Kodi Amachitiranji Zimenezi?
CHAKA chilichonse Mboni za Yehova zikwizikwi kuzungulira dziko lonse lapansi zimasonkhana pamisonkhano yachigawo. Pamenepo, iwo amasangalala ndi mayanjano ndipo amamvetsera programu yabwino kwambiri ya malangizo a m’Baibulo. Ena amachita kuvutikira kuti akapezeke pamisonkhano imeneyi. Mwachitsanzo, chaka chatha ku Malaŵi, mwamuna wina ndi mkazi wake azaka zakubadwa za m’ma 60, pamodzi ndi mwana wawo wamwamuna ndi mkazi wake ndi mwana wake, anayenda mtunda wamakilomita 80 panjinga kuti akapezeke pamsonkhano wachigawo. Ananyamuka kumudzi kwawo ndi nthaŵi ya 6 koloko mmaŵa ndipo anakafika pamalo a msonkhano patapita maola 15.
Ku Mozambique, gulu lina linayenda masiku atatu panjinga kuti akafike pamsonkhano wachigawo. Usiku wina, pamene anali pamsasa pamtetete, anamva mikango ikubangula chapafupi nawo. Ngakhale kuti anaponya nkhuni chakumene kunali nyamazo, mikangoyo sinachoke mpaka mbandakucha. Mboni inanso imene inali kupita kumsonkhano umodzimodziwo inakumana ndi mkango panjira maso ndi maso. Anangoima duu osayenda mpaka mkangowo utachoka. Pamsonkhanowo Mboni zimenezi zinasimba mosangalala mmene ‘zinalanditsidwira mkamwa mwa mkango.’—2 Timoteo 4:17.
Anthu ambiri mwa Mboni za Yehova amachita kuvutikira kuti akapezeke pamsonkhano wachigawo kapena ngakhale pamisonkhano yampingo ya mlungu ndi mlungu kuti akalambire. Chifukwa ninji? Nkhani zotsatirazi zidzakuthandizani kumvetsetsa chifukwa chimene kusonkhana pamodzi kulili kofunika kwambiri.