukhaladi chitaganya chimodzi cha padziko lonse: Chitukuko chenichenicho chili pafupi kutha! Nkhondo zamakono zikusonyeza kuti zidzawononga dziko lililonse limene likuloŵetsedwamo ndipo sipadzakhala opulumuka.
Kodi Umodzi wa Dziko Lonse Uli Pafupi?
Kodi pali ziyembekezo zotani ponena za umodzi wadziko lonse? Kodi anthu angathetse zogaŵanitsa anthu zimene zikusakaza dziko lapansi? Ena amaganiza choncho. Mkonzi wa nkhani zachitetezo wa nyuzipepala ya ku Britain ya Daily Telegraph, John Keegan, akulemba kuti: “Mosasamala kanthu za msokonezo ndi kusatsimikizika kwa zinthu, nzothekabe kuona pang’onopang’ono kuthekera kwa dziko lopanda nkhondo.”
Kodi chikumpatsa chiyembekezo chimenechi nchiyani? Nchifukwa ninji ambiri ali ndi chiyembekezo ngakhale kuti anthu akhala akuchita nkhondo kwa nthaŵi yaitali ndiponso alephera mwachionekere kudzilamulira mwachipambano? (Yeremiya 10:23) ‘Mtundu wa anthu ukutukuka. Mbiri imasonyeza kuti chitukuko chakhala chikupitabe patsogolo,’ ena anatero nthaŵi ina. Ngakhale lerolino, ambiri amakhulupirira kuti malingaliro abwino achibadwa a munthu adzathetsa kuipa. Kodi chiyembekezo chimenecho chidzakwaniritsidwa? Kapena changokhala malingaliro ogwiritsa mwala amene adzawonjezera kukhumudwa? M’buku lake lakuti Shorter History of the World, wolemba mbiri J. M. Roberts analemba molondola kuti: “Sitinganene kuti dziko lidzakhala labwino mtsogolomu. Palibenso chiyembekezo chakuti kuvutika kwa anthu kudzatha, kapena maziko alionse okhulupirira kuti zimenezi zingachitike.”
Kodi pali zifukwa zabwino zokhulupirira kuti anthu ndi maiko adzathetsadi kusakhulupirirana kwawo ndi mikangano yochititsa magaŵano? Kapena kodi pakufunika chinachake choposa zoyesayesa za anthu? Nkhani yotsatira idzayankha mafunso ameneŵa.
[Mawu a Chithunzi patsamba 2]
Dziko lapansi pachikuto: Mountain High Maps® Copyright © 1995 Digital Wisdom, Inc.